Mutu 8
Opulumuka a m’Mitundu Yonse
YEHOVA ngwokondwera mwachikondi ndi anthu a mitundu yonse ndi mafuko. Iye wapanga makonzedwe kotero kuti mabanja a dziko lapansi alandire chivomerezo chake ndi dalitso. Kwa Abramu (Abrahamu), mbadwa ya Semu mwana wa Nowa, Yehova anati: “Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kumka kudziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe; ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.” (Genesis 12:1-3; Machitidwe 7:2-4) “Mabanja onse a dziko lapansi”—amenewo amaphatikizapo ife lerolino, mosasamala kanthu mtundu umene tinabadwira kapena chinenero chimene timalankhula.—Salmo 65:2.
2 Uyo amene Yehova anaperekako lonjezoli anali mwamuna wachikhulupiriro, monga momwedi ife tiyenera kukhalira ndi chikhulupiriro ngati titi tidzalandire dalitso lochokera kwa Mulungu lolonjezedwa pano. (Yakobo 2:23; Ahebri 11:6) Chikhulupiriro cha Abrahamu sichinali kokha kukhulupirira kopanda ntchito koma chinagwirizanitsidwa ndi ntchito. Chinamchititsa kusamuka m’Mesopotamiya kumka kudziko lakutali limene sadaliwone kale. “Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake,” wosadzigwirizanitsa ndi maufumu alionse amzinda kumeneko. “Pakuti analindilira mudzi [Ufumu wa Mulungu] wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndi Mulungu.”—Ahebri 11:8-10.
3 Pamene Abrahamu anafika usinkhu wa zaka 100 ndipo mkazi wake Sara anali ndi zaka 90, mozizwitsa Yehova anawadalitsa ndi mwana wamwamuna, Isake. Mogwirizana ndi ameneyu, Abrahamu anakomana ndi chiyeso chofufuza chikhulupiriro ndi kumvera kulinga kwa Mulungu. Yehova analangiza Abrahamu kutengera Isake, amene tsopano anali mnyamata, ku dziko la Moriya ndipo komweko kukampereka nsembe yopsereza. Ndi chikhulupiriro m’kukhoza kwa Mulungu kubwezeretsa mwana wake kumoyo mwa chiukiriro, Abrahamu anapitirizabe kumvera. (Ahebri 11:17-19) Isake, wogonjera kwa atate wake, anali atanjatidwa kale pamwamba pa guwa lansembe ndipo Abrahamu anali ndi mpeni m’dzanja lake womphera nawo pamene mngelo wa Yehova anadodometsa. Chiyesocho chinali chitapita patali mokwanira kutsimikizira kuti Abrahamu sakanakaniza Mulungu chirichonse. Chifukwa cha chimenecho Mulungu anatsimikiziritsa pangano lake ndi Abrahamu, monga momwe Baibulo likulongosolera:
4 “Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikaniza mwana wako, mwana wako wa yekha, kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi zakumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja; ndipo mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo; m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa; chifukwa wamvera mawu anga.”—Genesis 22:15-18.
5 Pamene tizindikira kuti Abrahamu Wamkulu ndiye Yehova ndi kuti Isake anaphiphiritsira Yesu Kristu, tingayambe kuzindikira mmene zochitikazi ziriri zofunika kwa ife mwachindunji. Kwenikweni, ndiko mmene tikuchitira kulinga kwa Yehova Mulungu kumene kumatsimikiziritsa mtsogolo mwathu. Chiyembekezo cha moyo wamuyaya nchotheka kwa ife chifukwa chakuti Mulungu anaperekadi Mwana wake wobadwa yekha kukhala nsembe ya machimo athu, monga momwe kunasonyezedwera mwafanizo ndi kuyesayesa kwa Abrahamu kupereka nsembe Isake. (Yohane 3:16) Alionse amene akuumirira pa ‘kutemberera’ Yehova, kumnyoza kapena kunyozera zifuno zake zachikondi, amaloŵa pansi pa themberero limene lidzatanthauza chiwonongeko chawo chosatha. (Yerekezerani ndi 1 Samueli 3:12-14; 2:12.) Koma ngati ife tiri anthu oyamikira “tidzadalitsa” Abrahamu Wamkuluyo. Motani? Mwa kuvomereza poyera kuti zinthu zabwino zonse zimachokera kwa Yehova, kuphatikizapo mphatso yapadera ya moyo mwa Mwana wake. Ndiponso, tidzauza ena za ubwino wa Yehova ndi mikhalidwe yodabwitsa ya ufumu wake. (Yakobo 1:17; Salmo 145:7-13) M’njira imeneyi timadziika mu mzera wa kulandira madalitso ochokera kwa iye kosatha.
“MBEWU” YOLONJEZEDWA YA ABRAHAMU
6 Monga mbali ya kakonzedwe kake ka kudalitsa anthu Yehova analinganiza boma lakumwamba lolungama. Yesu Kristu anabadwa monga mbadwa ya Abrahamu, monga mwana wake wofunika koposa, kapena “mbewu,” ndipo ndi kwa iye kumene Yehova waperekako ufumu. (Agalatiya 3:16; Mateyu 1:1) Motero, monga momwe kwasonyezedwera ndi lumbiro la Mulungu kwa Abrahamu, kuli mwa njira ya Yesu Kristu chakuti anthu a m’mitundu yonse ya dziko lapansi adzadalitsidwa. Kodi inu mukuchita chimene chikufunika kuti mudzipezere dalitso limenelo? Mwachitsanzo, kodi njira yanu ya moyo imasonyeza kuti mukuzindikira mmene nsembe ya moyo wa Yesu iriri yofunika kwa inu? Kodi mukugonjeradi ku ulamuliro wake monga Mfumu?—Yohane 3:36; Machitidwe 4:12.
7 Mtumwi Yohane anapatsidwa kuwoneratu kolosera kwa zochitika zakumwamba m’zimene anawona ena ogwirizana ndi Yesu Kristu pa Phiri la Ziyoni wakumwamba. Iwo nawonso, ali mbali ya “mbewu ya Abrahamu.” Monga momwe kwalongosoledwera pa Chivumbulutso 14:1-5, iwo “anagulidwa mwa anthu” ndipo amakwanira 144 000. (Agalatiya 3:26-29) Kodi iwo amaphatikizapo ayani? Baibulo limamveketsa bwino lomwe kuti sichinakhale chifuno cha Mulungu kutengera anthu onse olungama kumwamba. (Mateyu 11:11; Machitidwe 2:34; Salmo 37:29) Mwaŵi waukulu wa kukhala limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba ngwa “kagulu kankhosa” kokha kamene kadzakhala mafumu ndi ansembe limodzi naye kwa zaka chikwi.—Luka 12:32; Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6.
8 Kodi ndimotani mmene kusankhidwa kwa “kagulu ka nkhosa” kameneko kunachitidwira? Chiitano chachikondi cha kukhala mu Ufumu wakumwamba choyamba chinaperekedwa kwa Aisrayeli akuthupi. Koma chifukwa cha kupanda kwawo chikhulupiriro iwo sanapereke 144 000 onse. Chotero Asamariya, ndipo pambuyo pake, anthu a amitundu yonse anaitanidwa. (Machitidwe 1:8) Oyamba a oloŵa nyumba anzake a Kristu anadzozedwa ndi mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E. Kusankhidwa kwa kagulu kameneka kukupitirizabe kufikira 144 000 asindikizidwa chizindikiro ndi Mulungu monga ovomerezedwa. Kenako chisamaliro chikuperekedwa kukusonkhanitsidwa kwa anthu amene adzakhala ndi moyo padziko lapansi monga nzika zoyamikira za boma lakumwamba.
9 Awo amene ali oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba limodzi ndi Kristu amatchedwa m’Malemba kukhala “osankhidwa,” “oyera mtima,” anthu “odzozedwa . . . [ndi] Mulungu.” (2 Timoteo 2:10; 1 Akorinto 6:1, 2; 2 Akorinto 1:21) Iwo amalongosoledwanso mwa chiungwe kukhala “mkwatibwi” wa Kristu. (Chivumbulutso 21:2, 9; Aefeso 5:22-32) Powonedwa kuchokera m’malingaliro ena, amatchedwa “abale” a Kristu, “oloŵa nyumba anzake a Kristu” ndi “ana” a Mulungu. (Ahebri 2:10, 11; Aroma 8:15-17; Aefeso 1:5) Mosasamala kanthu za mtundu wawo, polankhula mwauzimu, iwo ndiwo “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Aroma 2:28, 29; 9:6-8) Pamene Yehova anathetsa pangano lake Lachilamulo ndi Israyeli wakuthupi, analoŵetsa Israyeli wauzimu m’pangano latsopano ndi iye. Koma zochita zake ndi Israyeli wakuthupi pamene anali pansi pa Chilamulo zinapereka chitsanzo cha zinthu zirinkudza. (Ahebri 10:1) Kodi ndani, pamenepa, amene anaphiphiritsidwa ndi mtundu wa Israyeli wakuthupi, umene unasankhidwa ndi Mulungu kukhala “chuma chake chapadera”? Zenizeni zimasonya Israyeli wauzimu, awo amene Mulungu wasankha kulamulira ndi Kristu kumwamba. (Yerekezerani ndi Eksodo 19:5, 6 ndi 1 Petro 1:3, 4 ndi 2:9.) Limodzi ndi Kristu akupanga gulu kupyolera mwa limene madalitso adzaperekedwa kwa anthu ena onse omvera pakati pa mtundu wa anthu. Kuzindikiridwa kwa zimenezi ndiko mfungulo ya kumvetsetsa Baibulo.
AWO ODALITSIDWA MWANJIRA YA “MBEWU”
10 Mkati mwa nthaŵi imene Mulungu anali kuchita ndi mtundu wa Israyeli m’njira yapadera, iye anapanganso makonzedwe achikondi kaamba ka anthu osati a mtunduwo, koma amene mitima yawo inawasonkhezera kuloŵa m’kulambira kowona mogwirizana ndi Aisrayeli. Kutchulidwa kwapadera kwa iwo kwachitidwa m’cholembedwa Chabaibulo. Kodi, nawonso, ali ndi anzawo ofanana nawo amakono? Inde, ndithudi. Amaphiphiritsira m’njira zambiri awo amene saali Aisrayeli auzimu koma amene amayamikira chiyembekezo chodabwitsa cha moyo wamuyaya monga nzika zapadziko lapansi za Ufumu wa Mulungu. Amenewa ndiwo amene Mulungu analankhula kwa Abrahamu, akumanena kuti anthu “m’mitundu yonse yadziko lapansi” akadzidalitsa mwanjira ya “mbewu” yake.—Genesis 22:18; Deuteronomo 32:43.
11 Chakhala chifuno cha Mulungu nthaŵi zonse kuti anthu onse agwirizane m’kulambira kowona. Moyenerera, pakupatulidwa kwa kachisi womangidwa ndi Solomo m’Yerusalemu, mfumuyo inapemphera kuti Yehova akamve pemphero la alendo amene anafunafuna kupereka kulambira kuvomerezeka limodzi ndi Israyeli. (2 Mbiri 6:32, 33) Ndipo, pa Yesaya 56:6, 7, Mulungu analonjeza: “Alendo onse amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire iye ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, . . . nawonso ndimka nawo ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo; . . . pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.” Posonyeza mzimu woperekedwa pano, “alendo” amakono tsopano asonkhana kuchokera m’mitundu yonse, osati kokha monga owonerera wamba, koma monga anthu amene ‘akudzigwirizanitsa kwa Yehova.’ Amachita zimenezi mwa kupatulira miyoyo yawo kwa iye, akumasonyeza kumeneku mwa kumizidwa m’madzi ndiyeno kutumikira m’njira imene imasonyeza chikondi chawo kaamba ka “dzina la Yehova” ndi zonse zimene ilo limaimira.—Mateyu 28:19, 20.
12 Palibe kukhulupirika kocheperapo kumene kukufunika kwa iwo koposa kwa awo amene ali Akristu odzozedwa ndi mzimu. Pansi pa Chilamulo cha Mose, Yehova anafuna “mlendo wogonera” amene anayamba kulambira kowona kuti agwirizane ndi chilamulo chimodzimodzicho chimene chinagwira ntchito pa Israyeli. (Numeri 15:15, 16) Unansi pakati pawo sunali kokha wa kulekererana koma wachikondi chopanda mpeni kumphasa. (Levitiko 19:34) Mofananamo, awo ophiphiritsiridwa ndi alendo ogonera amafunafuna kugwirizanitsa kotheratu miyoyo yawo ndi zofunika za Yehova ndi kutumikira mu umodzi wachikondi ndi otsala a Israyeli wauzimu.—Yesaya 61:5.
13 Mwanjira ya mneneri wake Yesaya, Yehova analongosola gulu laphamphu la anthu a “m’mitundu yonse” amene lerolino akututirana kunyumba yolambirira ya chilengedwe chonse ya Yehova. Iye ananeneratu kuti: “Anthu ambiri adzamka, nati, Tiyeni tikwere kumka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” Chifukwa cha zimenezo iwo ‘asula malupanga awo kukhala zolimira’ ndipo, ngakhale pakati padziko lokanthidwa ndi nkhondo lino, iwo ‘sakuphunziranso nkhondo.’ (Yesaya 2:1-4) Kodi mukudziwona kukhala m’khamu lachimwemwe limenelo? Kodi muli ndi chikhumbo chawo cha kuphunzira zofunika za Yehova, kugwiritsira ntchito zimenezi m’moyo wanu ndi kuleka kudalira pa zida zankhondo? Mulungu walonjeza kuti khamu lalikulu limene likulondola njira imeneyi lidzatuluka m’chisautso chachikulu monga opulumuka kuloŵa ‘m’dziko lapansi lake latsopano’ lamtendere.—Chivumbulutso 7:9, 10, 14; Salmo 46:8, 9.
[Mafunso]
1. Kodi ndilonjezo lotani loperekedwa kwa Abrahamu limene limasonyeza kuti chivomerezo cha Mulungu nchothekera kwa “mabanja onse” a anthu?
2. (a) Mofanana ndi Abrahamu, kodi tifunikira mkhalidwe wotani? (b) Monga momwe kwasonyezedwera pa Ahebri 11:8-10, kodi ndimotani mmene Abrahamu anaperekera umboni wa mkhalidwewu?
3. Kodi ndichiyeso chofufuza chikhulupiriro chotani chimene Abrahamu anakumana nacho ponena za Isake?
4. Panthaŵi imeneyo, kodi ndilonjezo lina lofunika lotani limene Mulungu anapereka ponena za anthu a mitundu yonse?
5. (a) Kodi nchiyani chimene chinaphiphiritsiridwa ndi kuyesa kwa Abrahamu kupereka nsembe Isake? (b) M’kukwaniritsidwa kwa Genesis 12:3, kodi ndimotani mmene anthu ‘amatembererera’ Abrahamu Wamkuluyo, ndipo limodzi nzotulukapo zotani? (c) Kodi ndimotani mmene “tingamdalitsirire”?
6. (a) Kodi ndani amene ali “mbewu” yaikulu ya Abrahamu? (b) Kodi ndimotani mmene tingapezere dalitso limene limadza kupyolera mwa iye?
7. (a) Kodi ndaninso amene akuphatikizidwa mu “mbewu ya Abrahamu”? (b) Kodi timadziŵa motani kuti sionse amene amatumikira Mulungu mokhulupirika adzapita kumwamba?
8. Kodi ndiliti pamene kusankhidwa kwa “kagulu ka nkhosa” kunayamba, ndipo kodi kumapitirizabe kwa utali wotani?
9. (a) Kodi ndimawu ati m’Baibulo amene amagwira ntchito kukagulu kakumwamba kameneka? (b) Kodi ndani amene anaphiphiritsiridwa ndi Aisrayeli akuthupi?
10. Kodi ndani amene akuphiphiritsiridwa ndi olambira Yehova amene sanali Aisrayeli?
11. (a) Kodi nkutchulidwa kotani kumene kunapangidwa kwa kagulu kameneka pa kupatulidwa kwa kachisi wa Solomo? (b) Kodi ndimotani mmene “alendo” ‘akudzigwirizanitsira kwa Yehova’ m’nthaŵi yathu, monga momwe kunanenedweratu pa Yesaya 56:6, 7?
12. Kodi ndimotani mmene Chilamulo cha Mose chimasonyezera kuti kaya ngati awo amene akuyembekezera kukhala nzika zapadziko lapansi za Ufumu wa Mulungu ayenera kugwirizana ndi miyezo yapamwamba imene imagwira ntchito kwa Israyeli wauzimu?
13. Kodi ndizinthu zotani pa Yesaya 2:1-4 zimene tiyenera kulabadira ngati tifuna kupulumuka kuloŵa “m’dziko lapansi latsopano”?