PHUNZIRO 43
Kukamba Mfundo za M’nkhani Imene Mwapatsidwa
BAIBULO limafanizira mpingo wachikristu ndi thupi la munthu. Chiwalo chilichonse n’chofunika, koma sikuti ‘zonsezo zili nayo ntchito imodzimodzi’ ayi. Choncho ifenso tiyenera kuchita udindo uliwonse umene tapatsidwa. Zimenezi zimatanthauza kuti tiyenera kumvetsa ndi kukamba bwino nkhani iliyonse imene atipatsa. Tisaone nkhani zina kukhala zosafunikira kwenikweni chifukwa tikuganiza kuti pali nkhani zina zimene zingakhale zokondweretsa kwambiri. (Aroma 12:4-8) Gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lili ndi udindo wogaŵira chakudya chauzimu “panthaŵi yake.” (Mat. 24:45) Pamene tigwiritsa ntchito luso lathu kukamba nkhani malinga ndi malangizo amene talandira, timasonyeza kuyamikira dongosolo limenelo. Zimenezi zimathandiza kuti mpingo wonse uziyenda bwino.
Zoyenera Kukamba. Ngati mwapatsidwa nkhani m’sukulu, onetsetsani kuti mukukamba mfundo za nkhani imeneyo osatinso zina zosiyana. Nthaŵi zambiri, adzakuuzani nkhani yotengamo mfundo zanu. Ngati sanakuuzeni nkhani yosindikizidwa yoti mutengemo mfundo zokambira nkhani yanu, sankhani nokha gwero lopezako mfundozo. Komabe, pamene mukukonzekera nkhani yanu, tsimikizirani kuti mfundo zanu zonse zikugwirizana ndi nkhani imene akupatsani. Posankha zoyenera kulankhula, ganiziraninso omvera anu.
Ŵerengani mosamala nkhani zina zimene alozako, ndi kupenda malemba opezeka mmenemo. Ndiyeno onani mmene mungazifotokozere kuti mupindulitse omvera. Sankhani mfundo zazikulu ziŵiri kapena zitatu m’nkhani yosindikizidwayo zimene mungagwiritse ntchito m’nkhani yanu. Mofananamo, sankhani pankhani imene mwapatsidwayo malemba amene mungaŵerenge ndi kuwafotokoza.
Kodi muyenera kufotokoza mfundo zochuluka motani? Zokhazo zimene mungafotokoze mogwira mtima. Musanyalanyaze luso la kuphunzitsa kungoti mufotokoze mfundo zambiri. Ngati mfundo zina sizikugwirizana ndi cholinga cha nkhani yanu, tsatirani mfundo zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa cholingacho. Pankhani imene mwapatsidwa, fotokozani mfundo zimene omvera angaphunzirepo kanthu ndi kupindula nazo. Cholinga chanu pa mfundo yolangizira imeneyi, sindicho kuona kuchuluka kwa mfundo zimene mungafotokoze, koma kukamba zimene mwapatsidwa ngati maziko a nkhani yanu.
Nkhani yanu isangokhala chidule cha nkhani yosindikizidwa imene akulozerani kuti mutengeko mfundo zanu. Konzekerani kufotokoza mfundo zina mwatsatanetsatane, perekani mafanizo, ndipo ngati n’kotheka perekani chitsanzo cha mmene tingazigwiritsire ntchito. Gwiritsani ntchito mfundo zina pofotokoza mfundo zofunika kwambiri zimene mwapatsidwa m’malo mozisiya n’kutenga za kwina.
Abale okhala ndi luso lophunzitsa m’kupita kwa nthaŵi angapatsidwe mwayi wophunzitsa pa Msonkhano wa Utumiki. Iwo amazindikira kufunika kolankhula mfundo zoperekedwa m’malo motenga za kwina. Mofananamo, abale omwe amakamba nkhani za onse amapatsidwa autilaini yoti atsatire. Maautilaini ameneŵa amapereka ufulu wosankhapo mfundo, komanso amasonyeza bwino lomwe mfundo zazikulu zofunika kufotokoza, zifukwa zake, ndi malemba opereka maziko a nkhaniyo. Kudziŵa kuphunzitsa mwa kugwiritsa ntchito mfundo zochokera m’nkhani imene mwapatsidwa monga maziko a nkhani yanu ndi mbali yofunika kwambiri yokonzekera mwayi wodzakamba nkhani zokulirapo.
Kuphunzira luso limeneli kungakuthandizeninso kuchititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo. Mungaphunzire kuika maganizo pa mfundo zophunziridwa m’malo mochoka pa nkhaniyo ndi kuyamba kufotokoza zinthu zina zimene zingakhale zosangalatsa koma zosathandiza kwenikweni kumveketsa nkhani yanu. Komanso, ngati mwamvetsa bwino cholinga cha phunziroli, simudzangomamatira pa mfundozo moti n’kulephera kuwonjezapo malongosoledwe ena amene angathandize wophunzirayo.