Mutu 14
Kodi Ndani Amene Amapita Kumwanba, ndipo Nchifukwa Ninji?
1. Kodi anthu ambiri adzayankha motani funsolo, Kodi ndani amene amapita kumwamba, ndipo nchifukwa ninji?
ANTHU AMBIRI amati, ‘Anthu onse abwino amapita kumwamba.’ Komabe, pofunsidwa chifukwa chake iwo amapita kumwamba, iwo anganene kuti: ‘Ndicho kukakhala ndi Mulungu,’ kapena, ‘Ndicho mphotho ya kukhala wabwino.’ Kodi Baibulo limaphunzitsanji ponena za zimenezi?
2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji tingatsimikizire kuti anthu ena adzapita kumwamba? (b) Kodi ndifunso lotani limene likufuna kuyankhidwa?
2 Baibulo limamveketsa bwino lomwe kuti Yesu anaukitsidwa kwa akufa ndi kuti anapita kumwamba. Ndiponso, limanena kuti anthu ena adzatengeredwa komweko. Pausiku wotsatiridwa ndi imfa yake, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika, kuti: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kotero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.”—Yohane 14:1-3.
3 Mwachimvekere, Yesu anali kuuza atumwi ake kuti iwo akatengeredwa kumwamba kukakhala naye. Mtumwi Paulo anauza kawirikawiri Akristu oyambirira za chiyembekezo chodabwitsa chimenecho. Mwa chitsanzo, iye analemba kuti: “Ponena za ife, unzika wathu wuli kumwamba, ku malo amenenso tikuyembekezera mwaphamphu mpulumutsi, Ambuye Yesu Kristu.” (Afilipi 3:20, 21, NW; Aroma 6:5; 2 Akorinto 5:1, 2) Chifukwa cha malonjezo oterowo, mamiliyoni ambiri a anthu aika mitima yawo pa moyo wakumwamba. Komabe kodi anthu abwino onse adzapita kumwamba?
KODI ANTHU ABWINO ONSE AMAPITA KUMWAMBA?
4, 5. Kodi pali umboni wotani wakuti Davide ndi Yobu sanapite kumwamba?
4 Mwamsanga Yesu ataukitsidwa kwa akufa, mtumwi Petro anauza khamu la Ayuda, kuti: “Kholo lija Davide . . . adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lerolino. Pakuti Davide sanakwera kumwamba ayi.” (Machitidwe 2:29, 34) Motero munthu wabwinoyo Davide sanapite kumwamba. Bwanji ponena za munthu wolungamayo Yobu?
5 Povutika, Yobu anapemphera kwa Mulungu, kuti: “Ha! Mukadandibisa kumanda, mukadandisunga mtseri, mpaka wapita mkwiyo wanu, mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira!” Yobu anayembekezera kuti pamene afa iye akakhala wosadziwa kanthu m’manda. Iye anadziwa kuti sakapita kumwamba. Koma iye anali ndi chiyembekezo, monga momwe anafotokozera kuti: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga [nthawi yoikidwiratu m’manda], mpaka kwafika kusandulika kwanga. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani.”—Yobu 14:13-15.
6, 7. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti palibe aliyense amene anafa Kristu asanadze anapita kumwamba? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira anthu onse okhulupirika amene anafa Kristu asanadze?
6 Yohane, amene anabatiza Yesu, analinso munthu wabwino. Komabe Yesu anati: “Iye amane ali wochepa mu ufumu wa kumwamba amkulira iye.” (Mateyu 11:11) Zimenezi ziri choncho chifukwa chakuti Yohane Mbatizi sadzapita kumwamba. Pamene Yesu anali padziko lapansi, kumene kunali zaka zoposa 4,000 pambuyo pa chipanduko cha Adamu ndi Hava, iye anati: “Kulibe munthu anakwera kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.”—Yohane 3:13.
7 Chifukwa cha chimenecho, malinga ndi mawu ake enieni, kulibe munthu adapita kumwamba kwa zaka zonse 4,000 zimenezo za mbiri ya anthu kufikira m’nthawi yake. Davide, Yobu ndi Yohane Mbatizi adzalandira chiukiriro cha ku moyo padziko lapansi. Kunena zowona, amuna ndi akazi onse okhulupirika amene anamwalira Yesu asanafe anali ndi chiyembekezo cha kukhalanso ndi moyo padziko lapansi, osati kumwamba. Iwo adzaukitsidwa kuti akhale ena a nzika zapadziko lapansi za ufumu wa Mulungu.—Salmo 72:7, 8; Machitidwe 17:31.
CHIFUKWA CHAKE ANTHU ENA OKHULUPIRIKA AKUPITA KUMWAMBA
8. Kodi ndimayankho a mafunso otani amene ali ofunika, ndipo chifukwa ninji?
8 Kodi nchifukwa ninji Yesu anapita kumwamba? Kodi ndintchito yotani imene iye akufunikira kuchita kumeneko? Mayankho a mafunso amenewa ngofunika. Zimenezi ziri chifukwa chakuti awo amene akupita kumwamba adzagwirizana ndi Yesu m’ntchito yake. Iwo akupita kumwamba kaamba ka chifuno chimenechocho.
9, 10. Malinga ndi kunena kwa Danieli, kodi ndani kuphatikiza pa Kristu amene adzalamulira m’boma la Mulungu?
9 Tinaphunzira m’mitu yoyambirira kuti Yesu adzalamulira padziko lapansi latsopano laparadaiso monga mfumu ya boma lakumwamba la Mulungu. Kalekale Yesu asanadze kudziko lapansi, bukhu Labaibulo la Danieli linaneneratu kuti “mwana wa munthu wa munthu” akapatsidwa “ulamuliro.” “Mwana wa munthu” ndi Yesu Kristu. (Marko 14:41, 62) Ndipo Danieli akupitiriza kunena kuti: “Ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzawonongeka.”—Danieli 7:13, 14.
10 Komabe, nkofunika kuwona pano m’bukhu la Danieli kuti “mwana wa munthu” sakukalamulira yekha. Baibulo limati: “Ndipo ufumu, ndi ulamuliro . . . zinaperekedwa kwa anthu amene ali oyera a Wamkulukulu. Ufumu wawo ndiufumu wokhala chikhalire.” (Danieli 7:27, NW) Manenedwe amenewa “anthu” ndi “ufumu wawo” amatidziwitsa kuti ena adzalamulira limodzi ndi Kristu m’boma la Mulungu.
11. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti atsatiri oyambirira a Kristu adzalamulira limodzi naye?
11 Pa usiku wotsiriza umene Yesu anakhala ndi atumwi ake okhulupirika 11 anasonyeza kuti iwo akakhala olamulira limodzi naye muufumu wa Mulungu. Anawauza kuti: “Inu ndinu amene mwamamatirana nane m’mayeso anga; ndipo ndikupanga pangano ndi inu, monga momwedi Atate wanga wapanga pangano ndi ine, la ufumu.” (Luka 22:28, 29) Pambuyo pake, mtumwi Paulo ndi Timoteo anaphatikizidwa m’pangano limeneli, kapena chivomerezano, cha ufumu. Kaamba ka chifukwa chimenecho Paulo analembera kalata Timoteo kuti: “Ngati tipitiriza kupirira, tidzalamuliranso pamodzi monga mafumu.” (2 Timoteo 2:12, NW) Ndiponso, mtumwi Yohane analemba ponena za awo amene “adzalamulira monga mafumu padziko lapansi” limodzi ndi Yesu Kristu.—Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6, NW.
12. Kodi ndichenicheni chotani ponena za “mbewu” ya Abrahamu chimene chimavumbula kuti Kristu adzakhala ndi olamulira naye?
12 Motero awo amene akupita kumwamba akupita kumeneko kukatumikira monga olamulira limodzi ndi Kristu m’boma lakumwamba la Mulungu. Pamene kuli kwakuti Yesu ndiye “mbewu” yaikulu ya lonjezo, Mulungu amasankha ena kuchokera pakati pa anthu kuti alamulire ndi Yesu muufumuwo. Iwo motero amakhala mbali ya “mbewu,” monga momwe Baibulo likunenera kuti: “Ngati muli a Kristu, mulidi mbewu ya Abrahamu, olowa nyumba a lonjezo.”—Agalatiya 3:16, 29; Yakobo 2:5, NW.
KODI NDIANGATI AKUPITA KUMWAMBA?
13. (a) Kodi nchifukwa ninji makanda sadzapita kumwamba? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anafotokozera chiwerengero chimene chikulandira Ufumu?
13 Popeza kuti iwo ayenera kulamulira dziko lapansi, nkwachiwonekere kuti awo amene akupita kumwamba adzakhala atsatire a Kristu oyesedwe ndi otsimikiziridwa. Zimenezi zikutanthauza kuti makanda kapena ana ang’ono, amene sanatsimikiziridwe mokwanira mkati mwa zaka zambiri za utumiki Wachikristu, sadzatengeredwa kumwamba. (Mateyu 16:24) Komabe, achichepere oterowo amene akufa ali ndi chiyembekezo cha kuukitsidwa padziko lapansi. (Yohane 5:28, 29) Motero chiwerengero chonse chimene chikupita kumwamba chidzakhala chaching’ono poyerekezeredwa ndi ambiri amene adzalandira moyo padziko lapansi mu ulamuliro Waufumu. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.”—Luka 12:32.
14. Kodi ndiangati amene akupanga “kagulu kankhosa” kamene kakupita kumwamba?
14 Kodi kagulu ka olamulira Aufumu kameneko kadzakhala chiwerengero chochepa motani? Kodi kadzaphatikizapo atumwi ndi atsatiri a Yesu ena oyambirira okha? Ayi, Baibulo limasonyeza kuti “kagulu kankhosa” kadzaphatikizapo ambiri. Pa Chivumbulutso 14:1, 3 Baibulo limati: “Ndipo ndinapenya, tawonani, Mwanawankhosayo [Yesu Kristu] alikuimirira paphiri la Ziyoni [wakumwaba], ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai . . . ogulidwa [kapena, otengedwa] kuchokera kudziko.” Wonani kuti anthu 144,000 okha akuwonedwa limodzi ndi Mwanawankhosayo, Yesu Kristu, pa Phiri la Ziyoni wakumwamba. (Ahebri 12:22) Motero m’malo mwa kupita kumwamba kwa anthu onse abwino, Baibulo limavumbula kuti anthu okhulupirika ndi oyesedwa 144,000 okha adzatengeredwa kumeneko kukalamulira ndi Kristu.
CHIFUKWA CHAKE ASANKHIDWA PADZIKO LAPANSI
15. Kodi nchifukwa ninji Mulungu akusankha olamulira Aufumu kuchokera pakati pa anthu?
15 Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu akusankha olamulira amenewa kuchokera pakati pa anthu? Bwanji osachititsa angelo kulamulira ndi Kristu? Eya, panali padziko lapansi pano pamene kuyenera kwa Yehova kwa kulamulira kunakayikiridwa. Panali pano pamene kukhulupirika kwa anthu kwa Mulungu kukatha kuyesedwa pansi pa chitsutso chochokera kwa Mdyerekezi. Panali pano pamene Yesu anasonyeza kukhulupirika kwake kotheratu kwa Mulungu poyesedwa napereka moyo wake dipo kwa anthu. Motero panali padziko lapansi pamene Yehova analinganiza kutengapo “kagulu kankhosa” ka anthu koti kagwirizane ndi Mwana wake muufumu wakumwamba. Iwo ndiwo amene, mwa kukhulupirika kwawo kwa Mulungu, anatsimikizira chinenezo cha Mdyerekezi kukhala chonama chakuti anthu amatumikira Mulungu kokha kaamba ka zifukwa zadyera. Chifukwa cha chimenecho, nkoyenera kuti, Yehova akugwiritsira ntchito anthu amenewa kaamba ka ulemerero wake.—Aefeso 1:9-12.
16. Kodi nchifukwa ninji tingakhale othokoza kuti olamulira Aufumu akhala ndi moyo padziko lapansi?
16 Ndiponso, taganizirani mmene kudzakhalira kwabwino kwambiri kukhala nawo monga olamulira anthu amene asonyeza kukhala okhulupirika kwa Mulungu padziko lapansi, ambiri a iwo ngakhale kutaya miyoyo yawo chifukwa cha Ufumuwo. (Chivumbulutso 12:10, 11; 20:4) Angelo sanakumane ndi mtundu wa ziyeso woterowo. Ndiponso iwo sakudziwa mavuto ofala kwa anthu. Motero iwo sakazindikira mokwanira chimene chiri kukhala munthu wochimwa ndi kukhala ndi mavuto amene anthufe timakhala nawo. Koma a144,000wo adzazindikira chifukwa chakuti iwo anakhala ndi mavuto amenewawo. Ena a iwo anafunikira kulaka machitidwe auchimo amodzimodziwo, ndipo iwo akudziwa mmene kungakhalire kovuta kutero. (1 Akorinto 6:9-11) Chifukwa cha chimenecho, iwo adzachita ndi nzika zawo zapadziko lapansi mozindikira.—Ahebri 2:17, 18.
MPINGO WA MULUNGU
17. Kodi liwulo “mpingo” limatanthauza chiyani?
17 Baibulo limatiuza kuti Kristu ndiye mutu wa mpingo wa Mulungu, ndi kuti ziwalo zake ziri zogonjera kwa Yesu. (Aefeso 5:23, 24) Motero liwulo “tchalitchi,” kapena “mpingo wa Mulungu,” silimatanthauza nyumba. M’malo mwake, limatanthauza kagulu ka Akristu. (1 Akorinto 15:9) Lerolino tingatchule mpingo wa Akristu umene timagwirizana nawo. M’njira imodzimodziyo, timawerenga m’Baibulo ponena za “mpingo wa Laodikaya,” ndipo, m’kalata ya mtumwi Paulo kwa Filemoni, ponena za “mpingo umene [unali] m’nyumba mwake.”—Akolose 4:16; Filemoni 2, NW.
18. (a) Kodi ndani amene akupanga “mpingo wa Mulungu wamoyo”? (b) Kodi mpingo umenewo ukutchulidwanso ndi maina otani m’Baibulo?
18 Komabe, pamene Baibulo limatchula “mpingo wa Mulungu wamoyo,” likutanthauza kagulu kena ka atsatire a Kristu. (1 Timoteo 3:15, NW) Iwo amatchedwanso “mpingo wa oyamba kubadwa amene alembedwa kumwamba.” (Ahebri 12:23, NW) Motero “mpingo wa Mulungu” umenewu wapangika ndi Akristu onse padziko lapansi amene ali ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Onse pamodzi, anthu 144,000 okha potsirizira pake akupanga “mpingo wa Mulungu.” Lerolino owerengeka chabe a amenewa, otsalira, ali ndi chikhalirebe padziko lapansi. Akristu amene akuyembekezera kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi amafunafuna chitsogozo chauzimu kuchokera kwa ziwalo za “mpingo wa Mulungu wamoyo” umenewu. Baibulo limatchula mpingo wa ziwalo 144,000 umenewu ndi maina onga ngati “mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa,” thupi la Kristu,” “kachisi wa Mulungu,” “Israyeli wa Mulungu,” ndi “Yerusalemu Watsopano.”—Chivumbulutso 21:9; Aefeso 4:12; 1 Akorinto 3:17; Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 21:2, NW.
CHINTHU CHATSOPANO M’CHIFUNIRO CHA MULUNGU
19. Kodi ndichinthu chatsopano chotani chimene Mulungu anayambitsa kuti chikwaniritse chifuno chake choyamba cha dziko lapansi?
19 Yehova Mulungu sanasinthe chifuno chake cha dziko lapansi ndi anthu pa ilo Adamu atalowetsa mtundu wa anthu panjira ya uchimo ndi imfa. Ngati Mulungu akanatero, kukanatanthauza kuti iye sanali wokhoza kukwaniritsa chifuno chake choyamba. Chifuno chake kuyambira pachiyambi chinali cha kukhala ndi paradaiso wapadziko lonse lapansi wodzaza anthu osangalala ndi athanzi, ndipo chifuno chimenecho chiripobe. Chinthu chatsopano chokha chimene Mulungu anayambitsa chinali kakonzedwa kake ka boma latsopano kuti likwaniritse chifuno chake. Monga momwe tawonera, Mwana wake, Yesu Kristu, ndiye wolamulira wamkulu m’boma limeneli, ndipo anthu 144,000 adzatengedwa kuchokera pakati pa anthu kukalamulira kumwamba limodzi naye.—Chivumbulutso 7:4.
20. (a) Kodi ndani amene akupanga “miyamba yatsopano” ndi “dziko latsopano”? (b) Kodi muyenera kuchitanji kuti mukhale mbali ya “dziko latsopano”?
20 Olamulira amenewa kumwamba adzapanga “miyamba yatsopano” ya dongosolo latsopano la Mulungu. Komabe nkhwachiwonekere kuti ngati pati pakhale olamulira dziko lapansi olungama oterowo, pamenepo payenera kukhala awo amene iwo akulamulira. Baibulo limatcha anthu amenewa kukhala “dziko latsopano.” (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1-4) Iwo adzaphatikizapo Yobu, Davide ndi Yohane Mbatizi—inde, anthu onse okhulupirika amene anakhalako Kristu asanadze kudziko lapansi. Koma padzakhala ambirimbiri amene adzapanga “dziko latsopano,” kuphatikizapo anthu amene adzapyola mapeto a dongosolo la zinthu loipa lino. Kodi mudzakhala mmodzi wa opulumuka amenewa? Kodi mukufuna kukhala nzika ya boma la Mulungu? Ngati ndichocho, pali zofunika zimene muyenera kukwaniritsa.
[Zithunzi patsamba 121]
Kodi anthu abwino awa anapita kumwamba?
Mfumu Davide
Yobu
Yohane Mbatizi
[Chithunzi patsamba 122]
Pa usiku wotsiriza limodzi ndi atumwi, Yesu anati iwo akakhala olamulira limodzi naye muufumu wa Atate wake