Phunziro 9
Atumiki a Mulungu Ayenera Kukhala Oyera
Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kukhala oyera m’mbali zonse? (1)
Kodi kumatanthauzanji kukhala oyera mwauzimu? (2)
oyera m’makhalidwe? (3) oyera m’maganizo? (4) oyera kuthupi? (5)
Kodi ndi malankhulidwe odetsedwa ati amene tiyenera kupeŵa? (6)
1. Yehova Mulungu ali waukhondo ndi woyera. Amafuna olambira ake kukhala oyera—mwauzimu, m’makhalidwe, m’maganizo, ndi kuthupi. (1 Petro 1:16) Kukhala woyera pamaso pa Mulungu kumafuna kulimbikira. Tikukhala m’dziko lodetsedwa. Tilinso pankhondo ndi zikhoterero zathu za kuchita cholakwa. Koma sitiyenera kuleka.
2. Chiyero Chauzimu: Ngati tifuna kutumikira Yehova, sitingapitirize kuumirira ku ziphunzitso ndi miyambo ya chipembedzo chonyenga. Tiyenera kutuluka m’chipembedzo chonyenga ndi kusachichirikiza mwanjira iliyonse. (2 Akorinto 6:14-18; Chivumbulutso 18:4) Titaphunzira choonadi ponena za Mulungu, tiyenera kusamala kuti asatisokeretse anthu amene amaphunzitsa mabodza.—2 Yohane 10, 11.
3. Chiyero cha Makhalidwe: Yehova amafuna olambira ake kudzisunga monga Akristu oona nthaŵi zonse. (1 Petro 2:12) Amaona zonse zomwe timachita, ndi zamseri zomwe. (Ahebri 4:13) Tiyenera kupeŵa chisembwere ndi machitachita ena onyansa a dzikoli.—1 Akorinto 6:9-11.
4. Chiyero cha Maganizo: Ngati tidzaza maganizo athu ndi malingaliro oyera ndi abwino, khalidwe lathu lidzakhalanso loyera. (Afilipi 4:8) Koma ngati tisinkhasinkha zinthu zodetsedwa, zimene zidzatulukapo ndi ntchito zoipa. (Mateyu 15:18-20) Tiyenera kupeŵa mitundu ya zosangulutsa zimene zingadetse maganizo athu. Tingadzaze malingaliro oyera m’maganizo athu mwa kuphunzira Mawu a Mulungu.
5. Chiyero cha Kuthupi: Chifukwa chakuti Akristu amaimira Mulungu, iwo ayenera kusunga matupi awo ali oyera limodzi ndi zovala zawo. Tiyenera kusamba kumanja titachoka kuchimbudzi, ndipo tiyenera kusambanso kumanja tisanadye chakudya kapena kugwira chakudya. Ngati mulibe zimbudzi, muyenera kufotsera zonyansazo. (Deuteronomo 23:12, 13) Kukhala woyera kuthupi kumapatsa thanzi labwino. Nyumba ya Mkristu iyenera kukhala yaukhondo ndi yoyera mkati ndi kunja komwe. Iyenera kuonekera kumaloko monga chitsanzo chabwino.
6. Malankhulidwe Oyera: Atumiki a Mulungu nthaŵi zonse ayenera kulankhula choonadi. Abodza sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. (Aefeso 4:25; Chivumbulutso 21:8) Akristu samalankhula mawu onyoza. Samamvetsera njerengo zotukwana kapena nkhani zonyansa kapena kuzilankhula. Chifukwa cha malankhulidwe awo oyera, amakhala osiyana ndi ena kuntchito kapena kusukulu ndi kumene akhala.—Aefeso 4:29, 31; 5:3.
[Zithunzi pamasamba 18, 19]
Atumiki a Mulungu ayenera kukhala oyera m’mbali zonse