Phunziro 13
Kodi Mungachipeze Motani Chipembedzo Choona?
Kodi zipembedzo zonse zimamkondweretsa Mulungu, kapena ndi chimodzi chokha? (1)
Kodi n’chifukwa ninji pali zipembedzo zambiri zimene zimati n’zachikristu? (2)
Kodi mungawadziŵe motani Akristu oona? (3-7)
1. Yesu anayambitsa chipembedzo choona chimodzi chachikristu. Chotero lerolino payenera kukhala bungwe kapena gulu limodzi lokha la olambira oona a Yehova Mulungu. (Yohane 4:23, 24; Aefeso 4:4, 5) Baibulo limaphunzitsa kuti ndi anthu oŵerengeka chabe amene ali panjira yopapatiza yakumuka nayo ku moyo.—Mateyu 7:13, 14.
2. Baibulo linaneneratu kuti atumwi atatha kufa, ziphunzitso ndi machitachita achikunja zidzayamba kuloŵa mumpingo wachikristu pang’onopang’ono. Anthu adzakopa okhulupirira kuti atsatire iwo m’malo mwa Kristu. (Mateyu 7:15, 21-23; Machitidwe 20:29, 30) N’chifukwa chake tikuona zipembedzo zambiri zosiyanasiyana zimene zimati n’zachikristu. Kodi tingawadziŵe motani Akristu oona?
3. Chizindikiro chachikulu koposa cha Akristu oona n’chakuti iwo ali ndi chikondi chenicheni pakati pawo. (Yohane 13:34, 35) Iwo samaphunzitsidwa kuganiza kuti ali abwino kuposa anthu amafuko ena kapena akhungu losiyana. Samaphunzitsidwanso kuda anthu akumaiko ena. (Machitidwe 10:34, 35) Chotero samatengamo mbali m’nkhondo. Akristu oona amakhala ngati abale ndi alongo.—1 Yohane 4:20, 21.
4. Chizindikiro china cha chipembedzo choona n’chakuti anthu ake amalemekeza Baibulo kwambiri. Amalilandira monga Mawu a Mulungu ndipo amakhulupirira zimene limanena. (Yohane 17:17; 2 Timoteo 3:16, 17) Amaona Mawu a Mulungu kukhala ofunika kwambiri kuposa malingaliro a anthu kapena miyambo yawo. (Mateyu 15:1-3, 7-9) Amayesa kutsatira Baibulo m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Chotero samalalikira zosiyana ndi zimene amachita.—Tito 1:15, 16.
5. Chipembedzo choona chiyeneranso kulemekeza dzina la Mulungu. (Mateyu 6:9) Yesu anadziŵikitsa kwa ena dzina la Mulungu, Yehova. Akristu oona ayenera kuchita chimodzimodzi. (Yohane 17:6, 26; Aroma 10:13, 14) Kodi ndi anthu ati kwanuko amene amauza ena za dzina la Mulungu?
6. Akristu oona ayenera kulalikira za Ufumu wa Mulungu. Yesu anatero. Iye nthaŵi zonse analankhula za Ufumu. (Luka 8:1) Analamula ophunzira ake kulalikira uthenga umodzimodziwu padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Akristu oona amakhulupirira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzadzetsa mtendere ndi chisungiko padziko lino lapansi.—Salmo 146:3-5.
7. Ophunzira a Yesu sayenera kukhala mbali ya dziko loipali. (Yohane 17:16) Samaloŵa m’nkhani zandale ndi m’mikangano ya anthu. Amapeŵa khalidwe loipa, machitachita, ndi mzimu wovulaza, zimene zafala m’dziko. (Yakobo 1:27; 4:4) Kodi mungatchule kagulu kachipembedzo kwanuko kamene kali ndi zizindikiro zimenezi za Chikristu choona?
[Zithunzi pamasamba 26, 27]
Akristu oona amakondana, amalemekeza Baibulo, ndipo amalalikira za Ufumu wa Mulungu