Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 19 tsamba 155-165
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
    Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
  • Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili Chikwaniritsidwa Posachedwapa
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Ulamuliro Wolungama Udzampangitsa Paradaiso
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 19 tsamba 155-165

Mutu 19

Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso

1. (a) Kodi nchiyani chimene chiri lingaliro lofala la Harmagedo? (b) Kodi Baibulo limanenanji ponena za iyo?

“HARMAGEDO” ndiliwu lochititsa mantha kwa ambiri. Kawirikawiri atsogoleri adziko amaligwiritsira ntchito kutanthauza Nkhondo Yachitatu ya Dziko yothekera. Komabe, Baibulo limatcha Harmagedo kukhala malo a nkhondo yolungama yomenyedwa ndi Mulungu. (Chivumbulutso 16:14, 16, King James Version) Nkhondo ya Mulungu imeneyi idzalambulira njira dongosolo latsopano lolungama.

2. (a) Kodi ndani amene adzaphedwa pa Harmagedo? (b) Motero kodi ndi machitidwe otani amene tiyenera kupewa mwanzeru?

2 Mosafanana ndi nkhondo za anthu, zimene zimapha abwino ndi oipa omwe, Harmagedo, idzapha oipa okha. (Salmo 92:7) Yehova Mulungu adzakhala Woweruza, ndipo iye adzachotsa aliyense amene mwadala akukana kumvera malamulo ake olungama. Lerolino anthu ambiri samawona cholakwika ndi zinthu zonga ngati dama, kuledzera, kunama kapena kunyenga. Koma, malinga ndi kunena kwa Mulungu, zinthu zimenezi nzoipa. Motero pa Harmagedo iye sadzapulumutsa awo amene akupitiriza kuzichita. (1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8) Atadziwa malamulo a Mulungu pankhani zimenezi, nkofunika kwa anthu amene angakhale akuchita zinthu zoipa zoterozo kuti asinthe njira zawo.

3. (a) Kodi Yesu anayerekezera mapeto a dziko liripoli ndi chiyani? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira Satana ndi ziwanda zake? (c) Malinga ndi kunena kwa malemba pamasamba otsatirapowo, kodi ndi mtundu wotani wa mikhalidwe umene udzalandiridwa padziko lapansi laparadaiso?

3 Palibe mbali ya dziko loipa lino imene idzakhalapobe pambuyo pa Harmagedo. Anthu okha amene akutumikira Mulungu adzapitiriza kukhala ndi moyo. (1 Yohane 2:17) Yesu Kristu anayerekezera mkhalidwewo ndi uja wa nthawi ya Nowa. (Mateyu 24:37-39; 2 Petro 3:5-7, 13; 2:5) Pambuyo pa Harmagedo, ufumu wa Mulungu udzakhala boma lokha lolamulira padziko lapansi. Satana ndi ziwanda zake adzakhala kulibe. (Chivumbulutso 21:8) Lingalirani, pamasamba otsatirapowo, ena a madalitso amene Baibulo limasonyeza kuti anthu omvera adzalandira.

ANTHU ONSE PA MTENDERE

“Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala paphewa lake, ndipo adzamutcha . . . Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”—Yesaya 9:6, 7.

“Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.”—Salmo 72:7, 8.

KULIBENSO NKHONDO

“Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa padziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi.”—Salmo 46:8, 9.

NYUMBA ZABWINO NDI NTCHITO YOSANGALATSA KWA ALIYENSE

“Adzamanga nyumba ndi kukhalamo. . . Sadzamanga ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya . . . osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbewu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa awo adzakhala pamodzi ndi.”—Yesaya 65:21-23.

UPANDU, CHIWAWA NDI KUIPA ZACHOKA

“Pakuti ochita zoipa adzadulidwa . . . Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.”—Salmo 37:9, 10.

“Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:22.

DZIKO LONSE LAPANSI PARADAISO

Yesu anati: “Udzakhala nane m’Paradaiso.”—Luka 23:43, NW.

“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.

ZINTHU ZABWINO ZOCHULUKA ZAKUTI ONSE ADYE

“Yehova wa makamu adzakonzera anthu . . . onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha.”—Yesaya 25:6.

“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” “Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.”—Salmo 72:16; 67:6.

4, 5. (a) Kodi sipadzakhalanso mikhalidwe yotani padziko lapansi laparadaiso? (b) Kodi nchiyani chimene anthu adzakhala okhoza kuchita chimene, m’malo ambiri, sangathe kuchita lerolino?

4 Ndithudi mukufuna kukhala padziko lapansi laparadaiso longa munda mu umene munthu woyambayo Adamu analengedwera. (Genesis 2:8; Luka 23:43) Taganizirani—popandanso nkhondo, upandu kapena chiwawa. Mudzakhala wokhoza kuyenda kulikonse pa nthawi iriyonse yamasana kapena usiku popanda kuwopa kuvulazidwa. Oipa sadzakhalakonso.—Salmo 37:35-38.

5 Zimenezi zikutanthauza kuti sikudzakhala atsogoleri andale zadziko osawona mtima ndi atsogoleri abizinesi aumbombo kuti atsendereze anthu. Anthu sadzalemezedwa ndi misonkho yaikulu yolipirira zida zankhondo. Aliyense sadzakhalanso wopanda chakudya chabwino ndi nyumba yosangalatsa chifukwa chakuti sangazikwanitse. Kusakhala pantchito, kukwera mitengo kwa zinthu ndi mitengo yaikulu sizidzakhalakonso. Onse adzakhala ndi ntchito yokondweretsa yochita, ndipo iwo adzakhala okhoza kuwona ndi kusangalala ndi zipatso za ntchito yawo.

6. (a) Kodi opulumuka Harmagedo adzachita ntchito yotani? (b) Kodi Mulungu adzadalitsa motani ntchito imene irinkuchitidwa?

6 Choyambirira, awo amene akupulumuka Harmagedo adzakhala ndi ntchito yoyeretsa dziko lapansi ndi kuchotsa zipasu za dongosolo lakeleli. Ndiyeno iwo adzakhala ndi mwayi, motsogozedwa ndi ulamuliro Waufumu, wolima dziko lapansi ndi kulipangitsa kukhala malo okongola okhalamo. Imeneyo idzakhala ntchito yosangalatsa chotani nanga! Mulungu adzadalitsa chirichonse chimene chikuchitidwa. Iye adzapereka mtundu woyenera wa mphepo yolimira zakudya ndi kuweta zifuyo, ndipo iye adzalinganiza ndi zimenezi zikutetezeredwa ku nthenda ndi chivulazo.

7. (a) Kodi ndilonjezo lotani la Mulungu limene lidzakwaniritsidwa? (b) Kodi Akristu akuyembekezera chiyani malinga ndi lonjezo la Mulungu?

7 Lonjezo la Mlengi wachikondi limeneli, monga momwe laperekeredwera kupyolera mwa wamasalmo Wabaibulo, lidzakwaniritsidwa: “Muwolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:16) Inde, zikhumbo zonse zoyenera za anthu owopa Mulungu zidzakwaniritsidwa kotheratu. Sitingayerekezeredi mmene moyo udzakhalira wabwino kwambiri m’paradaiso padziko lapansi. Posimba kakonzedwe ka Mulungu ka kudalitsa anthu ake, mtumwi Petro analemba kuti: “Monga mwa lonjezano [la Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13; Yesaya 65:17; 66:22.

8. (a) Kodi nchifukwa ninji sitikufunikira miyamba yeniyeni yatsopano? (b) Kodi “miyamba yatsopano” nchiyani?

8 Kodi “miyamba yatsopano” imeneyi nchiyani? Iyo siri miyamba yeniyeni yatsopano. Mulungu anapanga miyamba yathu yeniyeni yangwiro, ndipo imamtamanda. (Salmo 8:3; 19:1, 2) “Miyamba yatsopano” imatanthauza ulamuliro watsopano wa dziko lapansi. “Miyambayo” tsopano yapangika ndi maboma opangidwa ndi anthu. Pa Harmagedo imeneyi idzachoka. (2 Petro 3:7) “Miyamba yatsopano” imene idzailowa m’malo idzakhala boma lakumwamba la Mulungu. Mfumu yake idzakhala Yesu Kristu. Koma olamulira naye monga mbali ya “miyamba yatsopano” adzakhala atsatiri ake okhulupirika 144,000wo.—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3.

9. (a) Kodi “dziko [lapansi] latsopano” nchiyani? (b) Kodi dziko lapansi limene lidzachotsedwalo nchiyani?

9 Pamenepa, kodi nchiyani chimene chiri “dziko latsopano”? Siliri pulaneti latsopano. Mulungu analenga pulaneti Dziko Lapansi lino labwino kwambiri kwa anthu kuti akhalepo, ndipo ndicho chifuniro chake kuti likhalebe kosatha. (Salmo 104:5) “Dziko latsopano” limatanthauza kagulu kapena gulu la anthu latsopano. Baibulo kawirikawiri limagwiritsira ntchito mawuwo “dziko lapansi” m’njira yoteroyo. Mwa chitsanzo, limati: “Dziko lapansi [kutanthauza, anthu] linali la chinenedwe chimodzi.” (Genesis 11:1) “Dziko lapansi” limene lidzawonongedwa ndilo anthu amene akudzipanga kukhala mbali ya dongosolo la zinthu loipa lino. (2 Petro 3:7) “Dziko [lapansi] latsopano” limene likulowa m’malo lidzapangika ndi atumiki owona a Mulungu amene adzilekanitsa ndi dziko la anthu oipa lino.—Yohane 17:14; 1 Yohane 2:17.

10. (a) Kodi ndani amene alinkusonkhanitsidwa tsopano, ndipo akusonkhanitsiridwa m’chiyani? (b) Malinga ndi kunena kwa malemba pamasamba otsatirapowo, kodi nchiyani chimene chidzachitidwa padziko lapansi laparadaiso chimene maboma aanthu sangachite?

10 Patsopano lino anthu a mafuko ndi mitundu yonse amene adzapanga mbali ya “dziko lapansi latsopano” alinkusonkhanitsidwira mu mpingo Wachikristu. Chigwirizano ndi mtendere zimene ziri pakati pawo ndicho chisonyezero chaching’ono chabe cha zimene zidzapangitsa kukhala padziko lapansi laparadaiso pambuyo pa Harmagedo kukhala chikondwerero chachikulu. Ndithudi, ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zimene palibe boma laanthu likanatha kuyembekezera ngakhale kuchita. Tangolingalirani owerengeka a madalitso oterowo pamasamba otsatirapowo.

UBALE WACHIKONDI WA ANTHU ONSE

“Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.

“Tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe . . . Sadzamvanso njala, kapena ludzu.”—Chivumbulutso 7:9, 16.

MTENDERE PAKATI PA ANTHU NDI NYAMA

“Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.”—Yesaya 11:6; Yesaya 65:25.

PALIBENSO KUDWALA, UKALAMBA KAPENA IMFA

“Pamenepa maso a khungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzayimba.”—Yesaya 35:5, 6.

“Ndi Mulungu yekha adzakhala nawo. . . Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

AKUFA AKUBWEZERETSEDWA KU MOYO

“Ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”Yohane 5:28, 29.

“Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m’menemo.”—Chivumbulutso 20:13.

11. Kodi nchiyani chimene kawirikawiri chimawononga mtundu wa paradaiso amene anthu amapanga tsopano?

11 Paradaiso muufumu wa Mulungu adzakhala wabwino kwambiri chotani nanga koposa chirichonse chimene dongosolo lakale lino lingapereke! Zowona, anthu ena lerolino apanga malo kumene iwo akukhala kukhala chimene chimawoneka ngati paradaiso. Koma anthu amene akukhala limodzi m’malo amenewa angakhale opanda chikondi ndi adyera, ndipo angadanedi wina ndi mnzake. Ndipo, m’kupita kwa nthawi, amadwala, kukalamba ndi kufa. Komabe, pambuyo pa Harmagedo, paradaiso padziko lapansi adzaphatikizapo zina zambiri koposa chabe nyumba zokongola, minda ndi mapaki.

12, 13. (a) Kodi ndimikhalidwe ya mtendere yotani imene idzakhalapo pambuyo pa Harmagedo? (b) Kodi nchiyani chimene chikufunika kuchititsa mikhalidwe imeneyi?

12 Taganizirani. Anthu a mafuko ndi mitundu yonse adzaphunzira kukhala limodzi monga banja limodzi la abale ndi alongo. Iwo adzakondanadi. Palibe adzakhala wodzikonda kapena wopanda chifundo. Palibe adzada munthu wina chifukwa chabe cha fuko lake, khungu, kapena malo kumene akuchokera. Tsankho lidzaleka kukhalako. Aliyense padziko lapansi adzakhala bwenzi ndi mnansi weniweni wa munthu aliyense. Ndithudi, lidzakhala paradaiso m’njira yauzimu. Kodi mungafune kukhala m’paradaiso ameneyu pansi pa “miyamba yatsopano”?

13 Lerolino anthu amalankhula kwambiri za kukhalira limodzi mu mtendere, ndipo akhazikitsadi gulu la “Mitundu Yogwirizana.” Komabe anthu ndi mitundu ngogawanika koposa kale lonse. Kodi nchiyani chimene chikufunika? Mitima ya anthu ikufunika kusintha. Koma nkosathekadi kuti maboma a dziko lino achite chozizwitsa choterocho. Komabe, uthenga wa Baibulo wonena za chikondi cha Mulungu, uli kuchichita.

14. Kodi nchiyani chimene chikuchitika tsopano kutsimikizira kuti mikhalidwe yaparadaiso imeneyi idzapezedwa?

14 Itaphunzira za dongosolo latsopano lolungama, mitima ya anthu ambiri irinkusonkhezeredwa kukonda Mulungu. Ndipo motero iwo amayamba kuchitanso mwachikondi kwa ena, monga momwedi Mulungu amachitira. (1 Yohane 4:9-11, 20) Kumeneku kumatanthauza kusintha kwakukulu m’miyoyo yawo. Ambiri amene anali oipa ndi anjiru, ngati nyama zoipa, motero akhala ofatsa ndi amtendere. Mofanana ndi nkhosa zomvera, iwo akusonkhanitsidwira m’gulu lankhosa Lachikristu.

15. (a) Kodi pali magulu awiri otani a Akristu? (b) Kodi ndani amene adzakhala oyambirira kupanga “dziko [lapansi] latsopano”?

15 Kwa zaka zoposa 1,900 pakhala kusonkhanitsidwira pamodzi kwa “kagulu kankhosa” ka Akristu 144,000 amene adzalamulira ndi Kristu. Owerengeka chabe a amenewa atsala padziko lapansi; ochuluka ali kale kulamulira ndi Kristu kumwamba. (Luka 12:32; Chivumbulutso 20:6) Koma ponena za Akristu ena, Yesu anati: “Nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili [la “kagulu kankhosa]; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Yohane 10:16) “Khamu lalikulu” la “nkhosa zina” zimenezi tsopano lirinkusonkhanitsidwa. Ilo lidzapanga oyambirira a “dziko [lapansi] latsopano.” Yehova adzalitetezera kupyola “chisautso chachikulu” pa mapeto a dongosolo loipa lino kuti likhalebe ndi moyo m’paradaiso wapadziko lapansi.—Chivumbulutso 7:9, 10, 13-15.

16. Kodi nchozizwitsa chotani chimene chidzapangitsa kukhala limodzi ndi nyama kukhala chosangalatsa?

16 Pambuyo pa Harmagedo chozizwitsa china chidzawonjezera mikhalidwe yaparadaiso. Nyama monga ngati mikango, anyalungwe, akambuku ndi zimbalangondo, zimene tsopano zingakhale zowopsa, zidzakhala pa mtendere. Pa nthawi imeneyo kudzakhala bwino kwambiri chotani nanga kuyenda m’nkhalango ndi kutsagana kwa kanthawi ndi mkango m’khundu mwanu, ndipo mwina mwake pambuyo pake ndi chimbalangondo chachikulu! Aliyense sadzafunikiranso kuwopa chamoyo china.

17, 18. (a) Kodi nchochititsa chisoni chotani chimene sichidzakhalakonso m’dziko lapansi laparadaiso? (b) Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti thanzi langwiro lidzapezedwa ndi onse?

17 Komabe mosasamala kanthu mmene nyumba ndi minda yamaluwa zingakhalire zokongola, mmene anthu angakhalire okoma mtima ndi achikondi, kapena mmene zinyama zingakhalire zaubwenzi, ngati tikadwala, kukalamba ndi kufa pakakhalabe chisoni. Koma kodi ndani amee angapereke thanzi langwiro kwa onse? Maboma aanthu alephera kuchotsa khensa, nthenda zamtima ndi nthenda zina. Komabe ngakhale ngati iwo akanati atero, madokotala amavomereza kuti zimenezi sizikaleketsa anthu kukalamba. Tikanakalambabe. M’kupita kwa nthawi maso athu akanagwa khungu, matupi athu akanafooka, khungu lathu likanachita makwinya ndipo ziwalo m’kati mwa matupi athu zikanaduka. Imfa ikanatsatira. Nzachisoni chotani nanga!

18 Pambuyo pa Harmagedo, m’dziko lapansi laparadaiso, chozizwitsa chachikulu chochitidwa ndi Mulungu chidzasintha zonsezo, pakuti lonjezo Labaibulo ndilo: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi anasonyeza mphamvu yake ya kuchiza mitundu yonse ya kudwala ndi nthenda, imene imapezeka chifukwa cha uchimo umene tinalandira kwa Adamu. (Marko 2:1-12; Mateyu 15:30, 31) Kukalamba kudzaleketsedwanso mu ulamuliro Waufumu. Nkhalamba zidzaphukiradi kachiwiri. Inde, ‘thupi la munthu lidzakhala lanthete kwambiri koposa mu ubwana wake.’ (Yobu 33:25) Chidzakhala chikondwerero chotani nanga pa nthawi imeneyo kudzuka mmawa uliwonse ndi kuzindikira kuti uli ndi thanzi labwino kwambiri koposa mmene unaliri dzulo!

19. Kodi ndimdani wotsiriza wotani amene adzafafanizidwa, ndipo motani?

19 Ndithudi palibe aliyense wokhala ndi thanzi launyamata ndi langwiro m’dziko lapansi laparadaiso adzafunanso kufa. Ndipo palibe aliyense adzafunikira kufa! Kulandira kwawo mapindu a nsembe yadipo kudzatanthauza potsirizira pake kusangalala ndi mphatso yabwino kwambiri ya Mulungu ya “moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Monga momwe Baibulo likunenera, Kristu “ayenera kuchita ufumu kufikira atayika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.”—1 Akorinto 15:25, 26; Yesaya 25:8.

20. Kodi ndani, kuphatikiza pa anthu okhala ndi moyo tsopano, amene adzasangalala ndi dziko lapansi laparadaiso, ndipo kodi zimenezo zidzakhala zothekera motani?

20 Ngakhale anthu amene ali akufa tsopano lino adzasangalala ndi dziko lapansi laparadaiso. Iwo adzabwerera kumoyo! Motero, pa nthawi imeneyo, m’malo mwa zilengezo za imfa, kudzakhala mbiri zosangalatsa zonena za awo amene aukitsidwa. Kudzakhala bwino chotani nanga kulandiranso kuchokera kumanda atate akufa, amayi, ana ndi okondedwa ena! Palibe nyumba zamaliro, manda kapena miyala yapamanda zidzatsala kuti ziwononge kukongola kwa dziko lapansi laparadaiso.

21. (a) Kodi ndani amene adzathandiza kuwona kuti malamulo ndi zilangizo za “miyamba yatsopano” zikuchitidwa? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti tikufunadi “miyamba yatsopano ndi “dziko [lapansi] latsopano”?

21 Kodi ndani amene adzalamulira kapena kutsogoza zochitika padziko lapansi laparadaiso? Malamulo ndi zilangizo zonse zidzachokera ku “miyamba yatsopano” kumwamba. Koma padziko lapansi padzakhala amuna okhulupirika oikidwa kuwona kuti malamulo ndi zilangizo zimenezi zikuchitidwa. Chifukwa chakuti amuna amenewa akuimira ufumu wakumwamba m’njira yapadera, Baibulo limawatcha “akalonga.” (Yesaya 32:1, 2; Salmo 45:16) Ngakhale mumpingo Wachikristu lerolino amuna amaikidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu kusamalira ndi kutsogoza zochita zake. (Machitidwe 20:28) Pambuyo pa Harmagedo tingakhale ndi chidaliro chakuti Kristu adzalinganiza kuti amuna oyenera akuikidwa kuimira boma Laufumu, pakuti pa nthawi imeneyo adzakhala ndi ulamuliro wachindunji m’zochitika za dziko lapansi. Kodi mungasonyeze motani kuti mukuyembekezera mwaphamphu “miyamba yatsopano” ya Mulungu ndi “dziko [lapansi] latsopano”? Mwa kuchita zonse zimene mungathe kukwaniritsa zofunika za kukhala ndi moyo m’dongosolo latsopano lolungama limenelo.—2 Petro 3:14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena