Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 5 tsamba 38-45
  • Mbaliŵali Zodalirika za Mtsogolo mwa Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbaliŵali Zodalirika za Mtsogolo mwa Anthu
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZITSANZO ZOLOSERA ZOKONDWERETSA
  • KODI ZONSEZO ZINALINGANIZIDWIRATU?
  • Khalani ndi Chikhulupiriro M’mawu Aulosi a Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Yehova Wachita Zimene Anali Kuganiza”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Maulosi Amene Anakwaniritsidwa
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Anaphunzira pa Zolakwa Zake
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 5 tsamba 38-45

Mutu 5

Mbaliŵali Zodalirika za Mtsogolo mwa Anthu

TIRI ndi zifukwa zamphamvu zodalirira zimene Baibulo limatiuza ponena zamtsogolo. Maulosi ake saali ozikidwa pa kuyerekezera kwa anthu amene apenda mikhalidwe ndiyeno naneneratu. “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kalelonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.” (2 Petro 1:​20, 21) Chifukwa cha chimenecho, ulosi wa Baibulo, watsimikizira kukhala wolondola pa chinthu chirichonse.

2 Lidaneneratu kuuka ndi kugwa kwa maulamuliro a dziko mwa maina​—⁠Babulo, ndi Aperisi ndi Grisi. Linalengeza pafupifupi zaka mazana aŵiri pasadakhale mmene Babulo akagwera ndi dzina la wowagonjetsa wake. Zimenezi zinakwaniritsidwa ndendende. Linaneneratu kuti mzinda wa Babulo potsirizira pake ukakhala bwinja, wosakhalidwanso ndi anthu. Mkhalidwewo ukupitirizabe motero kufikira lerolino. (Danieli 8:​3-8, 20-22; Yesaya 44:27–45:2; 13:​1, 17-20) Mitundu ina yosatchulidwa dzina m’Baibulo inalongosoledwa pasadakhale mwatsatanetsatane kwambiri chakuti anthu ophunzira bwino angaidziŵe mosavuta.

3 Komabe, kuyenera kuzindikiridwa kuti, pali mitundu yambiri ya mawu olosera m’Baibulo. Tawona kale zimenezi mogwirizana ndi zozizwitsa za Yesu, zimene zinatumikira monga zisonyezero za zimene anthu adzawona mu Ufumu wa Mulungu. Mbali zina za Malemba zimene sizingagwiritsire ntchito chinenero chimene chimamveka ngati ulosi zimakhalanso ndi zinthu zolosera.

ZITSANZO ZOLOSERA ZOKONDWERETSA

4 Mwachitsanzo, bukhu Labaibulo la Ahebri, limatsegulira maso athu ku tanthauzo lolosera la zinthu zimene woŵerenga wamba angaziwone kukhala mbiri chabe. Limavumbula kuti “Chilamulo [cha Mose] chiri ndi mthunzi wa zinthu zabwino zirinkudza.”​—⁠Ahebri 10:​1, NW.

5 Nthaŵi zina zinthu zinagwiritsiridwa ntchito kupanga zitsanzo zolosera. Mwachitsanzo, ponena za hema wopatulika, kapena chihema, chopangidwa ndi Mose motsogozedwa ndi Yehova, limodzi ndi mautumiki ochitidwapo, wolemba wouziridwa ndi Mulungu wa Ahebri akulongosola kuti chinali “chisonyezero chenicheni ndi mthunzi wa zinthu zakumwamba.” Chinaimira kachisi wa Yehova wamkulu wauzimu, wopatulikitsa amene ali kumwamba. Chotero, “pamene Kristu anadza mkulu wa ansembe wa zinthu zabwino zimene zachitika, mwa chihema chokulirapo ndi changwiro kwambiri chosamangidwa ndi manja, ndiko kuti osati cha chilengedwe chino, analoŵa, ayi, osati ndi mwazi wa mbuzi ndi wa ana a ng’ombe, koma ndi mwazi wake, kamodzi, kunthaŵi zonse m’malo opatulika natilandirira chiombolo chosatha. . . . Kristu sanaloŵe, m’malo opatulika opangidwa ndi manja, amene ali chitsanzo cha enieni, m’mwamba momwe, tsopano kukawonekera pamaso pa nkhope ya Mulungu chifukwa cha ife.” (Ahebri 8:​1-5; 9:​1-14, 24-28, NW) Mapindu aakulu amadza kwa Akristu kuchokera ku zinthu zauzimu zolongosoledwa panopa, ndipo kuyamikira zimenezi kuyenera kusonyezedwa m’kakhalidwe kathu.​—⁠Ahebri 9:14; 10:​19-29; 13:​11-16.

6 Anthu otchulidwa m’Malembawo amatumikiranso monga maphiphiritso. Pa Agalatiya 4:​21-31 chitsanzo chatsatanetsatane cha zimenezi chalongosoledwa m’chochitika cha mkazi wa Abrahamu Sara (wonenedwa kukhala wolingana ndi “Yerusalemu wakumwamba”) ndipo mdzakaziyo Hagara (wogwirizanitsidwa ndi “Yerusalemu wamakono” wapadziko lapansi) ndi ana awo. M’chochitika china Yesu anathandiza ophunzira ake kuzindikira kuti Eliya mneneriyo anali ndi wofanana naye Yohane Mbatizi, amene, mofanana ndi Eliya, anali wopanda mantha m’kuvumbula machitidwe achipembedzo onyenga.​—⁠Mateyu 17:​10-13.

7 Solomo, wodziŵika ndi nzeru yake ndi kulemera ndi mtendere wa ulamuliro wake, moyenerera anaphiphiritsira Yesu Kristu. (1 Mafumu 3:28; 4:25; Luka 11:31; Akolose 2:⁠3) Angakhale cholembedwa mu Genesis chonena za kukumana kwa Abrahamu ndi Melikizedeke chiri chachidule kwambiri, Salmo 110:​1-4, NW limasonyeza kuti, nachonso, nchodzala ndi tanthauzo, chifukwa chakuti Mesiya akakhala “wansembe kosatha molingana ndi mkhalidwe wa Melikizedeke,” ndiko kuti, iye akalandira unsembe wake mwa kuikidwa mwachindunji ndi Mulungu, osati chifukwa cha banja m’limene akabadwira. Pambuyo pake, kalata ya kwa Ahebri imafotokoza zimenezi ndipo imagwirizanitsa kuzindikiridwa kwa chowonadi chotero ndi uchikulire Wachikristu, mkhalidwe wofunika kwa iwo amene akufunafuna kukondweretsa Mulungu.​—⁠Ahebri 5:​10-14; 7:​1-17.

8 Nkwachiwonekere kuti zitsanzo zoloserazo zimaphatikizapo zambiri koposa malo antchito kapena udindo wa anthu. Zimaphatikizapo zokumana nazo zawo m’moyo. Panyengo ina pamene atsogoleri achipembedzo Achiyuda anasoyeza kusakhulupirira kwawo, Yesu anati kwa iwo: “Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri; pakuti monga Yona anali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.” (Mateyu 12:​38-40; Yona 1:17; 2:10) Komabe, Yesu sananene kuti chinthu chirichonse m’moyo wa Yona chinaphiphiritsira chimene iyemwini akakumana nacho. Pamene anapatsidwa ntchito ndi Yehova, Yesu sanathawe, monga momwe Yona anayesera kuthaŵira ku Tariso. Koma monga momwe Yesu anasonyezera, chokumana nacho cha Yona m’mimba mwa chinsomba chinaphatikizidwa m’cholembedwa Chabaibulo chifukwa chakuti chinatumikira kupereka zinthu zolosera zonena za imfa ya Yesu ndi chiukiriro.​—⁠Mateyu 16:​4, 21.

9 Nyengo zina za m’mbiri zimaperekanso mbaliŵali zolosera zimene ziri zokondweretsa kwambiri kwa ife. Potchula nthaŵi yofikitsa ku kuvumbuluka kwake m’mphamvu Yaufumu, Yesu anayerekezera ndi nyengo zina ziŵiri pamene chiweruzo cha Mulungu chinaperekedwa pa anthu oipa. Anatchula “masiku a Nowa” ndi “masiku a Loti” kukhala atanthauzo, makamaka akumagogomezera kutanganitsidwa kwa anthu panthaŵiyo ndi zochitika za moyo zatsiku ndi tsiku. Anatilimbikitsa kuchitapo kanthu mofulumira ndi kusacheuka tiri ndi kukhumbira zinthu zosiyidwa mmbuyo, monga momwe mkazi wa Loti anachitira. (Luka 17:​26-32) M’kalata yachiŵiri youziridwa ya mtumwi Petro zinthu zinanso zatanthauzo zikutchulidwa​—⁠kusamvera kwa angelo Chigumula chisanakhale, ntchito yolalikira ya Nowa, chisoni chimene Loti anamva chifukwa cha kumwerekera m’kuswa malamulo kwa anthu a Sodomu, chenicheni chakuti mwa kudula oipa m’nthaŵi yake yokwanira Mulungu anali kupereka chitsanzo cha zinthu zirinkudza, ndi umboni wakuti Mulungu angakhoze ndipo mosalephera adzapulumutsa atumiki ake okhulupirika.​—⁠2 Petro 2:​4-9.

10 Pamene maulosi akwaniritsidwa, zimenezi sizitanthauza kuti tsopano mawuwo angokhala chokondweretsa cha m’mbiri. Ponse paŵiri kudziŵitsidwa kwapasadakhale kwa chimene chinayenera kuchitika ndi mmene chinakwaniritsidwira kaŵirikaŵiri zolosera zochitika zazikuludi mtsogolo. Zimenezi ziri choncho ndi zimene zalembedwa ponena za Babulo wakale, ulamuliro umene unali wachipembedzo mwapadera ndi umene chisonkhezero chake chikali kumvedwabe padziko lonse lapansi m’nthaŵi yathu. Ngakhale kuli kwakuti Babulo anagwetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi mu 539 B.C.E., bukhu la Chivumbulutso, lolembedwa chakumapeto kwa zaka za zana loyamba C.E., limagwiritsira ntchito kanenedwe ka mneneri Yeremiya ndipo limasonya ku kukwaniritsidwanso kwamtsogolo kwa maulosi, ponena za Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wachipembedzo chonyenga. Monga zitsanzo za zimenezi, yerekezerani Chivumbulutso 18:4 ndi Yeremiya 51:​6, 45; Chivumbulutso 17:​1, 15 ndi 16:12 ndi Yeremiya 51:13 kudzanso 50:38; Chivumbulutso 18:21 ndi Yeremiya 51:​63, 64.

11 Mofananamo, zochita za Yehova ndi ufumu wa mafuko khumi wampatuko wa Israyeli ndipo ndi mafumu ndi ansembe opanda chikhulupiriro a ufumu wamafuko aŵiri wa Yuda nzolosera. Ponse paŵiri maulosi amene anagwirira ntchito ku maufumu akale amenewo ndi kukwaniritsidwa kwawo, zolembedwa m’Malemba, zimapereka chithunzi chowoneka bwino cha mmene Mulungu adzachitira ndi Dziko Lachikristu lamakono, limenenso limati likutumikira Mulungu wa Baibulo koma limene limaswa moipa malamulo ake olungama.

12 Chifukwa cha chimenecho, zolembedwa zonsezi, nzatanthauzo lerolino. Zimatithandiza kuzindikira mmene Mulungu amawonera mikhalidwe m’nthaŵi yathu ndi chimene ife eni tiyenera kuchita kuti tipulumuke chisautso chirinkudzacho. Motero tikuthandizidwa kuzindikira mokwanira kwambiri chenicheni chakuti “lemba lirilonse . . . lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.”​—⁠2 Timoteo 3:​16, 17.

KODI ZONSEZO ZINALINGANIZIDWIRATU?

13 Kodi tiyenera kuzindikira m’zonsezi kuti khalidwe la anthu ndi mitundu lolembedwa m’Baibulo lonse linalinganizidwiratu ndi Mulungu kotero kuti likakhala ndi tanthauzo lolosera? Nkwachiwonekere kuti Mulungu mwiniyo anachita ndi atumiki ake kalero mu mkhalidwe wina kuti apereke chitsanzo cha zinthu zokulirapo zimene analingalira kaamba ka mtsogolo. Koma bwanji ponena za machitidwe a anthu? Ena a iwo anachita machimo aakulu. Kodi Mulungu anawachititsa kuchita zimenezi kuti apange cholembedwa Chabaibulo? Wolemba Baibulo Wachikristu Yakobo akuyankha: “Munthu poyesedwa, asanena, ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo iyemwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Mulungu sanawachititse kuchita zolakwa kotero kuti zitsanzo zolosera zipangidwe.

14 Musaiŵale kuti Yehova ndi Mlengi wa anthu. Iye amadziŵa mmene tapangidwira ndi chimene chimachititsa anthu kuchita mmene iwo amachitira. (Genesis 6:5; Deuteronomo 31:21) Iye anganeneretu molondola chotulukapo kwa anthu amene akugwirizana ndi ziphunzitso zake zolungama ndi zimene zidzakhala zotulukapo kwa iwo amene amayesa kunyalanyaza kufunikira kwawo Mulungu kapena amene amaipitsa njira zake. (Agalatiya 6:​7, 8) Iye amadziŵa kuti Mdyerekezi adzapitirizabe kugwiritsira ntchito njira zofanana ndi zija zimene anawagwiritsira ntchito kale. Yehova amadziŵanso chimene iye mwini adzachita pamikhalidwe yakutiyakuti, kuti adzachita mogwirizana ndi mikhalidwe yapamwamba yachilungamo, kupanda tsankho, chikondi ndi chifundo, imene iye wasonyeza nthaŵi zonse. (Malaki 3:⁠6) Popeza zifuno za Yehova nzotsimikizirika kukwaniritsidwa, iye anganeneretu zotulukapo ndi njira zimene adzatsatira kuti azikwaniritse. (Yesaya 14:​24, 27) Motero iye anatha kusankha zochitika kuchokera m’miyoyo ya anthu ndi mitundu ndi kuchititsa zimenezi kuphatikizidwa m’Baibulo kuti zipereke mbaliŵali za chimene mtsogolo mudzakhala.

15 Chifukwa cha chimenecho, moyenerera, atasimba zochitika za m’mbiri ya Israyeli, mtumwi Paulo anati kwa Akristu anzake: “Izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi yapansi pano adafika pa ife.” (1 Akorinto 10:11) Ndipo kumpingo Wachikristu mu Roma iye adalemba kuti: “Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwachipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:⁠4) Motero pamene tizindikira kuti zolembedwa za Baibulo ziri zoposa mbiri chabe, tingayambe kupezamo mbaliŵali zodabwitsa za mtsogolo mwa anthu.

[Mafunso]

1. Kodi nchifukwa ninji ulosi wa Baibulo nthaŵi zonse umatsimikizira kukhala wolondola?

2. Perekani zitsanzo za maulosi onena za zochitika zadziko.

3. Kodi pali maulosi amene sanalongosoledwe m’mpangidwe wa zonenedweratu?

4. Kodi ndimotani mmene timagalamutsidwira kutanthauzo lolosera la Chilamulo cha Mose?

5. Kodi nchiyani chimene chimafotokoza mwa fanizo kuti zinthu zingaphiphiritsire kanthu kena kokulirapo?

6. Kodi nditanthauzo lolosera lotani limene limagwirizanitsidwa ndi anthu pa (a) Agalatiya 4:​21-31? (b) Mateyu 17:​10-13?

7. Kodi ndim’mbali zotani zimene Yesu Kristu anaphiphiritsiridwa ndi (a) Solomo? (b) Melikizedeke?

8. (a) Kodi ndichitsanzo chotani chimene chimasonyeza kuti zokumana nazo m’moyo zingakhale zolosera? (b) Kodi mbali iriyonse ya chokumana nacho choterocho kwenikweni imakhala ndi kukwaniritsidwa kofanana nako?

9. (a) Kodi ndimbali zotani zolosera zimene Yesu anasonyeza m’nyengo za ziŵiri m’mbiri? (b) Mouziridwa, kodi ndizinthu zina zatanthauzo zotani zimene Petro anatchula?

10. Mwa kuyerekezera Yeremiya ndi Chivumbulutso, sonyezani kuti maulosi okwaniritsidwa angakhale ndi phindu lina lolosera.

11. Kodi nditanthauzo lolosera lotani limene liripo m’cholembedwa cha zochita za Yehova ndi Israyeli wopatuka ndi Yuda pamene anali wosakhulupirika? Chifukwa ninji?

12. Kodi ndimotani mmene ife eni timapindulitsidwira ndi zolembedwa zotero?

13. Timadziŵa bwanji kuti Mulungu sanachititse anthu kuchita machimo kotero kuti zitsanzo zolosera zipangidwe?

14. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova amadziŵira zimene anthu, kapena ngakhale Satana, adzachita nthaŵi yamtsogolo? (b) Kodi ndi m’njira zotani mmene kuzidziŵa kwa Yehova ndi chifuno chake zimaloŵera mu ulosi wa Baibulo?

15. Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anagogomezera kuti zolembedwa za Baibulo ziri zoposa kwambiri mbiri chabe?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 41]

ZITSANZO ZOLOSERA​—⁠Zosonya ku Chiyani?

Masiku a Nowa

Chihema

Mfumu Solomo

Yona m’Mimba mwa Nsomba kwa Masiku Atatu

Kugwa kwa Babulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena