Kodi Buku Limeneli Limagwirizana ndi Sayansi?
Si nthaŵi zonse pamene chipembedzo chaona sayansi ngati bwenzi lake. Pazaka mazana zapitazo, akatswiri ena a zaumulungu anatsutsa zomwe asayansi anapeza pamene iwo anaona monga ngati zimenezo zidzasokoneza kumasulira kwawo Baibulo. Koma kodi sayansi ilidi mdani wa Baibulo?
NGATI olemba Baibulo akanavomereza zikhulupiriro za sayansi zomwe ambiri anali nazo masiku awo, ilo likanakhala buku lodzala zolakwa za sayansi zokhazokha. Komabe, olembawo sanachirikize zikhulupiriro zolakwika zimenezo za sayansi. M’malo mwake, analemba mawu angapo amene sali chabe oona malinga ndi sayansi komanso amene anatsutsa mwachindunji zikhulupiriro zimene anali kuvomereza masikuwo.
Kodi Mpangidwe wa Dziko Lapansi Ngwotani?
Funso limenelo lachititsa chidwi anthu kwa zaka zikwi zambiri. Kale ambiri amakhulupirira kuti dziko lapansi linali lophwatalala. Mwachitsanzo, Ababulo anali kukhulupirira kuti chilengedwe chonse chinali ngati bokosi kapena chipinda ndipo dziko lapansi linali pansi pake. Ansembe achiveda ku India anali kuganiza kuti dziko lapansi linali lophwatalala ndi kuti mbali imodzi yokha nkumene kumakhala anthu. Mtundu wina ku Asia unali kuganiza kuti dziko lapansi lili ngati mbale yaikulu yoperekera tiyi.
Kalelo m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., Mgiriki wafilosofi Pythagoras ananena kuti popeza kuti mwezi ndi dzuŵa nzampangidwe wobulungika, nalonso dziko lapansi liyenera kukhala lobulungika. Pambuyo pake Aristotle (m’zaka za zana lachinayi B.C.E.) anavomereza, akumafotokoza kuti mpangidwe wobulungika wa dziko lapansi umasonyezedwa pamene dziko lapansi lichinga mwezi. Chithunzithunzi cha dziko lapansi chimakhala chopindika pamwezi.
Komabe, chikhulupiriro chakuti dziko lapansi nlophwatalala (ndi kuti anthu amangokhala pamwamba pake pokha) sichinatheretu. Ena sanavomereze mafotokozedwe omveka akuti dziko lapansi nlozungulira—lingaliro lotchedwa antipodes.a Lactantius, wochirikiza Chikristu wa m’zaka za zana lachinayi C.E., anaseka lingaliro limeneli. Kuganiza kwake kunali kotere: “Kodi alipo munthu wopusa chotero amene angakhulupirire kuti kuli anthu amene mapazi awo ali m’mwamba ndipo mitu yawo ili pansi? . . . kuti mbewu ndi mitengo zimakula kupita pansi? kuti mvula, ndi chipale chofeŵa, ndi matalala zimagwa kupita m’mwamba?”2
Lingaliro la antipodes linapereka vuto kwa akatswiri angapo a zaumulungu. Ena anaphunzitsa kuti ngati kunali anthu okhala kumbali ina ya dziko lapansi, ndiye kuti sizingatheke kuti amvane ndi anthu odziŵika mwina chifukwa choti nyanja inali yotakata kwambiri yosatheka kuwoloka kapena chifukwa chakuti chigawo chotentha chinazungulira equator. Choncho kodi anthu okhala kumbali ina ya dziko lapansi angakhale atachokera kuti? Pozizwa, akatswiri ena a zaumulungu anangoti ndi bwino kukhulupirira kuti kunalibe anthu okhala kumbali ina ya dziko lapansi, kapena, malinga ndi kulingalira kwa Lactantius, kuti sizitheka kuti dziko lapansi nkukhala lobulungika nkomwe!
Ngakhale ndi choncho, lingaliro lakuti mpangidwe wa dziko lapansi ngwobulungika linafalikira, ndipo m’kupita kwa nthaŵi ambiri analivomereza. Komabe, ndi kuyambika kwa nyengo yopita m’mlengalenga m’zaka za zana la 20, zatheka kwa anthu kupita kutali m’mlengalenga ndi kutsimikiza kuti dziko lapansi ndi mbulunga mwa kudzipenyera okha.b
Nanga kodi Baibulo linatani pankhani imeneyi? M’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., pamene ambiri ankakhulupirira kuti dziko lapansi linali lophwatalala, zaka mazana ambiri afilosofi achigiriki asananene kuti dziko lapansi liyenera kukhala lozungulira, ndiponso zaka zikwi zambiri anthu asanaone ali m’mlengalenga kuti dziko lapansi ndi mbulunga, mneneri wachihebri Yesaya ananena mosavuta konse komanso modabwitsa kuti: “Alipo Wina amene akukhala pamwamba pa mbulunga ya dziko lapansi.” (Yesaya 40:22, NW) Liwu lachihebri lakuti chugh, lotembenuzidwa panopa kuti “mbulunga,” lingatembenuzidwenso kuti “chobulungika.”3 Mabaibulo ena amati, “mbulunga ya dziko lapansi” (Douay Version) ndi “dziko lapansi lozungulira.”—Moffatt.c
Wolemba Baibulo Yesaya anapeŵa nthanthi zofala zonena za dziko lapansi. M’malo mwake, analemba mawu amene kupita patsogolo kwa sayansi sikunapereke chiopsezo pa iwo.
Kodi Nchiyani Chimagwira Dziko Lapansi?
Kale, anthu anali kuvutika ndi mafunso ena okhudza chilengedwe: Kodi dziko lapansi lakhala pa chiyani? Kodi nchiyani chimagwira dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi? Iwo sanalidziŵe lamulo lachilengedwe la mphamvu yokoka, limene Isaac Newton analifotokoza ndi kulifalitsa m’chaka cha 1687. Lingaliro lakuti zinthu zakumwamba kwenikweni nzolenjekeka pachabe m’mlengalenga sanali kulidziŵa. Chifukwa cha zimenezo, mafotokozedwe awo amanena kuti zinthu zina zake zooneka zinagwira dziko lapansi ndi zinthu zina za kumwamba.
Mwachitsanzo, chiphunzitso china chakale, mwina choyambidwa ndi anthu omwe ankakhala pachisumbu, chinali chakuti madzi anazungulira dziko lapansi ndi kuti linali kuyandama pamadziwo. Ahindu anali kukhulupirira kuti dziko lapansi nlokhazikika pa maziko ambiri, osanjikizana. Linakhala panjovu zinayi, njovuzo zinaimirira pakamba wamkulu, kambanso anaimirira pachinjoka chachikulu, ndipo chinjoka choyanga nkhatacho chinali kuyandama pamadzi a chilengedwe. Empedocles, Mgiriki wafilosofi wa m’zaka za zana lachisanu B.C.E., anakhulupirira kuti dziko lapansi linali pa kavulumvulu ndi kuti kavulumvulu ameneyo ndiye amayendetsa zinthu zakumwamba.
Pamalingaliro omwe anali amphamvu kwambiri panali aja a Aristotle. Ngakhale kuti ananena kuti dziko lapansi nlozungulira, iye anakana kuti silingalenjekeke m’mlengalenga popanda kanthu. M’buku lake lakuti On the Heavens, potsutsa kuti dziko lapansi lili pamadzi, anati: “Si kwachibadwa kwa madzi, ngakhalenso dziko lapansi, kukhala m’mlengalenga: liyenera kuyedzamira china chake.”4 Chotero kodi dziko lapansi ‘limayedzamira’ chiyani? Aristotle anaphunzitsa kuti dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi zinali zomatirira pamwamba pa mbulunga zolimba zopenyekera. Mbulunga iliyonse inali mkati mwa mbulunga inzake, ndipo dziko lapansi—losayendalo—linali pakati. Pamene mbulungazo zinazungulira iliyonse mkati mwa inzake, zinthu zokhala pa izo—dzuŵa, mwezi, ndi mapulaneti—zinayenda modutsa thambo.
Kufotokoza kwa Aristotle kunamveka kwanzeru. Ngati zinthu zakumwamba sizinali zomatirira ku chinthu china chake, zikanakhala bwanji m’mlengalenga? Anthu kwa zaka ngati 2,000 anakhulupirira kuti malingaliro a Aristotle wolemekezekayo ali oona. Malinga ndi The New Encyclopædia Britannica, m’zaka za zana la 16 ndi la 17 ziphunzitso zake “zinafikira pakuonedwa monga chiphunzitso chosasinthika cha chipembedzo” m’maso mwa a tchalitchi.5
Telesikopo itapangidwa, openda zakuthambo anayamba kukayikira chiphunzitso cha Aristotle. Ngakhale ndi tero, sanalipeze yankho lake kufikira Bwana Isaac Newton atafotokoza kuti mapulaneti ali olenjekeka m’mlengalenga, ndi kuti amakhalabe m’mipita mwawo chifukwa cha mphamvu yosaoneka—mphamvu yokoka. Zimenezo sanathe kuzikhulupirira, ndipo anzake ena a Newton zinawavuta kukhulupirira kuti mlengalenga ungakhale wopanda kanthu.d6
Kodi Baibulo limati chiyani pankhaniyi? Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Baibulo linanena zomveka kwambiri kuti dziko lapansi nlolenjeka “pachabe.” (Yobu 26:7) M’Chihebri choyambirira, liwu la “pachabe” (beli-mahʹ) logwiritsiridwa ntchito panopa m’lingaliro lenileni limatanthauza “popanda kanthu.”7 Baibulo la Contemporary English Version limagwiritsira ntchito mawu akuti, “m’mlengalenga.”
Anthu ochuluka masikuwo sanayese konse kuti dziko lapansi lili pulaneti lolenjekeka “m’mlengalenga.” Komabe, akumatchula chidziŵitso chapatsogolo chosadziŵika panthaŵi yake, wolemba Baibulo analemba mawu oona malinga ndi sayansi.
Baibulo ndi Sayansi ya Zamankhwala —Kodi Zimagwirizana?
Sayansi yamakono ya zamankhwala yatiphunzitsa zambiri ponena za kufalikira kwa matenda ndi mowapewera. Kupita patsogolo pazamankhwala m’zaka za zana la 19 kunayambitsa mchitidwe wa zamankhwala woletsa kufalikira kwa tizilombo—ukhondo wochepetsa matenda. Zotsatira zake zinali zosangalatsa. Matenda ndi imfa zamwamsanga zinachepa kwambiri.
Komabe, asing’anga akale sanali kumvetsetsa mmene matenda amafalikira, ndipo sanali kuzindikira kuti ukhondo ngwofunika kwambiri kuti munthu apewe matenda. Ndiye chifukwa chake kuchiritsa kwawo kungaoneke kwaumbuli ndi konyansa poyerekeza ndi kuchiritsa kwamakono.
Limodzi la mabuku akale kwambiri a zamankhwala lomwe lilipo ndilo Ebers Papyrus la ku ma 1550 B.C.E., limene lili ndi chidziŵitso cha zamankhwala cha Aaigupto. Mpukutu umenewu umatchula mankhwala ngati 700 a matenda osiyanasiyana “kuyambira a chilonda cholumidwa ndi ng’ona mpaka a kupweteka kwa zikhadabo za zala zakumapazi.”8 The International Standard Bible Encyclopaedia ikunena kuti: “Chidziŵitso cha zamankhwala cha asing’anga amenewa chinkadalira ndi zimene iwo anaonapo, kwenikweni chinali chamatsenga ndiponso chosakhala cha sayansi ayi.”9 Mankhwala ochuluka anali osagwira ntchito konse, koma ena anali angozi kwambiri. Pofuna kuchiritsa chilonda, malangizo ena analimbikitsa kuti azigwiritsira ntchito msanganizo wa tudzi ta munthu ndi zinthu zina.10
Buku limeneli la mankhwala la Aaigupto linalembedwa pafupifupi nthaŵi imodzimodzi imene mabuku a Baibulo oyambirira analembedwa, amene anaphatikizapo Chilamulo cha Mose. Mose, amene anabadwa m’chaka cha 1593 B.C.E., anakulira ku Igupto. (Eksodo 2:1-10) Pokhala wa m’banja la Farao, “anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto.” (Machitidwe 7:22) Iye anali kuwadziŵa “asing’anga” a ku Igupto. (Genesis 50:1-3) Kodi machiritsidwe awo osathandiza kapena angoziwo anaonekera m’zolemba zake?
Ayi. M’malo mwake, Chilamulo cha Mose chinaphatikizapo malamulo aukhondo omwe anali otukuka kwambiri kusiyana ndi nthaŵiyo. Mwachitsanzo, lamulo lokhudzana ndi misasa ya asilikali linafuna kuti azifotsera tudzi kutali ndi msasa. (Deuteronomo 23:13) Njira yopewera matenda imeneyi inali yapatsogolo kwambiri. Inathandiza kukhala ndi madzi osadetsedwa ndipo inawateteza ku matenda a kamwazi ofalitsidwa ndi ntchentche ndi enanso a kutseguka m’mimba amene amaphabe anthu mamiliyoni ambiri chaka chilichonse m’maiko opanda zimbudzi zabwino.
Chilamulo cha Mose chinalinso ndi malamulo ena aukhondo amene analetsa Aisrayeli kufalitsa matenda oyambukira. Munthu amene anali ndi nthenda yoyambukira kapena amene anaganizidwa kuti ali nayo anali kumbindikiritsa. (Levitiko 13:1-5) Zovala kapena ziŵiya zomwe zinakhudza nyama yodzifera yokha (kapena ndi matenda) anayenera kuzichapa kapena kuzitsuka asanazigwiritsire ntchito kapena anayenera kuziwononga. (Levitiko 11:27, 28, 32, 33) Munthu aliyense amene anakhudza mtembo anamyesa wodetsedwa ndipo anafunikira kuyeretsedwa, kumene kunaphatikizapo kuchapa zovala zake ndi kusamba. Pamasiku asanu ndi aŵiri a kudetsedwa kwake, sanayenera kukhudzana ndi anthu ena.—Numeri 19:1-13.
Lamulo limeneli laukhondo limasonyeza nzeru imene asing’anga a mitundu yozungulira analibe panthaŵiyo. Zaka zikwi zambiri sayansi ya zamankhwala isanadziŵe za njira imene matenda amafalikirira, Baibulo linafotokoza njira zabwino zoteteza pakupeŵa matenda. Nchifukwa chake Mose mwachisawawa analankhula za Aisrayeli m’tsiku lake kuti anali kukhala ndi moyo zaka 70 kapena 80.e—Salmo 90:10.
Mwina mukuvomereza kuti mawu a m’Baibulowo ngolondola malinga ndi sayansi. Koma alimo mawu ena m’Baibulo amene sayansi singawatsimikize. Kodi ndiye kuti zimenezo zikutanthauza kuti Baibulo limatsutsa sayansi?
Kuvomereza Zosatheka Kutsimikizidwa
Sikuti ngati mawu ali osatheka kuwatsimikiza ndiye kuti ali onama ayi. Kulephera kwa munthu kupeza maumboni okwanira ndi kumasulira chidziŵitso molondola kumachititsa kuti pakhale umboni wochepa wa sayansi. Koma zinthu zina zoona nzosatheka kutsimikiza chifukwa umboni wake wonse sunasungike, umboni wake ngwosadziŵika bwino kapena sunapezekebe, kapena kuti maluso ndi ukatswiri wa asayansi zaperewera kuti iwo afike pogamula zinthuzo motsimikiza. Kodi mwina zili choncho ndi mawu ena a m’Baibulo amene alibe umboni wooneka wopezeka kwina kwake?
Mwachitsanzo, mawu a m’Baibulo onena za malo osaoneka amene kumakhala mizimu sangatsimikizidwe—kapenanso kutsutsidwa—ndi sayansi. Chimodzimodzinso ndi zozizwitsa zimene Baibulo limanena. Palibe umboni wokwana ndi womveka, wopezeka m’miyala, umene ungakhutiritse anthu ena kuti Chigumula cha dziko lonse chinalikodi m’tsiku la Nowa. (Genesis, chaputala 7) Kodi tiyenera kuganiza kuti sichinachitike? Umboni wa mbiri yakale umawonongeka chifukwa cha nthaŵi yopitapo ndi kusintha kwa zinthu. Chotero kodi sizotheka kuti kusintha kwa dziko lapansi ndi miyala yake pazaka zikwi zambiri kwawononga umboni wochuluka wa Chigumula?
Zoona, Baibulo limanena zinthu zimene sizingatsimikizidwe kapenanso kutsutsidwa ndi umboni wooneka womwe ulipo. Koma kodi zimenezo ziyenera kutidabwitsa? Baibulo si buku la sayansi ayi. Komabe, lili buku la choonadi. Tapenda kale umboni wamphamvu wakuti olemba ake anali amuna okhulupirika ndi oona mtima. Ndipo pamene atchula zinthu zokhudza sayansi, zonena zawo zimakhala zolondola ndipo zosatsata konse ziphunzitso “za sayansi” zimene pambuyo pake zinapezeka kukhala nthanthi wamba. Chotero sayansi siili mdani wa Baibulo. Pali chifukwa chabwino chopendera mwaufulu zimene Baibulo limanena.
[Mawu a M’munsi]
a “Antipodes . . . ndi malo aŵiri pambulunga amene akuyang’anana. Mzera wolunjika pakati pawo ungapyole pakati pa dziko lapansi. Liwu lakuti antipodes m’Chigiriki limatanthauza mapazi oyang’anana. Anthu aŵiri oimirira pamalo otchedwa antipodes amayandikana kwambiri kumapazi kwawo.”1—The World Book Encyclopedia.
b Kwenikweni, dziko lapansi si mbulunga yozungulira moti ndee bwinobwino; nlopamanthika pang’ono kunsonga zake.
c Ndiponso, chinthu cha mpangidwe wobulungika ndicho chokha chimaoneka ngati chozungulira kulikonse kumene mwachipenyera. Nthaŵi zambiri chinthu chophwatalala chimaoneka ngati dzira, osati chozungulira.
d M’tsiku la Newton chikhulupiriro chofala chinali chakuti miyamba inali yodzala madzi—“supu” wachilengedwe—ndi kuti mapote m’madziwo anazunguza mapulanetiwo.
e M’chaka cha 1900, zaka zomwe munthu anayembekezeredwa kukhala ndi moyo m’maiko ambiri a ku Ulaya ndi ku United States zinali zosakwana 50. Chiyambire nthaŵiyo, zawonjezeka kwambiri osati chabe chifukwa chakuti zamankhwala zapita patsogolo poletsa matenda komanso chifukwa cha ukhondo wabwino ndi kakhalidwe kabwino.
[Mawu Otsindika patsamba 21]
Sikuti ngati mawu ali osatheka kuwatsimikiza ndiye kuti ali onama ayi
[Chithunzi patsamba 18]
Zaka zikwi zambiri anthu asanaone kuti dziko lapansi ndi mbulunga poliyang’ana kuchokera m’mlengalenga, Baibulo linanena za “mbulunga ya dziko lapansi”
[Zithunzi patsamba 20]
Bwana Isaac Newton anafotokoza kuti mapulaneti amakhalabe m’mipita mwawo chifukwa cha mphamvu yokoka