Kodi ndi Buku la Inunso?
“Saleka kulemba mabuku ambiri,” anatero Solomo zaka ngati 3,000 zapitazo. (Mlaliki 12:12) Mawu amenewo alinso oona lero mofanana ndi kale lonse. Kuwonjezera pa mabuku achikhalire a akatswiri, mabuku atsopano zikwizikwi amasindikizidwa chaka chilichonse. Popeza pali mabuku ambiri amene mungasankhepo, nchifukwa ninji muyenera kuŵerenga Baibulo?
ANTHU ambiri amaŵerenga mabuku kungofuna kusangalala ndi nkhani zake kapena kuti aphunziremo kanthu kena, kapenanso pazifukwa zonse ziŵiri. Kuŵerenga Baibulo kungakhalenso chimodzimodzi. Kuliŵerenga kungakhale kolimbikitsa, ngakhale kosangalatsa. Koma Baibulo limaposa pamenepo. Ilo ndilo magwero apadera a chidziŵitso.—Mlaliki 12:9, 10.
Baibulo limayankha mafunso omwe anthu akhala akuwasinkhasikha pazaka zambirimbiri—mafunso onena za m’nthaŵi yakumbuyoku, zalero, ndi za mtsogolo. Ambiri amafunsa kuti: Kodi tinachokera kuti? Kodi chifuno cha moyo nchiyani? Kodi tingachipeze motani chimwemwe m’moyo? Kodi moyo udzakhalapo nthaŵi zonse padziko lapansi? Kodi kutsogoloku kuli zotani?
Mphamvu yonse ya umboni woperekedwa munomo ikutsimikiza bwino lomwe kuti Baibulo nlolondola ndi loona. Tapenda kale mmene uphungu wake wothandiza ungatithandizire kukhala ndi moyo watanthauzo ndi wachimwemwe lero. Popeza mayankho ake okhudza moyo uno ngokhutiritsa, ndithudi mayankho okhudza nthaŵi yapita ndi maulosi ake a mtsogolo ayeneradi kuwapenda bwinobwino.
Mmene Mungapindulire Kwambiri
Anthu ambiri ayamba kuŵerenga Baibulo koma asiya pamene apeza zigawo zake zovuta kumva. Ngati zimenezo zakuchitikirani, pali zinthu zina zomwe zingakuthandizeni.
Sankhani Baibulo lodalirika la chinenero chamakono, monga la New World Translation of the Holy Scriptures.a Anthu ena amayamba mwa kuŵerenga Mauthenga Abwino a moyo wa Yesu, amene ziphunzitso zake zanzeru, zonga zija zopezeka mu Ulaliki wa pa Phiri, zimasonyeza kuti anachimvetsa kwambiri chibadwa cha munthu ndipo zimasonyeza mmene tingawongolere moyo wathu kukhala wabwino.—Onani Mateyu, machaputala 5 mpaka 7.
Kuwonjezera pa kuŵerenga Baibulo lonse lathunthu, njira ina yothandiza kwambiri ndiyo kuliphunzira malinga ndi nkhani zake. Zimenezi zikuphatikizapo kupenda zimene Baibulo limanena pankhani ina yake. Mungadabwe kuphunzira zimene Baibulo limanenadi pankhani zonga sou, kumwamba, dziko lapansi, moyo, ndi imfa, limodzinso ndi Ufumu wa Mulungu—zimene uli ndi zimene udzachita.b Mboni za Yehova zili ndi programu yaulere yophunzira Baibulo malinga ndi nkhani zake. Mungafunse za zimenezo mwa kulembera ofalitsa kabuku kano, kugwiritsira ntchito keyala yoyenera imene ili patsamba 2.
Atapenda umboni wonse, anthu ambiri afika ponena kuti Baibulo linachokera kwa Mulungu, amene Malemba amamutcha “Yehova.” (Salmo 83:18) Mwina simungakhutire kuti Baibulo linachokera kwa Mulungu. Nanga bwanji osalipenda inu nokha? Tikhulupirira kuti mutaliphunzira, kuganizaganiza, ndipo mwinamwake kuona inu eni phindu la nzeru yake yosasinthayo, mudzazindikira kuti Baibulo lilidi buku la anthu onse, ndiponso—buku la inunso.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Buku limene lathandiza ambiri pophunzira Baibulo malinga ndi nkhani zake ndilo Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.