Chigawo 4
Mulungu Akutiuza za Zifuno Zake
1, 2. Kodi tikudziŵa bwanji kuti Mulungu amapereka mayankho kwa ofunsa mowona mtima?
MULUNGU wachikondi amaululadi zifuno zake kwa anthu owona mtima amene amamfunafuna. Iye amapereka mayankho kwa anthu ofunsa mafunso onga akuti chifukwa chake iye walola kuvutika.
2 Baibulo limafotokoza kuti: “Ukamfunafuna iye [Mulungu] udzampeza.” “Kuli Mulungu kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi.” “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.”—1 Mbili 28:9; Danieli 2:28; Amos 3:7.
Kodi Mayankhowo Ali Kuti?
3. Kodi tingapeze kuti chifukwa chake Mulungu akulola kuvutika?
3 Mayankho amafunso onga akuti chifukwa chake Mulungu walola kuvutika ndi zimene adzachita nawo akupezeka m’cholembedwa chimene anauzira kaamba ka phindu lathu. Cholembedwa chimenecho ndicho Mawu ake, Baibulo Lopatulika. “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pachiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
4, 5. Kodi n’chiyani chimapangitsa Baibulo kukhala buku lapadera?
4 Baibulo lilidi buku lapadera. Lili ndi cholembedwa cholondola kopambana cha mbiri ya anthu ndipo chimabwerera m’mbuyo kufikira ngakhale anthu asanalengedwe. Chilinso chamakono chifukwa chakuti maulosi ake amaphatikizapo zochitika za m’nthaŵi yathu ndiponso zamtsogolo pafupi.
5 Palibe buku lina lokhala ndi umboni wolondola wotero wa mbiri yakale. Mwachitsanzo, pali malembo apamanja oŵerengeka a olemba chabe amakedzana. Koma pali malemba apamanja okwanira 6,000 a mbali chabe kapena Malemba a Chihebri athunthu (mabuku 39 a “Chipangano Chakale”) ndi okwanira 13,000 a Malemba Achikristu Achigiriki (mabuku 27 “a Chipangano Chatsopano”).
6. Kodi tingakhale otsimikizira motani kuti Baibulo lerolino lili kwakukulukulu lofanana ndi pamene Mulungu analiuzira?
6 Mulungu wamphamvuyonse, amene anauzira Baibulo, watsimikizira kuti ubwino wake wa kalembedwe wasungidwa m’makope olembedwa pamanja amenewo. Chotero Mabaibulo athu lerolino ali kwenikweni ofanana ndi malembo ouziridwa oyambirira. Chinthu china chimene chimatithandiza kuzindikira zimenezi n’chakuti makope ena a malembo a pamanja a Malemba Achikristu Achigiriki amabwerera m’mbuyo mkati mwa zaka zana limodzi kuchokera panthaŵi yakulembedwa koyambirira. Makope a malembo a pamanja a olemba adziko amakedzana amene akalipobe mwakamodzikamodzi kuti ndi adeti la mkati mwa mazana angapo a olemba a oyambirira.
Mphatso ya Mulungu
7. Kodi kufalitsidwa kwa Baibulo nkofalikira motani?
7 Baibulo lili buku logaŵiridwa mofala koposa onse m’mbiri. Makope mabiliyoni atatu asindikizidwa. Palibe buku lina limene limafika pafupi ndi chiŵerengelo chimenecho. Ndipo Baibulo, kapena mbali yake, latembenuzidwa m’zinenero zokwanira 2,000. Chotero, kukuyerekezeredwa kuti 98 peresenti ya anthu okhala papulaneti lathuli akakhoza kukhala ndi Baibulo.
8-10. Kodi n’zifukwa zina ziti zimene zimapangitsa Baibulo kukhala loyenerera kulipenda kwathu?
8 Ndithudi buku limene limanena kuti n’lochokera kwa Mulungu ndipo lili ndi maumboni onse akunja ndi amkati akukhala kwake lodalirika n’loyenerera kulipenda kwathu.a Limalongosola chifuno cha moyo, tanthauzo la mikhalidwe ya dziko, ndi zimene zili mtsogolo. Palibe buku lina lingathe kuchita zimenezo.
9 Inde, Baibulo ndilo vumbulutso la Mulungu kubanja la anthu. Iye anatsogoza kulembedwa kwake mwamphamvu yake yogwira ntchito, kapena mzimu, anthu okwanira 40 akumalemba. Chotero Mulungu akulankhula nafe kupyolera mwa Mawu ake, Baibulo Lopatulika. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene munalandira mawu a Mulungu, munamva kwa ife, munawalandira, osati monga mawu a anthu, koma monga momwedi iwo alili, ndithu, mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.
10 Abraham Lincoln, pulezidenti wachi 16 wa United States, anatcha Baibulo “mphatso yabwino koposa imene Mulungu wapatsa kwa anthu . . . Pakuti pakanapanda ilo sitikadadziŵa chabwino ndi choipa.” Chotero, kodi mphatso yoposa zonse imeneyi ikutiuzanji za mmene kuvutika kunayambira, chifukwa chake Mulungu anakulola, ndi zimene adzachita nako?
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka chonena za kudalirika kwa Baibulo, wonani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, lofalitsidwa mu 1990 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 10]
Baibulo, n’louziridwa ndi Mulungu, ndilo njira yake yolankhulirana ndi banja la umunthu