Mutu 30
Kuyankha Omuimba Mlandu
PAMENE atsogoleri achipembedzo Achiyuda aimba mlandu Yesu wa kuswa Sabata, iye akuyankha kuti: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, inenso ndigwira ntchito.”
Mosasamala kanthu za chinenezo cha Afarisiwo, ntchito ya Yesu siri ya mtundu woletsedwa ndi lamulo la Sabata. Ntchito yake ya kulalikira ndi kuchiritsa ndiyo gawo lochokera kwa Mulungu, ndipo m’kutsanzira chitsanzo cha Mulungu, amaichita tsiku ndi tsiku. Komabe, yankho lake lapangitsa Ayudawo kukwiyadi kwambiri koposa mmene analiri, ndipo akufunafuna kumupha. Chifukwa ninji?
Chiri chifukwa chakuti tsopano iwo sakukhulupirira kokha kuti Yesu akuswa Sabata koma akulingalira kudzinenera kwakeko kwa kukhala Mwana weniweni wa Mulungu kukhala mwano. Komabe, Yesu saali wamantha ndipo akuwayankha mowonjezereka ponena za unansi wake woyanjidwa ndi Mulungu. “Atate akonda mwana,” iye akutero, “namuwonetsa zonse azichita yekha.”
“Monga Atate aukitsa akufa,” Yesu akupitiriza, “momwemonso mwana apatsa moyo iwo amene iye afuna.” Ndithudi, Mwanayo akuukitsa kale akufa m’njira yauzimu! “Iye wakumva mawu anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma ine,” Yesu akutero, “wachokera kuimfa, naloŵa m’moyo.” Inde, iye akupitiriza kuti: “Ikudza nthaŵi, ndipo iripo tsopano, imene akufa adzamva mawu a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.”
Ngakhale kuli kwakuti kulibe cholembedwa chirichonse chakuti Yesu pakali pano waukitsadi aliyense kuchokera kumanda, akuuza omuimba mlandu kuti kuukitsa kwenikweni kumeneko kwa akufa kudzachitika. “Musazizwe ndi ichi,” iye akutero, “kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”
Kufikira panthaŵi ino, Yesu mwachiwonekere sanafotokoze poyera ntchito yake yofunika m’chifuno cha Mulungu mwanjira yapadera ndi yotsimikizirika yotero. Koma oimba mlandu Yesu ali ndi umboni woposa wa iyemwini ponena za zinthu zimenezi. “Inu munatuma kwa Yohane,” Yesu akuwakumbutsa, “ndipo iye anachitira umboni chowonadi.”
Zaka ziŵiri zokha zapitazo, Yohane Mbatizi anauza atsogoleri achipembedzo Achiyuda ameneŵa za amene Analinkudza pambuyo pake. Powakumbutsa za kulingalira kwawo mwaulemu kaamba ka Yohane amene tsopano ali m’ndende, Yesu akuti: “Inu munafuna kukondwera m’kuunika kwake kanthaŵi.” Yesu akuwakumbutsa zimenezi ndi chiyembekezo cha kuthandiza, inde kuwapulumutsa. Komabe iye sakudalira paumboni wa Yohane.
“Ntchito zomwe ndizichita [kuphatikizapo chozizwitsa chimene wangochita kumene] zindichitira umboni, kuti Atate anandituma ine.” Komanso, Yesu akupitiriza kuti: “Atate wonditumayo, iyeyu wandichitira umboni.” Mulungu anachitira umboni Yesu, mwachitsanzo, paubatizo wake, akumati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa.”
Ndithudi, oimba mlandu Yesu alibe chodzikhululukira chomkanira. Malemba enieniwo amene iwo amadzinenera kukhala akufufuza amachitira umboni za iye! “Mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira ine,” Yesu akutero, “pakuti iyeyu analembera za ine. Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mawu anga?” Yohane 5:17-47; 1:19-27; Mateyu 3:17.
▪ Kodi nchifukwa ninji ntchito ya Yesu siiri yoswa Sabata?
▪ Kodi Yesu akufotokoza motani ntchito yake yofunika m’chifuno cha Mulungu?
▪ Kutsimikiziritsa kuti ali Mwana wa Mulungu, kodi Yesu akusonya ku umboni wa yani?