PHUNZIRO 39
Mawu Omaliza Ogwira Mtima
MUKHOZA kufufuza mosamala ndi kusanja bwino mfundo za thunthu la nkhani yanu. Mukhozanso kukonzekera mawu oyamba okopa chidwi. Komabe, palinso kanthu kena kofunikira—ndiko mawu omaliza ogwira mtima. Musachepetse kufunika kwake. Zimene mumanena pomaliza n’zimene zimakumbukika kwa nthaŵi yaitali. Ngati mawu omaliza akhala ofooka, ngakhale mfundo zoyambazo zimatha mphamvu yake.
Lingalirani zotsatirazi: Yoswa atayandikira mapeto a moyo wake, anakamba nkhani yosaiŵalika kwa akuluakulu a mtundu wa Israyeli. Atafotokoza mmene Yehova anachitira ndi Israyeli kuchokera m’masiku a Abrahamu, kodi Yoswa anatchula mfundo zazikulu mongodutsa? Ayi. M’malo mwake, mokhudzika mtima kwambiri analimbikitsa anthuwo kuti: “Opani Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wangwiro ndi woona.” Tadziŵerengerani nokha mawu omaliza a Yoswa pa Yoswa 24:14, 15.
Nkhani inanso yochititsa chidwi ili pa Machitidwe 2:14-36. Amene anaikamba ndi mtumwi Petro polankhula ndi khamu la anthu ku Yerusalemu pa Phwando la Pentekoste wa 33 C.E. Choyamba anafotokoza kuti iwo anali kuona kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yoweli wonena za kutsanulidwa kwa mzimu wa Mulungu. Kenako anasonyeza mmene chochitikacho chinakhudzira maulosi a Mesiya m’lemba la Masalmo, omwe ananeneratu za kuuka kwa Yesu Kristu ndi kukwezedwa kwake kudzanja lamanja la Mulungu. Ndiyeno m’mawu ake omaliza, Petro anatchula momvekera bwino mfundo imene aliyense mwa omvera akewo anafunikira kuidziŵa. Iye anati: “Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu Yesu, amene inu munam’pachika.” Analipowo anafunsa kuti: “Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?” Petro anayankha nati: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu.” (Mac. 2:37, 38) Tsiku limenelo, pafupifupi anthu 3,000 mwa omvera akewo, pokhudzika ndi zimene anamva, analandira choonadi chonena za Yesu Kristu.
Mfundo Zofunika Kuzikumbukira. Zimene munena m’mawu anu omaliza ziyenera kukhudzana mwachindunji ndi mutu wa nkhani yanu. Zikhale mawu omaliza a mfundo zimene mwafotokoza. Ngakhale kuti mungafune kuphatikizapo mawu ofunikira a m’mutu wa nkhani, mukhozanso kutchula mutu wonse wa nkhani.
Kwenikweni, cholinga cha nkhani yanu ndi kulimbikitsa ena kuchitapo kanthu pamfundo zimene mwawapatsa. Cholinga china chachikulu cha mawu omaliza ndicho kusonyeza zoyenera kuchita. Posankha mutu wa nkhani ndi mfundo zazikulu, kodi munalingalira mofatsa chifukwa chake nkhaniyo ikakhala yofunika kwa omvera anu ndi cholinga chanu choikambira? Ngati munatero, mukudziŵa zimene mukufuna kuti akachite. Tsopano muyenera kunena zimene ayenera kuchitazo mwinanso ndi mmene angachitire zimenezo.
Kuwonjezera pa kuuza omvera anu zimene ayenera kuchita, mawu anu omaliza ayeneranso kuwalimbikitsa. Zimenezo zimaphatikizapo kunena zifukwa zabwino zochitira zimenezo ndipo mwina mapindu ake. Ngati sentensi yomaliza mwaiganizira bwino, ndi kuinenanso bwinobwino, idzapatsa nkhani yonseyo mphamvu yofunikira.
Kumbukirani kuti nkhaniyo ikufika kumapeto. Zimene mukunena zisonyeze zimenezo. Liŵiro lanunso likhale loyenerera. Musalankhule mofulumira mpaka kumapeto kwenikweni kenako n’kutha mwadzidzidzi. Komanso, mawu anu asangozimiririka. Mphamvu ya mawu anu ikhalepobe ndithu, koma osati kwambiri. Masentensi anu omalizira amveke kuti mukufika kumathero. Muwalankhule motsimikiza ndi mwachidaliro. Pokonzekera kukamba nkhani yanu, musalephere kuyeseza mawu anu omaliza.
Kodi mawu omaliza azikhala autali wotani? Palibe mphindi zoikika. Koma asakhale amtatakuya kapena kuti ongopitirira. Utali wake umadalira mmene mawuwo akhudzira mtima omvera. Mawu omaliza osavuta ndi olunjika amakhala bwino kwambiri. Komanso otalikirapo ophatikizapo chitsanzo chachidule angakhale ogwira mtima ngati muwakonzekera mosamala. Yerekezani mawu omaliza a buku lonse la Mlaliki pa Mlaliki 12:13, 14, ndi mawu omaliza a nkhani yofupikirapo ya Ulaliki wa pa Phiri wolembedwa pa Mateyu 7:24-27.
Mu Utumiki wa Kumunda. Kuposa kwina kulikonse, mawu omaliza amafunikira kaŵirikaŵiri mu utumiki wa kumunda. Mwa kukonzekera ndi pokhala ndi chidwi chachikondi kwa anthu, mungathandize ambiri. Malangizo omwe tafotokoza pamasamba a m’mbuyoŵa angathandize ngakhale pokambirana ndi munthu mmodzi.
Nthaŵi zina makambirano angakhale achidule kwambiri. Munthunso angakhale wotanganidwa. Kucheza kwanu konse kungakhale kwa mphindi imodzi yokha. Ngati kuli koyenera, munganene zonga izi: “Inenso ndaona kuti mwatanganidwa. Koma ndingokusiirani mfundo imodzi yolimbikitsa. Baibulo limasonyeza kuti Mlengi wathu ali ndi cholinga chabwino kwambiri—akufuna kudzakonzanso dzikoli kuti lidzakhale malo mmene anthu adzasangalale ndi moyo kosatha. Ifenso tikhoza kudzakhalamo m’Paradaiso ameneyo, koma tiyenera kuphunzira zimene Mulungu amafuna.” Kapena mungangolonjeza kudzafikanso tsiku limene angapeze mpata wabwino.
Ngati mwininyumbayo akudulani—ngakhale mwamwano—mukhoza kuchitabe chinthu chanzeru. Kumbukirani uphungu wopezeka pa Mateyu 10:12, 13 ndi Aroma 12:17, 18. Kuyankha kwanu mofatsa kungasinthe maganizo ake kwa Mboni za Yehova. Pamenepo ndiye kuti mwachita chinthu chanzeru kwambiri.
Komanso, mwina mungakhale ndi makambirano abwino kwambiri ndi mwininyumba. Bwanji osatchulanso mfundo yaikulu imene mukufuna kuti akaikumbukire? M’limbikitseninso kuti akachitepo kanthu.
Ngati muona kuti mwayi ulipo wodzachezanso naye, siyirani munthuyo kanthu kena kokayembekezera. Funsani funso—mwina lochokera m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba kapena chofalitsa chopangitsira maphunziro a Baibulo. Musaiŵale cholinga chanu choperekedwa ndi Yesu pa Mateyu 28:19, 20.
Kodi mukumaliza phunziro la Baibulo? Kutchulanso mutu wa nkhani kudzathandiza wophunzirayo kukumbukira zimene mwakambirana. Kugwiritsa ntchito mafunso obwereza kumakhomereza mfundo zazikulu m’maganizo mwa wophunzira, makamaka ngati kubwerezako kuchitika modekha. Kufunsa wophunzirayo mmene zimene mwaphunzira zingam’thandizire, kapena mmene angauzireko ena kungam’thandize kulingalira za mmene angazigwiritsire ntchito.—Miy. 4:7.
Kumbukirani—mawu anu omaliza amachititsa zonse zimene mwalankhula kukhala zogwira mtima.