Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be tsamba 13-tsamba 16 ndime 5
  • “Yang’anirani Mamvedwe Anu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Yang’anirani Mamvedwe Anu”
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Konzekeretsani Mtima Wanu
  • Lunjikitsani Maganizo Anu
  • Kumvetsera Nkhani
  • Kumvetsera Pamakambirano
  • Kumvetsera pa Misonkhano Ikuluikulu
  • Kuphunzitsa Ana Kumvetsera
  • Khalani Mmvetseri Wabwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Mvetserani Bwinobwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Mmene Yehova Akutitsogolera
    Nsanja ya Olonda—2000
  • ‘Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be tsamba 13-tsamba 16 ndime 5

“Yang’anirani Mamvedwe Anu”

KUMVETSERA ndi mbali yofunika kwambiri pophunzira. Kukhoza kukhudzanso mwayi wa munthu wa kupulumuka. Pamene Yehova anali kukonzekera kulanditsa anthu ake mu ukapolo ku Igupto, anapatsa Mose malangizo, amene iyenso anauza amuna akulu a Israyeli zimene anayenera kuchita kuti apulumutse ana awo achisamba kwa mngelo wakupha. (Eks. 12:21-23) Ndiyeno amuna akuluwo anapereka malangizowo ku banja lililonse. Anachita zimenezo mwa mawu apakamwa. Choncho anthuwo anafunikira kumvetsera mosamala. Koma kodi iwo analabadira motani? Baibulo limati: “Ana onse a Israyeli anachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.” (Eks. 12:28, 50, 51) Zotsatira zake, Israyeli analanditsidwa mwa njira yochititsa mantha.

Lerolino, Yehova akutikonzera chilanditso chachikulu kuposa chimenecho. Ndithudi, malangizo omwe amawapereka tiyenera kuwasamalira. Malangizo amenewo amaperekedwa pamisonkhano yampingo. Kodi mumapindula mokwanira pamisonkhano imeneyo? Zimenezi zimadalira kwambiri mmene mumamvetsera.

Kodi mumakumbukira mfundo zazikulu za malangizo operekedwa pamisonkhano? Kodi muli nacho chizolowezi chakuti mlungu ndi mlungu mumafunafuna njira zogwiritsira ntchito malangizo operekedwawo pamoyo wanu kapena kuuzako anthu ena?

Konzekeretsani Mtima Wanu

Kuti tipindule mokwanira ndi malangizo operekedwa pamisonkhano yachikristu, tiyenera kukonzekeretsa mitima yathu. Tikhoza kuona kufunika kochita zimenezo mwa kuona zimene zinachitika m’nthaŵi imene Mfumu Yehosafati anali kulamulira Yuda. Yehosafati anali wolimbika mtima pa kulambira koona. “Anachotsanso misanje ndi zifanizo m’Yuda” ndipo anatuma akalonga, Alevi, ndi ansembe kuti aphunzitse Chilamulo cha Yehova kwa anthu okhala m’mizinda yonse ya Yuda. Chikhalirechobe, “misanje siinachotsedwa.” (2 Mbiri 17:6-9; 20:33) Kulambira milungu yonama ndi kulambira Yehova kosaloleka kumene kunali kuchitika pa misanje yachikunja kunali kutazika mizu mozama kwambiri, moti sikunatheretu.

N’chifukwa chiyani malangizo okonzedwa ndi Yehosafati sanathandize kwa nthaŵi yaitali? Nkhaniyo ikupitirira kuti: “Popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yawo kwa Mulungu wa makolo awo.” Iwo anamva koma analephera kulabadira. Mwina anaona kuti chinali chintchito chotopetsa kuyenda ulendo wopita ku Yerusalemu kukapereka nsembe. Kaya chifukwa chake chinali chotani, chikhulupiriro chawo chinali chosafika pamitima yawo.

Kuti tisabwerere ku njira za dziko la Satana, tiyenera kukonza mitima yathu kuti ilandire malangizo omwe Yehova amapereka lerolino. Motani? Njira imodzi yofunika kwambiri ndiyo pemphero. Tiyenera kutchula m’pemphero kuti tidzalandira ndi mtima woyamikira malangizo a Mulungu. (Sal. 27:4; 95:2) Zimenezo zidzatithandiza kuyamikira ntchito yaikulu imene abale athu amachita, chifukwa ngakhale ali opanda ugwiro, amadzipereka kuti Yehova awagwiritse ntchito kuphunzitsa anthu ake. Tidzakhala ndi mitima yothokoza Yehova, osati chabe chifukwa cha zinthu zatsopano zomwe tikuziphunzira, komanso chifukwa cha mwayi womwe tili nawo wozamitsa zimene tikudziwa pa nkhani zimene taziphunzirapo kale. Pokhala ndi chikhumbo chochita chifuniro cha Mulungu mokwanira, pemphero lathu likhale lakuti: “Mundionetse njira yanu, Yehova. . . . Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.”—Sal. 86:11.

Lunjikitsani Maganizo Anu

Pali zinthu zambiri zimene zimatilepheretsa kutchera khutu. Tingakhale ndi nkhaŵa m’maganizo mwathu. Phokoso komanso kuyendayenda kwa anthu m’katimo posonkhana kapena panja kungatidodometse. Kusamva bwino m’thupi kungatilepheretse kuika maganizo pa nkhani. Amene ali ndi ana aang’ono kaŵirikaŵiri amapeza kuti maganizo awo amadodometsedwa. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tizisunga maganizo athu pa pulogalamu?

Kaŵirikaŵiri, maso ndiwo amatsogolera maganizo athu. Gwiritsani ntchito maso anu kuti akuthandizeni kusunga maganizo pamodzi mwa kuyang’ana wolankhulayo. Pamene atchula lemba m’Baibulo—ngakhale lodziŵika—litseguleni, ndipo m’tsatireni pamene akuŵerenga. Kanizani mutu wanu kucheukira phokoso lililonse kapena munthu amene akuyenda. Ngati maso anu akupereka zododometsa zambiri ku maganizo anu, mungaphonye zambiri zimene zikulankhulidwa ku pulatifomu.

Ngati “zolingalira” zina zikukulepheretsani kuika maganizo anu pa pulogalamu, pempherani kwa Yehova kuti akhazikitse pansi maganizo ndi mtima wanu kuti mutchere khutu. (Sal. 94:19; Afil. 4:6, 7) Chitani zimenezo mobwerezabwereza ngati kuli kofunika. (Mat. 7:7, 8) Misonkhano yampingo ndi chogaŵira cha Yehova. Khalani ndi chidaliro chakuti iyenso amafuna kuti mupindule nayo.—1 Yoh. 5:14, 15.

Kumvetsera Nkhani

N’kwachidziŵikire kuti mukhoza kukumbukira mfundo zimene munazikonda pomvera nkhani zosiyanasiyana. Komabe, kumvetsera nkhani kumafunanso zinthu zina kuwonjezera pa kusonkhanitsa mfundo zapadera. Nkhani ili ngati ulendo. Ngakhale kuti m’njira mungakhale zinthu zosangalatsa kuona, chinthu chachikulu ndicho malo omwe mukupitako, cholinga cha ulendowo. Wokamba nkhani angayese kutsogolera omverawo ku mfundo inayake kapena kuwalimbikitsa kuchita kanthu kena.

Taganizani nkhani imene Yoswa anakamba ku mtundu wa Israyeli, yolembedwa pa Yoswa 24:1-15. Cholinga chake chinali kulimbikitsa anthuwo kulimbika mtima ndi kusagonja pochirikiza kulambira koona mwa kudzilekanitsa kotheratu ndi kulambira mafano kwa mitundu yowazungulira. N’chifukwa chiyani zimenezo zinali zofunika kwambiri? Kulambira konyenga kofalako kunaopseza kwambiri khalidwe labwino la mtunduwo pamaso pa Yehova. Anthuwo analabadira kuchonderera kwa Yoswa mwa kunena kuti: “Sikungatheke kuti tim’siye Yehova, ndi kutumikira milungu ina; . . . ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu.” Ndipo anaterodi kumene!—Yos. 24:16, 18, 31.

Pamene mukumvetsera nkhani, yesani kupeza cholinga chake. Onani mmene mfundo zimene wokambayo akutulutsa zikuthandizira kufika pa cholingacho. Dzifunseni chimene mfundozo zikufuna kuti inuyo mukachite.

Kumvetsera Pamakambirano

Phunziro la Nsanja ya Olonda, Phunziro la Buku la Mpingo, ndi mbali zina za Msonkhano wa Utumiki zimachitika ngati makambirano a mafunso ndi mayankho pa nkhani zolembedwa zozikidwa pa Baibulo.

Kumvetsera pamakambirano kumakhala ngati inunso mukutengapo mbali. Kuti mupindule mokwanira, mvetserani mosamala. Onani kumene makambiranowo akuloŵera. Onaninso mmene wochititsayo akutsindikira mutu wa nkhani ndi mfundo zazikulu. Yankhani mafunso ake m’maganizo mwanu. Mvetserani pamene ena akufotokoza ndi kusonyeza mmene mfundozo zimagwirira ntchito. Kuona mfundo mmene ena amazionera kungakupatseni kaonedwe katsopano pankhani imene mukuidziŵa kale. Limbikitsani kupatsana maganizoko mwa kulankhula mawu anu a chikhulupiriro.—Aroma 1:12.

Kuŵerengeratu nkhani zondandalikidwa kukakuthandizani kuloŵetsedwa m’makambiranowo ndi kutsatira ndemanga za ena. Ngati mikhalidwe yanu sikulolani kuphunzira bwinobwino nkhanizo, ingotengani mphindi zochepa kungoziŵerenga musanapite kumsonkhano kuti mukhale ndi chithunzi chake. Pochita zimenezo mudzatha kupindula pomvetsera makambiranowo.

Kumvetsera pa Misonkhano Ikuluikulu

Pamisonkhano ikuluikulu m’pamene pamakhala zocheutsa zambiri kusiyana ndi pamisonkhano yampingo. Pachifukwa chimenechi, kumvetsera kungakhale kovutirapo. Kodi chingathandize n’chiyani?

Chofunikanso china ndicho kupumula mokwanira usiku. Pulogalamu isanayambe tsiku lililonse, sungani m’maganizo mutu wa nkhani wa tsikulo. Yang’anani mutu wa nkhani iliyonse, ndipo yesani kuganizira mfundo zimene zingakambidwe. Gwiritsani ntchito Baibulo kwambiri. Anthu ambiri amaona kuti kulemba manotsi achidule a mfundo zazikulu kumawathandiza kusunga maganizo pa pulogalamuyo. Lembani malangizo amene mukufuna kuwagwiritsa ntchito pamoyo wanu kapena mu ulaliki. Tsiku lililonse pamene muli m’njira, popita kapena pobwerako ku msonkhano, kambiranani mfundo zingapo. Kuteroko kudzakuthandizani kusaiŵala mfundo zimenezo.

Kuphunzitsa Ana Kumvetsera

Makolo achikristu akhoza kuthandiza ana awo—ngakhale ali achichepere—‘kukhala anzeru kufikira chipulumutso’ mwa kupita nawo kumisonkhano yampingo, misonkhano yadera, yapadera, ndi yachigawo. (2 Tim. 3:15) Popeza kuti ana amakhala amaganizo osiyana ndiponso amagwira zinthu mosiyana, kuzindikira n’kofunika pofuna kuwathandiza kuti aphunzire kutchera khutu. Njira zotsatirazi zingakhale zothandiza kwa inu.

Kunyumba, khazikitsani nthaŵi imene ana anu aang’ono azikhala pansi ndi kuŵerenga kapena kuyang’ana zithunzi m’mabuku athu achikristu. Kumisonkhano, peŵani kupatsa ana zinthu zoseŵeretsa pofuna kuti asatope. Monga zinalili kwa Israyeli wakale, leronso ana aan’gono amakhalapo pamisonkhano kotero “kuti amve, ndi kuti aphunzire.” (Deut. 31:12) Kumene zili zotheka, makolo ena amapatsa ngakhale ana aang’ono kwambiri makope awoawo a mabuku omwe akuphunziridwa. Pamene anawo akusinkhukirapo, athandizeni kukonzekera kutenga mbali m’mapulogalamu ofuna omvetsera kukambapo.

Malemba amasonyeza mgwirizano waukulu umene uli pakati pa kumvetsera kwa Yehova ndi kumumvera. Tikhoza kuona zimenezi m’mawu a Mose polankhula ku mtundu wa Israyeli kuti: ‘Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, . . . [mwa] kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira iye.’ (Deut. 30:19, 20) Lerolino, kumvetsera malangizo amene Yehova amapereka ndi kuwamvera mwa kuwagwiritsa ntchito pamiyoyo yathu n’kofunika kuti tipeze chiyanjo cha Mulungu ndi dalitso la moyo wosatha. Ndithudi, n’kofunika kwambiri kuti tilabadire uphungu wa Yesu wakuti, “Yang’anirani mamvedwe anu”!—Luka 8:18.

MALANGIZO PA KUMVETSERA MOSAMALA

  • Pemphererani chithandizo kuti muike maganizo anu papulogalamu

  • Maso anu azikhala kwa wolankhulayo

  • Pamene malemba akutchulidwa, atseguleni m’Baibulo lanu, ndipo tsatirani poŵerenga

  • Yesani kupeza cholinga cha nkhani

  • M’maganizo mwanu, yankhani mafunso ofunsidwawo; mvetserani mosamala ndemanga zoperekedwa

  • Lembani manotsi achidule

  • Sankhani mfundo zimene mukufuna kukazigwiritsa ntchito

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena