Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-13 tsamba 2-5
  • Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo
  • Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Limadzitsutsa?
  • Mbiri ndi Sayansi
  • Kuneneratu Zamtsogolo
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira Baibulo
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo
T-13 tsamba 2-5

Chifukwa Chake Mungadalire Baibulo

Anthu ena amanena kuti Baibulo liri losadalirika, ndipo malingaliro awo avomerezedwa koposerapo. Motero ambiri lerolino amawona zimene Baibulo limanena kukhala zosadalirika.

Kumbali ina, zimene Yesu Kristu adanena m’pemphero kwa Mulungu zimabweretsa chidaliro: “Mawu anu ndichowonadi.” Ndipo Baibulo lenilenilo limadzinenera kukhala louziridwa ndi Mulungu.—Yohane 17:17; 2 Timoteo 3:16.

Kodi muganizanji za zimenezi? Kodi pali maziko omvekera a kudalira Baibulo? Kapena kodi pali umboni weniweni wakuti Baibulo liri losadalirika, kuti limadzitsutsa ndipo liri losagwirizana?

Kodi Limadzitsutsa?

Pamene kuli kwakuti anthu ena anganene kuti Baibulo limadzitsutsa, kodi pali aliyense amene anakusonyezani chitsanzo chenicheni? Sitinawonepo ngakhale chimodzi chimene chingaime ngati chitapendedwa mosamalitsa. Ndithudi, mungawonekere kukhala zophophonya m’zolembedwa zina za Baibulo. Koma kaŵirikaŵiri vutolo ndilo kupanda chidziŵitso chonena za maumboni ndi mikhalidwe za nthaŵi.

Mwachitsanzo, anthu ena adzasonya zimene akuzilingalira kukhala kuphophonya m’Baibulo, mwa kufunsa kuti: ‘Kodi Kaini anapeza kuti mkazi wake?’ Lingaliro liri lakuti Kaini ndi Abele anali ana okha a Adamu ndi Hava. Komatu lingalirolo liri lozikidwa pa kusazindikira zimene Baibulo limanena. Baibulo limalongosola kuti Adamu “anabala ana amuna ndi akazi.” (Genesis 5:4) Motero Kaini anakwatira mmodzi wa alongo ake kapena mwinamwake mwana wa mbale wake kapena wa mlongo wake.

Kaŵirikaŵiri osuliza amangoyang’ana zitsutso ndipo motero anganene kuti: ‘Wolemba Baibulo Mateyu amanena kuti kazembe wankhondo anadza kudzapempha chifundo kwa Yesu, pamene Luka amanena kuti zinali nthumwi zimene zinatumizidwa kukapempha. Kodi ndiuti amene ali wolondola?’ (Mateyu 8:5, 6; Luka 7:2, 3) Koma kodi pamenepa palidi kutsutsana?

Pamene thamo la chochitika kapena la ntchito za anthu liperekedwa kwa munthu amene kwenikweni walinganiza ntchito, munthu wanzeru samanena kuti pali cholakwika. Mwachitsanzo, kodi mumalingalira lipoti lakuti meya analambula khwalala kukhala lolakwika ngakhale kuli kwakuti kuswedwa kwenikweniko kwamsewu kunachitidwa ndi mainjiniya ake ndi antchito? Kutalitali! Mofananamo, sikulakwa kuti Mateyu amanena kuti kazembe wa nkhondo anapita ndi pempho kwa Yesu pamene kuli kwakuti, Luka, amanena kuti pempholo linaperekedwa kupyolera mwa nthumwi.

Pamene maumboni owonjezereka adziŵika, zowonekera kukhala zolakwika m’Baibulo zimazimiririka.

Mbiri ndi Sayansi

Kulondola kwa zochitika za mbiri ya Baibulo nthaŵi zina kunakaikiridwa kwambiri. Mwachitsanzo, osuliza, anakaikira kuti kunali anthu a m’Baibulo monga Mfumu Sargon wa Asuri, Belisazara wa Babulo, ndi bwanamkubwa wa Roma Pontiyo Pilato. Koma zotulukiridwa zaposachedwapa zatsimikizira zolembedwa za Baibulo zimenezi motsatizanatsatizana. Motero wolemba mbiri Moshe Pearlman analemba kuti: “Mwadzidzidzi, okaikira amene anali atakaikira kutsimikizirika ngakhale kwa mbali za zochitika za Chipangano Chakale anayamba kupendanso malingaliro awo.”

Ngati titi tidalire Baibulo, liyenera kukhalanso lolondola m’nkhani zasayansi. Kodi liri lotero? Osati kale kwambiri asayansi, motsutsa Baibulo, ananena kuti chilengedwe chinalibe chiyambi. Komabe, posachedwapa katswiri wa za m’mlengalenga Robert Jastrow anasonya ku chidziŵitso chamakono kwambiri chimene chimatsutsa zimenezi, akumalongosola kuti: “Tsopano tikuwona mmene umboni wa za m’mlengalenga umatsogolerera ku lingaliro labaibulo la magwero a dziko. Maumboniwo amasiyana, koma zinthu zofunika m’zolembedwa za sayansi ya za m’mlengalenga ndi zabaibulo za Genesis ziri zofanana.”—Genesis 1:1.

Anthu asinthanso malingaliro awo ponena za mpangidwe wa dziko lapansi. “Maulendo okatumba,” ikulongosola motero The World Book Encyclopedia, “anasonyeza kuti dziko linali lozungulira, osati lathyathyathya monga momwe anthu ambiri anakhulupiririra.” Koma Baibulo linalondola kuyambira kalekale! Zoposa zaka 2 000 zapitazo maulendowo asanapangidwe, Baibulo pa Yesaya 40:22 (NW) linati: “Pali Iye amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lozungulira,” kapena monga momwe matembenuzidwe ena amanenera, “mbulumbwa ya dziko lapansi” (Douay), “dziko lapansi lozungulira.” (Moffatt)

Motero pamene anthu aphunzira zowonjezereka, ndipamenenso umboni umawonjezereka wakuti Baibulo lingadaliridwe. Amene kale anali mtsogoleri wa British Museum, Sir Frederic Kenyon, adalemba kuti: “Zotulukapo zopezeka kale zikutsimikizira chimene chikhulupiriro chingavomere, kuti Baibulo silingachitire mwina kusiyapo kupindula ndi chidziŵitso chowonjezereka.”

Kuneneratu Zamtsogolo

Koma kodi tingadaliredi maulosi a Baibulo onena za mtsogolo, kuphatikizapo malonjezo ake a ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zolungama’? (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Eya, kodi cholembedwa cha Baibulo cha kudalirika m’nthaŵi zakale chakhala chotani? Mobwerezabwereza maulosi operekedwa ngakhale zaka mazana angapo pasadakhale akwaniritsidwa ndendende monga momwe adanenedwera!

Mwachitsanzo, Baibulo lidaneneratu kugwetsedwa kwa Babulo wamphamvu pafupifupi zaka 200 kusanachitike. Kwenikweni, Amedi, amene anagwirizana ndi Aperisi, anatchulidwa kukhala ogonjetsawo. Ndipo ngakhale kuli kwakuti Koresi, mfumu ya Peresiya, inali isanabadwe nkomwe, komabe Baibulo lidaneneratu kuti iye akakhala ndi mbali yaikulu m’kugonjetsako. Ilo lidanena kuti madzi otetezera a Babulo, mtsinje wa Firate, ‘ayenera kuphwa,’ ndipo ‘zipata [za Babulo] sizidzatsekedwa.’—Yeremiya 50:38; Yesaya 13:17-19; 44:27—45:1.

Maumboni otsimikizirika ameneŵa anakwaniritsidwa, monga momwe wolemba mbiri Herodotus anasimbira. Ndiponso, Baibulo lidaneneratu kuti Babulo potsirizira pake akakhala mabwinja osakhalidwa. Ndipo zimenezo ndizo zimene zinachitika kumene. Lerolino Babulo ali miunda yapululu. (Yesaya 13:20-22; Yeremiya 51:37, 41-43) Ndipo Baibulo nlodzala ndi maulosi ena amene anakwaniritsidwa mwamphamvu.

Pamenepo kodi nchiyani chimene Baibulo limaneneratu ponena za dongosolo la dziko la zinthu lamakono? Ilo limati: “Nthaŵi yomalizira ya dziko lino ikakhala nthaŵi ya mavuto. Anthu sadzakonda chirichonse kusiyapo ndalama ndi iwo eni; iwo adzakhala aliuma, onyang’wa, ndi otukwana; osachitira ulemu makolo, osayamikira, opanda chifundo, opanda chikondi chachibadwidwe . . . Adzakhala anthu oika chikondwerero m’malo mwa Mulungu, anthu amene amasunga mpangidwe wachipembedzo wachiphamaso, koma akumakana mkhalidwe wake weniweni.”—2 Timoteo 3:1-5, The New English Bible.

Ndithudi, tikuwona kukwaniritsidwa kwa zimenezi lerolino! Koma Baibulo limaneneratunso kaamba ka “nthaŵi zomalizira za dziko lino” zinthu izi: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala.” Kuwonjezera apa, “kudzakhala zivomezi zazikulu, . . . ndi mliri m’malo akutiakuti.”—Mateyu 24:7; Luka 21:11.

Ndithudi, maulosi Abaibulo akukwaniritsidwa lerolino! Eya, pamenepa, bwanji ponena za malonjezo amene sanakwaniritsidwebe, monga akuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha,” ndi, “adzasula malupanga awo akhale zolimira . . . ndipo sadzaphunziranso nkhondo”?—Salmo 37:29; Yesaya 2:4.

‘Zimenezo ziridi zabwino kopambanitsa kuti zikhale zowona,’ ena angatero. Koma kwenikweni, palibe chifukwa choti ife tikaikire kanthu kalikonse kamene Mlengi wathu alonjeza. Mawu ake angadaliridwe! (Tito 1:2) Mwa kupenda umboni mowonjezereka, mudzafikira pa kukhutiritsidwa mowonjezereka ponena za zimenezi.

Kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Zotulukapo zopezeka kale zimatsimikizira chimene chikhulupiriro chikasonyeza, kuti kupeza chidziŵitso chowonjezereka cha Baibulo kumapindulitsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena