Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jt tsamba 15-18
  • Uthenga Wabwino Umene Amafuna Kuti Muumve

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uthenga Wabwino Umene Amafuna Kuti Muumve
  • Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MADALITSO PADZIKO LAPANSI A UFUMUWO
  • Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Mayankho a Mafunso Anayi Okhudza Kutha kwa Dziko
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Moyo Umene Adzabweretse
    Galamukani!—2006
  • Mmene Tidziŵira Kuti Tiri mu “Masiku Otsiriza”
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
Onani Zambiri
Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
jt tsamba 15-18

Uthenga Wabwino Umene Amafuna Kuti Muumve

PAMENE Yesu anali pa dziko lapansi, ophunzira ake anadza kwa iye ndi kum’funsa kuti: “Chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Poyankha iye anati padzakhala nkhondo zophatikizapo mayiko ambiri, njala, miliri, zivomezi, kukula kwa kusaweruzika, aphunzitsi onama achipembedzo osocheza ambiri, kudedwa ndi kuzunzidwa kwa atsatiri ake oona, ndi kusakondanso chilungamo kwa anthu ambiri. Zikayamba kuchitika zinthu zimenezi, zidzasonyeza kuti Kristu alipo mosaoneka ndi kuti Ufumu wa kumwamba uli pafupi. Umenewu ndi uthenga—inde uthenga wabwino! Motero Yesu anawonjezera mawu aŵa monga mbali ya chizindikirocho: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:3-14.

Zochitika zaposachedwapa za padziko zenizenizo n’zoipa, koma chinthu chimene zimasonyeza, chimene chili kukhalapo kwa Kristu, ndi chinthu chabwino. Mikhalidwe imene tatchulayo inayamba kuonekera m’chaka cholankhulidwa kwambiricho cha 1914! Chakacho chinali mapeto a Nthaŵi za Akunja koma chinalinso chiyambi cha nyengo yosintha kuchoka ku ulamuliro wa anthu kupita ku Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000 (Chikwi).

Mfundo yakuti padzakhala nyengo ya kusintha koteroko timaipeza pa Salmo 110, mavesi 1 ndi 2, komanso pa Chivumbulutso 12:7-12. Pamenepo timauzidwa kuti Kristu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu kumwambako kufikira nthaŵi ya kukhala kwake Mfumu. Keneko nkhondo yakumwamba ikagwetsera Satana ku dziko lapansi, akumabweretsa tsoka padziko lapansi, ndipo Kristu adzalamulira pakati pa adani ake. Kutha kwenikweni kwa zoipa zonse kudzafika ndi “chisautso chachikulu,” chimene chidzafika pachimake pa nkhondo ya Armagedo kenako padzatsatira Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000 wa mtendere.—Mateyu 24:21, 33, 34; Chivumbulutso 16:14-16.

“Koma zindikira ichi,” limatero Baibulo, “kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.”—2 Timoteo 3:1-5.

Ena angatsutse ndi kunena kuti zinthu zimenezi zakhala zikuchitika m’mbiri yonse ya anthu, koma mfundo ndi yakuti sizinachitikepo pamlingo umenewu. Monga momwe amanenera olemba mbiri ndi othirira ndemanga, nthaŵiyi yochokera mu 1914 kumka m’tsogolo sinayambe yakhalapo padziko lapansi m’mbuyo monsemo. (Onani tsamba 7.) Masoka ochitikawo akhala aakulu kuposa panthaŵi ina iliyonse. Komanso, ponena za mbali zina za chizindikiro cha Kristu cha masiku otsiriza, tiyenera kulingalira mfundo izi: Chilengezo cha padziko lonse cha kukhalapo kwa Kristu ndi Ufumu chikuperekedwa pamlingo waukulu koposa m’mbiri yonse ya anthu. Mazunzo amene achitikira Mboni za Yehova chifukwa cha kulalikira sanachitikirepo anthu ena pamlingo waukulu choncho. Mazanamazana a iwo ananyongedwa m’ndende za a Nazi. Mpaka pano, Mboni za Yehova n’zoletsedwa mwalamulo m’malo ena, ndipo m’madera ena zimamangidwa, kuponyedwa m’ndende, kuzunzidwa, ngakhale kuphedwa kumene. Zonsezi ndi mbali ya chizindikiro chimene Yesu anapereka.

Monga kunanenedwa pa Chivumbulutso 11:18, ‘amitundu akwiyira’ Mboni zokhulupirika za Yehova, ndipo zimenezi zimasonyeza kuti Yehova adzatsanulira ‘mkwiyo wake’ pa amitunduwo. Lemba limeneli limanenanso kuti Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ Chiwopsezo chimene chakhalapo pa zinthu zochirikiza moyo padziko lapansi sichinayambe chakhalapo m’mbiri yonse ya anthu. Koma tsopano zinthu zasinthiratu! Asayansi ambiri achenjeza kuti ngati anthu apitiriza kuwononga dziko lapansi, anthu sadzatha kukhalamo. Koma Yehova “analiumba akhalemo anthu,” ndipo adzachotsamo onsewo amene akuliwononga asafike poliwonongeratu.—Yesaya 45:18.

MADALITSO PADZIKO LAPANSI A UFUMUWO

Kunena zakuti anthu adzakhala pa dziko lapansi monga nzika za Ufumu wa Mulungu kungamveke kwachilendo kwa ambiri amene amakhulupirira Baibulo amene amaganiza kuti onse amene adzapulumuka adzapita kumwamba. Baibulo limasonyeza kuti oŵerengeka okha ndiwo akupita kumwamba ndi kuti aja amene adzakhala pa dziko lapansi kosatha adzakhala khamu lalikulu losaŵerengeka. (Salmo 37:11, 29; Chivumbulutso 7:9; 14:1-5) Mfundo yakuti Ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Kristu udzakuta dziko lapansi ndi kulamulira imasonyezedwa ndi ulosi wa m’buku la m’Baibulo la Danieli.

Mmenemo, Ufumu wa Kristu ukuimiridwa ndi mwala wosemedwa ku ulamuliro wa Yehova wonga phiri. Mwalawo ukukantha ndi kutswanya fano loimira mitundu yamphamvu ya padziko lapansi, ndipo “mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.” Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:34, 35, 44.

Ufumu umenewu limodzi ndi chiyembekezo cha m’Malemba cha moyo wosatha wa padziko lapansi loyeretsedwa ndi lokongola n’zimene Mboni za Yehova zimafuna kukuuzani. Mamiliyoni a anthu omwe alipo ndi moyo tsopano, komanso mamiliyoni ambiri omwe ali kumanda adzakhala ndi mwayi wokhala m’dziko limenelo kwamuyaya. Pamenepo, mu Ulamuliro wa Kristu Yesu wa Zaka 1,000, cholinga choyambirira cha Yehova polenga dziko lapansi ndi kuikamo anthu aŵiri oyambirira aja chidzakwaniritsidwa. Paradaiso wa padziko lapansi ameneyu sadzatopetsa. Monga momwe Adamu anapatsidwira ntchito m’munda wa Edene, anthunso adzakhala ndi ntchito yaikulu yosamalira dziko lapansi, zomera ndi nyama zomwe. “Adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”—Yesaya 65:22; Genesis 2:15.

Titha kupereka malemba ambiri osonyeza mikhalidwe imene idzakhalepo poyankhidwa pemphero limene Yesu anatiphunzitsa lakuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Komatu pakali pano n’kokwanira kudziŵa izi: “Ndinamva mawu akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:3-5.

[Mawu Otsindika patsamba 15]

“Nthaŵi zoŵaŵitsa”

KOMA “pomwepo chidzafika chimaliziro”

[Chithunzi patsamba 18]

Netherlands

[Chithunzi patsamba 18]

Nigeria

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena