Mutu 18
Kodi Ndinu Wokhulupirika kwa Mfumu Yatsopano ya Dziko Lapansi?
PA Nisani 9 wa 33 C.E., Yesu Kristu anadzipereka kwa Ayuda monga Mfumu yawo, Mesiya wonenedweratuyo. Pamene anatsika pa Phiri la Azitona kupita ku Yerusalemu, khamu la ophunzira linakondwera ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zamphamvu zimene Yesu anali atachita. (Luka 19:37, 38; Zekariya 9:9) Koma kodi iwo akasonyeza kukhala okhulupirika kwa Ameneyo amene iwo anamtamanda monga Mfumu? Kukhulupirika kwawo kunayesedwa mwamsanga.
2 Chiyambire 1914 Yesu Kristu wolemekezedwayo wolamulira mwamphamvu ali kumwamba waperekedwa kwa anthu onse monga Mfumu yatsopano yadziko lapansi. Chiyembekezo cha moyo pansi pa boma lokhala m’manja mwa Kristu, ndi zothetsera zenizeni za mavuto a anthu, chachititsa anthu a m’mitundu yonse kukondwera. Koma kodi iwo adzasonyeza kukhala okhulupirika? Bwanji ponena za aliyense wa ife payekha?
MBIRI YA KUKHULUPIRIKA KWA MFUMU MWINIYO
3 Yesu Kristu wapereka umboni wochuluka wakuti kukhulupirika kwake kwa Yehova, Wolamulira Wachilengedwe chonse, kuli kosandenguma. Iye moyenerera akutchedwa m’Malemba kukhala “wokhulupirika” wa Yehova. (Salmo 16:10, NW; Machitidwe 2:24-27) Liwu Lachihebri lotanthauza “kukhulupirika” logwiritsiridwa ntchito panopa liri ndi lingaliro la kukhala wokoma mtima kwachikondi. Siliri kanthu kena kamphwayi, kozikidwa palamulo kapena chilungamo chabe, koma limasonkhezeredwanso ndi chikondi ndi chiyamikiro.—Yerekerezani Salmo 40:8; Yohane 14:31.
4 Kumwamba, pamene Satana anayamba kudzifunira ulemu umene unali wa Mulungu yekha ndi pamene ena a angelo anasiya malo awo oyenerera m’gulu lakumwamba la Yehova, Mwana wachisamba wa Mulungu sanatsanzire mchitidwe wawo. Kutero kunali kosaganizirika kwa iye! Kumeneko kunali kumvera kwake kodzipereka nsembe chakuti, chifuniro cha Atate wake, Mwana wokhulupirika ameneyu anasiya mmbuyo ulemelero wake wakumwamba, nakhala munthu ndipo ngakhale kuvomera imfa pamtengo wophedwerapo. Mwachikondi, anatsimikizira kuti, kufikira pamene zinadalira pa iye, palibe chinthu cha zimene Malemba anandandalikira chikakhala chosakwaniritsidwa.—Afilipi 2:5-8; Luka 24:44-48.
5 Pamene Yesu anali padziko lapansi, Satana anabweretsa chitsenderezo chachikulu pa iye kuti ampatutse pa ntchito imene Mulungu anampatsa kuti achite—ngati nkutheka, kumnyenga kuchita kanthu kena kamene kakachititsa Mulungu mwiniyo kukana Mwana wake. Analimbikitsa Yesu kuchita zinthu zimene zikanamchititsa kutchuka ndi mphamvu—koma monga mbali ya dziko limene Satana anali wolamulira wake. Yesu anakana, akumagwira mawu Malemba Opatulika monga chitsogozo chake. (Mateyu 4:1-10) Yesu anali ndi maluso apadera ndipo anawagwiritsira ntchito bwino lomwe, koma nthaŵi zonse mogwirizana ndi chifuniro cha Atate wake. Anadzitanganitsa kotheratu m’kuchita ntchito imene Mulungu anamtuma kudzachita. (Yohane 7:16-18; 8:28, 29; 14:10) Nchitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga cha kukhulupirika!
6 Chifukwa cha kukhulupirika kwa Yesu kotsimikizirika, Yehova anamuukitsa kwa akufa, “namkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo lirilonse lipinde . . . ndi malirime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.” (Afilipi 2:9-11) “Dzina limene liposa maina onse” limeneli limaimira mphamvu ndi ulamuliro zoikidwa pa Yesu kuti akwaniritse chifuniro cha Yehova. ‘Kupinda bondo’ kwa iye kumatanthauza kuvomereza malo ake antchito ndi kugonjera ku ulamuliro wake. Kumaphatikizapo kukhala nzika yokhulupirika kwa iye monga Mfumu.
CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA KWA ODZOZEDWA A YEHOVA
7 Chenicheni chakuti, atakwera kumwamba, Yesu sakanawonekanso ndi maso aumunthu chikachititsa mayeso ofufuza mtima a kukhulupirika kwa omtsatira. Kodi iwo akatsatira ziphunzitso zimene iye anali atawaphunzitsa? Kodi iwo akakhala olekana ndi dziko? Kodi iwo akalemekeza awo pa amene mzimu woyera unapereka mathayo a uyang’aniro? Kodi iwo akakhala amoyo wonse m’kuchita ntchito imene anawagaŵira?
8 M’nthaŵi yokwanira “nkhosa zina” zinayenera kusonkhanitsidwira m’chigwirizano ndi “kagulu ka nkhosa” ka oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba. Kodi iwo akayamikiradi malo awo antchito ogaŵiridwa mogwirizana ndi Kristu monga Mfumu ndi kwa wina ndi mnzake? Maumboni amasonyeza kuti kukondana kwenikweni kwakhala pakati pa onse amene ali mbali ya “gulu limodzi” pansi pa Yesu Kristu. Zimenezi zinachitiridwa chithunzi ndi chikondi champhamvu chosatha cha Jonatani, mwana wa Mfumu Sauli, kwa Davide. Atawona kudzipereka kotheratu kwa Davide kwa Yehova ndi kudalira kwake pa Mulungu m’kupha chimphonacho Goliati, Jonatani anasonkhezeredwa kwambiri ndipo ‘mtima wake . . . unalumikizana ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anayamba kumkonda ngati moyo wake.’ Chikondi chake sichinachepe pamene kunakhala kowonekera kuti Yehova akaika ufumu pa Davide ndipo osati pa Jonatani. Ndipo mobwerezabwereza Jonatani anaika moyo wake pachiswe kaamba ka Davide.—1 Samueli 17:45-47; 18:1; 23:16, 17.
9 Kuwonjezera pa Jonatani, panali anthu ena osakhala Aisrayeli amene anakondana ndi Davide. Iwo sanali asilikali omenyera nkhondo ndalama koma anali amuna amphamvu amene anachita modzipereka kwa Davide monga wodzozedwa wa Yehova. Akereti, Apereti ndi mbadwa zakale za mzinda wa Afilisiti wa Gati anali pakati pa amenewa. Iwo mokhulupirika anamamatirana ndi Davide pamene mwana wake Abisalomu mwachinyengo anafunafuna kuba mitima ya amuna a Israyeli. Mosasamala kanthu za kutchuka ndi kuchenjera kwa Abisalomu, iwo sanaloŵetsedwe m’njira yopanduka mwa mawu ake okopa.—2 Samueli 15:6, 10, 18-22.
10 Kufotokozedwa kwina kosangalatsa kwa unansi wa pakati pa Kristu, otsalira odzozedwa ndi “nkhosa zina” kukupezeka m’Salmo 45. Limeneli siliri kokha nyimbo yokongola koma nlolosera Ufumu Waumesiya—Mulungu mwiniyo akumakhala “mpando wachifumu,” Ndiko kuti, maziko ndi mchirikizo wa ufumu wa Yesu. (Salmo 45:1-7; Ahebri 1:8, 9) Wamasalmo akulongosola mkwatibwi wa Kristu, “mwana wamkazi wa mfumu,” kukhala akumatengeredwa kwa Mfumu patsiku lake laukwati. Okhala limodzi naye ndiwo “anamwali . . . atsamwali ake.” Kodi amenewa ndani? Iwo ndiwo amene akuyembekezera kukhala nzika zapadziko lapansi za Ufumu wa Mulungu. “Ndi chimwemwe ndi kusekera” iwo amaperekeza kagulu la “mkwatibwi” kufikira wotsirizira weniweni wa amenewa atagwirizana ndi Kristu kumwamba. Limodzi nawo, iwo ‘amaloŵa m’nyumba ya mfumu,’ osati mwa kukwera kumwamba, koma mwa kudzipereka iwo eni kaamba ka ntchito ya Mfumu. Kodi inu mwakhala mbali yadzoma lachimwemwe limenelo?—Salmo 45:13-15.
KODI KUKHULUPIRIKA KUMAFUNANJI KWA IFE?
11 Mikhalidwe yosaŵerengeka m’moyo imasonyeza mtundu wa anthu umene ife tiri. Kodi timakhulupiriradi Ufumu Waumesiya wa Yehova? Kodi ngweniweni kwa ife? Yesu ananena kuti otsatira ake owona sakakhala “mbali yadziko.” Kodi zimenezi ziri choncho ndi inu?—Yohane 17:15, 16.
12 Ponena za anthu opanda ungwirofe, kukhulupirika sikumafunikiritsa ungwiro. Koma kumafunadi kuti tipeŵe kuswa mwadala malamulo a Baibulo, kaya anthu ena akutiwona kapena ayi. Kudzatisokhezera kuyesayesa kugwiritsira ntchito ziphunzitso Zabaibulo mokwanira, koposa ndi kuwona mmene tingayandikirire kunjira zadziko. Kudzachititsa kukulitsa kuda kwenikweni chimene chiri choipa.—Salmo 97:10.
13 Ngati tidadi chimene chiri choipa, sitidzalola chidwi kutikopera kuyandikana nacho. Kuchita chidwi ndi moyo wa anthu achisembwere kungatsogolere munthu ku chiwonongeko. (Miyambo 7:6-23) Chomwechonso, chiwonongeko chauzimu chingagwere awo amene chifukwa cha chidwi amagula ndi kuŵerenga mabukhu otulutsidwa ndi ampatuko, anthu amene asiya Yehova ndi gulu lake ndi amene kenako mwa mawu “akumenya” amene poyamba anali mabwenzi awo. (Mateyu 24:48-51) Miyambo 11:9 (NW) imachenjeza kuti: “Mwa pakamwa pake munthu amene ali wampatuko amawononga mnzake.” Koma kukhulupirika kudzatitetezera kusasochezedwa ndi mawu awo okopa.—2 Yohane 8-11.
14 Imodzi ya njira zofunika koposa imene tingasonyezere kukhulupirika ndiyo mwa kukhala amoyo wonse m’ntchito imene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuchita. Iyemwini anapereka chitsanzo mwa kupita kumzinda ndi mzinda ndi mudzi ndi mudzi, akumalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Luka 8:1) Yesu adaneneratu zimene Akristu owona akakhala akuchita tsopano pamene anati: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Kuli mwa njira ya kulalikidwa kumeneku kwa mbiri yabwino chakuti nkhani ya Ufumu ikuperekedwa kwa anthu kulikonse kotero kuti angathe kupanga chosankha chawo. Kwa khamu lalikulu, chosankha chimenecho chidzachititsa kupulumutsidwa mkati mwa chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 7:9, 10) Kodi inu mukukhala ndi phande mokhulupirika m’ntchito yofulumirayi?
15 Kalekale wamasalmo Davide analemba kuti: “Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndipo okondedwa anu adzakulemekezani. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu; kudziŵitsa ana a anthu za mphamvu zake, ndi ulemerero waukulu waufumu wake. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.” (Salmo 145:10-13) Ufumu umenewo tsopano ukuchitidwa mwa Ufumu Waumesiya wokhala m’manja okhulupirika a Yesu Kristu, ndipo timasonyeza kukhulupirika kwathu kwa Mulungu ndi Kristu yemwe mwa kulankhula momasuka ndi motenthedwa maganizo za uwo.
16 Kodi ndikufunika kotani m’moyo wanu kumene mwapereka kuntchito imeneyi yochitira umboni za Ufumu? Kodi mumauikadi patsogolo pa zinthu zina? Zimene inu eni mumachita zingakhale zambiri kapena zochepa koposa zimene ena amachita. Mikhalidwe ya anthu imasiyana. Koma tonsefe tingapindule mwa kudzifunsa mafunso onga awa: ‘Kodi mbali yanga imasonyeza chabe kuumirizika, nsembe yachiphamaso? Kodi ndimaiwona kokha monga chofunika cha kupulumuka? Kapena kodi kukonda Yehova, kudzipereka ku Ufumu wake Waumesiya ndi nkhaŵa yeniyeni kaamba ka munthu mnzanga zimandisonkhezera kuipatsa malo oyamba kotero kuti zinthu zina m’moyo wanga zasumikidwa pa iyo?’ Kukhulupirika kudzatisonkhezera kufunafuna njira zosonyezera kuti ntchito imeneyi njofunika kwa ife monga momwe iriri kwa Mfumu yathu.
17 Mwamsanga Iye amene anatamandidwa mwachisangalalo monga Mfumu ndi ophunzira ake pamene analoŵa m’Yerusalemu m’33 C.E. adzawononga onse amene akukana ulamuliro wa Yehova wosonyezedwa mwa Mfumu Yake Yaumesiya. Koma iye “adzalankhula mtendere” ku “khamu lalikulu” limenelo la anthu lochokera m’mitundu yonse amene atsanzira chitsanzo chake cha kukhulupirika. Kodi mudzakhala pakati pawo?—Zekariya 9:10; Aefeso 4:20-24.
[Mafunso]
1. Pamene Yesu anaperekedwa monga Mfumu mu 33 C.E., kodi ndimotani mmene khamu lalikulu linachitira?
2. (a) Kodi ndimotani mmene anthu ambiri lerolino akuchitira ndi chilengezo chakuti Kristu ndi Mfumu yatsopano ya dziko lapansi? (b) Koma kodi ndimafunso otani amene amafunikira kulingalira kwamphamvu?
3. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu mwiniyo akutchedwa “wokhulupirika” wa Yehova? (b) Kodi kukhulupirika nchiyani?
4, 5. (a) Kodi ndimotani mmene kukhulupirika kwa Yesu kunasonyezedwera kumwamba, motsatizana ndi chipanduko cha Satana? (b) Kodi ndimotani mmene kukhulupirika kumeneko kunasonyezedweranso padziko lapansi?
6. Kodi ndim’njira yotani imene mphoto yoperekedwa kwa Yesu imafunika kukhulupirika kwa ife?
7. Kodi ndiponena za nkhani ziti zimene otsatira a Yesu amayesedwa ponena za kukhulupirika kwawo?
8. Kodi nchiyani chimene chinaphiphiritsiridwa ndi kukhulupirika kwachikondi pakati pa Jonatani ndi Davide?
9. Kodi ndimotani mmene kukhulupirika kofananako kunasonyezedwera ndi anthu osakhala Aisrayeli amene anatumikira m’gulu lankhondo la Davide?
10. (a) Kodi ndimotani mmene unansi weniweni pakati pa Kristu, otsalira odzozedwa ndi “nkhosa zina” walongosoledwera m’Salmo 45? (b) Kodi ndim’lingaliro liti mmene ‘atsamwali achisungwanawo amaloŵera nyumba ya mfumu’
11. Kodi ndimikhalidwe yotani imene imatiyesa ponena za kusakhala “mbali ya dziko”?
12. Ngakhale kuli kwakuti ndife opanda ungwiro, kodi ndim’njira zina ziti zimene tingaperekere umboni wa kukhulupirika?
13. Kodi ndimotani mmene kukhulupirika kudzatitetezerera ku mawu okopa a ampatuko?
14. (a) Kodi nchiyani chimene chiri imodzi ya njira zofunika koposa m’zimene tingasonyezere kukhulupirika kwathu kwa Kristu monga Mfumu? (b) Kodi nchifukwa ninji ntchito imeneyi iri yofunika kwambiri?
15. (a) Kodi nchiyani chimene Salmo 145:10-13 limanena kuti okhulupirika a Yehova akakhala akulankhula? (b) Kodi zimenezo zimatikhudza motani?
16. Kodi ndimotani mmene kukhulupirika kumasonkhezerera mlingo umene timakhalira ndi mbali m’kulalikira Ufumu ndi cholinga chimene timakuchitira?
17. Kodi nkwayani kumene Yesu “adzalankhula mtendere” pamene awononga oipa?