Nyimbo 176
Kulandira Mfumu Yakudzayo!
1. Nthaŵi yafika yakuti tilandire
M’lungu Wamphamvuyonse mwini zinthu.
Iye ndi Mwanayo aika mitundu,
Ndipo miyamba ikumveka ndi nyimbo yankhondo.
‘Dzutsani mitu, O zipata’ mokondwa;
Mfumu yaikulu idzapambana.
Nthaŵi ya magulu a Yehova yadza
Kudzetsera anthu Zaka Chikwizo.
Adzasonyeza mphamvu mu Ufumuwo,
Ulamuliro wake udzafalikira.
2. Ambuye Mfumu, Wamkuludi, Yehova,
Wadzetsa Ufumu womwe sudzatha.
Akuyenereradi kulandiridwa;
Tidziŵitse Mfumuyo kuti timaitamanda.
Zitseguketu, zipata! Mbiri yadza;
Nchikondwerero kuimba limodzi.
‘Yehova ngwamphamvu wamkulu munkhondo.’
Timumvetsere ndi kudza ndi mphatso,
Nthaŵi yadza kudalitsa oyanjidwa.
‘Tikulandirenitu!’ Mfumu yakudzanu.