Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fy mutu 5 tsamba 51-63
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
  • Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KULANDIRA LINGALIRO LA BAIBULO
  • KUKWANIRITSA ZOFUNIKA ZA MWANA WANU
  • PHUNZITSANI MWANA WANU MWACHANGU
  • CHILANGO—CHOFUNIKA CHACHIKULU
  • TETEZERANI MWANA WANU KU NGOZI
  • FUNANI CHITSOGOZO CHA MULUNGU
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Kuphunzitsa ana anu?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Zimene Mungachite Pophunzitsa Mwana Wanu
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Udindo Wanu Monga Kholo
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
fy mutu 5 tsamba 51-63

Mutu 5

Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake

1, 2. Kodi nkwayani kumene makolo ayenera kufunako chithandizo cholerera ana awo?

“ANA ndiwo cholandira cha kwa Yehova,” linatero kholo lina loyamikira pafupifupi zaka 3,000 kalelo. (Salmo 127:3) Ndithudi, chisangalalo cha kukhala kholo ndicho mphotho yochokera kwa Mulungu, imene okwatirana ochuluka ali nayo. Komabe, awo amene amakhala ndi ana posapita nthaŵi amazindikira kuti pamene ukholo umadzetsa chisangalalo, umafikanso ndi mathayo.

2 Makamaka lerolino, kulera ana ndi ntchito yaikulu kwambiri. Komabe, ambiri akuchita mwachipambano, ndipo wamasalmo wouziridwa amasonyeza njira yake mwakunena kuti: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.” (Salmo 127:1) Pamene mutsatira kwambiri malangizo a Yehova, mpamenenso mumakhala kholo labwino kwambiri. Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” (Miyambo 3:5) Kodi muli wofunitsitsa kumvetsera uphungu wa Yehova pamene mukuyamba ntchito yanu ya zaka 20 yolera mwana?

KULANDIRA LINGALIRO LA BAIBULO

3. Kodi atate ali ndi thayo lotani pa kulera ana?

3 M’nyumba zambiri kuzungulira dziko lonse, amuna amaona ntchito yophunzitsa ana kukhala ya mkazi. Nzoona kuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti ntchito yaikulu ya tate ndiyo kusamalira banja. Komabe, limanenanso kuti iye alinso ndi mathayo panyumba. Baibulo limati: “Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” (Miyambo 24:27) M’lingaliro la Mulungu, atate ndi amayi ali ogwirira ntchito pamodzi pa kuphunzitsa ana.—Miyambo 1:8, 9.

4. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuona ana aamuna kukhala ofunika kuposa aakazi?

4 Kodi mumawaona motani ana anu? Malipoti amanena kuti ku Asia “makanda achikazi kaŵirikaŵiri samalandiridwa ndi manja aŵiri [atabadwa].” Zikumveka kuti kusaŵerengera ana aakazi kudakalipo ku Latin America, ngakhale pakati pa “mabanja ophunzira bwino.” Komabe choonadi nchakuti, atsikana saali ana otsikirapo. Yakobo, tate wotchuka wa m’nthaŵi zakale, analongosola ana ake onse, kuphatikizapo ana aakazi obadwa kufikira nthaŵiyo, monga ‘ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu [ine].’ (Genesis 33:1-5; 37:35) Mofananamo, Yesu anadalitsa “tiana” (anyamata ndi atsikana) timene anthu anabweretsa kwa iye. (Mateyu 19:13-15) Tingakhale otsimikiza kuti iye anasonyeza lingaliro la Yehova.—Deuteronomo 16:14.

5. Kodi nzotani zimene okwatirana ayenera kulingalira posankha ukulu wa banja lawo?

5 Kodi kumene mumakhala anthu amayembekezera mkazi kubala ana ambiri malinga ndi mmene angakhozere? Kwenikweni, nkhani ya chiŵerengero cha ana ili chosankha cha aŵiri okwatirana. Bwanji ngati makolowo alibe njira yodyetsera ana ambiri, kuwaveka, ndi kuwapereka kusukulu? Ndithudi, okwatiranawo ayenera kulingalira zimenezi pamene akambitsirana za ukulu wa banja limene akufuna. Okwatirana ena amene amalephera kusamalira ana awo onse, amakawasungitsa kwa achibale kuti awalere. Kodi kachitidwe kameneka nkabwino? Osati kwenikweni. Ndipo sikamachotsera makolowo thayo lawo kulinga kwa ana awo. Baibulo limati: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye.” (1 Timoteo 5:8) Okwatirana anzeru amayesa kulinganiza ukulu wa “banja” lawo kotero kuti ‘adzisungire mbumba zawo.’ Kodi iwo ayenera kugwiritsira ntchito njira zoletsa kubala kuti achite zimenezo? Iyinso ndi nkhani ya chosankha chawo, ndipo ngati okwatirana asankha kuchita zimenezo, njira imene adzagwiritsira ntchito ilinso chosankha chawo. “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Komabe, njira yoletsa kubala imene imaloŵetsamo mtundu uliwonse wa kuchotsa mimba imawombana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Yehova Mulungu ali “chitsime cha moyo.” (Salmo 36:9) Motero, kuwononga moyo pambuyo pakuti wapangika kale kumasonyeza kupanda ulemu kwakukulu kulinga kwa Yehova ndipo ndi mbanda imeneyo.—Eksodo 21:22, 23; Salmo 139:16; Yeremiya 1:5.

KUKWANIRITSA ZOFUNIKA ZA MWANA WANU

6. Kodi kuphunzitsa mwana kuyenera kuyamba liti?

6 Miyambo 22:6 imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake.” Kuphunzitsa ana ndiko ntchito ina yaikulu ya makolo. Komabe, kodi kuphunzitsa kumeneko kuyenera kuyamba liti? Mwamsanga kwambiri. Mtumwi Paulo ananena kuti Timoteo anaphunzitsidwa “kuyambira ukhanda.” (2 Timoteo 3:15) Liwu lachigiriki logwiritsiridwa ntchito pano lingatanthauze khanda laling’ono kapena ngakhale mwana wosabadwa. (Luka 1:41, 44; Machitidwe 7:18-20) Chotero, Timoteo anaphunzitsidwa kuyambira pamene anali wamng’ono kwambiri—ndipo zimenezo zinali zoyenera. Ukhanda ndiyo nthaŵi yabwino yoyambirapo kuphunzitsa mwana. Ngakhale khanda laling’ono limafuna kudziŵa zinthu.

7. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa makolo onse aŵiri kukulitsa unansi wabwino ndi khanda? (b) Kodi panali unansi wotani pakati pa Yehova ndi Mwana wake wobadwa yekha?

7 “Pamene ndinaona khanda langa nthaŵi yoyamba,” akutero mayi wina, “ndinalikonda pomwepo.” Amateronso amayi ambiri. Chikondi champhamvu pakati pa mayi ndi khanda chimakula pamene akhala pamodzi pambuyo pa kubadwa. Kuyamwitsa kumawonjezeranso chikondano chawo. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:7.) Kusisita khanda kwa mayi ndi kulankhula nalo kuli kofunika kwambiri pa kukwaniritsa zofunika za khanda za maganizo. (Yerekezerani ndi Yesaya 66:12.) Koma bwanji ponena za tate? Iyenso ayenera kukhala ndi unansi waukulu ndi mwana wake watsopanoyo. Yehova mwiniyo ali chitsanzo pa zimenezi. M’buku la Miyambo, timauzidwa za unansi wa Yehova ndi Mwana wake wobadwa yekha, amene amanenedwa kukhala atanena kuti: “Mulungu anali nane poyamba njira yake, . . . ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku.” (Miyambo 8:22, 30; Yohane 1:14) Mofananamo, tate wabwino amakulitsa unansi wabwino ndi wachikondi kwa mwana wake kuyambira pachiyambi penipeni pa moyo wa mwanayo. “Sonyezani chikondi chochuluka,” linatero kholo lina. “Palibe mwana amene anafapo ndi kumkumbatira ndi kupsompsona kochuluka.”

8. Kodi ndi chisonkhezero cha maganizo chotani chimene makolo ayenera kupereka kwa makanda mwamsanga kwambiri?

8 Koma makanda amafunikira zambiri. Kungoyambira pa kubadwa, ubongo wawo umakhala wokonzekera kulandira chidziŵitso ndi kuchisunga, ndipo chachikulu chimachokera kwa makolo. Titenge chitsanzo cha chinenero. Ofufuza akunena kuti mmene mwana amaphunzirira bwino kulankhula ndi kuŵerenga “kumadalira kwambiri pa zochita zapaukhanda pakati pa mwanayo ndi makolo ake.” Lankhulani ndi mwana wanu ndi kumuŵerengera kuyambira paukhanda. Posapita nthaŵi adzafuna kukutsanzirani, ndipo mwamsanga mudzakhala mukumthandiza kuŵerenga. Mwachionekere, adzayamba kuŵerenga asanaloŵe sukulu. Zimenezo zidzakhala zothandiza kwambiri ngati mukukhala m’dziko kumene aphunzitsi ali ochepa ndi ana ali ochuluka kwambiri m’kalasi.

9. Kodi nchiyani chimene chili chonulirapo chachikulu koposa chimene makolo ayenera kukumbukira?

9 Nkhaŵa yoyambirira ya makolo achikristu iyenera kukhala kukwaniritsa zofunika zauzimu za mwana wawo. (Onani Deuteronomo 8:3.) Ndi chonulirapo chotani? Cha kuthandiza mwana wawo kukhala ndi umunthu wonga wa Kristu, ndiko kuti, kuvala “umunthu watsopano.” (Aefeso 4:24, NW) Kuti achite zimenezi ayenera kulingalira za zinthu zomangira zoyenera ndi njira zomangira zoyenera.

PHUNZITSANI MWANA WANU MWACHANGU

10. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene ana afunikira kukulitsa?

10 Kulimba kwa nyumba kumadalira kwambiri pa mtundu wa zomangira zogwiritsiridwa ntchito. Mtumwi Paulo ananena kuti zomangira zabwino kwambiri za umunthu wachikristu ndizo “golidi, siliva, miyala ya mtengo wake.” (1 Akorinto 3:10-12) Zimenezi zimaimira mikhalidwe yonga chikhulupiriro, nzeru, luntha, kukhulupirika, ulemu, ndi kuyamikira Yehova ndi malamulo ake mwachikondi. (Salmo 19:7-11; Miyambo 2:1-6; 3:13, 14) Kodi ndi motani mmene makolo angathandizire ana awo kukulitsa mikhalidwe imeneyi kuyambira paubwana weniweni? Mwa kutsatira njira imene inaperekedwa kalelo.

11. Kodi makolo achiisrayeli anathandiza motani ana awo kukulitsa umunthu waumulungu?

11 Mtundu wa Israyeli utakhala pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anauza makolo achiisrayeli kuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Inde, makolo afunikira kukhala zitsanzo, mabwenzi, olankhulana nawo, ndi aphunzitsi.

12. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti makolo akhale zitsanzo zabwino?

12 Khalani chitsanzo. Choyamba, Yehova anati: “Mawu awa . . . azikhala pamtima panu.” Ndiyeno anawonjeza kuti: “Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu.” Chotero mikhalidwe yaumulungu choyamba iyenera kukhala mumtima mwa kholo. Kholo liyenera kukonda choonadi ndi kukhala ndi moyo mogwirizana nacho. Ndiyo njira yokha imene angafikire mtima wa mwana wawo. (Miyambo 20:7) Chifukwa ninji? Chifukwa ana amasonkhezeredwa kwambiri ndi zimene amaona kuposa zimene amamva.—Luka 6:40; 1 Akorinto 11:1.

13. Posamalira ana awo, kodi ndi motani mmene makolo achikristu angatengere chitsanzo cha Yesu?

13 Khalani bwenzi. Yehova anauza makolo mu Israyeli kuti: ‘Lankhulani ndi ana anu pamene mukhala pansi m’nyumba mwanu ndi pamene mukuyenda panjira.’ Izi zimafuna kupatula nthaŵi yomakhala ndi ana mosasamala kanthu kuti makolo ali otanganitsidwa motani. Mwachionekere Yesu anaona kuti ana anafunikira nthaŵi imeneyi. Mkati mwa masiku omalizira a utumiki wake, anthu “analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti [Iye] akatikhudze.” Kodi Yesu anachitanji? “Anatiyangata, natidalitsa.” (Marko 10:13, 16) Tangolingalirani, maola omalizira a moyo wa Yesu anali kutha. Chikhalirechobe, iye anapatula nthaŵi napereka chisamaliro chake pa tiana timeneti. Phunziro labwino kwenikweni!

14. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kwa makolo kupatula nthaŵi yokhala ndi mwana wawo?

14 Khalani wolankhulana naye. Kukhala pamodzi ndi mwana wanu kudzakuthandizani kulankhulana naye. Pamene mulankhulana naye kwambiri, mpamenenso mudzazindikira bwino kakulidwe ka umunthu wake. Komabe, kumbukirani kuti kulankhulana kumaloŵetsamo zoposa kulankhula chabe. “Ndinakulitsa luso la kumvetsera,” anatero mayi wina ku Brazil, “kumvetsera ndi mtima wanga.” Kuleza mtima kwake kunabala zipatso pamene mwana wake wamwamuna anayamba kukambitsirana naye zakukhosi kwake.

15. Kodi tiyenera kukumbukiranji ponena za zosangulutsa?

15 Ana amafunikira “mphindi yakuseka . . . ndi mphindi yakuvina,” ndiyo mphindi yakusanguluka. (Mlaliki 3:1, 4; Zekariya 8:5) Kusanguluka kumakhala kopindulitsa kwambiri pamene makolo ndi ana akuchitira pamodzi. Nkomvetsa chisoni kuti m’mabanja ambiri kusanguluka kumatanthauza kupenyerera wailesi yakanema basi. Pamene maprogramu ena apawailesi yakanema angakhale okondweretsa, ambiri amawononga makhalidwe abwino, ndipo kupenyerera wailesi yakanema kumaletsa kulankhulana m’banja. Chifukwa chake, bwanji osachita kanthu kena kothandiza limodzi ndi ana anu? Imbani, chitani maseŵero, chezerani mabwenzi, kachezeni kumalo osangalatsa. Machitachita oterowo amalimbikitsa kulankhulana.

16. Kodi nchiyani chimene makolo ayenera kuphunzitsa ana awo ponena za Yehova, ndipo kodi ayenera kuchita motani zimenezo?

16 Khalani mphunzitsi. “Muziwaphunzitsa mwachangu [mawu awa] kwa ana anu,” anatero Yehova. Nkhani yake imasonyeza zimene muyenera kuphunzitsa ndi mmene muyenera kuphunzitsira. Choyamba, “muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” (Deuteronomo 6:5) Ndiyeno, ‘mawu aŵa . . . muziwaphunzitsa mwachangu.’ Perekani chilangizo chokulitsa chikondi cha mtima wonse pa Yehova ndi malamulo ake. (Yerekezerani ndi Ahebri 8:10.) Mawu akuti “phunzitsa mwachangu” amatanthauza kuphunzitsa mobwerezabwereza. Chotero Yehova kwenikweni akukuuzani kuti njira yaikulu yothandizira ana anu kukulitsa umunthu waumulungu ndiyo kulankhula za iye nthaŵi zonse. Zimenezi zimaphatikizapo kuphunzira nawo Baibulo nthaŵi zonse.

Zithunzi patsamba 57

Makolo, khalani zitsanzo, mabwenzi, olankhulana nawo, ndi aphunzitsi

17. Kodi makolo angafunikire kukulitsa chiyani mwa mwana wawo? Nchifukwa ninji?

17 Makolo ambiri amadziŵa kuti kuloŵetsa chidziŵitso mumtima wa mwana si kopepuka. Mtumwi Petro analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Monga makanda obadwa chatsopano, kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu.” (1 Petro 2:2, NW) Mawu akuti “kulitsani chilakolako” amapereka lingaliro lakuti ambiri samakhala ndi njala yachibadwa ya chakudya chauzimu. Makolo angafunikire kupeza njira zokulitsira chilakolako chimenecho mwa mwana wawo.

18. Kodi ndi njira zina zotani zophunzitsira za Yesu zimene makolo akulimbikitsidwa kutsanzira?

18 Yesu anafika anthu pamtima mwa kugwiritsira ntchito mafanizo. (Marko 13:34; Luka 10:29-37) Njira yophunzitsira imeneyi imagwira ntchito kwambiri kwa ana. Phunzitsani mapulinsipulo a Baibulo mwa nkhani zokopa ndi zokondweretsa, mwinamwake zija zopezeka mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.a Chititsani anawo kuloŵetsedwamo. Aloleni kugwiritsira ntchito luntha lawo mwa kulemba zithunzi za zinthu za m’Baibulo ndi kuchita maseŵero a zochitikazo. Yesu anagwiritsiranso ntchito mafunso. (Mateyu 17:24-27) Tsanzirani njira ya kaphunzitsidwe kake paphunziro lanu la banja. M’malo mwakungotchula lamulo la Mulungu, funsani mafunso onga akuti, Kodi nchifukwa ninji Yehova anatipatsa lamulo ili? Kodi nchiyani chimene chidzachitika ngati tilisunga? Kodi chidzachitika nchiyani ngati sitilisunga? Mafunso oterowo amathandiza mwana kulingalira ndi kuona kuti malamulo a Mulungu amathandiza ndipo ali abwino.—Deuteronomo 10:13.

19. Ngati makolo atsatira mapulinsipulo a Baibulo pochita ndi ana awo, kodi ndi mapindu aakulu otani amene anawo angapeze?

19 Mwa kukhala chitsanzo, bwenzi, wolankhulana naye, ndi mphunzitsi, mungathandize mwana wanu kuyambira m’zaka zake zaukhanda kukulitsa unansi wapafupi ndi Yehova Mulungu. Unansi umenewu udzalimbikitsa mwana wanu kukhala Mkristu wachimwemwe. Adzayesayesa kusunga chikhulupiriro chake ngakhale poyang’anizana ndi chisonkhezero cha mabwenzi ndi mayesero. Mthandizeni nthaŵi zonse kuyamikira unansi wamtengo wapatali umenewu.—Miyambo 27:11.

CHILANGO—CHOFUNIKA CHACHIKULU

20. Kodi chilango nchiyani, ndipo chiyenera kuperekedwa motani?

20 Chilango ndicho kuphunzitsa kumene kumawongolera maganizo ndi mtima. Chimafunikira kwa ana nthaŵi ndi nthaŵi. Paulo akulangiza atate ‘kupitiriza kulera [ana awo] m’chilango cha Yehova ndi kuwawongolera maganizo m’njira yake.’ (Aefeso 6:4, NW) Makolo ayenera kulanga mwa chikondi, monga momwe Yehova amachitira. (Ahebri 12:4-11) Chilango chozikidwa pa chikondi chingaperekedwe mwa kukambitsirana. Chifukwa chake, timauzidwa kuti “imvani mwambo [“chilango,” NW].” (Miyambo 8:33) Kodi chilango chiyenera kuperekedwa motani?

21. Kodi ndi mapulinsipulo ati amene makolo ayenera kukumbukira polanga ana awo?

21 Makolo ena amaganiza kuti kulanga ana awo kumangotanthauza kulankhula kwa iwo ndi mawu owopseza, kuwakalipira, kapena ngakhale kuwatukwana. Komabe, pankhani imodzimodziyo, Paulo akuchenjeza kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu.” (Aefeso 6:4) Akristu onse akulimbikitsidwa kukhala ‘odekha kwa onse . . . akumalangiza mofatsa otsutsa.’ (2 Timoteo 2:24, 25, NW) Pamene kuli kwakuti makolo achikristu amazindikira kufunika kwa kukhala okhwima, amayesa kukumbukira mawu ameneŵa polanga ana awo. Komabe, nthaŵi zina mawu okha samakhala okwanira, ndipo mtundu wina wa chilango ungakhale wofunika.—Miyambo 22:15.

22. Ngati mwana afunikira kupatsidwa chilango chamkwapulo, kodi ayenera kuthandizidwa kudziŵanji?

22 Ana osiyanasiyana amafunikira mitundu yosiyanasiyana ya chilango. Ena “sangalangizidwe ndi mawu.” Kwa iwo, chilango chamkwapulo choperekedwa panthaŵi zina chifukwa cha kusamvera kwawo chingakhale chopulumutsa moyo. (Miyambo 17:10; 23:13, 14; 29:19) Komabe, mwana ayenera kudziŵa chifukwa chake akulangidwa. “Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru.” (Miyambo 29:15; Yobu 6:24) Ndiponso, chilango chamkwapulo chiyenera kukhala ndi malire. “Ndidzakulanga pamlingo woyenera,” anatero Yehova kwa anthu ake. (Yeremiya 46:28b, NW) Baibulo silimavomereza konse kukwapula kwaukali kapena kumenya kowopsa, kumene kungachititse mwana mikwingwirima ndipo ngakhale kumvulaza.—Miyambo 16:32.

23. Kodi mwana ayenera kuzindikiranji pamene alangidwa ndi makolo ake?

23 Pamene Yehova anachenjeza anthu ake kuti adzawalanga, choyamba anati: “Usawope . . . pakuti Ine ndili ndi iwe.” (Yeremiya 46:28a) Mofananamo, chilango chaukholo choyenera chilichonse sichiyenera kuchititsa mwana kudziona kukhala wosafunika. (Akolose 3:21) M’malo mwake, mwanayo ayenera kuona kuti chilangocho chikuperekedwa chifukwa chakuti khololo lili ‘ndi iye,’ kuti lili kumbali yake.

TETEZERANI MWANA WANU KU NGOZI

24, 25. Kodi ana ayenera kutetezeredwa ku chiwopsezo chachikulu chotani chomwe chilipo masiku ano?

24 Achikulire ambiri amayang’ana kumbuyo ku ubwana wawo ndi kuona kuti inali nthaŵi yakusangalala. Amakumbukira mmene anali kumvera kukhala otetezereka ndi okondedwa ndi makolo awo, chitsimikiziro chakuti anali okonzeka kuwasamalira zivute zitani. Makolo amafuna ana awo kumva chimodzimodzi, koma m’dziko lamakono loipali, kutetezera ana nkovutirapo kuposa mmene kunalili kale.

25 Chiwopsezo chachikulu chimene chakhalapo m’zaka zaposachedwapa ndicho kugona ana. Ku Malaysia, malipoti a ana ogonedwa anawonjezereka kanayi panyengo ya zaka khumi. Ku Germany pafupifupi ana 300,000 amagonedwa chaka chilichonse, pamene m’dziko lina la ku South America, malinga ndi kufufuza kwina, chiŵerengero chowopsa cha pachaka chinafika pafupifupi 9,000,000! Mwatsoka lake, ochuluka a ana ameneŵa amagonedwa m’nyumba mwawo mwenimwenimo ndi anthu amene amadziŵa ndi kuwakhulupirira. Koma ana ayenera kupeza chitetezo chachikulu kwa makolo awo. Kodi ndi motani mmene makolo angakhalire otetezera?

26. Kodi ndi njira zina zotani zimene ana angakhalire otetezereka, ndipo ndi motani mmene chidziŵitso chingatetezerere mwana?

26 Popeza kuti zochitika zimasonyeza kuti ana amene samadziŵa zochuluka za kugonana ndiwo ali pangozi yaikulu kwa ogona ana, njira yaikulu yowatetezera nayo ndiyo kuphunzitsa mwana, ngakhale pamene adakali wamng’ono. Chidziŵitso chingamtetezere “ku njira yoipa, kwa anthu onena zokhota.” (Miyambo 2:10-12) Chidziŵitso chotani? Chidziŵitso cha mapulinsipulo a Baibulo, onena za mkhalidwe wabwino ndi woipa. Chidziŵitsonso chakuti achikulire ena amachita zinthu zoipa ndi kuti wachichepere sayenera kumvera pamene anthu amuuza kuchita zosayenera. (Yerekezerani ndi Danieli 1:4, 8; 3:16-18.) Chilangizo chimenecho chisakhale cha nthaŵi imodzi chabe. Ana ambiri amakumbukira bwino chilangizo pamene chiphunzitsidwa kwa iwo mobwerezabwereza. Pamene ana akulirapo, tate ayenera kuyamba kupatsa ulemu mwana wamkazi, mayinso mwana wake wamwamuna—mwakutero adzakulitsa lingaliro la mwana la kuzindikira chimene chili choyenera. Ndiponso, chitetezo china chabwino koposa pa nkhanza ya kugonedwa kwa ana ndicho chiyang’aniro chatcheru cha inu makolo.

FUNANI CHITSOGOZO CHA MULUNGU

27, 28. Kodi ndani amene ali Magwero aakulu koposa a chithandizo kwa makolo pamene ayang’anizana ndi vuto la kulera mwana?

27 Zoona, kuphunzitsa mwana kuyambira paukhanda wake kulidi kovuta, koma makolo okhulupirira sayenera kulimbana ndi vutolo paokha. Kale m’masiku a Oweruza, pamene mwamuna wotchedwa Manowa anadziŵa kuti adzakhala tate, anapempha chitsogozo cha Yehova pakulera mwana wake. Yehova anayankha mapemphero ake.—Oweruza 13:8, 12, 24.

28 Mwa njira imodzimodzi lerolino, pamene makolo okhulupirira alera ana awo, iwonso angalankhule kwa Yehova m’pemphero. Kukhala kholo ndi ntchito yaikulu, koma kumadzetsa mphotho zazikulu. Okwatirana achikristu ku Hawaii anati: “Muli ndi zaka 12 zakuchita ntchito yanu zisanafike zaka zovuta zaunyamata kuyambira 13 mpaka 19. Koma ngati mwalimbikira kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo, imeneyo imakhala nthaŵi yotuta chisangalalo ndi mtendere pamene iwo asankha kutumikira Yehova ndi mtima wonse.” (Miyambo 23:15, 16) Pamene mwana wanu apanga chosankha chimenecho, inunso mudzasonkhezereka kunena kuti: “Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.”

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . MAKOLO KUPHUNZITSA ANA AWO?

Khulupirirani Yehova.—Miyambo 3:5.

Samalirani thayo lanu.—1 Timoteo 5:8.

Yehova ali Atate wachikondi.—Miyambo 8:22, 30.

Makolo ali ndi thayo la kuphunzitsa ana awo.—Deuteronomo 6:6, 7.

Chilango nchofunika.—Aefeso 6:4.

CHILANGO CHOGWIRA NTCHITO

Mtundu umodzi wothandiza wa chilango ndiwo kuchititsa ana kuona kuipa kwa zotulukapo za kusamvera. (Agalatiya 6:7; yerekezerani ndi Eksodo 34:6, 7.) Ngati, mwachitsanzo, mwana wanu aipitsa malo, kumchititsa kuyeretsa iye mwini kungampatse phunziro lamphamvu. Kodi wachitira wina choipa? Kumuuza kuti apepese kungawongolere mkhalidwe wake wosayenera. Mtundu wina wa chilango ndiwo kummana mwaŵi winawake kwakanthaŵi kuti atengepo phunziro lofunika. Mwa njira imeneyi mwanayo amaphunzira nzeru ya kutsatira mapulinsipulo olungama.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena