Mutu 9
Mphamvu ya Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa
KODI munatayikidwa okondedwa anu? Popanda kuyembekezera kuti akufa adzauka, sitikanalingalira zodzawaonanso. Akanakhalabe monga mmene Baibulo limafotokozera kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi, . . . pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda uli kupitako.”—Mlaliki 9:5, 10.
2 Mwa kuukitsa akufa, Yehova wapereka mwachifundo mwayi wosaneneka kwa anthu miyandamiyanda amene anamwalira woti adzakhalenso ndi moyo wosatha. Izi zikutanthauza kuti mungakhale ndi chiyembekezo chosangalatsa chakuti tsiku lina, m’dziko latsopano la Mulungu, mudzakhalanso limodzi ndi okondedwa anu amene agona mu imfa.—Marko 5:35, 41, 42; Machitidwe 9:36-41.
3 Sitifunika kuopa imfa mosayenera chifukwa akufa adzauka. Yehova akhoza kulola Satana kuchitira atumiki ake okhulupirika chilichonse chimene angathe potsimikizira bodza lake lamkunkhuniza lakuti “munthu adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake,” koma sangalole kuti awavulaziretu. (Yobu 2:4) Yesu anali wokhulupirika kwa Mulungu mpaka kufa kwake, choncho Mulungu anamuukitsa kuti akakhale ndi moyo kumwamba. Motero Yesu anali wokhoza kupereka ku mpando wachifumu wakumwamba wa Atate wake mtengo wa nsembe yake yaumunthu yangwiro, yomwe ili ndi mphamvu yotipulumutsa. Mwa kuuka kwa akufa, a “kagulu ka nkhosa,” pokhala oloŵa ufumu limodzi ndi Kristu, ali ndi chiyembekezo chokakhala limodzi naye mu Ufumu wakumwamba. (Luka 12:32) Kwa ena, pali chiyembekezo choukitsidwa kuti akhale ndi moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. (Salmo 37:11, 29) Akristu onse amaona kuti kuyembekezera kuti akufa adzauka kumawapatsa mphamvu ‘kuposa zachibadwa’ pamene akukumana ndi mayesero omwe angawataitse moyo.—2 Akorinto 4:7.
Chifukwa Chake N’kofunika Kwambiri pa Chikristu
4 Malinga ndi kunena kwa Ahebri 6:1, 2, chiphunzitso cha kuuka kwa akufa chili “mawu a chiyambidwe.” Chili mbali ya maziko a chikhulupiriro amene popanda mazikowo sitikanakhala Akristu okhwima mwauzimu. (1 Akorinto 15:16-19) Komabe, zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya kuuka kwa akufa n’zachilendo kwa anthu ambiri. Chifukwa chosakonda zinthu zauzimu, anthu ochuluka amangoona moyo uno monga ndiwo wokha umene ulipo. Motero amangofuna zinthu zoti azisangalala nazo. Ndiyeno pali anthu omwe ali m’zipembedzo zikuluzikulu, kaya zotchedwa zachikristu kapena ayi, amene amaganiza kuti munthu ali ndi chinthu chinachake m’kati mwake chimene sichifa. Koma chikhulupiriro chimenecho n’chosagwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa za kuuka kwa akufa. Chifukwa ngati anthu ali ndi chinthu chimene sichifa chomwe chimapitiriza kukhala ndi moyo thupi likafa ndiye kuti kukanakhala kosafunika kuukitsa akufa. Kuyesa kugwirizanitsa malingaliro aŵiri ameneŵa n’kosokoneza kwambiri m’malo mopatsa munthu chidaliro. Kodi anthu ofunadi kudziŵa zoona zake tingawathandize bwanji?
5 Anthu oterowo asanamvetse kuti kuuka kwa akufa ndi makonzedwe abwino kwambiri, afunika kudziŵa molondola mmene akufa alili. Nthaŵi zambiri malemba oŵerengeka ndi okwanira kuti munthu amene ali ndi njala ya choonadi cha Baibulo amvetsetse nkhani imeneyi. (Salmo 146:3, 4; Mlaliki 9:5, 10; Machitidwe 7:60) Komabe, mabaibulo ena amakono ndiponso ena olembedwa mofotokozera, amaphimba zoona zake za mmene akufa alili. Motero n’kofunika kupenda mawu amene anagwiritsidwa ntchito mu zinenero zoyambirira za m’Baibulo.
6 M’mabaibulo ena, monga la Revised Nyanja (Union) Version, mawu a Chihebri akuti neʹphesh ndiponso mawu ofanana nawo a Chigiriki akuti psy·kheʹ amatembenuzidwa mosiyanasiyana monga kuti “munthu,” “zamoyo,” “cholengedwa,” ndi “mzimu.” Kuunika mosamalitsa mmene Baibulo lagwiritsira ntchito mawu a Chihebri ndi Chigiriki ameneŵa, kungathandize munthu wofunadi kuphunzira Baibulo kudziŵa kuti mawuŵa nthaŵi zambiri amanena za munthu wathunthu (Genesis 2:7; Machitidwe 2:43; 1 Petro 3:20) ndiponso kuti amanenanso za nyama. (Genesis 1:20, 24) Koma mawuŵa sapereka lingaliro lakuti chinthu chosakhudzika ndi chosaoneka chingathe kutuluka m’thupi pamene thupilo likufa, icho n’kukhalabe ndi moyo kwinakwake.
7 Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version limagwiritsira ntchito mawu akuti “manda” pafupifupi paliponse pamene pali mawu a Chihebri akuti sheʼohlʹ ndipo limagwiritsira ntchito mawu akuti “Hade” pamene pali mawu a Chigiriki akuti haiʹdes komanso mawu akuti “gehena” pamene pali mawu a Chigiriki akuti geʹen·na. Mawu akuti “Hade” ndi chimodzimodzi ndi kunena kuti “manda.” (Salmo 16:10; Machitidwe 2:27) Baibulo limalongosola bwino kuti ku manda ndi ku Hade ndi kwa zinthu zakufa, osati zamoyo. (Salmo 89:48; Chivumbulutso 20:13) Malemba amanenanso za chiyembekezo chakuti wakufa akhoza kubwerako ku manda mwa kuukitsidwa. (Yobu 14:13; Machitidwe 2:31) Mosiyana ndi zimenezi, palibe chiyembekezo chilichonse chakuti amene amapita ku Gehena adzakhalanso ndi moyo m’tsogolo, ndipo kumeneko sikunenedwa kuti kuli chamoyo chilichonse.—Mateyu 10:28.
8 Pamene nkhani zimenezo zalongosoledwa momveka, munthu tsopano angathandizidwe kumvetsa zimene kuuka kwa akufa kungatanthauze kwa iye. Angayambe kuyamikira kuti Yehova ndi wachikondi potikonzera zabwino zoterezi. Chisoni cha anthu amene atayikidwa okondedwa awo chingachepeko poyembekezera mwachimwemwe kudzakhalanso limodzi nawo m’dziko latsopano la Mulungu. Kumvetsa nkhaniyi n’kofunikanso kwambiri kuti tithe kumvetsa zimene imfa ya Kristu imatanthauza. Akristu oyambirira anazindikira kuti kuuka kwa Yesu Kristu n’kofunika kwambiri pa Chikristu, kuti kumatsegula njira yakuti anthu enanso akaukitsidwe. Iwo analalikira mwachangu za kuuka kwa Yesu komanso chiyembekezo chimene anthu amakhala nacho chifukwa cha kuukako. Lerolinonso anthu amene amamvetsa ndi kuyamikira kuti akufa adzauka amauza ena ndi mtima wonse choonadi chokoma chimenechi.—Machitidwe 5:30-32; 10:42, 43.
Kugwiritsira Ntchito ‘Chofungulira cha Hade’
9 Onse amene adzakhala ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba ayenera kufa m’kupita kwa nthaŵi. Koma iwo amadziŵa bwino zimene iye anawatsimikizira pamene anati: “Ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthaŵi za nthaŵi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi Hade.” (Chivumbulutso 1:18) Kodi anatanthauzanji? Anali kunena zimene zinamuchitikira iyeyo. Iyenso anafa. Koma Mulungu sanamusiye mu Hade. Patsiku lachitatu, Yehova mwiniyo anamuukitsa iye n’kumupatsa moyo wauzimu ndi wosafa. (Machitidwe 2:32, 33; 10:40) Ndiponso, Mulungu anamupatsa “zofungulira za imfa ndi Hade” kuti azigwiritsire ntchito potulutsa ena kumanda ndi kuwamasula ku zotsatirapo za kuchimwa kwa Adamu. Popeza kuti Yesu ali ndi zofungulira zimenezo, iye akhoza kuukitsa otsatira ake okhulupirika amene anamwalira. Choyamba iye akuukitsa anthu odzozedwa a mu mpingo wake. Ameneŵa akuwapatsa mphatso yabwino kwambiri yokhala ndi moyo wosafa kumwamba, monga mmene Atate ake anam’patsira iye.—Aroma 6:5; Afilipi 3:20, 21.
10 Kodi ndi liti pamene Akristu odzozedwa okhulupirika akuukitsidwira kumwamba? Baibulo limaonetsa kuti kuuka kumeneku kunayamba kale. Mtumwi Paulo analongosola kuti iwo akaukitsidwa panthaŵi ya ‘kukhalapo kwa Kristu,’ kumene kunayamba m’chaka cha 1914. (1 Akorinto 15:23, NW) Akristu odzozedwa okhulupirika akamwalira masiku anoŵa a kukhalapo kwake kwa Kristu, safunika kukhalabe akufa mpaka kubweranso kwa Ambuye wawo. Akangomwalira amaukitsidwa mu mzimu, ‘amasandulika, m’kamphindi, m’kutwanima kwa diso.’ Amakhalatu osangalala kwambiri chifukwa ntchito zabwino zimene anachita ‘zimatsatana nawo pamodzi.’—1 Akorinto 15:51, 52; Chivumbulutso 14:13.
11 Koma oloŵa Ufumu amene akuukitsidwa kuti akakhale ndi moyo kumwamba sindiwo okha omwe adzaukitsidwa. Popeza kuti kuuka kwawo kukutchedwa kuti “kuuka koyamba” pa Chivumbulutso 20:6, ndiye kuti payenera kukhala kuuka kwinanso. Amene adzauka pa kuuka kotsatiraku adzasangalala kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso. Kodi zimenezi zidzachitika liti? Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti zidzachitika pambuyo pa kuchoka kwa “dziko ndi m’mwamba,” ndiko kuti dziko loipa lilipoli limodzi ndi olamulira ake. Kutha kumeneko kwa dziko lakaleli kwayandikira zedi. Pambuyo pa zimenezi, pa nthaŵi yake ya Mulungu, anthu odzakhala padziko lapansi adzayamba kuuka.—Chivumbulutso 20:11, 12.
12 Kodi ndani amene adzaukitsidwa kuti akhale padziko lapansi? Ena a iwo adzakhala atumiki okhulupirika a Yehova akale kwambiri, amuna ndi akazi amene chifukwa chokhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka ‘sanalole kuomboledwa’ mwa njira ina. Ndiko kuti, sanaleke kukhala okhulupirika kwa Mulungu pofuna kupeŵa kufa mozunzika ndi mwamsanga. Zidzakhalatu zokondweretsa kwambiri kudziŵana nawo ndi kumva eni akewo akulongosola mwatsatanetsatane zochitika zimene zinalembedwa mwachidule m’Baibulo! Enanso amene adzaukitsidwa kuti adzakhale padziko lapansi ndi Abele, yemwe anali mboni yokhulupirika yoyamba ya Yehova; Enoke ndi Nowa, omwe analengeza mosaopa uthenga wochenjeza wa Mulungu Chigumula chisanachitike; Abrahamu ndi Sara, omwe anachereza angelo; Mose, yemwe analandira Chilamulo pa phiri la Sinai; aneneri olimba mtima monga Yeremiya, yemwe anaona Yerusalemu akuwonongedwa mu 607 B.C.E.; ndi Yohane Mbatizi, yemwe anamva Mulungu mwiniyo akunena kuti Yesu ndi Mwana Wake. Ndiponso, padzakhala amuna ndi akazi okhulupirika ambiri amene anafa m’masiku otsiriza ano a dziko loipali.—Ahebri 11:4-38; Mateyu 11:11.
13 M’nthaŵi yake, anthu ena kuwonjezera pa atumiki okhulupirika a Mulungu adzaukitsidwanso, ndipo m’manda simudzatsala aliyense. Tingadziŵe kuti m’manda mudzachotsedwa akufa onse mwa kuona mmene Yesu adzagwiritsira ntchito ‘chofungulira cha Hade’ pothandiza anthu. Zimenezi zikusonyezedwa m’masomphenya amene anamuonetsa mtumwi Yohane. Iye anaona Hade ‘akuponyedwa m’nyanja yamoto.’ (Chivumbulutso 20:14) Kodi zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti Hade, manda a anthu, akuwonongedwa popanda chotsalako. Palibenso manda pena paliponse, akufa onse achotsedwamo, chifukwa kuwonjezera pa kuukitsa olambira okhulupirika onse a Yehova, mwachifundo Yesu adzaukitsanso osalungama. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15.
14 Palibe aliyense wa osalungama ameneŵa yemwe akuukitsidwa kungoti aweruzidwe kuti ndi woyenera kufanso. M’makonzedwe olungama amene adzakhalapo pa dziko lonse mu Ufumu wa Mulungu, iwo adzathandizidwa kuchita zinthu mogwirizana ndi njira za Yehova. Masomphenyawo anasonyeza kuti ‘buku la moyo’ lidzatsegulidwa. Motero iwo adzakhala ndi mwayi woti mayina awo alembedwe m’bukulo. ‘Adzaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake’ zimene adzachite ataukitsidwa. (Chivumbulutso 20:12, 13) Motero kuchokera pa zimene adzakhala atachita potsirizira pake, kuuka kwawo kungadzakhale ‘kuuka kwa moyo’ ndipo sikudzakhala ‘kuuka kwa kuweruza [kosawakomera]’ koti sangakupeŵe.—Yohane 5:28, 29.
15 Komabe, sikuti aliyense amene anafa adzaukitsidwa. Ena anachita machimo oti n’kosatheka kuwakhululukira. Oterowo sali ku Hade koma ku Gehena kumene amawonongekeratu. Ameneŵa adzaphatikizaponso anthu amene adzaphedwa pa ‘chisautso chachikulu’ chomwe tsopano chili pafupi. (Mateyu 12:31, 32; 23:33; 24:21, 22; 25:41, 46; 2 Atesalonika 1:6-9) Motero, ngakhale kuti Yehova akuchita chifundo mwapadera potulutsa akufa mu Hade, kuyembekezera kuti akufa adzauka sikutipatsa mphamvu yoti tsopanoli tizikhala mosasamala. Amene mwakufuna kwawo amapandukira ulamuliro wa Yehova sadzaukitsidwa. Kudziŵa zimenezi kuyenera kutichititsa kusonyeza kuti timayamikira kwambiri kukoma mtima kwa Mulungu mwa kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake.
Kulimbikitsidwa ndi Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa
16 Ife amene timakhulupiriradi kuti akufa adzauka timalimbikitsidwa kwambiri ndi chiyembekezo chimenechi. Panopo, tikatsala pang’ono kufa, timadziŵa kuti sitingapeŵe imfa mpaka kalekale—ngakhale titagwiritsira ntchito mankhwala otani. (Mlaliki 8:8) Ngati tatumikira Yehova mokhulupirika tili m’gulu lake, tingayembekezere za m’tsogolo mtima uli m’malo. Timadziŵa kuti tidzakhalanso ndi moyo panthaŵi yake ya Mulungu chifukwa chakuti akufa adzauka. Ndipotu udzakhala moyo wabwino kwambiri! Mtumwi Paulo anautchula kuti “moyo weniweniwo.”—1 Timoteo 6:19; Ahebri 6:10-12.
17 Kudziŵa kuti akufa adzauka ndiponso kudziŵa Yemwe wakonza zimenezi kumatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Izi zimatilimbikitsa kukhala okhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene anthu otizunza akutiopseza kuti atipha. Kwanthaŵi yaitali Satana wagwiritsa ntchito kuopa kufa mwadzidzidzi kuti achititse anthu kukhala akapolo. Komatu Yesu sanaope zimenezo. Iye anali wokhulupirika kwa Yehova mpaka kufa kwake. Mwa nsembe yake ya dipo, Yesu anapereka njira yomasulira ena ku mantha oterowo.—Ahebri 2:14, 15.
18 Chifukwa chokhulupirira nsembe ya Kristu ndiponso kuuka kwa akufa, atumiki a Yehova akhala ndi mbiri yabwino yoti ndi okhulupirika. Pokumana ndi mavuto, iwo asonyeza kuti ‘sakonda moyo wawo’ kuposa mmene amakondera Yehova. (Chivumbulutso 12:11) Mwanzeru iwo saleka kutsatira mfundo zachikristu za makhalidwe abwino pofuna kupulumutsa moyo umene ali nawo panopa. (Luka 9:24, 25) Amadziŵa kuti ngakhale atamwalira panopo chifukwa cha kuchirikiza mokhulupirika ulamuliro wa Yehova, iye adzawafupa mwa kuwaukitsa kwa akufa. Kodi muli ndi chikhulupiriro choterocho? Mudzakhala nacho ngati Yehova mumamukondadi ndiponso ngati mumayamikira ndi mtima wonse zimene kuyembekezera kuti akufa adzauka kumatanthauzadi.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• N’chifukwa chiyani munthu ayenera kuyamba wamvetsa bwino mmene akufa alili asanafike poyamikira chiyembekezo cha kuuka kwa akufa?
• Kodi ndani adzauka kwa akufa, nanga kudziŵa zimenezi kuyenera kutikhudza motani?
• Kodi kuyembekezera kuti akufa adzauka kumatilimbikitsa motani?
[Mafunso]
1. Popanda chiyembekezo chakuti akufa adzauka, kodi tsogolo lawo likanakhala lotani?
2. Kodi kuuka kwa akufa kukutipatsa chiyembekezo chosangalatsa chotani?
3. (a) Kodi kuuka kwa akufa kwakhala kofunika m’njira zotani pokwaniritsa cholinga cha Yehova? (b) Kodi ndi nthaŵi iti makamaka pamene chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chimatipatsa mphamvu?
4. (a) Kodi chiphunzitso cha kuuka kwa akufa chili “mawu a chiyambidwe” m’lingaliro lotani? (b) Kodi kuuka kwa akufa kumatanthauzanji kwa anthu ambiri?
5. (a) Munthu asanamvetsetse za kuuka kwa akufa, kodi afunika kudziŵa chiyani? (b) Kodi ndi malemba ati amene mungagwiritse ntchito polongosola mmene akufa alili? (c) Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu agwiritsa ntchito Baibulo limene limaphimba choonadi?
6. Kodi kuphunzira Baibulo mosamalitsa kumasonyezanji za zimene zimachitika munthu akafa?
7. Kodi mungalongosole motani kuchokera m’Baibulo za mmene alili anthu omwe ali m’manda? m’Hade? m’Gehena?
8. Kodi kumvetsa bwino za kuuka kwa akufa kungakhudze motani maganizo a munthu ndi zochita zake?
9. Kodi Yesu poyamba akugwiritsira ntchito motani “zofungulira za imfa ndi Hade”?
10. Kodi ndi liti pamene Akristu odzozedwa okhulupirika akuukitsidwa?
11. Kodi ndi kuuka kotani kumene kudzakhalapo kwa anthu ena onse, nanga kudzayamba liti?
12. Kodi ndani ena amene adzaukitsidwa mwa anthu okhulupirika omwe adzauka kuti akhale ndi moyo padziko lapansi, nanga n’chifukwa chiyani kuyembekezera zimenezi n’kosangalatsa?
13, 14. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikira Hade komanso akufa amene ali mmenemo? (b) Ndaninso ena amene adzaukitsidwa, nanga n’chifukwa chiyani?
15. (a) Kodi ndani amene sadzaukitsidwa? (b) Kodi kudziŵa zoona zake za kuuka kwa akufa kuyenera kutikhudza motani?
16. Kodi kuyembekezera kuti akufa adzauka kungakhale kolimbikitsa kwambiri motani?
17. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova?
18. Kodi n’chiyani chathandiza atumiki a Yehova kukhala ndi mbiri yabwino kwambiri yakuti ndi okhulupirika?
[Chithunzi pamasamba 84, 85]
Yehova akulonjeza kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama