Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wt mutu 3 tsamba 23-31
  • Gwiritsitsani Mawu a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gwiritsitsani Mawu a Mulungu
  • Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Thandizani Ena Kulimvetsetsa
  • Kuŵerenga Baibulo Patokha
  • Cholinga Chathu
  • Gwirani Zolimba pa Mawu a Mulungu
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuŵerenga Baibulo—N’kopindulitsa ndi Kosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Baibulo—Buku Loyenera Kuŵerengedwa
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Lambirani Mulungu Woona Yekha
wt mutu 3 tsamba 23-31

Mutu 3

Gwiritsitsani Mawu a Mulungu

“MUDZIŴA m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu.” (Yoswa 23:14-16) Izi ndi zimene Yoswa anauza akuluakulu a Israyeli atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa. Inde, malonjezo a Yehova anakhala odalirikadi. Nkhani imeneyi, ndiponso zina zonse zimene zili m’Baibulo, zinasungidwa kuti ife “tikhale ndi chiyembekezo.”—Aroma 15:4.

2 Ngakhale kuti polemba Baibulo anagwiritsa ntchito anthu 40, Yehova mwiniyo ndiye Mlembi wake. Kodi izi zikutanthauza kuti anachitadi kutsogolera zonse zimene zinalembedwamo? Inde. Anachita zimenezi mwa kugwiritsa ntchito mzimu wake woyera wamphamvuwo, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito. Molondola mtumwi Paulo anati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu . . . kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” Anthu onse amene amakhutira ndi zimenezi amalabadira zomwe Baibulo limanena ndipo pamoyo wawo amatsata zimene zili m’Baibulozo.—2 Timoteo 3:16, 17; 1 Atesalonika 2:13.

Thandizani Ena Kulimvetsetsa

3 Ena amene timalankhula nawo sakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Kodi tingawathandize bwanji? Kaŵirikaŵiri njira yabwino ndi kutsegula Baibulo n’kuwasonyeza zimene limanena. “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) “Mawu a Mulungu” sali ngati imene tingati mbiri yakufa; iwo ndi amoyo! Malonjezo a Baibulo amakwaniritsidwa mosaletseka. Uthenga wa Baibulo umakhudza kwambiri mtima wa munthu ndi kumulimbikitsa kuchitapo kanthu kuposa mawu alionse amene tinganene ifeyo.

4 Kuona dzina la Mulungu m’Baibulo kwachititsa ena kuzama nalo Baibulo. Ena aganiza zophunzira Baibulo atasonyezedwa zimene limanena zokhudza cholinga cha moyo, chifukwa chake Mulungu walola kuipa, zomwe zochitika za masiku ano zimatanthauza, kapena chiyembekezo chokhala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi la paradaiso. M’mayiko amene miyambo ya chipembedzo yachititsa anthu kuvutika ndi mizimu yoipa, ena achita chidwi ndi mmene Baibulo limafotokozera chomwe chimachititsa zimenezi ndiponso mmene munthu angamasukire ku mizimuyo. N’chifukwa chiyani mfundo zimenezi zimapatsa chidwi anthu oona mtima? Chifukwa chakuti Baibulo ndilo buku lokhalo limene limanena zodalirika pa nkhani zofunika zonsezo.—Salmo 119:130.

5 Komabe, bwanji nanga anthu akatiuza kuti sakhulupirira Baibulo? Kodi tiyenera kulekera pomwepo kukambirana nawo? Sitiyenera kuleka ngati iwo akufuna kuganiziranso nkhaniyo. Mwina iwo amati Baibulo ndi buku la Matchalitchi Achikristu. Mbiri ya Matchalitchi Achikristu yochita zachinyengo ndi kuloŵerera m’zandale, ndiponso kupemphetsa ndalama nthaŵi zonse, ingawachititse kusafuna kumva za Baibulo. Bwanji osafunsa ngati zimenezi n’zimene salifunira? Ataona kuti Baibulo limatsutsa njira za dziko zimene Matchalitchi Achikristu amatsatira ndiponso mfundo zosiyanitsa Matchalitchi Achikristu ndi Chikristu choona, angakhale ndi chidwi.—Mika 3:11, 12; Mateyu 15:7-9; Yakobo 4:4.

6 Kwa ena, kukambirana mwachindunji umboni wakuti Baibulo ndi louziridwa ndi Mulungu kungakhale kothandiza. Kodi n’chiyani chimakutsimikizirani bwino inuyo kuti Baibulo linachokera kwa Yehova Mulungu? Kodi ndi zomwe Baibulo lenilenilo limafotokoza zokhudza chiyambi chake? Kapena n’chifukwa chakuti Baibulo lili ndi maulosi ambirimbiri omwe amaonetsa kuti mwini wake amadziŵa mwatsatanetsatane za m’tsogolo, maulosi amene ayenera kuti anaperekedwa ndi wina woposa anthu? (2 Petro 1:20, 21) Kapena kodi n’chifukwa chakuti mabuku onse a m’Baibulo ndi ogwirizana modabwitsa pa nkhani imodzi, ngakhale kuti analembedwa ndi amuna 40 panyengo ya zaka ngati 1,600? Kapena popeza n’lolondola pa nkhani za sayansi kusiyana ndi mabuku ena amene analembedwa nthaŵi imeneyo? Kapena n’chifukwa chakuti olemba ake analemba mosabisa kalikonse? Kapena n’chifukwa chakuti lasungikabe ngakhale kuti anthu ena anali ndi maganizo oipa akuti aliwononge? Mfundo iliyonse imene inuyo imakuchititsani chidwi mungaigwiritse ntchito kuthandizira ena.a

Kuŵerenga Baibulo Patokha

7 Kuwonjezera pa kuthandiza ena kukhulupirira Baibulo, ifeyo tiyenera kukhala ndi nthaŵi yoliŵerenga mokhazikika. Kodi mukuchita zimenezo? Pa mabuku onse amene afalitsidwapo, limeneli ndilo buku lofunika kwambiri. Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti ngati tiŵerenga Baibulo patokha, ndiye kuti basi sitifunikiranso zina. Malemba amatichenjeza kuti tisadzipatule. Tisaganize kuti tikhoza kudziŵa zonse mwa kufufuza kwathu kokha. Kuti tikhale Akristu olingalira mwanzeru, tifunika kuphunzira patokha ndiponso kufika nthaŵi zonse pa misonkhano ya anthu a Mulungu.—Miyambo 18:1; Ahebri 10:24, 25.

8 Pankhaniyi, Baibulo limasimba za mdindo wa ku Aitiopiya amene anali kuŵerenga ulosi wa Yesaya. Mngelo anatsogolera mlaliki wachikristu Filipo kuti akafunse munthuyo kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” Modzichepetsa Mwaitiopiyayo anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Iye anapempha Filipo kuti amulongosolere chigawo cha Malemba chimenecho. Eya, Filipo sanali munthu wongoŵerenga Baibulo payekha n’kumafotokoza maganizo akeake pa Malemba. Anali kuchita zinthu mogwirizana kwambiri ndi gulu looneka la Mulungu. Motero anatha kuthandiza Mwaitiopiyayo kupindula ndi malangizo amene Yehova anali kupereka mwa gulu limenelo. (Machitidwe 6:5, 6; 8:5, 26-35) N’chimodzimodzinso lerolino, palibe amene payekha amafika pomvetsetsa bwino zolinga za Yehova. Tonse timafunika thandizo limene Yehova akupereka mwachikondi kupyolera mwa gulu lake looneka.

9 Potithandiza kumvetsetsa Baibulo, gulu la Yehova limatipatsa nkhani za m’Malemba zabwino kwambiri m’mabuku osiyanasiyana. Ndiponso, nthaŵi zonse limatikonzera ndandanda yoŵerenga Baibulo mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imene imachitika m’mipingo yonse ya Mboni za Yehova padziko lonse. Tingapeze phindu lalikulu pamene ifeyo patokha tipenda zimene zili m’Malemba Opatulika. (Salmo 1:1-3; 19:7, 8) Chitani khama mwapadera kuti muziŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. Ngakhale musamvetsetse zonse zimene mwaŵerenga, kudziŵa kwanu zina ndi zina m’Malemba kudzakuthandizanibe kwambiri. Mwachitsanzo, mutati muziŵerenga masamba anayi kapena asanu okha patsiku, mukhoza kumaliza Baibulo lonse chaka chimodzi.

10 Kodi ndi liti pamene mukhoza kumaŵerenga Baibulo? Ngati mulinganiza zoti muziliŵerenga ngakhale mphindi 10 kapena 15 patsiku, mudzapindula kwambiri. Ngati simungathe zimenezi, musalephere mlungu uliwonse kukhala ndi nthaŵi yeniyeni yoti muziŵerenga, ndiyeno tsatirani ndandanda imeneyo nthaŵi zonse. Ngati muli pabanja, inu ndi mnzanu mungasangalale kuŵerengera Baibulo pamodzi mokweza. Ngati m’banja lanulo muli ana odziŵa kuŵerenga, angamasinthanesinthane kuŵerenga mokweza. Kuŵerenga Baibulo kuyenera kukhala chizoloŵezi cha moyo wonse, mofanana ndi kudya chakudya. Monga mudziŵa, ngati munthu sadya mokwanira, sakhala ndi thanzi labwino. N’chimodzimodzinso moyo wathu wauzimu, ndiponso moyo wathu wamuyaya, umadalira kuti tizidya nthaŵi zonse “mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.”—Mateyu 4:4.

Cholinga Chathu

11 Kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chiyani poŵerenga Baibulo? Chisangokhala chakuti tiŵerenge masamba angapo basi. Cholinga chathu chiyenera kukhala kufuna kumudziŵa bwino Mulungu kuti tizimukonda kwambiri ndi kumulambira movomerezeka. (Yohane 5:39-42) Tikhale ndi mtima ngati umene anali nawo wolemba Baibulo wina amene anati: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.”—Salmo 25:4.

12 Pamene Yehova akutiphunzitsa, tiyenera kukhala n’chikhumbo chofuna ‘kudziŵa zinthu molondola.’ Popanda kutero, kodi tingathe bwanji kugwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu pa moyo wathu kapenanso kuwalongosola molondola kwa ena? (Akolose 3:10, NW; 2 Timoteo 2:15) Pamafunika kuŵerenga mosamalitsa kuti tidziŵe zinthu molondola, ndipo ngati ndimeyo ili yovuta kuimvetsa, tingafunike kuŵerenga kangapo kuti tizindikire mfundo yake yeniyeni. Tidzapindulanso ngati tikhala ndi nthaŵi yosinkhasinkha nkhani taŵerengayo, kuganizira mbali zake zosiyanasiyana. Njira zopindulitsa zinayi zomwe tingagwiritse ntchito posinkhasinkha zasonyezedwa patsamba 30. Ndime zambiri za Malemba zikhoza kupendedwa mopindulitsa mwa kugwiritsa ntchito mfundo imodzi kapena zingapo mwa zimenezi. Pamene mukuyankha mafunso amene ali pamasamba otsatiraŵa, mudzaona kuti zimenezi n’zoona.

(1) Nthaŵi zambiri, ndime ya Malemba imene mukuŵerenga ingakuuzeni chinachake chokhudza umunthu wa Yehova. Mwachitsanzo, pa Salmo 139:13, 14, timaphunzira za chidwi chachikulu chimene Mulungu amakhala nacho pa ana osabadwa. Lembali limati: “Munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu n’zodabwiza; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.” Zimene Yehova analenga n’zodabwitsatu kwambiri! Chipangidwe cha anthu ndi umboni wakuti amatikonda kwambiri.

Mwa zimene zikunenedwa pa Yohane 14:9, 10, tikamaŵerenga zimene Yesu anali kuchita ndi anthu ena, timaona momwe Yehova mwiniyo akanachitira. Polingalira zimenezi, kodi tinganenenji za Yehova mwa zochitika zimene zinalembedwa pa Luka 5:12, 13 ndi Luka 7:11-15?

(2) Lingalirani momwe nkhaniyo ikugwirizirana ndi mfundo yaikulu ya m’Baibulo lonse ya: kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndi kuyeretsedwa kwa dzina lake mwa Ufumu umene Yesu Kristu, Mbewu yolonjezedwayo, ndiye wolamulira wake.

Kodi mfundo yaikulu ya m’Baibulo lonse anaitsindika motani Ezekieli ndi Danieli? (Ezekieli 38:21-23; Danieli 2:44; 4:17; 7:9-14)

Kodi Baibulo limaonetsa motani kuti Yesu ndiyedi Mbewu yolonjezedwa? (Agalatiya 3:16)

Kodi Chivumbulutso chimalongosolanji kusonyeza kuti nkhani ya Ufumu yafika pachimake? (Chivumbulutso 11:15; 12:7-10; 17:16-18; 19:11-16; 20:1-3; 21:1-5)

(3) Dzifunseni mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuŵerengazo pamoyo wanu. Mwachitsanzo, timaŵerenga mu Eksodo mpaka Deuteronomo za makhalidwe oipa a Aisrayeli ndi kupandukira kwawo. Timaphunzira kuti maganizo ndi zochita zawozo zinawadzetsera tsoka. Choncho zitilimbikitse kuchita zokondweretsa Yehova mwa kusatengera chitsanzo choipa cha Aisrayeli. “Izi zinachitika kwa iwoŵa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.”—1 Akorinto 10:11.

Kodi nkhani yakuti Kaini anapha Abele imatiphunzitsanji? (Genesis 4:3-12; Ahebri 11:4; 1 Yohane 3:10-15; 4:20, 21)

Kodi uphungu umene Baibulo limapereka kwa Akristu oyembekeza kupita kumwamba umagwiranso ntchito kwa amene akuyembekeza kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi? (Numeri 15:16; Yohane 10:16)

Ngakhale kuti mbiri yathu mu mpingo wachikristu ndi yabwino, n’chifukwa chiyani tiyenera kulingalira za mmene tingagwiritsire ntchito bwino kwambiri uphungu wa Baibulo umene tikuudziŵa kale? (2 Akorinto 13:5; 1 Atesalonika 4:1)

(4) Ganizirani mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuŵerenga kuti muthandize ena. Anthu onse amada nkhaŵa ndi nkhani za umoyo, motero tikhoza kuŵerenga nawo zimene Yesu anachita kuti tiwasonyeze zomwe adzachita pamlingo wokulirapo pamene adzagwiritsa ntchito mphamvu za Ufumu: “Makamu ambiri a anthu anadza kwa iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, . . . ndipo iye anawachiritsa.”—Mateyu 15:30.

Kodi ndani amene tingamuthandize ndi nkhani ya kuukitsidwa kwa mwana wamkazi wa Yairo? (Luka 8:41, 42, 49-56)

13 Kuŵerenga Baibulo kumakhala kwaphindu kwambiri ngati poŵerenga tilingalira mfundo zinayi zimene tatchulazo. Zoonadi, kuŵerenga Baibulo n’kovuta. Koma tikhoza kupindula moyo wathu wonse, chifukwa pamene tikuŵerenga Malemba timalimba mwauzimu. Chifukwa choŵerenga Baibulo nthaŵi zonse tidzayandikira kwa Atate wathu wachikondi, Yehova, ndiponso kwa abale athu achikristu. Tidzatha kulabadira uphungu woti tigwiritsitse “mawu a moyo.”—Afilipi 2:16.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze mfundo zonena za chifukwa chake tiyenera kukambirana za Baibulo, onani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Bwerezani Zimene Mwakambirana

• N’chifukwa chiyani Baibulo linalembedwa ndi kusungidwa mpaka masiku athu ano?

• Kodi tingawathandize bwanji ena kumvetsetsa Baibulo?

• N’chifukwa chiyani kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse patokha kuli kopindulitsa? Ngati tikufuna kupenda zimene tikuŵerenga moti n’kupindula nazo, tifunika kugwiritsa ntchito mfundo zinayi ziti?

[Mafunso]

1. (a) Kodi Aisrayeli akale anaona motani kuti mawu a Mulungu alidi oona? (b) N’chifukwa chiyani zimenezi zimatichititsa chidwi?

2. (a) Kodi Baibulo “adaliuzira Mulungu” mu lingaliro lotani? (b) Kodi tili ndi udindo wotani podziŵa kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu?

3. Kodi njira yabwino ndi iti yothandizira amene sakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu?

4. Kodi ndi kufotokoza choonadi cha Baibulo kotani kumene kwasintha mmene anthu ena amaonera Baibulo, ndipo n’chifukwa chiyani?

5. (a) Anthu akamati sakhulupirira Baibulo, kodi chingakhale chifukwa chiyani? (b) Kodi anthu oterowo tingawathandize motani?

6. (a) Kodi n’chiyani chimene inuyo chimakukhutiritsani kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu? (b) Kodi ndi mfundo zina ziti zimene zingagwiritsidwe ntchito kuthandiza anthu kumvetsetsa kuti Baibulo n’lochokeradi kwa Mulungu?

7, 8. (a) Kodi tiyenera kuchitanji ndi Baibulo? (b) Kodi tifunikanji kuwonjezera pa kuŵerenga Baibulo patokha? (c) Kodi inuyo mwachita zotani kuti mumvetsetse zolinga za Yehova?

9. Kodi ndi ndondomeko yotani yoŵerenga Baibulo imene ingapindulitse tonsefe?

10. (a) Kodi inuyo mumaŵerenga liti Baibulo? (b) Ndani ena amene tiyenera kuŵerenga nawo limodzi Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani kuŵerenga nthaŵi zonse n’kofunika?

11. Kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chiyani poŵerenga Baibulo?

12. (a) Kodi n’chifukwa chiyani ‘kudziŵa zinthu molondola’ n’kofunika, nanga ndi khama lotani limene lingafunike poŵerenga kuti munthu adziŵe zinthu moteromo? (b) Kodi zimene timaŵerenga m’Baibulo tingazipende mopindulitsa mwa kugwiritsa ntchito mfundo zinayi ziti? (Onani bokosi patsamba 30.) (c) Sonyezani mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimenezi mwa kuyankha mafunso amene ali m’ndime ino. Ŵerengani m’Baibulo malemba amene asonyezedwa koma sanagwidwe mawu.

13. Kodi tingayembekezere zotani ngati tipitiriza kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo ndi gulu la Yehova?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 30]

MUKAŴERENGA NDIME INA M’BAIBULO, LINGALIRANI IZI

Zimene ndimeyo ikukuuzani za umunthu wa Yehova

Mmene ikugwirizirana ndi mfundo yaikulu ya m’Baibulo lonse

Mmene iyenera kukhudzira moyo wanu inuyo

Mmene mungaigwiritsire ntchito pothandiza ena

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena