Mutu 82
Yesu Apitanso ku Yerusalemu
MWAMSANGA Yesu alinso paulendo, akumaphunzitsa pamzinda ndi mzinda, ndi pamudzi ndi mudzi. Mwachiwonekere iye ali m’chigawo cha Pereya, patsidya pa Mtsinje wa Yordano kuchokera ku Yudeya. Koma ulendo wake ngwa ku Yerusalemu.
Chiphunzitso cha Ayuda chakuti chiŵerengero chokhala ndi polekezera chokha ndicho chidzalandira chipulumutso mwinamwake ndicho chimene chikusonkhezera mwamuna wina kufunsa kuti: “Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo oŵerengeka kodi?” Mwa yankho lake, Yesu akukakamiza anthuwo kuganiza za chimene chiri chofunika kaamba kachipulumutso: “Yesetsani [ndiko kuti, limbanirani, kapena dzimvetseni ululu] kuloŵa pakhomo lopapatiza.”
Kuyesayesa kwamphamvu kotero nkofulumira “chifukwa anthu ambiri,” Yesu akupitiriza motero, “adzafunafuna kuloŵamo, koma sadzakhoza.” Kodi nchifukwa ninji iwo sadzakhoza? Iye akufotokoza kuti ‘pamene mwini nyumba auka natseka chitseko ndipo anthu aimirira kunja ndi kugogoda, akumati, “Ambuye titsegulireni ife,” iye adzati: “Sindidziŵa kumene muchokera inu; chokani pa ine, nonse akuchita chosalungama!” ’
Mwachiwonekere awo otsekeredwa kunja akudza panthaŵi yowakomera. Komatu panthaŵiyo khomo la mwaŵilo latsekedwa ndi kukhomedwa. Kuti aloŵe, akanayenera kukhala atabwera mofulumira, ngakhale kuti kutero panthaŵiyo kukanakhala kosawakomera. Ndithudi, chotulukapo cha chisoni chikuyembekezera awo amene amakankhira pambali kupanga kulambiridwa kwa Yehova kukhala chifuno chawo chachikulu m’moyo!
Kwakukulukulu, Ayuda kwa amene Yesu watumidwako kukatumikira, analephera kugwiritsira ntchito mwaŵi wawo wodabwitsawo wa kuvomereza makonzedwe a Mulungu a chipulumutso. Chotero Yesu akunena kuti iwo adzalira ndi kukukuta mano awo pamene aponyedwa kunja. Kumbali ina, anthu ochokera ‘kumadera akummaŵa ndi kumadzulo, ndi ochokera kumpoto ndi kumwera,’ inde, ochokera kumitundu yonse, ‘adzakhala pansi mu ufumu wa Mulungu.’
Yesu akupitiriza kuti: “Alipo akunthungo amene adzakhala oyamba [osakhala Ayuda onyozedwa, kudzanso Ayuda oponderezedwa] ndipo alipo oyamba [Ayuda oyanjidwa mwakuthupi ndi mwachipembedzo] adzakhala akuthungo.” Kukhala kwawo omalizira kukutanthauza kuti ozengereza, ndi anthu osayamikira otero sadzakhala konse mu Ufumu wa Mulungu.
Afarisi tsopano akudza kwa Yesu nati: “Tulukani, chokani kuno, chifukwa Herode [Antipa] afuna kupha inu.” Kungakhale kwakuti Herode mwiniyo anayambitsa mphekesera imeneyi kuchititsa Yesu kuti achoke m’chigawocho. Herode angakhale anali akuchita mantha pakuphatikizidwa mu imfa ya mneneri wina wa Mulungu monga momwe anachitira m’kuphedwa kwa Yohane Mbatizi. Koma Yesu akuuza Afarisiwo kuti: “Pitani kauzeni nkhandweyo kuti, Tawonani! nditulutsa ziŵanda, nditsiriza machiritso lero ndi maŵa, ndipo mkucha nditsirizidwa.”
Atatsiriza ntchito yake kumeneko, Yesu akupitirizabe ulendo wake wa ku Yerusalemu chifukwa chakuti, monga momwe akufotokozera, “sikuloleka kuti mneneri awonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu.” Kodi nchifukwa ninji kuyenera kuyembekezeredwa kuti Yesu akaphedwera ku Yerusalemu? Chifukwa chakuti Yerusalemu ndiwo malikulu, kumene ziŵalo 71 za bwalo lalikulu lamilandu la Sanhedrin ziri ndi kumene nsembe za nyama zimaperekedwerako. Chifukwa chake, kukakhala kosaloleka kuti “Mwanawankhosa wa Mulungu” asaphedwere kulikonse koma ku Yerusalemu.
“Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe!” Yesu akulira motero, “ha! kaŵirikaŵiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m’mapiko ake, ndipo simunafunayi! Wonani! nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja.” Chifukwa cha kukana Mwana wa Mulungu, mtunduwo ukuweruzidwa!
Pamene Yesu akupitirizabe kupita ku Yerusalemu, iye akuitanidwa kunyumba ya wolamulira wa Afarisi. Liri tsiku la Sabata, ndipo anthu akumuyang’anitsitsa, popeza kuti pamenepo pali munthu wina amene akudwala mbulu, kuunjikana kwa madzi mwinamwake m’mikono yake ndi miyendo. Yesu akulankhula kwa Afarisi ndi akatswiri Achilamulo amene alipo, akumafunsa kuti: “Kodi nkololedwa tsiku la sabata kuchiritsa, kapena iyayi?”
Palibe aliyense akuyankha. Chotero Yesu akuchiritsa munthuyo namuuza kuchoka. Pamenepo akufunsa kuti: “Ndani wa inu bulu wake kapena ng’ombe yake itagwa m’chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la sabata kodi?” Kachiŵirinso, palibe amene akuyankha. Luka 13:22–14:6; Yohane 1:29.
▪ Kodi Yesu akusonyeza kuti nchiyani chimene chifunika kaamba ka chipulumutso, ndipo nchifukwa ninji ambiri atsekeredwa kunja?
▪ Kodi ndani amene ali “akuthungo” amene akukhala oyamba, ndi “oyamba” amene akukhala akuthungo?
▪ Kodi nchifukwa ninji mwinamwake kunanenedwa kuti Herode anafuna kupha Yesu?
▪ Kodi nchifukwa ninji kuli kosaloleka kuti mneneri aphedwere kunja kwa Yerusalemu?