Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo
“Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.” (Aroma 8:22) Kuvutika kwa anthu kunali kwakukulu pamene zimenezo zinalembedwa zaka zoposa 1,900 zapitazo. Ambiri anapsinjika maganizo. Chifukwa chake, Akristu anafulumizidwa kuti: “Lankhulani motonthoza kwa miyoyo yopsinjika.”—1 Atesalonika 5:14, New World Translation.
Lerolino, nsautso ya anthu iridi yokulirapo, ndipo anthu owonjezereka koposa kale ngopsinjika maganizo. Koma kodi zimenezo ziyenera kutidabwitsa? Osati kwenikweni, pakuti Baibulo limadziŵikitsa ano kukhala “masiku otsiriza” ndipo limawatcha “nthaŵi zowaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Yesu Kristu ananeneratu kuti mkati mwa masiku otsiriza, pakakhala “mitundu ya anthu, ali kuthedwa nzeru” ndipo “anthu akakomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza kudziko.”—Luka 21:7-11, 25-27; Mateyu 24:3-14.
Pamene anthu akhala ndi nkhaŵa yaikulu kwa nthaŵi yaitali, mantha, chisoni, kapena malingaliro ena otero, kaŵirikaŵiri amakhala opsinjika maganizo. Chochititsa kupsinjika maganizo kapena chisoni chachikulu chingakhale imfa ya wokondedwa, chisudzulo, kuchotsedwa ntchito, kapena nthenda yosachiritsika. Anthu amafikiranso kukhala opsinjika maganizo pamene akulitsa lingaliro lakuti ali opanda pake, pamene alingalira kuti ngolephera kuchita zinthu ndipo agwiritsa mwala aliyense. Munthu aliyense angaonongeke ndi mkhalidwe wotsendereza, koma pamene munthu akulitsa lingaliro losoŵa chiyembekezo ndipo ali wosakhoza kupeza njira yothetsera mkhalidwe woipawo, kupsinjika maganizo kwakukulu kungachitike.
Anthu m’nthaŵi zakale anakumana ndi malingaliro ofananawo. Yobu anadwala nagwiritsidwa mwala. Analingalira kuti Mulungu anali atamsiya, chotero anasonyeza kuipidwa ndi moyo. (Yobu 10:1; 29:2, 4, 5) Yakobo anapsinjika maganizo ndi imfa yachiwonekere ya mwana wake wamwamuna, akumakana kutonthozedwa ndi kukhumba kufa. (Genesis 37:33-35) Pomva kukhala waliwongo la cholakwa chachikulu, Mfumu Davide analira kuti: “Ndimayenda woliralira tsiku lonse. Ndafooka ine.”—Salmo 38:6, 8; 2 Akorinto 7:5, 6.
Lerolino, ambiri afikira kukhala opsinjika maganizo chifukwa cha kudzilemetsa, akumayesayesa kulondola njira ya tsiku ndi tsiku imene iri yosatheka kusenzedwa ndi maganizo awo, ndi malingaliro, ndi nyonga zawo zakuthupi. Mwachiwonekere chitsenderezo, limodzi ndi maganizo achabe ndi malingaliro, zingayambukire thupi ndi kuchititsa kusokonekera kwa makemikolo muubongo, motero kukumachititsa kupsinjika maganizo.—Yerekezerani ndi Miyambo 14:30.
Chithandizo Chimene Amafuna
Epafrodito, Mkristu wa m’zaka za zana loyamba wa ku Filipi, anakhala ‘wovutika mtima chifukwa [mabwenzi ake] anamva kuti anadwala.’ Epafrodito, amene anadwala atatumidwa ku Roma ndi mabwenzi ake atatenga zokapatsa mtumwi Paulo, mwinamwake analingalira kuti anali atagwiritsa mwala mabwenzi akewo ndi kuti anali atamlingalira kukhala wolephera. (Afilipi 2:25-27; 4:18) Kodi mtumwi Paulo anathandiza motani?
Iye anatumiza Epafrodito kwawo ndi kalata kwa mabwenzi a ku Filipi imene inati: “Mumlandire [Epafrodito] mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu oterewa.” (Afilipi 2:28-30) Chenicheni chakuti Paulo anamtamanda kwambiri ndi kuti Afilipiwo anamlandira mwachikondi, chiyeneradi kukhala chitatonthoza Epafrodito ndi kumthandiza kuthetsa kupsinjika maganizo kwakeko.
Mosakayikira, uphungu wa Baibulo wa ‘kulankhula motonthoza kwa miyoyo yopsinjika’ ndiwo wabwino koposa. “Mufunikira kudziŵa kuti ena amakusamalirani monga munthu,” anatero mkazi wina amene anavutika ndi kupsinjika maganizo. “Mumafuna kumva wina akunena kuti, ‘Ndikuzindikira; zidzakhala bwino.’”
Kaŵirikaŵiri munthu amene ali wopsinjika maganizo afunikira kuyambirira kufunafuna munthu womvera chisoni amene angamuululire zakukhosi. Munthu ameneyu ayenera kukhala womvetsera wabwino ndi woleza mtima. Iye ayenera kupeŵa kumangouza wopsinjika maganizoyo kapena kugamula ndi mawu akuti, ‘Simuyenera kulingalira motero,’ kapena, ‘Umenewo ndiwo mkhalidwe wolakwika.’ Mtima wa munthu wopsinjika maganizo ngwapachala, ndipo mawu osuliza oterowo adzangompangitsa kokha kudzilingalira kukhala woipa kwambiri.
Munthu amene ali wopsinjika maganizo angalingalire kukhala wopanda pake. (Yona 4:3) Komabe, munthu ayenera kukumbukira kuti chimene chiri chofunika kwenikweni ndi mmene Mulungu amawonera munthu. Anthu anawona Yesu Kristu ‘monga wosalemekezeka,’ koma zimenezi sizinasinthe kufunika kwake kwenikweni kwa Mulungu. (Yesaya 53:3) Khalani wotsimikizira kuti, monga momwedi Mulungu amakondera Mwana wake wokondedwayo, nanunso amakukondani.—Yohane 3:16.
Yesu anamvera chisoni awo amene anali m’mavuto nayesa kuwathandiza kuwona kufunika kwawo monga munthu payekha. (Mateyu 9:36; 11:28-30; 14:14) Anafotokoza kuti Mulungu amaŵerengera ngakhale mpheta zochepetsetsa, zosanunkha kanthuzo. “Palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu,” iye anatero. Iye amaŵerengera kwambiri chotani nanga anthu amene amayesayesa kuchita chifuniro chake! Ponena za amenewa Yesu anati: “Ngakhale matsitsi onse a pamutu panu aŵerengedwa.”—Luka 12:6, 7.
Zowona, kungakhale kovuta kwa munthu amene ali wopsinjika maganizo kwambiri, amene walemetsedwa ndi zofooka zake ndi zophophonya, kukhulupirira kuti Mulungu amamuŵerengera kwambiri. Iye angalingalire motsimikizirika kuti ali wosayenerera chikondi cha Mulungu ndi chisamaliro. “Mtima wathu utitsutsa,” Mawu a Mulungu amavomereza motero. Koma kodi umenewo ndiwo muyezo? Ndithudi ayi. Mulungu amazindikira kuti anthu ochimwa angalingalire mosatsimikizirika ndipo ngakhale kudziŵeruza iwo eni. Chotero Mawu ake amawatonthoza: “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.”—1 Yohane 3:19, 20.
Inde, Atate wathu wakumwamba wachikondiyo amawona zoposa machimo athu ndi zophophonya. Amadziŵa za mikhalidwe yochititsa, njira yathu yonse yamoyo, zisonkhezero zathu ndi zolinga. Amadziŵa kuti tinabadwira muuchimo, matenda, ndi imfa ndipo chotero tiri ndi zofooka zazikulu. Chenicheni chakuti timamva chisoni ndi kudzivutitsa ndicho umboni weniweni wakuti sitimafuna kuchimwa ndipo sitinankitse. Baibulo limati ‘tinagonjetsedwa ku utsiru’ mosafuna. Chotero Mulungu amamvera chisoni kuvutika kwathuku, ndipo iye mwachifundo amalingalira zofooka zathu.—Aroma 5:12; 8:20.
“Yehova ndiye wansoni zokoma ndi chisomo,” timatsimikiziridwa motero. “Monga kummwaŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:8, 12, 14) Ndithudi, Yehova ndiye “Mulungu wachitonthozo chonse, wotitonthoza ife munsautso yathu yonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
Chithandizo chimene opsinjika maganizo amafunikira koposa chimadza m’kuyandikira pafupi ndi Mulungu wawo wachifundo ndi kulandira chiitano chake cha ‘kumseza nkhaŵa zawo.’ Ndithudi iye angathe “kutsitsimutsa mtima wa osweka.” (Salmo 55:22; Yesaya 57:15) Chotero Mawu a Mulungu amalimbikitsa kupemphera akumati: ‘Ponyani nkhaŵa yanu yonse pa [Yehova], chifukwa akusamalirani.’ (1 Petro 5:7) Inde, mwanjira yapemphero ndi mapembedzero anthu angayandikire kwa Mulungu ndi kukhala ndi “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.”—Afilipi 4:6, 7; Salmo 16:8, 9.
Masinthidwe othandiza m’njira yamoyo angathenso kuthandiza munthu kugonjetsa mkhalidwe wopsinjika. Kudzilimbitsa thupi, kudya chakudya chabwino, kupuma mpweya wabwino ndi kupumula kokwanira, ndipo kupeŵa kuwonera TV kopambanitsa zonsezo nzofunika. Mkazi wina wathandiza anthu opsinjika maganizo mwakuwachititsa kuyenda kwambiri. Pamene dona wina wopsinjika maganizo anati: “Sindikufuna kumka kokayenda,” mkaziyo mofatsirira koma mwamphamvu anayankha kuti: “Inde, mukupitatu.” Mkaziyo anasimba kuti: ‘Tinayenda [makilomitala asanu ndi limodzi]. Pamene tinabwerera, anali wotopa, koma iye anapeza bwino. Simungakhulupirire mmene kudzilimbitsa thupi kwamphamvu kuliri kothandiza kufikira mutakuyesa.’
Komabe, nthaŵi zina nkosatheka kugonjetsa kotheratu kupsinjika maganizo, ngakhale pamene zonse zayesedwa, kuphatikizapo njira zochiritsira za madokotala. “Ndayesa zonse,” inatero ntchembere mbaya ina, “koma kupsinjika maganizoko kudakalipo.” Mofananamo, kaŵirikaŵiri tsopano nkosatheka kuchiritsa wakhungu, wogontha, kapena wopunduka. Komabe, anthu opsinjika maganizo angapeze chitonthozo ndi chiyembekezo mwakuŵerenga mokhazikika Mawu a Mulungu, amene amapereka chiyembekezo chotsimikizirika cha mpumulo wosatha kumavuto onse a anthu.—Aroma 12:12; 15:4.
Pamene Munthu Aliyense Sadzapsinjikanso Maganizo
Pamene Yesu anafotokoza zinthu zowopsa zakudza kudziko lapansi m’masiku otsiriza, iye anawonjezera kuti: “Koma poyamba kuchitika izi, weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.” (Luka 21:28) Yesu anali kunena za kuwomboledwa kuloŵa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu, m’mene ‘chilengedwecho chidzamasulidwanso kuukapolo wa chivundi ndi kuloŵa muufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:21.
Ndimpumulo wotani nanga mmene umenewo udzakhalira kwa mtundu wa anthu kumasulidwa kuzolemetsa zakale ndi kuuka tsiku lirilonse ndi maganizo abwino kwambiri, okonzekera kuyamba ntchito ya tsikulo! Sipadzakhalanso aliyense wovutitsidwa ndi vuto lakupsinjika maganizo. Lonjezo lotsimikizirika kwa anthu nlakuti Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kusiyapo ngati kutasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.