Mafunso Amene Anthu Achidwi Amafunsa Kaŵirikaŵiri
Ngati Mulungu ndi chikondi, n’chifukwa chiyani amalola zoipa kuchitika?
MULUNGU amalola zinthu zoipa kumachitika, ndipo mamiliyoni a anthu padziko lapansi amachita dala zinthuzo. Mwachitsanzo, amayambitsa nkhondo, amaphulitsira ana mabomba, amaotcha nthaka, ndi kuchititsa njala. Anthu mamiliyoni ochuluka amasuta fodya ndi kudwala kansa ya m’mapapu, amachita zachiwerewere ndi kutenga matenda opatsirana mwakugonana, amamwa mwauchidakwa ndi kudwala matenda a m’chiŵindi, ndi zina zotero. Anthu oterowo safuna kwenikweni kuti zoipa zithe. Chimene amangofuna kuti chithe ndi zotsatira zake basi. Akatuta zimene afesa, amadandaula kuti, “Kalanga ine, ndalakwanji kodi kuti tsoka lotere lindigwere ine?” Akatero amapatsa mlandu Mulungu, monga momwe Miyambo 19:3 imanenera kuti: “Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova.” Ndipo kuti Mulungu awaletse kuchita zoipa zawozo, angadandaulenso kuti akuwalanda ufulu wawo wochita zinthuzo!
Chifukwa chachikulu chimene Yehova walolera zinthu zoipa n’chofuna kuti atsimikizire Satana kukhala wabodza. Satana Mdyerekezi ananena kuti Mulungu sangathe kukhala ndi anthu okhulupirika kwa Iye padziko lapansi ngati anthuwo akumana ndi zovuta. (Yobu 1:6-12; 2:1-10) Yehova walola Satana kukhalapobe pofuna kum’patsa mpata wakuti atsimikizire zonena zakezo. (Eksodo 9:16) Satana akupitiriza kubweretsa masoka, kunyenga anthu kuti apandukire Mulungu, pofuna kuonetsa kuti zimene ananenazo n’zoona. (Chivumbulutso 12:12) Komabe, Yobu anakhalabe wokhulupirika. Yesunso anatero. Akristu oona akuteronso lerolino.—Yobu 27:5; 31:6; Mateyu 4:1-11; 1 Petro 1:6, 7.
Ndikufuna kuti ndizikhulupirira za paradaiso wa padziko lapansi mmene anthu adzakhala ndi moyo wamuyaya, koma kodi zidzachitikadi?
Inde malinga n’kunena kwa Baibulo. N’zovuta kuzikhulupirira chifukwa anthu azoloŵera zinthu zoipa kwa zaka mazana ambiri. Yehova analenga dziko lapansi ndipo anauza anthu kuti alidzaze ndi amuna ndi akazi olungama, amene adzasamalira zomera ndi nyama zake, ndi kuliyang’anira kuti likhalebe lokongola m’malo moliwononga. (Onani masamba 12 ndi 17.) Chimene chiyenera kukhala chosatheka si kubwera kwa Paradaiso wolonjezedwayo ayi, koma kuti mkhalidwe womvetsa chisoniwu upitirire mpaka kalekale. Udzaloŵedwa m’malo ndi Paradaiso.
Kodi ndingawayankhe motani anthu amene amaseka ndi kunena kuti Baibulo ndi nthano chabe ndipo zimene limanena sizigwirizana ndi sayansi?
Kukhulupirira malonjezo ameneŵa si kukhulupirira kongotengeka maganizo ayi. “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri.” Mwa kuphunzira Mawu a Mulungu, nzeru yake imaonekera ndipo chikhulupiriro chimakula.—Aroma 10:17; Ahebri 11:1.
Zofukula m’mabwinja zokhudza Baibulo zimatsimikizira kuti zochitika zakale zimene Baibulo limanena n’zolondola. Ngakhale sayansi yoona imagwirizana ndi Baibulo. Mfundo zenizeni zotsatirazi zinalimo kale m’Baibulo kwa nthaŵi yaitali akatswiri a zamaphunziro asanazitulukire: dongosolo la mmene dziko lapansi linapangidwira, kuti dziko lapansi n’lozungulira, kuti n’lolenjekeka pachabe m’malere, ndi kuti mbalame zimasamuka kukakhala kumayiko ena akutali ndi kubweranso.—Genesis, chaputala 1; Yesaya 40:22; Yobu 26:7; Yeremiya 8:7.
Kukwaniritsidwa kwa maulosi uli umboni wakuti Baibulo lilidi Mawu ochokera kwa Mulungu. Danieli ananeneratu kale za kubwera ndi kutha kwa maulamuliro amphamvu padziko lonse, limodzinso ndi nthaŵi ya kubwera kwa Mesiya ndi kuphedwa kwake. (Danieli, machaputala 2, 8; 9:24-27) Lerolinonso, maulosi ena akukwaniritsidwabe, ndipo akusonyeza kuti ano ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu, chaputala 24) Kudziŵiratu zinthu kotereku sikungatheke mwa mphamvu ya munthu ayi. (Yesaya 41:23) Kuti mupeze umboni wowonjezera, onani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi lachingelezi lakuti Is There a Creator Who Cares About You?, ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society.
Kodi ndingadziŵe motani kuyankha mafunso okhudza Baibulo?
Muyenera kuphunzira Baibulo ndi kulisinkhasinkha, panthaŵi imodzimodziyo muyenera kumapempha mzimu wa Mulungu kuti ukutsogolereni. (Miyambo 15:28; Luka 11:9-13) “Wina wa inu ikam’soŵa nzeru,” limatero Baibulo, “apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, ndi wosatonza; ndipo adzam’patsa iye.” (Yakobo 1:5) Ndiponso, pali mabuku ophunzirira Baibulo amene muyenera kuwaŵerenga. Nthaŵi zambiri pamafunika kuthandizidwa ndi anthu ena, monga momwe anachitira Filipo pamene anaphunzira ndi Mwaitopiya uja. (Machitidwe 8:26-35) A Mboni za Yehova amaphunzitsa Baibulo kwaulere kwa anthu ofuna kutero panyumba pawo. Khalani omasuka kuwapempha thandizo limeneli.
N’chifukwa chiyani anthu ambiri amatsutsa a Mboni za Yehova ndi kumandichenjeza kuti ndisawalole kundiphunzitsa?
Panali anthu amene anatsutsa ulaliki wa Yesu, ndipo iye anati otsatira akenso adzatsutsidwa. Pamene ena anachita chidwi ndi chiphunzitso cha Yesu, otsutsa achipembedzo anawadzudzula kuti: “Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi?” (Yohane 7:46-48; 15:20) Ambiri amene amakuuzani kuti musaphunzire ndi a Mboni amatero chifukwa cha kusadziŵa kapena chidani. Taphunzirani ndi a Mboni ndi kudzionera nokha ngati chidziŵitso chanu cha Baibulo chidzawonjezeka kapena kuchepa.—Mateyu 7:17-20.
N’chifukwa chiyani a Mboni amalalikiranso kwa anthu omwe ali kale ndi chipembedzo chawo?
Pochita zimenezi iwo amatengera chitsanzo cha Yesu. Iye anapita kwa Ayuda. Ayudawo anali ndi chipembedzo chawo, koma m’njira zambiri chinali chitasemphana ndi Mawu a Mulungu. (Mateyu 15:1-9) Mayiko onse ali ndi zipembedzo zosiyanasiyana, zachikristu kapena zosakhala zachikristu. N’kofunika kwambiri kuti anthu akhale ndi chikhulupiriro chogwirizana ndi Mawu a Mulungu, khama limene Mboni zimachita pothandiza anthu kuchita zimenezo limasonyeza chikondi chawo kwa mnansi.
Kodi a Mboni amakhulupirira kuti chipembedzo chawo ndicho chokha choona?
Aliyense amene amakhulupiriradi chipembedzo chake ayenera kukhala wotsimikiza kuti ndi choona. Chifukwa ngati satero, akhaliramo chiyani? Akristu amalangizidwa kuti: “Yesani zonse; sungani chokomacho.” (1 Atesalonika 5:21) Munthu ayenera kutsimikiza kuti zimene amakhulupirira zili ndi umboni wa Malemba, pakuti chikhulupiriro choona chilipo chimodzi chokha basi. Aefeso 4:5 amatsimikizira zimenezi, ponena kuti, “Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.” Yesu sanavomereze maganizo ololera omwe alipo lero akuti pali njira zambiri, zipembedzo zambiri, zonse zotsogolera ku chipulumutso. Mosiyana ndi zimenezo, iye anati: “Chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti njirayo anaipeza. Ndiye chifukwa chake sakufunafuna chipembedzo china.—Mateyu 7:14.
Kodi amakhulupirira kuti ndiwo okha amene adzapulumuka?
Ayi. Anthu mamiliyoni ambiri amene anafa m’zaka mazanamazana zapitazo amene sanali Mboni za Yehova adzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo. Ambiri amene ali ndi moyo tsopano akhoza kubwerabe kumbali ya choonadi ndi chilungamo, chisanafike “chisautso chachikulu,” ndipo adzapulumuka. Ndiponso, Yesu anati tisaweruzane. Ife timangoona maonekedwe akunja; Mulungu amaona mumtima. Amaona zenizeni ndipo amaweruza mwachifundo. Kuweruza anakuika m’manja mwa Yesu, si mwathu ayi.—Mateyu 7:1-5; 24:21; 25:31.
Kodi aja amene amafika pamisonkhano ya Mboni za Yehova amayembekezeka kupereka ndalama zotani?
Ponena za zopereka za ndalama, mtumwi Paulo anati: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Pa Nyumba za Ufumu ndi pamisonkhano ikuluikulu ya Mboni za Yehova, sipakhala kusonkhetsa ndalama kulikonse. Pamakhala mabokosi mmene aliyense wofuna kupereka mwaufulu amaponyamo chopereka chake. Palibe aliyense amadziŵa zimene ena amapereka kapena ngati wina wapereka kapena sanapereke. Ena amatha kupereka zoposa anzawo; ena satha kupereka chilichonse. Yesu anasonyeza maganizo oyenera pamene analankhula za bokosi la chopereka pa kachisi ku Yerusalemu komanso za operekawo: Chimene chili kanthu ndi mphamvu ya munthu ya kupereka limodzi ndi mzimu wa kupereka, osati kuchuluka kwa ndalama ayi.—Luka 21:1-4.
N’takhala wa Mboni za Yehova, kodi adzafuna kuti inenso ndizilalikira mmene iwo amachitira?
Pamene munthu aphunzira zambiri ponena za Paradaiso wapadziko lapansi wolonjezedwayo mu Ufumu wa Kristu, amafuna kumauzako ena za zimenezo. Inunso mudzatero. Inde, uli uthenga wabwino!—Machitidwe 5:41, 42.
Kuchita zimenezi ndi njira yofunika kwambiri yosonyezera kuti ndinu wophunzira wa Yesu Kristu. M’Baibulo, Yesu amatchedwa “mboni yokhulupirika ndi yoona.” Pamene anali padziko lapansi analalikira kuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira,” ndipo anatumiza ophunzira ake kukachita zofananazo. (Chivumbulutso 3:14; Mateyu 4:17; 10:7) Pambuyo pake, Yesu analamula ophunzira ake kuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” Ananenanso kuti mapeto asanafike, “uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Pali njira zambiri zolengezera uthenga wabwinowu. Kukambirana ndi mabwenzi ndi anthu achinansi kaŵirikaŵiri kumapereka mpata wochitira zimenezo. Ena amalalikira mwa kulemba makalata kapena mwa kuimba telefoni. Ena amatumiza mabuku okhala ndi nkhani zimene akuganiza kuti mnzawoyo adzazikonda. Posafuna kusiya aliyense, a Mboni amafikira khomo ndi khomo ndi uthengawo.
Baibulo limapereka chiitano chachikondi chakuti: “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Kuuza ena za dziko la Paradaiso ndi madalitso ake kuyenera kuchitidwa modzifunira, ndi mtima wofunitsitsa kuuza ena za uthenga wabwino umenewu.
Tikhulupirira kuti muli ndi mafunso enanso ponena za Mboni za Yehova ndi ziphunzitso zawo. Zingakhalepo nkhani zina zovuta kwambiri. Koma ife tili ofunitsitsa kuyankha mafunso anu. Sitingathe kufotokoza zambiri m’kabuku kano, choncho langizo lathu n’lakuti funsirani kwa Mboni za kwanuko. Mutha kukafunsa mafunso anu ku Nyumba ya Ufumu kumene amasonkhana kapena pamene akufikirani panyumba panu. Kapenanso mukhoza kutumiza mafunso anu ku Watch Tower, pogwiritsa ntchito maadiresi ali m’munsiŵa.