Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jt tsamba 3-5
  • Kodi Iwo Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Iwo Ndani?
  • Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • DZINA LAWO
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Dzina la Mulungu ndi “Chipangano Chatsopano”
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani?
    Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani?
Onani Zambiri
Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
jt tsamba 3-5

Kodi Iwo Ndani?

A MBONI za Yehova amafuna kuti inu muwadziŵe bwino lomwe. Mwina mwakumanapo nawo pokhala nawo pafupi kwanuko ndi pogwira nawo ntchito kapenanso m’zochitika zina za moyo wa tsiku ndi tsiku. Mwina mwakhala mukuwaona mumsewu, pamene akugaŵira magazini awo kwa anthu odutsa. Kapenanso munalankhulapo nawo kwa nthaŵi yochepa pakhomo panu.

Ndithudi, a Mboni za Yehova amasamala za inu ndi moyo wanu. Amafuna kukhala mabwenzi anu ndi kuti akuuzeni zochuluka ponena za iwo, zimene amakhulupirira, gulu lawo, ndi mmene amaonera anthu komanso dzikoli limene tonse tikukhalamo. Pofuna kuchita zimenezo, iwo akulemberani kabuku kano.

M’njira zambiri a Mboni za Yehova amafanana ndi munthu wina aliyense. Nawonso amakumana ndi mavuto—a zachuma, a m’thupi, ndi a m’maganizo. Iwonso amalakwa chifukwa sali angwiro, sali ouziridwa ndi Mulungu, kapenanso osachimwa. Komabe amayesetsa kuphunzira mwa zolakwa zawo ndi kuphunzira Baibulo mwakhama kotero kuti awongolere mofunikiramo. Iwo anadzipatulira kwa Mulungu kuti achite chifuniro chake, ndipo amadzipereka kuti akwaniritse kudzipatulira kwawoko. M’zochita zawo zonse amafuna kuti Mawu a Mulungu awatsogolere limodzinso ndi mzimu wake woyera.

Ndi chinthu chofunika kwambiri kwa iwo kuti zimene amakhulupirira zikhale zochokera m’Baibulo, osati m’maganizo a munthu kapena ziphunzitso wamba zachipembedzo. Amaganiza mofanana ndi mmene mtumwi Paulo anaganizira pamene anauziridwa kunena kuti: “Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama.” (Aroma 3:4, Revised Nyanja (Union) Versiona) Pophunzitsa zinthu za choonadi cha m’Baibulo, Mbonizo zimalimbikitsa kwambiri kuti anthu azichita mmene Abereya anachitira pamene anamva ulaliki wa mtumwi Paulo: “Analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.” (Machitidwe 17:11) A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti ziphunzitso zonse zachipembedzo ziyenera kuyesedwa mwa njira imeneyi yoziyerekeza ngati zikugwirizana ndi Malemba ouziridwa, kaya chiphunzitsocho chikuperekedwa ndi iwowo kapena munthu winawake. Mbonizo zikukupemphani—inde kukulimbikitsani—kuti muzichita zimenezi pokambirana nazo.

Mwa zimenezi mutha kuona kuti a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Amakhulupirira kuti mabuku ake onse 66 ndi ouziridwa komanso olondola pankhani za mbiri yakale. Malemba amene anthu ambiri amawatcha Chipangano Chatsopano, iwo amawatcha Malemba Achigiriki Achikristu, ndipo Chipangano Chakale amachitcha Malemba Achihebri. Iwo amagwiritsa ntchito mbali zonse ziŵiri, Malemba Achigiriki ndi Malemba Achihebri, ndipo zolembedwa mmenemo amazitenga kukhala zenizeni monga momwe zinalembedweramo, kupatulapo ngati mawuwo kapena zochitika zake zikusonyeza moonekeratu kuti ndi zophiphiritsa kapena zizindikiro. Amazindikira kuti maulosi ambiri operekedwa m’Baibulo akwaniritsidwa kale, ena akukwaniritsidwa panopo, ndipo enanso adzakwaniritsidwabe m’tsogolo.

DZINA LAWO

Mboni za Yehova? Inde, limeneli ndilo dzina limene amadzitcha nalo. Ndi dzina lokhala ndi tanthauzo lake, posonyeza kuti amachitira umboni za Yehova, Umulungu wake, ndi zofuna zake. Mayina akuti “Mulungu,” “Ambuye,” ndi “Mlengi,” ali mayina a udindo ndipo angagwiritsidwe ntchito kwa anthu osiyanasiyana—mofanana ndi mayina oti “Pulezidenti,” “Mfumu,” ndi “Kazembe.” Koma dzina lakuti “Yehova” ndi dzina lakelake la Mulungu wamphamvu yonse ndi Mlengi wa chilengedwe chonse. Titha kuona zimenezi pa Salmo 83:18, pomwe pamati: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”

Dzina lakuti Yehova (kapena Yahve, malinga ndi Baibulo la Akatolika lotchedwa Malembo Oyera ndiponso akatswiri ena) limapezeka pafupifupi m’malo 7,000 m’Malemba Achihebri oyambirira. Mabaibulo ambiri satchula dzinalo, m’malo mwake amatchula “Mulungu” kapena “Ambuye.” Komabe, ngakhale m’mabaibulo amenewo, munthu akhoza kudziŵabe mmene malemba Achihebri oyambirira anatchula Yehova chifukwa mayina olembedwa mmenemo alembedwa m’zilembo zazikulu, ngati motere: MULUNGU, AMBUYE. Mabaibulo ambiri amakono amatchula Yehova kapena Yahve. Choncho, Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version, pa Yesaya 42:8 limati, “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli.”

Nkhani ya m’Malemba imene Mboni za Yehova zimatengapo dzina lawo ili pa Yesaya chaputala 43. Pamenepo, dziko lonse likusonyezedwa ngati kuti lili m’bwalo la milandu: Milungu ya mitundu ya anthu ikuuzidwa kubweretsa mboni zawo kuti zipereke umboni wonena za chilungamo chawo, kapena kuti imvetsere mboni zoimira Yehova ndi kuti ivomereze kuti zikunena zoona. Pamenepo Yehova akulengeza kwa anthu ake kuti: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziŵe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.”—Yesaya 43:10, 11.

Yehova Mulungu anali ndi mboni zake kwa zaka zikwizikwi Yesu asanabadwe. Pambuyo pondandalika ena mwa anthu okhulupirika amenewo mu Ahebri chaputala 11, Ahebri 12:1 amati: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwa chipiriro makaniwo adatiikira.” Yesu anauza Pontiyo Pilato kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” Iye amatchedwa “mboni yokhulupirika ndi yoona.” (Yohane 18:37; Chivumbulutso 3:14) Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”—Machitidwe 1:8.

Motero, anthu pafupifupi 6,000,000 lerolino amene akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mwa Kristu Yesu m’mayiko oposa 230 akuona kuti n’koyeneradi kwa iwo kudzitcha Mboni za Yehova.

[Mawu a M’munsi]

a Limenelo ndilo Baibulo logwidwa mawu m’kabuku kano, kupatulapo ngati tasonyeza lina.

[Mawu otsindika patsamba 4]

Anadzipatulira kwa Mulungu kuti achite chifuniro chake

[Mawu otsindika patsamba 4]

Amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu

[Mawu otsindika patsamba 5]

Dzinalo m’nkhani yonga ya m’bwalo la milandu

[Mawu otsindika patsamba 5]

Mboni pafupifupi 6,000,000 m’mayiko oposa 230

[Chithunzi patsamba 3]

Amasamala za inu

[Chithunzi patsamba 4]

Dzina lakelake la Mulungu m’Chihebri chakale

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena