Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 40 tsamba 223-tsamba 225 ndime 3
  • Kunena Zoona Zokhazokha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kunena Zoona Zokhazokha
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula Zoona Komanso Zofika Pamtima
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Mmene Mungafufuzire
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Phunziro Limapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Zimene Mungachite Kuti Muzipindula Powerenga Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 40 tsamba 223-tsamba 225 ndime 3

PHUNZIRO 40

Kunena Zoona Zokhazokha

Kodi muyenera kunena zotani?

Nenani mawu ogwirizana kwenikweni ndi zoona zake.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Kunena zinthu zoona kumapereka chithunzi chabwino cha inuyo, chipembedzo chimene mukuchiimira, ndi Mulungu amene mumam’lambira.

KODI n’chiyani chimene chingachititse Mkristu kunena mawu osakhala oona? Anganene zimene anangomva, popanda kufufuza zoona zake. Kapena angakokomeze nkhani chifukwa chakuti anaiŵerenga molakwa, iye osazindikira. Pamene tikhala osamala kunena zoona zokhazokha, ngakhale m’nkhani zazing’ono, omvera athu amaona kuti angadalirenso zinthu zazikulu za uthenga wathu.

Mu Utumiki wa Kumunda. Ambiri poona kuti sanaphunzire zambiri, angachite mantha kuloŵa mu utumiki wa kumunda. Komabe, posapita nthaŵi oterowo amapeza kuti akutha kupereka umboni wogwira mtima, pogwiritsa ntchito mfundo zoyambirira zokha za choonadi zimene akuzidziŵa. Nanga zimatheka bwanji? Chinsinsi chake ndi kukonzekera.

Musanaloŵe mu utumiki wa kumunda, idziŵeni bwino nkhani imene mukakambirane ndi anthu. Yesani kuganizira mafunso amene omvera anu angafunse. Fufuzani mayankho okhutiritsa okhala ndi umboni wa m’Baibulo. Mukamatero muzitha kupereka mwachidaliro mayankho olondola. Kodi mukachititsa phunziro la Baibulo? Ŵerengani mosamala nkhani imene mukukaphunzira. Tsimikizani kuti mukumvetsa mayankho okhala ndi umboni wa Malemba pamafunso olembedwawo.

Bwanji ngati mwininyumba kapena mnzanu wa kuntchito afunsa funso limene simunakonzekere kuyankha? Ngati simuli wotsimikiza, musayese kungoyerekeza. “Mtima wa wolungama uganiza za mayankhidwe.” (Miy. 15:28) Mungapeze chithandizo chimene mukuchifuna m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba kapena mu “Nkhani Zokambirana za m’Baibulo,” ngati zilipo m’chinenero chanu. Ngati zimenezi mulibe, pemphani kuti mukafufuze ndipo mukabweranso. Ngati wofunsayo akufunadi kudziŵa, sadandaula kuyembekeza yankho lolondola. Ndipo angayamikire poona kudzichepetsa kwanu.

Kugwira ntchito mu utumiki wa kumunda ndi ofalitsa ozoloŵera kungakuthandizeni kupeza luso lolunjika nawo Mawu a Mulungu. Onani malemba omwe akugwiritsa ntchito ndi mmene akuwafotokozera. Modzichepetsa landirani maganizo alionse kapena kuwongolera kumene angapereke. Wophunzira wokangalika, Apolo, anapindula mwa kuthandizidwa ndi ena. Luka anati Apolo anali “wolankhula mwanzeru,” “wamphamvu m’malemba,” ‘wokhala nawo mzimu wachangu,’ ndi kuti “ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu.” Komabe, anali wosadziŵa zambiri. Prisikila ndi Akula ataona zimenezo “anam’tenga, nam’fotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.”—Mac. 18:24-28.

‘Kugwiritsa Mawu Okhulupirika.’ Nkhani zathu pamisonkhano ziyenera kuonetsa kuti timalemekeza kwambiri mpingo monga “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Tim. 3:15) Kuti tilemekeze choonadi, m’pofunika kuti timvetse lingaliro la malemba omwe tikufuna kuwagwiritsa ntchito m’nkhani zathu. Lingaliraninso mmene lembalo aligwiritsira ntchito komanso cholinga chake.

Dziŵaninso kuti zimene mumanena pamsonkhano wampingo ena akazilankhulanso. N’zoona kuti “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.” (Yak. 3:2) Koma mungapindule mwa kukulitsa chizoloŵezi cholankhula zinthu zoona. Abale ambiri omwe analembetsa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, m’kupita kwa nthaŵi adzakhala akulu. Okhala ndi udindo umenewo amayembekezeka ‘kubwezera zoposa.’ (Luka 12:48) Ngati mkulu mosasamala apereka uphungu wolakwika kwa ofalitsa umene ungagwetsere ofalitsawo m’mavuto aakulu, mkuluyo amapalamula kwa Mulungu. (Mat. 12:36, 37) Choncho, mbale woyeneretsedwa kukhala mkulu ayenera kudziŵika kuti ndi ‘wogwiritsa mawu okhulupirika monga mwa chiphunzitso.’ —Tito 1:9.

Onetsetsani kuti maganizo amene mukupereka akugwirizana ndi “mawu a moyo” opezeka m’Malemba onse. (2 Tim. 1:13) Zimenezi zisakuopseni. Mwina simunamalizebe kuŵerenga Baibulo lonse. Limbikirani mpaka mukalimalize. Koma pakali pano, onani mmene maganizo otsatiraŵa angakuthandizireni kupenda mfundo zimene mungafune kugwiritsa ntchito m’kuphunzitsa kwanu.

Choyamba dzifunseni kuti: ‘Kodi mfundoyi ikugwirizana ndi zimene ndaphunzira m’Baibulo? Kodi idzathandiza omvera anga kuyandikira Yehova, kapena kodi imakweza nzeru ya dziko ndi kulimbikitsa anthu kuika chidaliro chonse pa nzeru ya dzikoyo?’ Yesu anati: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yoh. 17:17; Deut. 13:1-5; 1 Akor. 1:19-21) Kenako, gwiritsani ntchito bwino zofalitsa zophunzirira Baibulo zoperekedwa ndi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Zofalitsazi zidzakuthandizani kumvetsa malemba molondola komanso kuwagwiritsa ntchito moyenerera ndi mwanzeru. Ngati nkhani zanu zizikika pa “mawu a moyo” ndipo ngati mudalira mthenga wa Yehova pofotokoza ndiponso mugwiritsa ntchito malemba, mawu anu azikhala olondola.

Tsimikizani Zochokera ku Magwero Ena Kuti N’zolondola. Zochitika za tsiku ndi tsiku, mawu ogwidwa, ndi zokumana nazo zingakhale zothandiza pamene mukupereka chitsanzo kapena pofotokoza mfundo zina. Koma mungatsimikize bwanji kuti zimenezo n’zolondola? Njira imodzi ndiyo kutenga zimenezi ku magwero odalirika. Kumbukirani kutsimikizira kuti zinthuzo n’zatsopano. Ziŵerengero zimasintha; zofufuza za asayansi zimakhala zakale mofulumira; ndipo pamene akatswiri akudziŵiradziŵira zochuluka za zochitika ndi zinenero zamakedzana, maganizo awo ochokera pa zimene ankadziŵa kale amasintha. Samalani kwambiri ngati mukufuna kugwiritsa ntchito nkhani za m’nyuzipepala, za pawailesi yakanema, wailesi yamawu, makalata otumiza pakompyuta, kapena za pa Intaneti. Miyambo 14:15 imalangiza kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” Dzifunseni kuti: ‘Kodi gwero limeneli n’lodziŵika kuti limanena zoona? Kodi pali njira zina zotsimikizira mfundoyi?’ Ngati mukuikayikira, isiyeni musaigwiritse ntchito.

Kuwonjezera pa kutsimikizira ngati gwero ndi lodalirika, lingaliraninso mosamala mmene mukufunira kugwiritsa ntchito mfundoyo. Onetsetsani kuti mawu ogwidwa ndiponso ziŵerengero zimene mukugwiritsa ntchito zikugwirizana ndi gwero lake, kumene mwazitenga. Pofuna kutsindika mfundo yanu, samalani kuti mawu akuti “anthu ena” asamakhale “anthu ambiri,” “anthu ambiri” asamakhale “anthu onse,” ndi “nthaŵi zina” zisamakhale “nthaŵi zonse.” Kukokomeza kapena kusinjirira malipoti okhudza ziŵerengero, ukulu wa chinthu, kapena kuopsa kwa chinthu kumachititsa anthu kuyamba kukayikira zimene mukunena.

Ngati munena zoona zokhazokha, mudzadziŵika monga munthu wolemekeza choonadi. Zimenezi zimapereka chithunzi chabwino cha Mboni za Yehova monga gulu. Chofunika koposa, zimalemekeza “Yehova, Mulungu wa choonadi.”—Sal. 31:5.

MMENE MUNGACHITIRE ZIMENEZO

  • Musaumirizike kupereka yankho pamene muli wosatsimikiza.

  • Mawu anu azikike pa “mawu a moyo” a m’Baibulo.

  • Fufuzani nkhani yanu.

  • Tsimikizani kuti ziŵerengero, mawu ogwidwa, ndi zochitika, n’zolondola ndipo zigwiritseni ntchito mosakokomeza. Peŵani kuyerekeza zinthu zimene simukumbukira bwinobwino.

ZOCHITA: Pemphani Mboni yodziŵa zambiri kuti imvetsere ndi kuona ngati zimene mukunena n’zoona pamene mukufotokoza zotsatirazi m’mawu anuanu: (1) Kodi Yehova ndi Mulungu wa mtundu wanji, ndipo mukudziŵa bwanji zimenezo? (2) Kodi Yesu anaperekeranji moyo wake monga nsembe, ndipo tingapindule motani ndi nsembeyo? (3) Kodi Yesu Kristu wakhala akuchitanji chim’khazikitsire ngati Mfumu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena