Mutu 53
Wolamulira Woposa Waumunthu Wokhumbidwayo
PAMENE Yesu mozizwitsa adyetsa zikwi zambirizo, anthuwo akuzizwa. “Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m’dziko lapansi,” iwo akutero. Iwo akumaliza osati kokha kuti Yesu ayenera kukhala mneneri wamkulu kwambiri kuposa Mose komanso kuti akakhala wolamulira wabwino koposa. Chotero iwo akuchita upo kuti amgwire ndi kumpanga iye mfumu.
Komabe, Yesu, wadziŵa za chimene anthuwo akulinganiza. Chotero iye mwamsanga akuchoka kuti apeŵe kugwidwa ndi iwo mokakamiza. Iye akuuza anthu kuchoka nafulumizitsa ophunzira ake kuloŵa m’bwato lawo nabwerera mmbuyo cha ku Kapernao. Pamenepo iye akuloŵa m’phiri kukapemphera. Usiku umenewo Yesu ali kumeneko yekhayekha.
Mwamsanga kusanache Yesu akuunguza kuchokera pamalo ake apamwambawo nawona mafunde akunyamuka panyanja ndi mphepo yaikulu. Mounikiridwa ndi pafupifupi mwezi wathunthu, popeza kuti iri nthaŵi ya pafupi ndi Paskha, Yesu akuwona bwato limene liri ndi ophunzira ake liri m’mavuto kuti lipyole mafundewo. Amunawo akupalasa ndi mphamvu zawo zonse.
Powona izi, Yesu akutsika kuchokera m’phirimo nayamba kuyenda kumka cha kubwatolo modutsa mafunde. Bwatolo layenda pafupifupi makilomitala asanu kapena asanu ndi limodzi pamene Yesu akulifikira. Komabe, iye akupitirirabe monga ngati kuti adzalilambalala. Pamene ophunzira amuwona, iwo akufuula kuti: “Ndinzukwa!”
Mowatonthoza Yesu akuyankha kuti: “Ndine; musawope.”
Koma Petro akuti: “Ambuye, ngati ndinutu, mundiuzeni ndidze kwa inu pamadzi.”
“Idza,” Yesu akuyankha.
Pamenepo, Petro, akutuluka m’ngalaŵa, nayenda pamadzi kumka kwa Yesu. Koma powona mphepoyo, Petro akuchita mantha, nayamba kumira, nafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni ine!”
Mwamsanga potambasula dzanja lake, Yesu akumgwira, akumati: “Iwe wokhulupirira pang’ono, wakayikiranji mtima?”
Petro ndi Yesu atabwerera m’ngalaŵa, mphepoyo ileka, ndipo ophunzirawo akuzizwa. Koma kodi iwo ayenera kutero? Ngati iwo anazindikira ‘tanthauzo la mikate’ mwa kuzindikira chozizwitsa chachikulu chimene Yesu anachita maola ochepekera apitawo pamene anadyetsa zikwi zambiri ndi mitanda isanu yokha ndi tinsomba tiŵiri, pamenepo sikukanakhala kozizwitsa kwambiri kuti iye akanakhoza kuyenda pamadzi nachititsa mphepo kuchita bata. Komabe, tsopano, ophunzirawo akugwadira Yesu naati: “Zowonadi ndinu Mwana wa Mulungu.”
M’nthaŵi yaifupi, iwo akufika pa Genesarete, chigwa chokongola, ndi chachonde, pafupi ndi Kapernao. Kumeneko iwo akuimikako ngalaŵa. Koma pamene akupita kugombe, anthu akuzindikira Yesu ndipo akumka kumilaga yozungulira, kukapeza odwala. Pamene ameneŵa abweretsedwa pamakama awo ndi kukhudza kokha mphonje ya zovala za Yesu, akuchira kotheratu.
Pakali pano, khamu limene linawona kudyetsedwa kozizwitsa kwa zikwi zambiri likuzindikira kuti Yesu wachoka. Chotero pamene ngalaŵa zazing’ono zochokera ku Tiberiya zifika, iwo akukwera zimenezi napalasa kumka ku Kapernao kukafunafuna Yesu. Pamene ampeza, akufunsa kuti: “Rabi, munadza kuno liti?” Yesu akuwadzudzula, monga momwe tidzawonera mwamsanga. Yohane 6:14-25; Mateyu 14:22-36; Marko 6:45-56.
▪ Yesu atatha kudyetsa mozizwitsa zikwizo, kodi anthu akufuna kutani naye?
▪ Kodi Yesu akuwonanji kuchokera m’phiri mmene adapita, ndipo kenako akuchitanji?
▪ Kodi nchifukwa ninji ophunzirawo sayenera kuzizwa ndi zinthu zimenezi?
▪ Kodi nchiyani chimene chikuchitika atafika kumtunda?