PHUNZIRO 51
Kusunga Nthaŵi ndi Kuigaŵa Bwino
NGAKHALE kuti muyenera kusamala kwambiri luso la kuphunzitsa, kusunga nthaŵi ya nkhani zanu n’kofunikanso. Misonkhano yathu imakonzedwa kuti iziyamba ndi kutha panthaŵi yoikika. Kuti zimenezi zitheke zimadalira aliyense wokhala ndi mbali pamsonkhano kusunga nthaŵi yake.
M’masiku otchulidwa m’Baibulo, anthu moyo anali kuuona mosiyana ndi mmene zilili m’mayiko ambiri lerolino. Potchula nthaŵi, anthu ankangoti “dzuŵa litakwera” kapena “monga ola lakhumi.” (Mat. 20:3-6; Yoh. 1:39) Panalibe chifukwa chodera nkhaŵa za nthaŵi yeniyeni yochitira zinthu za tsiku ndi tsiku. Lerolinonso, ndi mmene zinthu zilili m’madera ena a dziko.
Komabe, ngakhale kuti chikhalidwe cha anthu kapena chizoloŵezi cha munthu chingachititse anthu ena kusasamala kwenikweni za nthaŵi, tingapindule tikadziŵa kuisamala bwino. Pamene anthu angapo apatsidwa mbali pa pulogalamu, m’pofunika kusamala nthaŵi yoperekedwa pa mbali iliyonse. Mfundo yakuti “zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka” imagwiranso ntchito pa kusunga nthaŵi ya magawo athu pamsonkhano.—1 Akor. 14:40.
Kusunga Nthaŵi. Chinsinsi chake ndi kukonzekera. Kaŵirikaŵiri, okamba nkhani amene ali ndi vuto la kusasunga nthaŵi, chimakhala chifukwa cha kusakonzekera mokwanira. Ena amadzidalira kwambiri. Kapena amakonzekera nthaŵi itatha kale. Kusunga nthaŵi kumayamba ndi kuyamikira mwayi wopatsidwa nkhaniyo ndi kukhala ndi mtima wofuna kukonzekera bwino.
Kodi mwapatsidwa mbali ya kuŵerenga? Choyamba, ŵerengani Maphunziro 4 mpaka 7, amene amafotokoza za kulankhula mosadodoma, kupuma, kumveketsa ganizo, ndi kugogomeza mfundo zazikulu. Ndiyeno, tsatirani malangizo amenewo pamene mukuŵerenga mokweza mbali imene mwapatsidwa. Yesani nthaŵi. Kodi muyenera kuŵerenga mofulumirirapo kuti musunge nthaŵi imene mwapatsidwa? Fulumirani poŵerenga mfundo zing’onozing’ono, koma muzipumira ndi kudekherapo pogogomeza mfundo zofunika kwambiri. Yesezani mobwerezabwereza. Pamene muyamba kuŵerenga mosadodoma, kumakhala kosavuta kulinganiza nthaŵi.
Kodi muzilankhula kuchokera pa manotsi? Pofuna kusunga nthaŵi simufunikira kuchita kulemba manotsi ambiri—ngati kuti ndi nkhani yoŵerenga. Phunziro 25 linakuphunzitsani njira yabwino. Kumbukirani mfundo zisanu izi: (1) Konzekerani mfundo zoyenerera, koma zisachuluke kwambiri. (2) Khalani ndi mfundo zazikulu zoonekera bwino m’maganizo mwanu, koma musachite kuloŵeza pamtima masentensi athunthu. (3) Lembani pa autilaini yanu nthaŵi imene mwagaŵira chigawo chilichonse cha nkhani yanu, kapena nthaŵi imene iyenera kutha pofika pa mfundo zakutizakuti. (4) Pokonzekera, onani mfundo zimene mungasiye poona kuti nthaŵi ikukuthaŵani. (5) Yesezani kuikamba nkhani yonseyo.
Kuyeseza n’kofunika. Pamene mukuyeseza, samalani nthaŵi ya chigawo chilichonse cha nkhani yanu. Bwerezani nkhani yonseyo kangapo konse kufikira mutakwanitsa kuikamba m’nthaŵi yoperekedwayo. Musayese kukanikiziramo mfundo zambirimbiri. Siyani mpata wa nthaŵi chifukwa kukamba nkhani pamaso pa anthu kumatenga nthaŵi yambiri kuposa pamene mukuyeseza panokha.
Gaŵani Nthaŵi Malinga ndi Zigawo za Nkhani. Kusunga nthaŵi kumayendera limodzi ndi kuigaŵa nthaŵiyo malinga ndi zigawo za nkhani. Nthaŵi yaikulu iyenera kuthera pa kukamba thunthu la nkhani. Thunthu la nkhani n’limene limakhala ndi mfundo zazikulu za malangizo. Mawu oyamba ayenera kukhala achidule okwaniritsa zolinga zitatu zofotokozedwa m’Phunziro 38. Komabe, thunthulo lisakhale lalitali kwambiri moti n’kusoŵa nthaŵi yokamba mawu omaliza ogwira mtima, malinga n’kunena kwa Phunziro 39.
Pochita khama la kusunga nthaŵi, mudzakhoza kumakamba nkhani zabwino kwambiri komanso mudzasonyeza ulemu kwa anzanu amene ali ndi mbali zawo pa pulogalamuyo. Mudzasonyezanso ulemu ku mpingo wonse.