Wokana Kristu
Tanthauzo: Liwu lakuti Wokana Kristu limatanthauza wotsutsana kapena woloŵa m’malo mwa Kristu. Liwulo limagwira ntchito kwa onse amene amakana zimene Baibulo limanena ponena za Yesu Kristu, onse amene amatsutsa Ufumu wake, ndi onse amene amachitira nkhalwe otsatira ake. Limaphatikizanso anthu, magulu, ndi mitundu imene monyenga imanena kukhala ikuimira Kristu kapena imene mosayenerera imadzipatsa ntchito ya Mesiya.
Kodi Baibulo limatchula wokana Kristu mmodzi yekha?
1 Yoh. 2:18: “Ana inu, ndinthaŵi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Kristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Kristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndinthaŵi yotsiriza iyi.”
2 Yoh. 7: “Onyenga ambiri adatuluka kuloŵa m’dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Kristu anadza m’thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Kristu.” (Tamverani kuti “okana Kristu ambiri” a 1 Yoh. 2:18 panopa akutchulidwa mwa chiungwe kukhala “Wokana Kristu.”)
Kodi kudza kwa wokana Kristu kunasungidwira nthaŵi yamtsogolo?
1 Yoh. 4:3: “Mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Kristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m’dziko lapansi tsopano lomwe.” (Zimenezo zinalembedwa pafupifupi cha kumapeto kwa zaka za zana loyamba C.E.)
1 Yoh. 2:18: “Ngakhale tsopano alipo okana Kristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndinthaŵi yotsiriza iyi.” (Mwa kunena kuti “nthaŵi yotsiriza” Yohane mwachiwonekere anatanthauza mapeto a nyengo ya atumwi. Atumwi ena anali atafa, ndipo Yohane mwiniyo anali wokalamba kwambiri.)
Ena a odziŵika kukhala wokana Kristu—
Anthu amene amakana kuti Yesu alidi Mesiya
1 Yoh. 2:22: “Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Kristu [kapena, Mesiya, wodzozedwayo]? Iye ndiye wokana Kristu.”
Onse okana kuti Yesu ali Mwana wapadera wa Mulungu
1 Yoh. 2:22: “Iye ndiye wokana Kristu, amene akana Atate ndi Mwana.”
Yerekezerani ndi Yohane 10:36; Luka 9:35.
Ampatuko
1 Yoh. 2:18, 19: “Alipo okana Kristu ambiri . . . Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife.”
Otsutsa atsatiri owona a Kristu
Yoh. 15:20, 21: “Ngati anandilondalonda ine, adzakulondalondani inunso . . . Izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa.”
Anthu alionse paokha ndi mitundu imene imatsutsa Kristu monga Mfumu kapena amene monyenga amadzinenera kukhala akuchita ntchito Yaumesiya
Sal. 2:2: “Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, kutsutsana naye Yehova, ndi wodzozedwa wake [Kristu, kapena Mesiya].”
Wonaninso Chivumbulutso 17:3, 12-14; 19:11-21.
Mat. 24:24: “Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzawonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe.”