Mutu 44
Kutontholetsa Namondwe Wochititsa Mantha
TSIKU la Yesu lakhala lodzazidwa ndi zochitika, kuphatikizapo kuphunzitsa makamu pagombe lanyanja ndipo pambuyo pake kufotokoza mafanizo mwamtseri kwa ophunzira ake. Pamene madzulo afika, iye akuti: “Tiwolokere tsidya lina.”
Chakugombe lakummaŵa kwa Nyanja ya Galileya kuli chigawo chotchedwa Dekapoli, kuchokera ku Chigiriki deʹka kutanthauza “khumi,” ndi poʹlis, kutanthauza “mzinda.” Mizinda ya Dekapoli ndiyo phata la anthu Achigiriki, ngakhale kuti mosakayikira iyo irinso kwawo kwa Ayuda ambiri. Komabe, ntchito ya Yesu m’chigawochi njochepa kwambiri. Ngakhale paulendo uno, monga momwe tidzawonera pambuyo pake, iye akulepheretsedwa kukhala nthaŵi yaitali.
Pamene Yesu apempha kuti awolokere kumbali ina, ophunzirawo akumka naye m’ngalaŵa. Komabe, kuchoka kwawoko kwawonedwa. Mwamsanga, ena akukwera ngalaŵa zawo kumkera nawo limodzi. Kutsidyako sikuli kutali kwambiri. Kwenikweni, Nyanja ya Galileya iri kokha yotalika pafupifupi makilomitala 21 ndipo mtunda waukulu woposa kwambiri mbwambi ndiwo makilomitala 12.
Mwachiwonekere Yesu watopa. Chotero, mwamsanga atangochoka iye akugona kumbuyo kwa ngalaŵa, naika mutu wake pamtsamiro, ndipo akugona tulo tofa nato. Angapo a atumwiwo ali amalinyero odziŵa bwino, pokhala atakhala asodzi kwanthaŵi yaitali pa Nyanja ya Galileya. Chotero iwo ali ndi udindo wakuyamba kuyendetsa ngalaŵayo.
Koma umenewu sindiwo ulendo wosavuta. Chifukwa cha mphepo yofunda ya m’mphepete mwa nyanjayo, imene iri pafupifupi mamitala 210 kuchokera pamlingo wanyanja, ndiponso mpweya wozizirira wa m’mapiri apafupiwo, mphepo yamphamvu nthaŵi zina imawomba ndi kuchititsa anamondwe achiwawa panyanjapo. Izi ndizo zimene tsopano zikuchitika. Mwamsanga mafunde akuyenda molimbana ndi ngalaŵa ndipo akugaviriramo, kotero kuti iri pafupi kumira. Komabe, Yesu akupitirizabe kugona!
Amalinyero odziŵa bwinowo akugwira ntchito mwamphamvu kuwongolera bwatolo. Mosakayikira iwo anayamba adutsapo kale mikuntho yotero. Koma panthaŵi ino nzeru zawathera. Powopera miyoyo yawo, iwo akudzutsa Yesu. ‘Ambuye, kodi simusamala? Tikumira!’ iwo akufuula motero. ‘Tipulumutseni, tikumira!’
Podzuka, Yesu akulamulira mphepoyo ndi nyanja kuti: “Tonthola, khala bata.” Ndipo mphepo yowombayo ikuima ndipo nyanja ikukhala bata. Potembenukira kwa ophunzira ake, iye akufunsa kuti: ‘Kodi muchitiranji mantha? Kodi mulibe chikhulupiriro kufikira tsopano?’
Pamenepo, mantha aakulu akugwira ophunzirawo. ‘Kodi kwenikweni munthuyu ndani?’ iwo akufunsana, ‘chifukwa chakuti iye alamula ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera.’
Ndimphamvu yotani nanga imene Yesu akusonyeza! Ndikopereka chitsimikiziro chotani nanga kudziŵa kuti Mfumu yathu iri ndi mphamvu pazinthu zachilengedwe ndi kuti pamene chisamaliro chake chonse chisumikidwa kudziko lathu lapansi mkati mwaulamuliro wake Waufumu, anthu onse adzakhala osungika kuzigumukire za chilengedwe zochititsa mantha!
Pambuyo pakuti namondwe watonthola, Yesu ndi ophunzira ake akufika mosungika pagombe lakummaŵa. Mwinamwake ngalaŵa zina sizinawombedwe ndi namondwe wamphamvuyo ndipo zinabwerera mosungika kwawo. Marko 4:35–5:1; Mateyu 8:18, 23-27; Luka 8:22-26.
▪ Kodi Dekapoli nchiyani, ndipo ali kuti?
▪ Kodi ndimbali zachilengedwe zotani zimene zikuchititsa mikuntho yachiwawa pa Nyanja ya Galileya?
▪ Pamene maluso awo aumalinyero sakuwapulumutsa, kodi ophunzirawo akuchita chiyani?