Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ed tsamba 19-25
  • Miyezo ya Makhalidwe Imene Iyenera Kulemekezedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Miyezo ya Makhalidwe Imene Iyenera Kulemekezedwa
  • Mboni za Yehova ndi Maphunziro
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchitira Mbendera Suluti
  • Thayo la Makolo
  • Mabanja a Zipembedzo Zosiyana
  • Ufulu wa Ana wa Kugwiritsira Ntchito Chikumbumtima
  • “Chipulumutso N’cha Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amakana Mwaulemu Kuchita Nawo Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lawo?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Kuchitira Sailuti Mbendera, Kuvota Ndiponso Kugwira Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kugonjera Kwathu Kochepa ku Maulamuliro Aakulu
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Mboni za Yehova ndi Maphunziro
ed tsamba 19-25

Miyezo ya Makhalidwe Imene Iyenera Kulemekezedwa

M’mbiri yonse, amuna ndi akazi olimba mtima atenga kaimidwe kosiyana ndi zikhulupiriro zofala m’nthaŵi yawo. Apirira nkhalwe za ndale, chipembedzo, ndi mafuko, kaŵirikaŵiri akumapereka miyoyo yawo kaamba ka chikhulupiriro chawo.

AKRISTU oyambirira anali olimba mtima kwenikweni. Pamene zizunzo zowopsa zinali kuchitika m’zaka mazana atatu oyambirira, ambiri anaphedwa ndi Aroma achikunja chifukwa cha kukana kulambira mfumu. Nthaŵi zina, guwa la nsembe linamangidwa m’bwalo la maseŵero. Kuti amasulidwe, Akristu anangofunikira kuwotcha zonunkhira pang’ono pamotowo kusonyeza kuvomereza kwawo umulungu wa mfumuyo. Komabe, ndi oŵerengeka okha amene anagonja. Ambiri anasankha kufa m’malo mwa kukana chikhulupiriro chawo.

M’nthaŵi yamakono, Mboni Zachikristu za Yehova zatenga kaimidwe kofanana ndi kameneko pankhani ya kusatenga mbali m’zandale. Mwachitsanzo, mbiri imachitira umboni za kaimidwe kawo kolimba pamene anayang’anizana ndi chitsutso cha Anazi. Isanayambe nkhondo ya dziko yachiŵiri, ndipo itayamba, pafupifupi chimodzi mwa zigawo zinayi za Mboni Zachijeremani zinataya miyoyo yawo, makamaka m’misasa yachibalo, chifukwa chakuti sizinatenge mbali m’zandale ndipo zinakana kunena kuti “Heil Hitler.” Ana aang’ono anawalanda kwa makolo awo amene anali Mboni. Ngakhale kuti anavutika, anawo analimba nakana kudetsedwa ndi ziphunzitso zosemphana ndi Malemba zimene ena anayesa kuwakakamiza kuziphunzira.

Kuchitira Mbendera Suluti

Lerolino, si kaŵirikaŵiri pamene Mboni za Yehova zimakhala chandamale cha zizunzo zankhalwe zotero. Komabe, zovuta zimabuka nthaŵi zina chifukwa chakuti potsatira chikumbumtima chawo, Mboni zachichepere zimakana kuchitako miyambo ina ya fuko, monga kuchitira mbendera suluti.

Ana a Mboni za Yehova amaphunzitsidwa kusaletsa ena kuchitira mbendera suluti; imeneyo ndi nkhani ya munthu mwini. Komabe, kaimidwe kawo ka Mboni ndi kolimba: Sizimachita suluti ku mbendera ya dziko lililonse. Pokana kuchita chimenechi, sikuti izo zilibe ulemu ayi. Zimalemekeza mbendera ya dziko lililonse limene akukhalamo, ndipo zimasonyeza ulemu umenewu mwa kumvera malamulo a dzikolo. Izo sizimaloŵa m’machitachita alionse otsutsa boma. Kwenikweni, Mboni zimakhulupirira kuti maboma aumunthu omwe alipowa ali “choikika ndi Mulungu” chimene wachilola kukhalapo. Chotero amadziŵa kuti ali pansi pa lamulo la Mulungu la kupereka misonkho ndi kulemekeza “maulamuliro aakulu” amenewo. (Aroma 13:1-7) Zimenezi zikugwirizana ndi mawu otchuka a Kristu: “Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”—Mateyu 22:21.

Ena angafunse kuti, ‘Nangano, nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizimalemekeza mbendera mwa kuichitira suluti?’ Chifukwa chakuti amaona kuchitira mbendera suluti kukhala kulambira, ndipo kulambira nkwa Mulungu; chifukwa cha chikumbumtima chawo sangalambire wina aliyense kapena chintu china koma Mulungu yekha. (Mateyu 4:10; Machitidwe 5:29) Chifukwa chake, iwo amayamikira pamene aphunzitsi alemekeza kaimidwe kolimba kameneka ndi kulola ana a Mboni kutsatira zikhulupiriro zawo.

Si zachilendo kuti Mboni za Yehova sindizo zokha zimene zimakhulupirira kuti kuchitira mbendera suluti kuli kogwirizana ndi kulambira, monga momwe ndemanga zotsatirazi zikusonyezera:

“Mbendera zoyambirira zinali zachipembedzo kwenikweni. . . . Kukuoneka kuti nthaŵi zonse chipembedzo chinapemphedwa kuthandiza kupatulikitsa mbendera za mtundu.” (Kanyenye ngwathu.)—Encyclopædia Britannica.

“Mbendera, monga mtanda, ili yopatulika. . . . Malamulo ndi malangizo onena za mkhalidwe wa munthu kulinga ku miyezo ya mtundu amagwiritsira ntchito mawu amphamvu, osabisa, onga, ‘Utumiki ku Mbendera,’ . . . ‘Ulemu ku Mbendera,’ ‘Kupembedza Mbendera.’” (Kanyenye ngwathu.)—The Encyclopedia Americana.

“Akristu anakana . . . kupereka nsembe ku fano la mfumu [ya Roma]—zimene sizili zosiyana kwenikweni lerolino ndi kukana kuchitira mbendera suluti kapena kutchula lumbiro la kukhulupirika.”—Those About to Die (1958), yolembedwa ndi Daniel P. Mannix, tsamba 135.

Kachiŵirinso, sikuti Mboni za Yehova zimafuna kukhala zopanda ulemu ku boma lililonse kapena kwa olamulira ake mwa kukana kuchitira mbendera suluti. Chifukwa chabe nchakuti, izo sizimagwadira fano loimira Boma kapena kulichitira suluti mumkhalidwe wa kulambira. Zimaona zimenezo mofanana ndi kaimidwe kamene anyamata atatu Achihebri anakatenga m’nthaŵi za Baibulo amene anakana kugwadira fano loikidwa m’chigwa cha Dura ndi Mfumu Nebukadinezara ya Babulo. (Danieli, chaputala 3) Chotero, pamene ena amachita mwambo umenewo ndi kulumbira kukhulupirika, ana a Mboni za Yehova amaphunzitsidwa kutsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo. Chifukwa chake, iwo mwakachetechete ndi mwaulemu amapeŵa kuchitako zimenezo. Pa zifukwa zimodzimodzi, ana a Mboni samaimbako pamene nyimbo ya fuko ikuimbidwa.

Ulemu, Koma Osati Kulambira

Mmaŵa wina pasukulu ina ku Canada, mtsikana wina Mboni wazaka 11 wotchedwa Terra anaona kuti mphunzitsi anatenga mwana wa sukulu wina natuluka naye kunja kwa kalasi kwa mphindi zingapo. Posapita nthaŵi, mphunzitsiyo mwakachetechete anapempha Terra kupita naye ku ofesi ya hedimasitala.

Atangoloŵa mu ofesi, Terra anaona mbendera ya Canada yoyalidwa pathebulo la hedimasitala. Ndiyeno mphunzitsiyo anauza Terra kulavulira mbenderayo. Iye anati popeza kuti Terra sanali kuimba nyimbo ya fuko kapena kuchitira mbendera suluti, panalibe chifukwa chimene akanakanira kulavulira mbenderayo atauzidwa kutero. Terra anakana, nafotokoza kuti ngakhale kuti Mboni za Yehova sizimalambira mbendera, zimailemekeza.

Atabwerera m’kalasi, mphunzitsi analengeza kuti anali atangoyesa ana a sukulu aŵiri, akumawauza kulavulira mbendera. Ngakhale kuti mwana wa sukulu woyamba anachitako miyambo ya fuko, iye analavulirabe mbendera atauzidwa kutero. Komabe, ngakhale kuti Terra sanaimbe nyimbo ya fuko kapena kuchitira mbendera suluti, iye anakana kuinyoza mwa njira imeneyo. Mphunzitsiyo anati pa aŵiriwo, Terra ndiye amene anasonyeza ulemu woyenera.

Thayo la Makolo

Lerolino, maiko ochuluka amalemekeza thayo la makolo la kuphunzitsa ana awo za chipembedzo mogwirizana ndi zikhulupiriro zawo. Zipembedzo zonse zimavomereza thayo limeneli, monga momwe limasonyezera lamulo la tchalitchi lomwe likugwirabe ntchito m’Tchalitchi cha Katolika: “Pokhala anapatsa moyo ana awo, makolo ali ndi thayo lalikulu la kuwaphunzitsa, ndipo ali ndi kuyenera kwa kutero; nchifukwa chake makolo makamaka ndiwo ayenera kuphunzitsa ana awo Zachikristu malinga ndi chiphunzitso cha Tchalitchi.”—Canon 226.

Mboni za Yehova sizimafuna zoposa pamenepo ayi. Pokhala makolo osamala, zimayesa kuphunzitsa ana awo miyezo yoona Yachikristu ndi kukulitsa mwa iwo chikondi cha mnansi ndi kuwopa zinthu za anthu ena. Zimafuna kutsatira uphungu umene mtumwi Paulo anapatsa Akristu a ku Efeso: “Makolo, musachite ndi ana anu mwa njira imene idzawakwiyitsa. M’malo mwake, alereni m’chilango ndi chilangizo Chachikristu.”—Aefeso 6:4, Today’s English Version.

Malamulo Ena a Makhalidwe Amene Mboni za Yehova Zimatsatira

Ponena za miyezo ya makhalidwe, Mboni za Yehova zimaphunzitsa ana awo kupeŵa khalidwe, machitachita, ndi mzimu zimene, ngakhale kuti zili zofala m’dziko lerolino, zingawawononge iwo ndi ena. (Yakobo 1:27) Chotero zimauza ana awo za ngozi ya anamgoneka ndi machitachita ena, onga kusuta fodya ndi kumwetsa moŵa. (Miyambo 20:1; 2 Akorinto 7:1) Zimakhulupirira kufunika kwa kuona mtima ndi khama pantchito. (Aefeso 4:28) Zimaphunzitsa ana awo kupeŵa kutukwana. (Aefeso 5:3, 4) Zimawaphunzitsanso kutsatira malamulo a Baibulo pa nkhani za kugonana ndi kulemekeza ulamuliro ndi anthu ndi zinthu za ena. (1 Akorinto 6:9, 10; Tito 3:1, 2; Ahebri 13:4) Zimakhulupirira kwambiri kuti kutsatira malamulo amenewo kumapindula ana awo.

Mabanja a Zipembedzo Zosiyana

M’mabanja ena, kholo limodzi chabe ndilo Mboni ya Yehova. Mumkhalidwe wotero, kholo limene lili Mboni liyenera kudziŵa kuti, kholo linalo limene silili Mboni lilinso ndi thayo la kuphunzitsa ana malinga ndi zikhulupiriro za chipembedzo chake. Ana amene amadziŵa zikhulupiriro zosiyana za zipembedzo amakhala ndi ziyambukiro zoipa zochepa, ngati zingakhalepo nkomwe.a Ndipotu, ana onse ayenera kusankha chipembedzo chimene adzatsatira. Ndithudi, si achichepere onse amene amasankha kutsatira zikhulupiriro za chipembedzo cha makolo awo, akhale Mboni za Yehova kapena ena.

Ufulu wa Ana wa Kugwiritsira Ntchito Chikumbumtima

Muyeneranso kudziŵa kuti Mboni za Yehova zimaona chikumbumtima cha Mkristu aliyense payekha kukhala chofunika kwambiri. (Aroma, chaputala 14) Pangano lotchedwa Convention on the Rights of the Child, limene General Assembly ya United Nations inakhazikitsa mu 1989, linazindikira kuyenera kwa mwana kukhala ndi “ufulu wa kulingalira, chikumbumtima ndi chipembedzo” ndi kuyenera kwa “kusonyeza malingaliro ake mwaufulu ndi kuti malingaliro amenewo ayenera kulingaliridwa m’nkhani iliyonse kapena chochitika chokhudza mwanayo.”

Ana aŵiri safanana. Chotero, mungayembekezeredi kusiyana kwina pa zosankha zimene Mboni zachichepere kapena ana ena a sukulu angapange ponena za zochita zina ndi ntchito za kusukulu. Tikhulupirira nanunso mudzachirikiza lamulo la ufulu wa chikumbumtima.

a Ponena za ana a m’mabanja a zipembedzo zosiyana, Steven Carr Reuben, Ph.D., m’buku lake lakuti Raising Jewish Children in a Contemporary World, akuti: “Ana amasokonezeka pamene makolo amakhala ndi moyo wobisa zimene iwo ali kwenikweni, wosokoneza, wamseri, ndi wopeŵa nkhani za chipembedzo. Pamene makolo ali omasuka, oona mtima, ofotokoza bwino zikhulupiriro zawo, miyezo, ndi za mapwando awo, ana amakula ndi chisungiko ndi odzimva kukhala ofunika mumkhalidwe wa chipembedzo umene uli wofunika kwambiri pa kukula kwa chidaliro chawo ndi chidziŵitso ponena za malo awo m’dziko.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena