Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lr mutu 18 tsamba 97-101
  • Kodi Umakumbukira Kunena Kuti Zikomo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Umakumbukira Kunena Kuti Zikomo?
  • Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Nkhani Yofanana
  • Wakhate Mmodzi Analemekeza Mulungu
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Pa Anthu 10 Akhate, Mmodzi Anathokoza Yesu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Akhate Khumi Achiritsidwa Mkati mwa Ulendo Wotsirizira wa Yesu Womka ku Yerusalemu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Akhate Khumi Achiritsidwa Mkati Mwa Ulendo Womaliza wa Yesu Wopita ku Yerusalemu
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
lr mutu 18 tsamba 97-101

Mutu 18

Kodi Umakumbukira Kunena Kuti Zikomo?

KODI lero wadya chakudya?— Ndani anakonza?— Mwina anakonza ndi amayi ako kapena munthu wina, koma kodi ndi chifukwa chiyani tifunika kuthokoza Mulungu chifukwa cha chakudyacho?— Ndi chifukwa chakuti Mulungu ndiye amene amakulitsa zomera zimene zimatipatsa zakudya. Komabe, tiyenera kuthokozanso amene anatikonzera chakudyacho ndi amene anatipatsira.

Nthaŵi zina timaiŵala kunena kuti zikomo anthu ena akatichitira zinthu zabwino, si choncho? Panthaŵi imene Mphunzitsi Waluso anali padziko lapansi pano, panali anthu ena odwala khate amene anaiwala kunena kuti zikomo.

Kodi munthu wakhate umamudziŵa?— Munthu wakhate ndi amene akudwala matenda otchedwa khate. Matendaŵa amafika mpaka podula ziwalo za munthu. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anthu akhate anali kukhala kutali ndi anthu ena. Ndipo panthaŵiyo wakhate akaona munthu wina akubwera, anali kukuwa kuti achenjeze munthuyo kuti asafike pafupi. Anali kuchita zimenezi pofuna kuti anthu ena asayandikire kwambiri kwa iye kuti nawonso angatengere khatelo.

Yesu anali wokoma mtima kwa anthu akhate. Tsiku lina popita ku Yerusalemu Yesu anadzera pa mudzi winawake. Atayandikira mudziwo, anthu teni akhate anabwera kuti amuone. Iwo anali atamva kuti Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zochiritsa matenda ena alionse.

Akhatewo sanafike pafupi ndi Yesu. Anaima patali ndithu. Komatu anakhulupirira kuti Yesu akhoza kuwachiritsa khate anali kudwalalo. Ndiye akhatewo ataona Mphunzitsi Walusoyo, anafuula kuti: ‘Yesu, Mphunzitsi, tithandizeni!’

Kodi iwe anthu amene akudwala amakumvetsa chisoni?— Yesu anamva nawo chisoni. Anadziŵa kuti munthu wakhate amavutika kwambiri. Choncho anawayankha kuti: ‘Pitani mukadzionetse kwa ansembe.’—Luka 17:11-14.

Akhate 10 akupempha Yesu kuti awachiritse

Kodi akhate aŵa Yesu akuwauza kuti achite chiyani?

N’chifukwa chiyani Yesu anawauza kuchita zimenezi? Chinali chifukwa cha lamulo lonena za anthu akhate limene Yehova anapatsa anthu Ake. Lamulo limeneli linali kunena kuti wansembe wa Mulungu ayenera kuona thupi la wakhate. Wansembeyo anali kuuza munthu wakhateyo kuti matenda ake onse atha. Ndiye wodwalayo akachira, anali kuyambiranso kukhala limodzi ndi anthu abwino.—Levitiko 13:16, 17.

Koma akhate aŵa anali asanachire. Ndiye kodi iwo anapita kwa wansembe monga anawauzira Yesu?— Inde, ananyamuka nthaŵi yomweyo. Amuna ameneŵa ayenera kuti anakhulupirira kuti Yesu awachiritsa basi. Ndiyeno chinachitika ndi chiyani?

Eya, popita kwa wansembe uja, matenda awo anatha ali m’njira. Thupi lawo linakhala mmene linalili asanayambe kudwala. Iwo anachira! Anathandizika chifukwa chokhulupirira mphamvu ya Yesu. Tsonotu anasangalala kwambiri! Koma kodi iwo anafunika kuchita chiyani posonyeza kuyamikira? Kodi ukanakhala iweyo ukanachita chiyani?—

Mmodzi wa anthu omwe anachiritsidwa anagwada ndi kuthokoza Yesu

Kodi wakhate uyu anakumbukira kuchita chiyani?

Mmodzi mwa anthu amene anachiritsidwa aja anabwerera kwa Yesu. Anayamba kulemekeza Yehova mwa kunena zabwino za Mulungu. Pamenepa anachita bwino kwambiri chifukwa mphamvu imene inamuchiritsa inachokera kwa Mulungu. Munthuyu anagwadanso pamaso pa Mphunzitsi Waluso ndi kumuthokoza. Anayamikira kwambiri zimene Yesu anamuchitira.

Nanga bwanji nayini ena aja? Yesu anafunsa kuti: ‘Panali akhate teni amene anachiritsidwa, si choncho? Kodi nayini ena aja ali kuti? Kodi wangobwerera mmodzi yekha kuti adzalemekeze Mulungu?’

Zinalidi choncho. Mmodzi yekha mwa teni onse aja ndiye analemekeza Mulungu ndipo anabwerera kukathokoza Yesu. Nanga ukudziŵa kodi, munthu ameneyu analitu Msamariya, wochokera ku dziko lina. Anthu nayini ena aja sanayamike Mulungu. Ndiponso sanathokoze Yesu.—Luka 17:15-19.

Kodi iweyo uli ngati munthu uti mwa anthu ameneŵa? Tiyenera kukhala ngati Msamariya uja, si choncho?— Ndiye munthu wina akatichitira zabwino, kodi tiyenera kukumbukira chiyani?— Tifunika kunena kuti zikomo. Nthaŵi zambiri anthu amaiŵala kunena kuti zikomo. Komatu kunena kuti zikomo ndi kwabwino. Tikamachita zimenezi, Yehova ndi Mwana wake, Yesu, amakondwera.

Mayi wagwira mwana wake amene akudwala ndipo akumupatsa mankhwala

Kodi uyenera kuchita chiyani kuti ukhale ngati wakhate amene anabwerera kwa Yesu?

Utati uganizire, ungaone kuti anthu ena akuchitira zinthu zambiri. Mwachitsanzo, kodi iwe unayamba wadwalapo?— Mwina sunadwale kwambiri ngati akhate teni aja, koma mwina unadwalapo chifuwa kapena m’mimba. Kodi pali amene anakusamalira?— Mwina iwo anakupatsa mankhwala kuti umwe ndi kukuchitiranso zinthu zina. Kodi unasangalala kuti anakuthandiza kupezanso bwino?—

Msamariya uja anathokoza Yesu pomuchiritsa, ndipo Yesu anakondwera nazo. Kodi ukuganiza kuti amayi ako kapena atate ako adzasangalala iwe utawauza kuti zikomo pamene akuchitira zinthu zabwino?— Inde adzasangalala.

Mphunzitsi akusangalala mwana wasukulu atamuthokoza

Kodi ndi chifukwa chiyani tifunika kukumbukira kunena kuti zikomo?

Anthu ena amakuchitira zinthu tsiku lililonse kapena mlungu uliwonse. Mwina ndi ntchito yawo kuchita zimenezo. Mwinanso amasangalala kumene kuti amachita zinthu zimenezo. Komatu iweyo ungamaiŵale kunena kuti zikomo. Aphunzitsi ako kusukulu amalimbikira kwambiri kuti iweyo uphunzire. Imeneyi ndi ntchito yawo. Komatu iwo adzasangalala kwambiri ngati iwe uwathokoza pokuphunzitsa.

Nthaŵi zina anthu ena amakuchitira zinthu zazing’ono. Kodi munthu wina anakuthandizapo kusenza katundu wolemera? Kapena kodi munthu wina anayamba wakupatsirako chakudya? Ndi pofunika kumanena kuti zikomo ngakhale pa zinthu zazing’ono ngati zimenezi.

Mwana wakumbatira mayi ake n’kuwapatsa maluwa

Ngati tikumbukira kunena kuti zikomo kwa anthu padziko lapansi pano, ndiye kuti tidzakumbukiranso kunena kuti zikomo kwa Atate wathu wakumwamba. Ndipotu Yehova tingamuyamike pa zinthu zambiri zedi! Iye anatipatsa moyo komanso zinthu zonse zabwino zimene timasangalala nazo. Tilitu ndi zifukwa zambiri zoti tsiku lililonse tizilemekeza Mulungu mwa kulankhula zinthu zabwino zokhudza iye.

Pankhani ya kukhala oyamika, ŵerengani Salmo 92:1; Aefeso 5:20; Akolose 3:17; ndi 1 Atesalonika 5:⁠18.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena