Mutu 50
Kukonzekera Kuyang’anizana ndi Chizunzo
ATALANGIZA atumwi ake njira zochitira ntchito yolalikira, Yesu akuwachenjeza za otsutsa. Iye akuti: “Tawonani, ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi . . . Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo, ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine.”
Mosasamala kanthu za kukula kwa chizunzo chimene otsatira ake adzayang’anizana nacho, Yesu akulonjeza motsimikizira kuti: “Pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhaŵa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzalankhula chidzapatsidwa kwa inu nthaŵi yomweyo; pakuti wolankhula sindinu, koma ndiwo mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.”
“Ndipo,” Yesu akupitirizabe, “mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.” Iye akuwonjezera kuti: “Adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.”
Kulalikira kuli ndi kufunika kwakukulu. Kaamba ka chifukwa chimenechi Yesu akugogomezera kufunika kwa kuchita mwanzeru kotero kuti akhalebe omasuka kupitiriza ntchitoyo. “Pamene angakuzunzeni inu m’mudzi uwu, thaŵirani mwina,” iye akutero, “indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli kufikira Mwana wa munthu atadza.”
Nzowona kuti Yesu anapereka malangizo ameneŵa, chenjezo, ndi chilimbikitso kwa atumwi ake 12, komanso iwo anali malangizo kwa awo amene akakhala ndi phande m’kulalikira kwapadziko lonse lapansi pambuyo pa imfa yake ndi chiukiriro. Izi zasonyezedwa mwa mawu ake akuti ophunzira ake ‘akadedwa ndi anthu onse,’ osati kokha ndi Aisrayeli kwa amene atumwiwo anatumidwako kukalalikira. Ndiponso, mwachiwonekere atumwiwo sanatengeredwe kwa akazembe ndi mafumu pamene Yesu anawatuma pamkupiti wawo waufupi wokalalikira. Ndi iko komwe, okhulupilira panthaŵiyo sanaperekedwe kuimfa ndi ziŵalo za banja.
Chotero pamene ananena kuti ophunzira ake sadzatha kulalikira kwawo mizinda “kufikira Mwana wa munthu atadza,” Yesu anali kutiuza molosera kuti ophunzira ake sakamaliza kulalikira kuzungulira dziko lapansi lonse lokhalidwa ndi anthu ponena za Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu Mfumu yolemekezedwayo Yesu Kristu isanadze monga woimira wolipsira wa Yehova pa Armagedo.
Popitirizabe ndi malangizo ake a kulalikira, Yesu akuti: “Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena kapolo saposa mbuye wake.” Chotero otsatira a Yesu ayenera kuyembekezera kuchitiridwa moipa kumodzimodziko ndi chizunzo monga momwe iye anachitira polalikira Ufumu wa Mulungu. Komabe iye akulangiza kuti: “Musamawopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muwope iye, wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.”
Yesu anali kudzakhazikitsa chitsanzo m’nkhani imeneyi. Iye akakhoza kupirira imfa mosawopa mmalo mwa kugonjera kukhulupirika kwake motsutsana ndi Uyo amene ali ndi mphamvu yonse, Yehova Mulungu. Inde, ali Yehova amene angathe kuwononga “moyo” wamunthu (panopa kutanthauza ziyembekezo zam’tsogolo za munthuyo monga wamoyo), kapena mmalomwake angathe kuukitsa munthuyo kudzasangalala ndi moyo wosatha. Yehova ali Atate wachikondi, ndi wokoma mtima chotani nanga!
Kenako Yesu akulimbikitsa ophunzira ake ndi fanizo limene limagogomezera chisamaliro chachikondi cha Yehova kwa iwo. “Kodi mpheta ziŵiri sizigulidwa ndi kakobiri?” iye akufunsa motero. “Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: komatu inu, matsitsi onse a m’mutu mwanu aŵerengedwa. Chifukwa chake musamawopa; inu mupambana mpheta zambiri.”
Uthenga wa Ufumu umene Yesu akutuma ophunzira ake kukalalikira udzagaŵanitsa mabanja, pamene ziŵalo zina ziulandira ndipo zina ziukana. “Musalingalire kuti ndinadzera kudzaponya mtendere padziko lapansi,” iye akufotokoza motero, “sindinadzera kudzaponya mtendere, koma lupanga.” Motero, kuti chiŵalo cha banja chilandire chowonadi cha Baibulo chimafunikira kulimba mtima. “Iye wakukonda atate wake kapena amake koposa ine, sayenera ine,” Yesu akutero, “ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa ine, sayenera ine.”
Pomaliza malangizo ake, Yesu akufotokoza kuti olandira ophunzira ake akulandiranso iye. “Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa aang’ono aŵa chikho chokha cha madzi ozizira, padzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.” Mateyu 10:16-42.
▪ Kodi ndimachenjezo otani amene Yesu akuwapereka kwa ophunzira ake?
▪ Kodi ndichilimbikitso chotani ndi chitonthozo zimene akuwapatsa?
▪ Kodi nchifukwa ninji malangizo a Yesu amagwiranso ntchito kwa Akristu amakono?
▪ Kodi ndim’njira yotani imene wophunzira wa Yesu aliri wosaposa mphunzitsi wake?