Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 17 tsamba 129-137
  • Mkhalidwe Wosiyana Kulinga ku Kumvera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mkhalidwe Wosiyana Kulinga ku Kumvera
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHIFUKWA CHAKE KUMVERA SIKUNGAKHALE KOSAVUTA
  • MALAMULO AMENE AMATIPINDULITSA
  • Ankafuna Kuthandiza Ena
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kamtsikana Kanathandiza Mkulu wa Asilikali
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Poyamba Anakana Kumvera Koma Kenako Anamvera
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mtsikana Athandiza Ngwazi
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 17 tsamba 129-137

Mutu 17

Mkhalidwe Wosiyana Kulinga ku Kumvera

KWA zaka zambiri Yerusalemu asanawonongedwe ndi Ababulo, Yehova anachenjeza a Yuda za chimene chinalinkudza, ndi chifukwa chake. Iwo anali kutsatira zikhoterero za mitima yawo yokanika mmalo mwa kumvera Mulungu.​—⁠Yeremiya 25:​8, 9; 7:​24-28.

2 Yehova samakakamiza aliyense kuti amtumikire, koma moyenerera, amafuna kumvera kwa onse amene amafuna chivomerezo chake ndi madalitso a moyo amene amatsagana nacho. Atalanditsa Aisrayeli ku Igupto, Yehova anawauza kuti: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndilanga; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.” (Eksodo 19:​5, 6) Mulungu atafotokoza zofuna zake kwa iwo ndipo atamva kuŵerengedwa kwa “bukhu lachipangano,” mwa kufuna kwawo anavomereza thayo limene linali logwirizana ndi unansi umenewo ndi Mulungu.​—⁠Eksodo 24:⁠7.

3 Komabe, inali kokha nthaŵi yaifupi kufikira pamene mzimu wopanduka unayamba kuwoneka. Ana a Israyeli sanalandule poyera chikhulupiriro chawo mwa Yehova; koma, mwa kuswa chilamulo chake, ambiri anayesa kusanganiza zizoloŵezi za Aigupto ndi kulambiridwa kwa Yehova. (Eksodo 32:​1-8) Pambuyo pake ena anapeza chifukwa ndi anthu amene Yehova anagwiritsira ntchito monga omuimira owoneka. (Numeri 12:​1-10; 16:​1-3, 31-35) Monga mtundu, Israyeli anasonyeza kupanda chikhulupiriro cha kuchita mogwirizana ndi mawu a Mulungu, akumasonkhezeredwa ndi kuwopa anthu. (Numeri 13:​2, 31-33; 14:​1-4; Ahebri 3:​17-19) Pamene zolakwa sizinali zadala, olapa modzichepetsa anatha kupeza chikhululukiro. Koma mkati mwa nyengo ya zaka mazana asanu ndi anayi mtunduwo mwadala unanyalanyaza poyamba chofuna chimodzi cha Mulungu, ndiyeno china, ndipo kaŵirikaŵiri zambiri za izo. Zinthu zimene anachita nzotulukapo zake zalembedwa m’Baibulo monga zitsanzo zochenjeza kwa ife.​—⁠2 Mbiri 36:​15-17; 1 Akorinto 10:​6-11.

4 M’nthaŵi ya Yeremiya, machenjezo obwerezabwereza ataperekedwa ponena za zotulukapo zoipa za njira yawo, Yehova anapereka pamaso pa Ayuda chitsanzo​—⁠Arekabu. Amenewa sanali Aisrayeli, anali mbadwa za Yehonadabu amene anasonyeza kuti anali wogwirizana kotheratu ndi kusalekerera kwa Yehu kupandukira Yehova. Yehonadabu ameneyu (kapena, Yonadabu) monga kholo la fuko la Arekabu adawalamulira kusamwa vinyo kunthaŵi yonse, ndiponso kusakhala m’nyumba kapena kuloŵa m’kulima koma kukhala m’mahema monga anthu oyendayenda. Motero iwo akakhala ndi moyo wodekha, wosavuta, wopanda kudzikondweretsa ndi zoipa za moyo wa mzinda, uku akulambira Yehova ndi Aisrayeli, amene iwo anakhala pakati pawo.

5 Popeza kuti Ayuda analinkukana kumvetsera Yehova, Mfumu Yachilengedwe chonse, kodi kukanayembekezeredwa kuti Arekabu akamvera kholo lawo laumunthu? Iwo anatero, ndipo mu mkhalidwe wabwino. Ngakhale kuli kwakuti Arekabu anathaŵira m’Yerusalemu pamene magulu ankhondo a Ababulo ndi a Asuri anaukira Yuda, anapitirizabe kukhala m’mahema. Koma kodi chitsimikizo chawo cha kusamwa vinyo chinali champhamvu motani, ngakhale kuli kwakuti anthu amene iwo anakhala pakati pawo analoledwa kumwa? Yehova anachititsa Yeremiya kuloŵetsa Arekabu m’chipinda chodyera cha kachisi, kuyala zikho zavinyo ndi kuwauza kuti amwe. Anakana. Chifukwa? Mwachiwonekere iwo anazindikira kudzipereka kwa kholo lawo kwa Yehova, anazindikira kudera kwake nkhaŵa kwachikondi thanzi lawo, ndipo motero iwo anamvera lamulo lake. Yehova anakondwera ndi chitsanzo chabwino kwambiri chimenechi cha kumvera chimene chinavumbula kusamvera Yehova kosonyezedwa ndi Ayuda.​—⁠Yeremiya 35:​1-11.

6 Pali anthu lerolino amene ali ngati Arekabu. Amenewa ndiwo “nkhosa zina” za Ambuye. Kuti kaya iwo adzamwa vinyo ameneyo sindiyo nkhani imene ikukambitsiridwa lerolino. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:23.) Imeneyi ndinkhani ya aliyense payekha malinga ngati sakumwa mopambanitsa kapena ngakhale kukhala chidakwa. (Miyambo 23:20; 1 Akorinto 6:​9, 10) Koma kumvera kwaumulungu nkofunika. Mosiyana ndi Dziko Lachikristu, limene liri Israyeli wopatuka wophiphiritsiridwa, kagulu ka Arekabu kamakono kamasonyeza mwa zochita zawo kuti kamadziŵa kufunika kwa kumvera kwaumulungu. Kodi kumeneku kudzawapindulitsa motani?

7 Chifukwa cha kudzipereka kwawo, Yehova anapatsa Arekabu lonjezo limene liri ndi tanthauzo lamphamvu lolosera kaamba ka nthaŵi yathu, kuti: “Chifukwa mwamvera lamulo la Yehonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kuchita monga mwa zonse anakuuzani inu; chifukwa chake atero Yehova wamakamu, Mulungu wa Israyeli: Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasoŵa munthu wa kuima pamaso panga kumuyaya.” (Yeremiya 35:​18, 19) Iwo anali pakati pa opulumuka chiwonongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E. Ndipo kagulu kophiphiritsiridwa ndi iwo kadzapulumuka chiwonongeko chirinkudza cha Dziko Lachikristu ndi mbali ina yonse ya dziko limene modzigangira limachita zofuna zake, likumakana kuvomereza ulamuliro wa Yehova.

CHIFUKWA CHAKE KUMVERA SIKUNGAKHALE KOSAVUTA

8 Anthu ambiri amawona kumvera kukhala kovuta kukuphunzira. Iwo akulira m’dziko mmene munthu aliyense ‘akuchita zofuna zake.’ Iwo angakondwere ndi zimene amaphunzira ponena za moyo pansi pa Ufumu wa Mulungu. Koma ngati kunyada kuphimba maganizo awo, iwo angakane zina za zofunika za Mulungu kapena kupezera chifukwa njira imene zimenezi zaperekedweramo. (Miyambo 8:13; 16:18) Namani, kazembe wa gulu lankhondo la Asuri m’nthaŵi ya mneneri Elisa, anali ndi vuto limenelo.

9 Namani anagwidwa khate. Koma chifukwa chakuti wandende wina wachichepere Wachiisrayeli analankhula molimba mtima chikhulupiriro chake kuti Namani akachiritsidwa ngati kokha atapita kwa mneneri wa Yehova Elisa, Namani anapita ku Israyeli. Anapita kunyumba ya Elisa ali ndi akavalo ndi magaleta ankhondo. Tsopano, Namani anali munthu wotchuka ndipo anayembekezera Elisa kutuluka kudzamlandira ndiyeno nkuchita dzoma, akumapempha Yehova ndi kuweyula dzanja lake cha uku ndi uko pathupi lamatendalo kufikira litachiritsidwa. Mmalo mwake, Elisa anangotuma mthenga kukamuuza kuti apite ku Mtsinje wa Yordano ndipo kumeneko kukasamba kasanu ndi kaŵiri.​—⁠2 Mafumu 5:​1-12.

10 Kudzikuza kwa Namani kunanyanyulidwa. Anachoka wokwiya. Koma atumiki ake atakambitsirana naye, anadzichepetsa m’chikhulupiriro. “Potero anatsika, namira m’Yordano kasanu ndi kaŵiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng’ono, nakonzeka.” Namani anatsimikiza kuti Yehova ndiye Mulungu wowona yekha, ndipo anazindikira kuti, mosasamala kanthu za kachitidwe kake koyamba, malangizo operekedwa ndi Elisa anachokeradi kwa Mulungu.​—⁠2 Mafumu 5:​13-15.

11 Kodi mwinamwake mumawona ina ya mikhalidwe ya Namani mwa inu? Monga momwe kuliri ndi ena osakhala Aisrayeli amene anasonyeza chikhulupiriro, Namani akugwiritsiridwa ntchito m’Malemba kuphiphiritsira “nkhosa zina” zimene zimaloŵa m’kulambira kowona. Onsewa, pokhala obadwira mu uchimo, panthaŵi ina anali amatenda mwauzimu. Iwo onse anafunikira kufunafuna chithandizo cha kagulu kamtumiki wodzozedwa wa Yehova ndiyeno kuchita momvera zimene “mtumiki” ameneyu wawaphunzitsa m’Mawu a Mulungu. (Mateyu 24:45) Panthaŵi ina ena sanazindikire uphungu wonse Wamalemba woperekedwa kwa iwo​—⁠monga ngati kufunikira kwa kufika pamisonkhano yampingo mokhazikika, kufunika kwa kukhala wolekana ndi dziko kapena kwa ubatizo wa m’madzi Wachikristu. Iwo angakhale atazengereza kudzipatulira ndi ubatizo wa m’madzi chifukwa chakuti mtima wawo unatsutsa kufunikira kwa ‘kudzikana’ kuti akhale otsatira Kristu. Nthaŵi zina iwo anasuliza njira imene uphungu unaperekedweramo kwa iwo ndi okhala ndi thayo mu mpingo. Koma m’kupita kwa nthaŵi onse amene akakhaladi “nkhosa zina” za Ambuye afunikira kuphunzira kufunika kwa kudzichepetsa ndi kumvera kwachikondi.​—⁠Yakobo 4:6; Mateyu 16:⁠24.

MALAMULO AMENE AMATIPINDULITSA

12 Pamene tifika pa kudziŵa Yehova ndi njira zake, timafika pa kuzindikira mmene mawu amene iye analankhula kwa mtumiki wake m’nthaŵi zakale aliri owona akuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo, mwenzi utamvera malamulo anga!” (Yesaya 48:​17, 18) Chikhumbo chaphamphu cha Yehova chakuti anthu ake apeŵe tsoka ndi kusangalala ndi moyo mwa kulabadira malamulo ake. Iye amadziŵa mmene tapangidwira ndi chimene chidzatipatsa chimwemwe chenicheni. Amatichenjeza pakhalidwe limene lingatiluluze kapena kuwononga unansi wathu ndi ena.

13 Awo amene alabadira chenjezo lake la dama ndi chigololo apeŵetsedwa vuto la maganizo, nthenda ndi ana apathengo amene zimenezi zimatulutsa. (1 Akorinto 6:18; Ahebri 13:⁠4) Mwa kugwiritsira ntchito uphungu wonga wa pa 2 Akorinto 7:​1, iwo akhala opanda kumwerekera ndi fodya ndi anamgoneka ena, zimene zimawononga thanzi lawo ndipo zingachititse imfa yamwamsanga. Lamulo lake la ‘kusala mwazi’ lathandiza atumiki ake kulimbikitsa kudalira kwawo pa iye monga Uyo amene ziyembekezo zawo zonse za moyo wamtsogolo zimadalirapo, ndipo panthaŵi imodzimodziyo lawatetezera ku nthenda zowopsa zimene zingafalitsidwe mwa kuikiridwa mwazi.​—⁠Machitidwe 15:​28, 29.

14 Malinga ngati tiri m’dziko, pali kukhudzana nalo kwina kofunika. Koma Yehova amatichenjeza kuti tisaike ziyembekezo zathu pa ilo, tisakhale mbali yake. Iye amadziŵa chimene chiri mtsogolo mwa dziko. Kukakhala kopusa chotani nanga kuthera moyo wanu mukumanga chimene Mulungu adzawononga! Zoipanso, awo amene akutero adzawona kuti akulandira choikidwiratu cha dziko limene iwo aperekako miyoyo yawo. Chifukwa cha chimenecho, ngwopindulitsa chotani nanga, uphungu woperekedwa ndi Mwana wa Mulungu: Funafunani Ufumu wa Mulungu! Uikeni poyamba m’moyo wanu!​—⁠1 Yohane 2:17; Mateyu 6:⁠33.

15 Pozindikira mokwanira zimene timafunikira, Yehova akukonzekeretsera anthu ake moyo m’dongosolo lake latsopano la zinthu. Kusamvera kwa Adamu kunachititsa kupanda ungwiro kwa anthu, kutayika kwa moyo wamuyaya ndi kuthamangitsidwa m’Paradaiso. Ndithudi ngati titi tikhale pakati pa awo amene akudzapatsidwa chimene Adamu anataya, tiyenera kupereka umboni wakuti timamvetsera pamene Mulungu alankhula. Ndipo kodi ndimotani mmene iye adzalankhulira nafe mkati mwa Zaka Chikwi zirinkudza, pamene anthu alinkufikitsidwa ku ungwiro? Kupyolera mwa Ufumu Waumesiya. Kodi boma limeneli lidzakhalanso ndi oimira a padziko lapansi owoneka? Inde. Mfumuyo idzakhala ndi omtumikira “akalonga m’dziko lonse lapansi.” (Salmo 45:16; yerekezerani ndi Yesaya 32:​1, 2.) Mwa kumvera kwachikondi akalonga amenewa, anthuwo adzasonyeza kugonjera kwa Mfumu yawo yakumwamba.

16 Mokonzekera nthaŵi imeneyo, tsopano Yehova akupereka maphunziro kupyolera mwa gulu lake lowoneka lateokratiki. Mkati mwa mipingo iye wadzutsa amuna achikulire mwauzimu, kapena akulu. Iwo amapereka chitsogozo chofunika kaamba ka misonkhano yampingo ndipo amatsogolera m’kulalikidwa kwa uthenga Waufumu. Mothandiza onse amene akufuna kutumikira Yehova kuphunzira mmene angagwiritsirire ntchito ziphunzitso Zabaibulo m’miyoyo yawo ndipo mwachikondi amachenjeza misampha imene ikatha kuwononga unansi wawo ndi Mulungu. Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zazindikiranso kuti kumvera malangizo a akulu kaŵirikaŵiri kwachititsa kupulumutsidwa kwa moyo mkati mwa mikuntho, zivomezi ndi kuulika kwa chiwawa chankhondo. Mpingo siwaakulu; ngwa Mulungu. Akulu samanena kuti ngouziridwa. Koma, monga momwe Malemba amasonyezera, Mulungu amawagwiritsira ntchito kutsogoza, ndipo kuwamvera kumasonyeza kulemekeza kakonzedwe kamene Yehova akugwiritsira ntchito kukonzekeretsa atumiki ake kaamba ka kupulumuka kuloŵa m’Dongosolo lake Latsopano.​—⁠Machitidwe 20:28; Ahebri 13:⁠17.

17 Komabe, sichikhumbo chabe cha kukhala pakati pa opulumuka chiwonongeko cha dziko chirinkudzacho chimene chimasonkhezera kumvera koteroko. Pali zina zambiri. Ziti? Kuyamikira moyo ndi zinthu zonse zimene Mulungu wapereka kuuchirikiza. Kuthokoza mphatso zake zimene zimakometsa miyoyo yathu​—⁠kukhoza kulingalira, kuzindikira kukongola ndi mapindu auzimu, kukhoza kudziŵa ndi kulambira Mlengi wathu. Ndiponso, kudziŵa chikondi chachikulu cha Mulungu chimene chinamsonkhezera kupereka Mwana wake kupereka nsembe moyo wake kotero kuti tikhale ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha.

18 Kwa awo amene afika pa kudziŵa Mulungu bwino lomwe, kumvera sikuli chinthu chosakondweretsa. Kumvetsera zofuna ndi malamulo ake, limodzi ndi kuwona zipatso zabwino zochokera m’kugwiritsira ntchito zimenezi, sizimasiya chikaikiro m’maganizo mwawo chakuti kuchita zinthu m’njira ya Mulungu ndiyo njira yokha yoyenera ndi yanzeru. Iwo amakuzindikira kukhala chitetezero. Irinso njira yosonyezera kukonda kwawo Mulungu. Amapeza chikondwerero chachikulu m’kumumvera.​—⁠1 Yohane 5:3; Salmo 119:129.

[Mafunso]

1. Kodi nchifukwa ninji Yehova analola Ababulo kuwononga Yerusalemu?

2. (a) Moyenerera, kodi ndimapindu ati amene amadalira pa kumvera Mulungu? (b) Kodi ndimotani mmene Israyeli anafikira kukhala mu unansi wa pangano ndi Yehova

3. (a) Kodi ndim’njira ziti zimene Israyeli pambuyo pake anasonyeza mzimu wopandukira Yehova? (b) Kodi nchifukwa ninji zochitika zimenezo zalembedwa m’Baibulo?

4. (a) Kodi Arekabu anali ayani? (b) Kodi ndimalamulo otani amene Yehonadabu anaika pa iwo?

5. Kodi ndimotani mmene Arekabu analiri chitsanzo m’kumvera?

6. (a) Kodi ndani lerolino ali ngati Arekabu? (b) Kodi ndani amene watsimikizira kukhala wophiphiritsiridwa ndi Israyeli wosamverayo?

7. (a) Kodi ndilonjezo lolimbikitsa lotani limene Yehova anapereka kwa Arekabu? (b) Kodi nchiyembekezo chotani chimene limenelo limapereka kwa kagulu ka Arekabu amakono?

8. Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri amawona kumvera kukhala kovuta?

9. (a) Kodi zinachitika motani kuti Namani anakawona Elisa? (b) Kodi anayembekezeranji, koma kodi nchiyani chimene kwenikweni chinachitika?

10. (a) Kodi Namani anachita motani? (b) Kodi nchiyani chimene potsirizira pake chinamsonkhezera kumvera? (c) Kodi chotulukapo chinali chiyani?

11. (a) Kodi ndim’njira ziti zimene “nkhosa zina” zinaphiphiritsiridwa ndi Namani? (b) Kodi ndimaphunziro ofunika otani amene tonsefe tiyenera kuphunzira?

12, 13. (a) Kodi nchifukwa ninji kumvera malamulo a Yehova kumatipindulitsa? (b) Kodi ndimotani mmene zimenezi zingafotokozedwere mwa fanizo?

14. Kodi timapindulitsidwa motani mwa kufunafuna choyamba Ufumuwo mmalo mwa kudziphatikiza ife eni mosafunikira ndi dziko?

15. (a) Kuti tikhale pakati pa awo amene adzapeza chimene Adamu anataya, kodi tiyenera kuphunzira kuchitanji? (b) Kodi Yehova adzalankhula nafe motani mkati mwa Zaka Chikwi?

16. Kodi nchifukwa ninji kumvera akulu kuli tchinjirizo tsopano, ndipo kodi ndimotani mmene kuliri kukonzekera kwabwino kaamba ka moyo m’Dongosolo Latsopano la Mulungu?

17. Kodi nchiyani chimene chiyenera kutisonkhezera kukhala omvera?

18. Pamene tifika pa kudziŵa Mulungu bwino lomwe, kodi ndimotani mmene timalingalirira kumvera kwa iye ndi gulu lake?

[Zithunzi patsamba 135]

Ena amafunikira kulaka kunyada, monga momwe anachitira Namani wakhate

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena