Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 78
  • Khalani Okonzekera!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Okonzekera!
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Okonzekera!
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Woyang’anira Nyumba Wokhulupirika Ayenera Kukhala Wokonzeka
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Muzichita Zinthu Mwanzeru Pokonzekera Zakutsogolo
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Fanizo la Matalente Limatiphunzitsa Kufunika Kochita Zinthu Mwakhama
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 78

Mutu 78

Khalani Okonzekera!

PAMBUYO pa kuchenjeza makamuwo za chisiliro, ndi kuchenjeza ophunzira ake za kupereka chisamaliro chopambanitsa pazinthu zakuthupi, Yesu akulimbikitsa kuti: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.” Chotero iye akuvumbula kuti ndichiŵerengero chochepa chokha (chodziŵidwa pambuyo pake monga 144,000) chimene chidzakhala mu Ufumu wakumwamba. Ambiri a amene akulandira moyo wosatha adzakhala nzika za padziko lapansi za Ufumuwo.

Ndimphatso yodabwitsa chotani nanga, ‘ufumuwo’! Pofotokoza kulabadira koyenerera kumene ophunzirawo ayenera kukhala nako kuti ayilandire, Yesu akuwafulumiza kuti: “Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo.” Inde, iwo akayenera kugwiritsira ntchito chuma chawo kupindulitsa ena mwauzimu ndipo motero kusonkhanitsira “chuma chosatha m’mwamba.”

Kenako Yesu akulangiza ophunzira ake kukhala okonzekera za kubweranso kwake. Iye akuti: “Khalani odzimangitsa m’chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka; ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wawo, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo. Odala akapolowo amene mbuye wawo, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m’chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.”

M’fanizo limeneli, kukonzekera kwa akapolowo pakubwera kwa mbuye wawo kukusonyezedwa mwa kukwinya kwawo mikanjo yaitali ndi kuimangitsitsa m’chuuno mwawo ndi kupitirizabe kusamalira kwawo mathayo awo mkati mwa usiku ndi kuunika kwa nyali zodzadzidwa mafuta bwino lomwe. Yesu akufotokoza kuti: ‘Ngati mbuyeyo akadza paulonda wachiŵiri [kuyambira pafupifupi 9 koloko usiku mpaka pakati pa usiku], ngakhale paulonda wachitatu [kuyambira pakati pa usiku mpaka pafupifupi 3 koloko mbandakucha], nawapeza ali okonzekera, odala ameneŵa!’

Mbuyeyo akupatsa mphotho akapolo ake m’njira yachilendo. Iye akuwachititsa kuseyama pagome nayamba kuwatumikira. Iye akuwachitira osati, monga akapolo, koma monga mabwenzi ake okhulupirika. Ndimphoto yabwino kwambiri chotani nanga chifukwa cha kupitirizabe kugwirira ntchito mbuye wawo mkati mwa usiku wonse poyembekezera kubweranso kwake! Yesu akumaliza mwa kunena kuti: “Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthaŵi imene simulingilira, Mwana wa munthu akudza.”

Tsopano Petro akufunsa kuti: “Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?”

Mmalo mwa kuyankha mwachindunji, Yesu akupereka fanizolo lina. “Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru,” iye akufunsa motero, “amene mbuye wake adzamuika kapitawo wa pabanja lake, kuwapatsa iwo phoso lawo panthaŵi yake? Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero. Ndinena ndinu zowona, kuti adzamuika iye kapitawo wa pazonse ali nazo.”

Mwachiwonekere ‘mbuyeyo’ ndiye Yesu Kristu. “Kapitawo” amaphiphiritsira “kagulu ka nkhosa” ka ophunzira monga kagulu, ndipo “banja lake” limasonya kukagulu kamodzimodzika ka 144,000 kamene kakulandira Ufumu wakumwamba, koma mawu ameneŵa amagogomezera ntchito yawo monga munthu aliyense payekha. “Zonse” zimene kapitawo wokhulupirika waikidwa kuyang’anira ziri chuma chaufumu cha mbuyeyo padziko lapansi, chimene chimaphatikizapo nzika za padziko lapansi za Ufumuwo.

Popitiriza fanizolo, Yesu akusonya kukuthekera kwakuti sionse a ziŵalo za kagulu ka mdindo, kapena kapolo, adzakhala okhulupirika, akumafotokoza kuti: “Kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera; mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera . . . , nadzamuika dera lake.”

Yesu akupitirizabe kusonyeza kuti kudza kwake kwadzetsa nthaŵi yowopsa kwa Ayuda, pamene ena akuvomereza ndipo ena akukana ziphunzitso zake. Zoposa zaka zitatu zapitazo, iye anabatizidwa m’madzi, koma tsopano ubatizo wake mu imfa ukuyandikira nthaŵi zonse, ndipo monga mmene akunenera kuti: “Ndikanikizidwa ine kufikira ukatsirizidwa.”

Atalankhula mawu ameneŵa kwa ophunzira ake, Yesu kachiŵirinso akulankhula ndi khamulo. Iye akudandaula chifukwa cha kukana kwawo mouma khosi kuvomereza umboni wowoneka wa amene iye ali ndi chizindikiro chake. “Pamene paliponse muwona mtambo wokwera kumadzulo,” iye akutero, “pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero. Ndipo pamene mphepo yakummwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi. Onyenga inu, mudziŵa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziŵa bwanji kuzindikira nyengo ino?” Luka 12:32-59.

▪ Kodi ndiangati amene amapanga “kagulu ka nkhosa,” ndipo kodi akulandiranji?

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akugogomezera kufunika kwa kukhala okonzekera kwa ophunzira ake?

▪ M’fanizo la Yesu, kodi ndani amene ali “mbuye,” “mdindo,” “banja lake,” ndi “zonse”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena