Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-22 tsamba 2-6
  • Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko?
  • Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mfungulo Yodziŵira Yankho la Mikhalidwe ya Dziko
  • Olamulira a Dziko Adziŵikitsidwa
  • Tsutsani Mizimu Yoipa
  • Mdani wa Moyo Wosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Pali Mizimu Yoipa?
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko?
T-22 tsamba 2-6

Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko?

Anthu ambiri akayankha funso lapamwambali ndi liwu limodzi—Mulungu. Koma kwenikweni, m’Baibulo mulibe pamene pamanena kuti Yesu Kristu kapena Atate wake ali olamulira enieni a dzikoli. Mosiyana, Yesu anati: “Mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.” Ndipo anawonjezera kuti: “Mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa ine.”—Yohane 12:31; 14:30; 16:11.

Chotero wolamulira wa dziko lino amatsutsana ndi Yesu. Kodi ameneyu angakhale yani?

Mfungulo Yodziŵira Yankho la Mikhalidwe ya Dziko

Mosasamala kanthu za zoyesayesa za anthu okhala ndi zolinga zabwino, dziko lakanthidwa ndi mavuto owopsa m’mbiri yake yonse. Zimenezi zimapangitsa anthu anzeru kudabwa, monga momwe anachitira mkonzi wina malemu David Lawrence kuti: “‘Mtendere padziko lapansi’—pafupifupi munthu aliyense amaufuna. ‘Chiyanjo kulinga kwa anthu’—pafupifupi anthu onse adzikoli amachifuna kulinga kwa wina ndi mnzake. Nangano chalakwika nchiyani? Kodi nchifukwa ninji nkhondo zikuwopseza mosasamala kanthu za chikhumbo chobadwa nacho cha anthu?”

Zikuwonekera kukhala zosatheka, kodi sichoncho? Pamene chikhumbo chobadwa nacho cha anthu chiri cha kukhala pamtendere, iwo kaŵirikaŵiri amadana ndi kuphana—ndipo amatero mwankhanza kwambiri. Talingalirani kupambanitsa m’kupha kwanjiru kokhetsa mwazi. Anthu agwiritsira ntchito utsi wakupha, misasa yachibalo, malaŵi amoto oponyedwa, mabomba amoto, ndi njira zina zankhalwe kwadzawoneni kuzunza ndi kuphana mwankhanza.

Kodi mukhulupirira kuti anthu, amene amafuna mtendere ndi chimwemwe, ali okhoza, mwa iwo okha, kuchita zoipa zazikulu kwa ena? Kodi ndimphamvu ziti zimene zimasonkhezera anthu kuchita zinthu zonyansa zotero kapena kuwasonkhezera kuloŵa mumkhalidwe umene amakhala okakamizidwa kuchita nkhanza zotero? Kodi munayamba mwadabwa kuti kaya mphamvu ina yoipa, yosawoneka ikulamulira anthu kuchita zinthu zachiwawa zotero?

Olamulira a Dziko Adziŵikitsidwa

Palibe kufunikira kwa kuyerekezera za nkhaniyo, chifukwa chakuti Baibulo limasonyeza momvekera bwino kuti munthu wina waluntha, wosawoneka wakhala akulamulira ponse paŵiri anthu ndi mitundu. Limati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Ndipo Baibulo limamdziŵikitsa, kuti: “Iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, . . . wonyenga wa dziko lonse.”—1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9.

Panthaŵi imene Yesu “anayesedwa ndi Mdyerekezi,” Yesu sanakayikire ntchito ya Satana monga wolamulira wa dzikoli. Baibulo limafotokoza zimene zinachitika: “Mdyerekezi anamuka naye ku phiri lalitali, namuwonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo; nati kwa iye, Zonse ndikupatsani inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana!”—Mateyu 4:1, 8-10.

Tangoganizirani za zimenezi. Satana anayesa Yesu mwakumpatsa “maufumu, onse adziko lapansi.” (New World Translation) Komabe, kodi kupereka kochitidwa ndi Satana kukanakhaladi chiyeso ngati Satana sanali wolamulira weniweni wa mafumu amenewa? Ayi, sikukanatero. Ndipo wonani kuti, Yesu sanakane kuti maboma onse a dzikoli anali a Satana, zimene akanachita ngati Satana sanali mwini wake. Chotero, pamenepa, Satana Mdyerekezi alidi wolamulira wosawoneka wa dzikoli! Kunena zowona, Baibulo, limamutcha kuti “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (2 Akorinto 4:4, NW) Komabe, kodi ndimotani mmene munthu woipa chotero anafikira kukhala pamalo aulamuliro amenewa?

Munthu amene anakhala Satana adali mngelo wolengedwa ndi Mulungu, koma anasirira malo a Mulungu. Iye anakayikira kuyenera kwa ulamuliro wa Mulungu. Kuti atero anagwiritsira ntchito njoka monga yomlankhulira kunyenga mkazi woyamba, Hava, ndipo chotero anali wokhoza kupatutsa mkaziyo ndi mwamuna wake, Adamu, kuchita zimene iye analamula mmalo mwa lamulo la Mulungu. (Genesis 3:1-6; 2 Akorinto 11:3) Iye ananenso kuti akatha kupatutsa mbadwa zonse za Adamu ndi Hava zimene zinali zosabadwa kuzichotsa kwa Mulungu. Chotero Mulungu analola nthaŵi yakuti Satana ayese kutsimikizira zonena zake, komatu Satana sanapambane.—Yobu 1:6-12; 2:1-10.

Kwakukulukulu, Satana sali yekha muulamuliro wake wa dzikoli. Anapeza chipambano m’kukopa angelo ena kugwirizana naye kupandukira Mulungu. Amenewa anakhala ziŵanda, atsamwali ake auzimu. Baibulo limanena za iwo pamene limafulumizitsa Akristu kuti: ‘Chirimikani pokana machenjera a Mdyerekezi. Chifukwa tikulimbana, osati ndi mwazi ndi thupi, koma . . . ndi olamulira dziko, a mdima uno, tikulimbana ndi magulu oipa ankhondo okhala m’mwamba.’—Aefeso 6:11, 12.

Tsutsani Mizimu Yoipa

Olamulira adziko, osawoneka amenewa ali otsimikizira kusocheza mtundu wonse wa anthu, kuwapatutsa pakulambira Mulungu. Njira imodzi imene mizimu yoipa imachitira zimenezi ndiyo mwa kugwiritsira ntchito lingaliro la kupulumuka kwa moyo pambuyo pa imfa, ngakhale kuli kwakuti Mawu a Mulungu amasonyeza mwachiwonekere kuti akufa sadziŵa kanthu. (Genesis 2:17; 3:19; Ezekieli 18:4; Salmo 146:3, 4; Mlaliki 9:5, 10) Motero, mzimu woipa, wotsanzira mawu a munthu amene anafa, ungalankhule ndi achibale amoyo a munthu wakufayo kapena mabwenzi, mwina kupyolera mwa wolankhula ndi mizimu kapena mwa “mawu” ochokera kumalo osawoneka. “Mawuwo” amayesezera kukhala a munthu amene anafa, komabe kwenikweni ndicho chiŵanda!

Chotero ngati mumva “mawu” aliwonse otero, musanyengedwe. Kanani ziri zonse zimene zikunenedwa, ndipo bwerezani mawu a Yesu akuti: “Choka Satana!” (Mateyu 4:10; Yakobo 4:7) Musalole chidwi chofuna kudziŵa malo amizimu kukupangitsani kukhala wophatikizidwa ndi mizimu yoipa. Kuphatikizidwa kotero kumatchedwa kulambira mizimu, ndipo Mulungu amachenjeza olambira ake kupeŵa mipangidwe yake yonse. Baibulo limatsutsa “wosamalira mitambo . . . kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.”—Deuteronomo 18:10, 12; Agalatiya 5:19-21; Chivumbulutso 21:8.

Popeza kuti kulambira mizimu kumaloŵetsa munthu m’chiyambukiro cha ziŵanda, kanizani zizoloŵezi zake zonse mosasamala kanthu za mmene zingawonekerere kukhala zoseketsa, kapena kukhala zonyanyula. Zizolowezi zimenezi zimaphatikizapo kuyang’ana mpila wa galasi, kugwiritsiridwa ntchito kwa matabwa owombezera, ESP (kudziŵa zinthu mwa kulota), kupenda mizere ya chikhatho, ndi kupenda nyenyezi. Ziŵanda zapangitsanso mapokoso ndi zochitika zina za malodza m’nyumba zimene zimapanga kukhala malo awo okhala.

Ndiponso, mizimu yoipa imagwiritsira ntchito modzipindulitsa chikhoterero cha uchimo cha anthu mwakugwiritsira ntchito mabukhu, akanema, ndi maprogramu a wailesi yakanema zimene zimasonyeza mikhalidwe yachisembwere chakugonana kosakhala kwachibadwa. Ziŵanda zimadziŵa kuti ngati malingaliro oipa sachotsedwa m’maganizo amapangitsa zikhoterero zokhomerezeka mosafafanizika ndipo zimatsogolera anthu kuchita chisembwere—mofanana ndi ziŵanda zenizenizo.—Genesis 6:1, 2; 1 Atesalonika 4:3-8; Yuda 6.

Zowona, ambiri angaseke lingaliro lakuti dzikoli likulamulidwa ndi mizimu yoipa. Komatu kusakhulupirira kwawo sikuli kwachilendo, popeza kuti Baibulo limati: “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 11:14) Chinyengo chake choposa chakhala kupangitsa ambiri kukhala a khungu ku chenicheni chakuti iye ndi ziŵanda zake alikodi. Komatu musanyengedwe! Mdyerekezi ndi ziŵanda zake ndienieni, ndipo mufunikira kuwatsutsa mosalekeza.—1 Petro 5:8, 9.

Mosangalatsa, nthaŵi tsopano yayandikira pamene Satana ndi magulu ake a nkhondo sadzakhalakonso! “Dziko lapansi [kuphatikizapo olamulira ake a ziŵanda] lipita,” Baibulo limatitsimikiziritsa kuti, “koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17) Nchitothozo chotani nanga chimene chidzakhalako kuchotseredwa chiyambukiro choipa chimenecho! Chifukwa cha chimenecho, tikhaletu pakati pa awo amene amachita chifuniro cha Mulungu ndi kusangalala nawo moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama la Mulungu.—Salmo 37:9-11, 29; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.

Kusiyapo ngati kutasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.

[Chithunzi patsamba 4]

Kodi Satana akanapatsa Yesu maboma adziko onsewa ngati iwo sanali ake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena