Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 62
  • Phunziro la Kudzichepetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunziro la Kudzichepetsa
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Apereka Phunziro m’Kudzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kufunika Kokhala Wodzichepetsa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Changu cha Kulambira Yehova
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 62

Mutu 62

Phunziro la Kudzichepetsa

ATACHIRITSA mnyamata wogwidwa ndi chiŵanda m’dera la pafupi ndi Kaisareya wa Filipi, Yesu akukhumba kubwerera kwawo ku Kapernao. Komabe, iye akufuna kukhala paulendo ndi ophunzira ake okha kotero kuti awakonzekeretse mowonjezereka kaamba ka imfa yake ndi mathayo awo pambuyo pake. “Mwana wa munthu aperekedwa m’manja mwa anthu,” akuwafotokozera motero, “ndipo adzamupha iye; koma ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.”

Ngakhale kuti Yesu analankhula za zimenezi poyambapo, ndipo atumwi atatu anawonadi kusandulika mwa kumene ‘kuchokapo’ kwake kunakambitsiridwa, otsatira ake sakumvetsetsabe nkhaniyo. Ngakhale kuti palibe aliyense wa iwo amene akukana kuti iye adzaphedwa, monga mmene Petro adachitira poyamba paja, iwo akuchita mantha kumfunsa zowonjezereka za izo.

Pomalizira pake akufika m’Kapernao, komwe kwakhala ngati malikulu mkati mwa uminisitala wa Yesu. Ilinso tauni ya kwawo kwa Petro ndi atumwi ena angapo. Kumeneko, amuna okhometsa msonkho wa kachisi akufikira Petro. Mwinamwake kuyesa kuloŵetsa Yesu m’kulakwira mwambo wovomerezedwa, iwo akufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu sapereka lupiyalo [la pakachisi] ? ”

“Apereka,” Petro akuyankha motero.

Yesu, yemwe ayenera kukhala atangofika kumene panyumbapo pambuyo pake, akudziŵa chimene chachitika. Motero ngakhale pamene Petro asananene nkhaniyo kwa iye, Yesu akufunsa kuti: “Simoni, uganiza bwanji? mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? kwa ana awo kodi, kapena kwa akunja?”

“Kwa akunja,” Petro akuyankha motero.

“Chifukwa chake anawo ali aufulu,” akutero Yesu. Popeza kuti Atate wa Yesu ali mfumu yachilengedwe chaponseponse, Amene akulambiridwa pakachisi, sichiri kwenikweni chofunika cha lamulo kwa Mwana wa Mulungu kupereka msonkho wa kachisi. “Koma kuti ife tisawakhumudwitse,” Yesu akutero, “pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo lupiya; [madrakima anayi] tenga limeneli, nuwapatse pamutu pa iwe ndi ine.”

Pamene ophunzirawo asonkhana pamodzi atabwerera ku Kapernao, mwinamwake panyumba ya Petro, akufunsa kuti: “Ndani kodi ali wopambana muufumu wakumwamba?” Yesu akudziŵa chimene chikusonkhezera funso lawo, pokhala akuzindikira chimene chinali kuchitika pakati pawo pamene ankamtsatira m’mbuyo pakubwerera kwawo kuchokera ku Kaisareya wa Filipi. Chotero iye akufunsa kuti: “Munali kutsutsana ninji?” Pochititsidwa manyazi, ophunzirawo akukhala chete, popeza anatsutsana iwo okha za amene akakhala wamkulu.

Pambuyo pa pafupifupi zaka zitatu za kuphunzitsa kwa Yesu, kodi kukuwoneka kukhala kosakhulupirika kuti ophunzirawo akakhala ndi mkangano wotero? Eya, kumavumbula chiyambukiro champhamvu cha kupanda ungwiro kwaumunthu, ndiponso ndi chiyambi cha chipembedzo. Chipembedzo Chachiyuda chimene ophunzirawo analeledweramo chinagogomezera malo antchito kapena udindo wa munthu m’zochita zonse. Ndiponso, mwinamwake Petro, chifukwa cha lonjezo la Yesu la kulandira ‘mfungulo’ zina za Ufumu, analingalira kukhala wamkulu. Yakobo ndi Yohane angakhale anali ndi malingaliro ofananawo chifukwa cha kukhala atayanjidwa kuwona kusandulika kwa Yesu.

Mulimonse mmene zingakhalire, Yesu akukhazikitsa chitsanzo chosonkhezera mtima poyesayesa kuwongolera maganizo awo. Iye akuitana kamwana, nakaimitsa pakati pawo, nakakoloŵeka dzanja m’khosi, nati: “Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzaloŵa konse muufumu wakumwamba. Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana muufumu wakumwamba. Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka chifukwa cha dzina langa, alandira ine.”

Ndinjira yabwino kwambiri chotani nanga yowongolera ophunzira ake! Yesu sakuwakwiyira ndi kuwatcha odzikuza, aumbombo, kapena odzifunira malo. Ayi, koma iye akupereka fanizo la chiphunzitso chake chowongolera mwa kugwiritsira ntchito chitsanzo cha ana achichepere amene ali odekha mwamakhalidwe ndi osadzifunira malo ndi amene mozoloŵereka alibe lingaliro la kukhala ndi udindo pakati pawo. Motero Yesu akusonyeza kuti ophunzira ake afunikira kukulitsa mikhalidwe imeneyi imene imasonyeza ana odzichepetsa. Monga momwe Yesu akumalizira kuti: “Iye wakukhala wamng’onong’ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.” Mateyu 17:22-27; 18:1-5; Marko 9:30-37; Luka 9:43-48.

▪ Paulendo wobwerera ku Kapernao, kodi ndi chiphunzitso chotani chomwe Yesu akubwereza, ndipo kodi chikulandiridwa motani?

▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu saali pansi pa thayo la kupereka msonkho wa kachisi, komabe kodi nchifukwa ninji iye akuwupereka?

▪ Kodi mwinamwake nchiyani chinadzutsa mkangano wa ophunzirawo, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu akuwongolelera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena