Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jd mutu 4 tsamba 43-55
  • Yehova Ndi Mulungu Amene Amalosera Zam’tsogolo N’kuzikwaniritsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Ndi Mulungu Amene Amalosera Zam’tsogolo N’kuzikwaniritsa
  • Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • YEHOVA NDI WOLAMULIRA WACHIKONDI AMENE AMATSOGOLERA ZONSE
  • YEHOVA AMAKWANIRITSA MALONJEZO AKE NTHAWI ZONSE
  • YEHOVA NDI ATATE AMENE AMATISAMALIRA
  • ANTHU AKAKHULULUKIDWA MACHIMO, ANGATHE KUDZAPULUMUKA
  • Aneneri Amene Uthenga Wawo Ungatithandize
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Mfundo Yaikulu mu Uthenga wa Aneneri 12 Inali Yokhudza Tsiku la Yehova
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • “Kodi Yehova Akufuna Chiyani Kwa Iwe?”
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • “Madalitso Oti Mudzasowa Powalandirira”
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
Onani Zambiri
Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
jd mutu 4 tsamba 43-55

MUTU 4

Yehova Ndi Mulungu Amene Amalosera Zam’tsogolo N’kuzikwaniritsa

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amaona kuti palibe amene angathetse mavuto a anthu padzikoli? (b) Kodi mabuku a aneneri 12 akusonyeza bwanji makhalidwe a Yehova?

ANTHU ambiri akuona kuti sangathenso kulamulira moyo wawo. Ndipo akawerenga nkhani za m’manyuzi, amaona kuti mavuto amene anthu onse akukumana nawo akuchulukirachulukira ndipo palibe chiyembekezo choti adzatha. Zimene anthu akuchita pofuna kuthetsa mavuto a m’dzikoli zikuoneka kuti zikungowonjezeranso mavuto ena. Ngakhale kuti ena mwa aneneri 12 amene tikukambirana m’buku lino nawonso anakumana ndi mavuto akuluakulu, uthenga wopatsa chiyembekezo umene analemba ungatithandize ndipo tingaugwiritse ntchito polimbikitsa ena.—Mika 3:1-3; Habakuku 1:1-4.

2 Mfundo yofunika kwambiri imene mupeze m’mabuku aulosiwa ndi yakuti Yehova, Wolamulira wa chilengedwe chonse, ali ndi mphamvu zonse ndipo akufunitsitsa kutithandiza pa moyo wathu. Ndipotu aliyense wa ife sangakayikire zoti Mulungu akufunitsitsa kumuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino. Aneneri 12 amenewa anafotokoza momveka bwino makhalidwe a “Yehova wa makamu.” Mwachitsanzo, Baibulo limati Mulungu ‘angakhudze dziko ndipo lingasungunuke.’ Komabe, iye akutsimikizira anthu ake kuti: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.” (Zekariya 2:8; Amosi 4:13; 9:5) N’zolimbikitsatu kwambiri kuwerenga nkhani zimene zimasonyeza kuti Mulungu amachita chilichonse chifukwa cha chikondi. Komanso n’zolimbikitsa kuona mmene amasonyezera chifundo ndiponso kuti ndi wokonzeka kukhululukira anthu. (Hoseya 6:1-3; Yoweli 2:12-14) N’zoona kuti zimene aneneriwa analemba sizikufotokoza mbali zonse za makhalidwe a Mulungu. Koma makhalidwe amenewa akufotokozedwa m’mabuku onse 66 a m’Baibulo. Komabe, mabuku a aneneri 12 amenewa akutithandiza kuona bwino kwambiri makhalidwe osangalatsa a Mulungu komanso mmene iye amachitira zinthu.

3. Kodi aneneri 12 amenewa anasonyeza bwanji kuti Yehova amakwaniritsa zolinga zake?

3 Mabuku a aneneri 12 amatithandiza kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amakwaniritsa zimene walosera komanso amakwaniritsa zolinga zake. Mabukuwa amatitsimikiziranso kuti Mulungu adzabweretsa paradaiso padziko lapansi ndipo iye azidzalamulira anthu okhala mmenemo. (Mika 4:1-4) Ena mwa aneneriwa anafotokoza zimene Yehova anachita pokonzekera kutumiza Mesiya padziko lapansi komanso mmene anakonzera zopereka dipo lomasula anthu ku uchimo ndi imfa. (Malaki 3:1; 4:5) N’chifukwa chiyani kudziwa zonsezi kuli kofunika kwambiri?

YEHOVA NDI WOLAMULIRA WACHIKONDI AMENE AMATSOGOLERA ZONSE

4, 5. (a) Kodi aneneri 12 anatsindika mfundo yofunika kwambiri iti yokhudza Mulungu? (b) Kodi mfundo yakuti Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse imakukhudzani bwanji?

4 Kumbukirani kuti m’mutu wapitawu tinaphunzira kuti Satana anatsutsa zoti Mulungu ndi woyenera kulamulira. Chifukwa chakuti Satana anagalukira ulamuliro wa Yehova komanso anakayikira zolinga zake, angelo ena kumwamba anasiya kumvera Mulungu ndipo zimenezi zinabweretsa chisokonezo padziko lapansi. Choncho zikuonekeratu kuti kulemekeza ndiponso kugonjera ulamuliro wa Yehova n’kofunika kwambiri kuti zinthu ziziyenda bwino kumwamba ndi padziko lapansi, komanso kuti anthu onse akhale mwa mtendere. M’pomveka kuti Yehova akufunitsitsa kusonyeza kuti ndi iye yekha amene ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Tiyeni tione mmene mabuku 12 a aneneri angatithandizire kuti timvetse bwino zimenezi.

5 Popeza aneneriwa anatumizidwa ndi Yehova, mu uthenga wawo, ankatsindika zakuti iye ndi wolemekezeka kwambiri. Mwachitsanzo, polemekeza dzina la Yehova komanso pofuna kusonyeza kuti iye monga Wamphamvuyonse ndi woyenera kulamulira, m’buku la Amosi mawu akuti “Ambuye Wamkulu Koposa” alimo okwana 21. Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu woona ali ndi mphamvu zopanda malire komanso angathe kuchita chilichonse. (Amosi 9:2-5; onani bokosi lakuti “Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse.”) Yehova yekha ndi amene ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndipo sangafanane ndi mafano. (Mika 1:7; Habakuku 2:18-20; Zefaniya 2:11) Popeza Yehova ndi Mlengi wa zinthu zonse, iye ali ndi mphamvu ndiponso ufulu wonse wolamulira zinthuzo. (Amosi 4:13; 5:8, 9; 9:6) Koma kodi n’chifukwa chiyani mukufunikira kudziwa zimenezi?

6. Kodi munthu aliyense angathandizire bwanji kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu?

6 Ngati nthawi ina munasalidwapo kapena kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo, mungatonthozedwe podziwa kuti Mulungu wathu wachikondi amasamalira anthu onse. Kale, Yehova anali pa ubwenzi wapadera ndi mtundu umodzi wokha. Komabe iye ananena kuti ankafunitsitsa kuti anthu a m’mitundu yonse ndi zinenero zonse nawonso adzapeze madalitso. Iye ndi “Ambuye woona wa dziko lonse lapansi.” (Mika 4:13) Mulungu analonjeza kuti dzina lake “lidzakhala lokwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.” (Malaki 1:11) Popeza Atate wathu wakumwamba alibe tsankho, amafuna kuti anthu amitundu yonse amudziwe. Zimenezi zachititsa kuti anthu “ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina,” amene aitanidwa ndi Yehova, ayambe kumulambira.​—Zekariya 8:23.

7. N’chifukwa chiyani tanthauzo la dzina la Yehova lili lofunika kwambiri?

7 Kuti munthu amvetse bwino mmene Mulungu alili komanso zimene adzachite, ayenera kumvetsa bwino tanthauzo la dzina la Mulunguyo. (Salimo 9:10) Mu nthawi ya mneneri Mika, dzina la Yehova linkanyozedwa chifukwa chakuti anthu amene ankadziwika ndi dzinali sankamvera Mulungu. Mneneriyu anauziridwa kuti atsindike mfundo yakuti ‘dzina la Yehova ndi lalikulu,’ komanso yakuti “munthu wanzeru zopindulitsa adzaopa dzina [la Mulungu].” (Mika 5:4; 6:9) N’chifukwa chiyani mneneriyu anauziridwa kuchita zimenezi? N’chifukwa chakuti madalitso alionse amene tikuyembekezera kuti adzakwaniritsidwa m’tsogolo adzakwaniritsidwa chifukwa cha tanthauzo la dzinalo. Dzinalo limatanthauza kuti: “Iye Amachititsa Kukhala.” Werengani Yoweli 2:26, ndipo ganizirani za mwayi umene aliyense angakhale nawo wodziwika ndi dzina la Mulungu. Ganiziraninso za mmene aliyense angasangalalire akamauza ena za Mulungu amene amatha kukhala chilichonse chimene akufuna, n’cholinga chakuti athandize chamoyo chilichonse chimene analenga. Mulungu wakhala akusonyeza kuti iye yekha ali ndi mphamvu zopanda malire ndipo amachita chilichonse chomwe akufuna. Kukwaniritsidwa kwa maulosi ambirimbiri amene aneneri 12 analemba kukusonyeza kuti zimenezi ndi zoona.

YEHOVA NDI MULUNGU WAMPHAMVUYONSE

M’Chiheberi, mawu akuti Shad·daiʹ, kapena kuti “Wamphamvuyonse,” ndi dzina laudindo la Mulungu. Mawu amenewa amapezeka kamodzi kokha m’mabuku 12 a aneneri, palemba la Yoweli 1:15. Anthu ena amanena kuti tanthauzo lalikulu la mawuwa ndi lakuti “khala wamphamvu” kapena kuti “chita zinthu mwamphamvu.” Mawu ena ofanana ndi amenewa akuti “Yehova wa makamu,” kapena akuti “Yehova Mulungu wa makamu,” amapezeka m’malo okwana 107 m’mabuku 12 a aneneri. Munthu amene ali ndi mphamvu kapena nyonga angathe kukwaniritsa zolinga zake. Izi zikutanthauza kuti angathe kugonjetsa chilichonse chimene chikanamulepheretsa kukwaniritsa zolinga zakezo. Mfundo yakuti Yehova ndi wamphamvuyonse imasonyeza kuti ali ndi mphamvu zochuluka ndipo angakwaniritse zimene walosera n’cholinga choti chifuniro chake chichitike.

8. Kodi dzina la Yehova lakulimbikitsani m’njira ziti?

8 Anthu mamiliyoni ambiri alimbikitsidwa ataphunzira kuti Yehova amatha kuchita kapena kukwaniritsa chilichonse chimene akufuna. Mneneri Yoweli anasonyeza zimenezi pamene analemba mfundo yodziwika bwino yomwenso inatchulidwa m’malemba achigiriki. Iye analemba kuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32; Machitidwe 2:21; Aroma 10:13) Kodi ifenso tinganene motsimikiza mawu amene Mika ananena akuti, “ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya”? (Mika 4:5) Zoonadi, pa nthawi imene tikuzunzidwa kapena tikukumana ndi mavuto, tisamakayikire zoti ‘tingapeze chitetezo m’dzina la Yehova.’​—Zefaniya 3:9, 12; Nahumu 1:7.

9. Kodi Mulungu ali ndi mphamvu zochita chiyani ndi olamulira adzikoli?

9 Pamene mukuwerenga mabuku aulosi amenewa mungatsimikizire kuti Yehova amatha kulowerera pa zimene olamulira kapena anthu amene ali ndi mphamvu padzikoli angachite. Iye amatha kuwachititsa zinthu zogwirizana ndi zimene iyeyo akufuna. (Miyambo 21:1) Mwachitsanzo, taganizirani za Dariyo Wamkulu, mfumu ya ku Perisiya. Anthu omwe ankadana ndi kulambira koona anayesa kumupempha kuti awathandize pofuna kuimitsa ntchito yomanganso kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Koma zimene zinachitika zinali zosiyana ndi zimene anthuwo ankafuna. Cha m’ma 520 B.C.E., Mfumu Dariyo analamula zoti lamulo limene Koresi anakhazikitsa loti Yerusalemu amangidwenso, litsatiridwe ndipo anathandiza Ayuda pa ntchito yomangayo. Pamene Ayudawo anayamba kukumana ndi mavuto ena, Mulungu anauza bwanamkubwa wachiyuda, Zerubabele kuti: “‘Sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,’ watero Yehova wa makamu. Ngakhale pataikidwa chopinga chachikulu ngati phiri pamaso pa Zerubabele, chidzasalazidwa kukhala malo athyathyathya.” (Zekariya 4:6, 7) Palibe chimene chidzalepheretse Yehova kuwononga dziko loipali kapena kumulepheretsa kubweretsa paradaiso amene anthu omulambira adzakhalemo mosangalala.​—Yesaya 65:21-23.

10. Kodi Mulungu angasankhe kugwiritsa ntchito zinthu ngati ziti akafuna kuwononga adani ake, ndipo n’chifukwa chiyani mfundo imeneyi ndi yofunika kuiganizira mozama?

10 Yehova amathanso kulamulira zinthu zachilengedwe monga mphepo ndi mvula ndipo angasankhe kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi akafuna kuwononga adani ake. (Nahumu 1:3-6) Pofuna kutsindika mfundo yoti Yehova angateteze anthu ake, mneneri Zekariya anagwiritsa ntchito fanizo. Iye anati: “Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake, ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga lanyanga ya nkhosa, ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho ya kum’mwera.” (Zekariya 9:14) Ndiye kodi zingakhale zovuta kuti Mulungu asonyeze mphamvu zake kwa mitundu ya anthu osamumvera masiku ano? N’zodziwikiratu kuti sizingamuvute.​—Amosi 1:3-5; 2:1-3.

YEHOVA AMAKWANIRITSA MALONJEZO AKE NTHAWI ZONSE

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani anthu ankaganiza kuti mzinda wa Nineve unali wosagonjetseka? (b) Kodi n’chiyani chinachitikira mzinda wa Nineve pokwaniritsa ulosi wa Mulungu?

11 Tayerekezerani kuti munalipo m’zaka za m’ma 800 B.C.E., m’dera limene panopa limatchedwa Middle East. Mosakayikira, mukanamva za mzinda wa Nineve umene unali m’dziko la Asuri ndipo unali wotchuka kwambiri pa nthawiyo. Mzindawu unali kum’mawa, m’mphepete mwa mtsinje wa Tigirisi, womwe unali pa mtunda wa makilomita 900 kumpoto chakum’mawa kwa mzinda wa Yerusalemu. Mwina munamvapo kuti mzindawu unali waukulu kwambiri, moti munthu amayenda makilomita 100 kuti auzungulire. Anthu amene anaonapo mzindawo ankanena kuti unali wokongola mofanana ndi mzinda wa Babulo, chifukwa unali ndi nyumba zachifumu, akachisi, misewu ikuluikulu, minda yamaluwa ndiponso laibulale yabwino kwambiri. Komanso akatswiri ankhondo ananena kuti mpanda wake wamkati ndiponso wakunja unali wolimba kwambiri moti zinali zovuta kuugumula.

12 N’kutheka kuti anthu ambiri akamafotokoza za mzinda wa Nineve, ankanena kuti zinali zosatheka kuugonjetsa. Komabe aneneri ena ochokera m’dziko la Yuda, lomwe linali laling’ono, ankanena mobwerezabwereza kuti Yehova anali ataweruza kuti “mzinda wokhetsa magazi” umenewu uwonongedwe. Anthu a mumzindawo atamvera zimene mneneri Yona ankalengeza, Mulungu anawakhululukira ndipo sanawawononge pa nthawiyo. Koma patapita nthawi, anthu a ku Nineve anayambiranso kuchita zoipa. Choncho mneneri Nahumu analosera kuti: “Nineve . . . , lupanga lidzakuduladula . . . Masoka ako sadzakupatsa mpata wopuma.” (Nahumu 3:1, 7, 15, 19; Yona 3:5-10) Chapanthawi yomweyi, Mulungu anagwiritsa ntchito mneneri Zefaniya kuti alosere zoti mzinda wa Nineve udzakhala bwinja. (Zefaniya 2:13) Kodi zikanathekadi kuti mzinda wamphamvu umenewu, womwe unkaoneka ngati wosagonjetseka, uwonongedwe pokwaniritsa mawu a Yehova? Zimenezi zinachitikadi cha m’ma 632 B.C.E., pamene Ababulo, Asukuti komanso Amedi, anazungulira mzinda wa Nineve. Mwadzidzidzi madzi osefukira anachititsa kuti mpanda wake ufewe ndipo adaniwo sanavutikenso kuugumula. (Nahumu 2:6-8) Posakhalitsa, mzinda umenewu, womwe unkaoneka ngati wosagonjetseka, unasanduka mabwinja okhaokha. Mpaka pano pamalo pamene panali mzinda wa Nineve pali mabwinja okhaokha.a Anthu a mumzinda umenewu omwe poyamba anali ‘osangalala’ sanalepheretse mawu a Mulungu kukwaniritsidwa.—Zefaniya 2:15.

13. Kodi m’mabuku a aneneri 12 mungapezemo umboni wotani wa maulosi amene anakwaniritsidwa?

13 Zimene zinachitikira mzinda wa Nineve ndi chitsanzo chimodzi cha ulosi umene unakwaniritsidwa. Tayang’anani pa mapu a makono a mayiko a ku Middle East. Kodi mungapeze malo otchedwa Amoni, Asuri, Babeloniya, Edomu kapena Mowabu? Ayi simungawapeze. Ngakhale kuti mitundu imeneyi inali yotchuka kwambiri pa nthawi ina, aneneri 12 amenewa analosera kuti mitunduyi idzatha. (Amosi 2:1-3; Obadiya 1, 8; Nahumu 3:18; Zefaniya 2:8-11; Zekariya 2:7-9) M’kupita kwa nthawi, mitundu imeneyi inatheratu umodzi ndi umodzi, mogwirizana ndi zimene Yehova ananeneratu. Komanso zimene aneneriwa analosera zoti Ayuda amene anagwidwa ndi kupita ku ukapolo ku Babulo adzabwerera kwawo, zinakwaniritsidwa.

14. N’chifukwa chiyani zochita zanu za tsiku ndi tsiku ziyenera kusonyeza kuti mumakhulupirira ndi mtima wonse malonjezo a Yehova?

14 Kodi mfundo yoti Yehova amatha kulosera zam’tsogolo n’kuzikwaniritsa ingakhudze bwanji chikhulupiriro chanu? Mungakhale wotsimikizira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake chifukwa iye ndi Mulungu “amene sanganame.” (Tito 1:2) Kuwonjezera pamenepa, kudzera m’Mawu ake, Mulungu amatiuza zimene tikufunikira kudziwa. Choncho mawu akewo angakuthandizeni kuti pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku muzichita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova. Komanso angakuthandizeni kuti mukhale ndi chikhulupiriro choti nthawi zonse maulosi ake amakwaniritsidwa. M’mabuku 12 a aneneri muli zitsanzo za maulosi amene anakwaniritsidwa kale. Komanso ambiri mwa maulosi amene ali m’mabukuwa akukwaniritsidwa panopa kapena akuyenera kukwaniritsidwa posachedwapa. Ndipo uthenga umene uli m’mabukuwa ungakuthandizeni kukhulupirira kuti maulosi onena za nthawi ino komanso zam’tsogolo, adzakwaniritsidwa. Choncho muziona mabukuwa kuti ndi ofunika kwambiri.

Chithunzi patsamba 48

Ngakhale kuti mzinda wa Nineve unkaoneka ngati sungagonjetsedwe, kodi maulosi a Yehova anakwaniritsidwa bwanji?

YEHOVA NDI ATATE AMENE AMATISAMALIRA

15. Ngati mukuvutika kuthana ndi mavuto enaake, kodi zimene zinachitikira Mika zingakuthandizeni bwanji?

15 Mfundo yakuti Mulungu ndi wodalirika simangoonekera pa zimene analosera kuti zidzachitikira anthu kapena zimene zikuchitika m’dziko lonseli. Yehova ndi wodalirikanso chifukwa angalosere ndi kukwaniritsa maulosi amene akukukhudzani mwachindunji. Kodi amachita bwanji zimenezi? Mwina nthawi zina mungamavutike kuti muthane ndi mavuto enaake. Pa nthawi ngati imeneyi, simungangofuna munthu woti amvetse mavuto anu koma mungafunikire munthu amene mumamukhulupirira, kuti akuthandizeni. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 700 B.C.E., mneneri Mika ayenera kuti ankaona kuti anali munthu yekhayo wokhulupirika pamene ankalosera pakati pa anthu onyada a ku Yuda, moti ngakhale achibale ake sankawakhulupirira. Anthu amene ankakumana nawo kulikonse anali okonda kupha anzawo, achinyengo komanso okonda ziphuphu. Komabe, Mika analimbikitsidwa ndi zimene Mulungu analonjeza anthu ake okhulupirika zoti adzawasamalira ngakhale anthu ena atawachitira zoipa. Inunso mungalimbikitsidwe ndi mawu amenewa ngati nthawi zina mungapezeke kuti muli m’kagulu ka anthu ochepa olambira Yehova kapena muli nokhanokha pakati pa anthu ambirimbiri amene salemekeza Mulungu.—Mika 7:2-9.

16. N’chifukwa chiyani mungakhulupirire kuti Mulungu amaona anthu akamachita katangale ndiponso akamapondereza anzawo, nanga n’chifukwa chiyani mungakhulupirire kuti iye adzapulumutsa anthu olungama?

16 Mofanana ndi zimene zimachitika kawirikawiri masiku ano, anthu olemera komanso amphamvu ku Yuda ndi ku Isiraeli anali adyera komanso ankapondereza ena. Anthu ankaumirizidwa kupereka msonkho wochuluka komanso ankalandidwa malo awo, ndipo zimenezi zinachititsa kuti pazichitika malonda osayenera aukapolo. Anthu ankadana ndi anthu osauka ndipo ankawachitira nkhanza. (Amosi 2:6; 5:11, 12; Mika 2:1, 2; 3:9-12; Habakuku 1:4) Kudzera mwa aneneri ake, Mulungu ananena mosapita m’mbali kuti amadana ndi anthu akatangale komanso opondereza anzawo, ndipo ananena kuti adzalanga anthu amene ankapitirizabe kuchita zoipa. (Habakuku 2:3, 6-16) Iye analosera kuti “adzakonza zinthu zokhudza anthu ochokera m’mitundu yamphamvu,” komanso kuti mtumiki wake aliyense wokhulupirika “adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.” (Mika 4:3, 4) Zimenezi zikusonyeza kuti atumiki ake adzakhala pamtendere. Popeza Mulungu analosera zinthu zambirimbiri n’kuzikwaniritsa, musakayikire zoti lonjezo limenelinso lidzakwaniritsidwa.

17, 18. (a) N’chiyani chimachititsa Mulungu kuti athandize anthu ake kukhala ndi chiyembekezo? (b) Kodi tiyenera kuona bwanji chilango chimene Yehova amapereka?

17 Sikuti Yehova amakwaniritsa maulosi ake pongofuna kugometsa anthu amene aona kuti iye ali ndi mphamvu zotha kukwaniritsa maulosiwo. Chilichonse chimene amachita, amachichita chifukwa cha chikondi, pakuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Kumbukirani nkhani ya Hoseya amene anakhalapo m’zaka za m’ma 700 B.C.E. Mkazi wa Hoseya anali Gomeri, ndipo anali wosakhulupirika kwa mwamuna wake. Mofanana ndi Gomeri, Aisiraeli anali osakhulupirika kwa Yehova ndipo ankalambira mafano, zomwe zinali ngati kuchita chigololo. Mwachitsanzo, Aisiraeli ankalambira Baala ndipo pa nthawi imodzimodziyo ankalambiranso Yehova. Komanso mophiphiritsa iwo ‘ankachita dama’ ndi Asuri ndiponso Iguputo. Kodi Yehova anachita chiyani chifukwa cha zimenezi? Ganizirani zimene Hoseya ankafunika kuchita. Iye ankafunika kufunafuna mkazi wake wosakhulupirikayo n’kubwera naye kunyumba. Chimodzimodzinso Yehova. Chifukwa cha chikondi chake, iye anafunafuna anthu akewo ndipo Mawu ake amati: “Ndinali kuwakoka mokoma mtima ndi mwachikondi, . . . ndipo mwachikondi ndinali kubweretsera aliyense wa iwo chakudya.” (Hoseya 2:5; 11:4) Ngati anthuwa akanalapa mochokera pansi pa mtima, Mulungu akanatha kuwakhululukira, ndipo zikanatheka kuti akhalenso naye pa ubwenzi. (Hoseya 1:3, 4; 2:16, 23; 6:1-3; 14:4) Kodi simumachita chidwi mukaganizira chikondi chimene Yehova ali nacho? Dzifunseni kuti, ‘Ngati Yehova anasonyeza chikondi choterechi m’mbuyomu, kodi masiku anonso sangasonyeze chikondi chimenechi, chomwe ndi chokhalitsa, chosasintha komanso chosatha?’—Hoseya 11:8.

Chithunzi patsamba 52

18 Mabuku 12 aulosiwa angakuthandizeninso kuona kuti Mulungu amafunikanso kupereka chilango chifukwa chakuti ndi wachikondi. Yehova anatsimikizira anthu ake ochimwawo kuti ‘sadzawafafaniza onse.’ (Amosi 9:8) Choncho Mulungu ankalanga anthu ake akaona kuti pakufunika kutero. Komabe ziyenera kuti zinali zolimbikitsa kudziwa kuti chilangocho chinali cha nthawi yochepa. Lemba la Malaki 1:6, limayerekezera Yehova ndi bambo wachikondi. Tikudziwa kuti bambo wachikondi angalange ana ake n’cholinga choti awathandize. (Nahumu 1:3; Aheberi 12:6) Komabe, chikondi cha Atate wathu wakumwamba chimamuchititsa kuti asamakwiye msanga ndipo lemba la Malaki 3:10, 16, limatitsimikizira kuti iye adzapereka madalitso kwa atumiki ake mowolowa manja.

19. Kodi mungachite bwino kudzifunsa mafunso ati?

19 M’mawu oyamba a buku lake, mneneri Malaki analemba kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Ine ndimakukondani anthu inu.’” (Malaki 1:2) Pamene mukuganizira mawu olimbikitsa amenewa, omwe Mulungu anauza Aisiraeli, dzifunseni kuti: ‘Kodi pali zimene ndimachita zomwe zingachititse kuti Mulungu asamandikonde? Kodi ndi zinthu ziti zokhudza chikondi cha Mulungu zomwe ndingafune kudziwa komanso zimene ndingasangalale nazo kwambiri?’ Mukamvetsa bwino chikondi cha Mulungu, simungakayikire ngakhale pang’ono kuti iye adzakukondani mpaka kalekale.

ANTHU AKAKHULULUKIDWA MACHIMO, ANGATHE KUDZAPULUMUKA

20. Kodi kukhululukidwa machimo kumathandiza bwanji munthu kuti adzapulumuke?

20 Mukamawerenga mabuku aulosi amenewa, mungaone kuti nthawi zina Yehova ankalosera za mavuto. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Nthawi zambiri ankafuna kulimbikitsa anthu ake kuti alape. Choncho kuti zimenezi zitheke, iye analola kuti anthu a m’mayiko ena awononge Samariya m’chaka cha 740 B.C.E. komanso Yerusalemu m’chaka cha 607 B.C.E. Zimene Mulungu analosera zinachitikadi. Komabe patapita nthawi iye analola kuti anthu olapa abwerere kudziko lawo. N’zoonadi, mabuku amenewa akutsindika mfundo yakuti Mulungu amakhululukira ndi mtima wonse anthu amene alapa ndipo amayambanso kuwakonda. (Habakuku 3:13; Zefaniya 2:2, 3) M’pake kuti mneneri Mika ananena mawu akuti: “Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu amene amakhululukira zolakwa ndi machimo a anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake? Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale, pakuti kusonyeza kukoma mtima kosatha kumakusangalatsani.” (Mika 7:18; Yoweli 2:13; Zekariya 1:4) Kukwaniritsidwa kwa maulosi kumasonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yoona.

21. (a) Kodi ena mwa aneneri 12, analosera mfundo ziti zokhudza Mesiya? (b) Kodi ndi maulosi ati okhudza Mesiya amene amakusangalatsani kwambiri?

21 Pofuna kukhala ndi njira yabwino ndiponso yodalirika yoti anthu azitha kukhululukidwa machimo, Yehova analosera za kubwera kwa Mesiya, amene anali woti apereke nsembe ya “dipo lokwanira ndendende” m’malo mwa anthu onse ochimwa. (1 Timoteyo 2:6) Mneneri Amosi analosera kuti zimene Mesiya, mwana wa Davide, adzachite zidzathandiza anthu kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Mulungu. (Amosi 9:11, 12; Machitidwe 15:15-19) Yesu anali woti adzathandize anthu onse amene adzakhulupirire nsembe yake kuti adzapeze moyo wosatha. Ndipo mneneri Mika anachita kutchula malo enieni amene Yesu adzabadwire. (Mika 5:2) Komanso mneneri Zekariya ananena za “Mphukira,” yomwe ndi Yesu, ndipo anasonyeza kuti iye “azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu.” (Zekariya 3:8; 6:12, 13; Luka 1:32, 33) Mosakayikira, chikhulupiriro chanu chidzalimba mukaphunzira zambiri zokhudza maulosi ngati amenewa.​—Onani bokosi lakuti “Maulosi Akuluakulu Okhudza Mesiya.”

22. Kodi zimene zinalembedwa m’mabuku a aneneri 12 zakuthandizani bwanji kuti muzikhulupirira kwambiri Yehova?

22 Pamene mukuwerenga uthenga wa aneneri 12, chikhulupiriro chanu chakuti Mulungu adzawononga adani ake pa nkhondo yake yomaliza chidzalimba. Yehova amatimenyera nkhondo ndipo adzabweretsa chilungamo chenicheni. Mulungu sanama ndipo nthawi zonse amakumbukira zimene analonjeza atumiki ake komanso amawasamalira ndi kuwapulumutsa kwa onse owapondereza. (Mika 7:8-10; Zefaniya 2:6, 7) Yehova sanasinthe. (Malaki 3:6) N’zolimbikitsatu kudziwa kuti palibe chomwe chingalepheretse Mulungu kukwaniritsa zolinga zake. Mulungu ananena kuti tsiku lake lachiweruzo likubwera, ndipo libweradi. Choncho khalani maso chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi. Baibulo limati: “Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse lapansi. Pa tsiku limenelo, Yehova adzakhala mmodzi ndipo dzina lake lidzakhala limodzi.” (Zekariya 14:9) Yehova analosera zimenezi ndipo adzazikwaniritsa.

MAULOSI AKULUAKULU OKHUDZA MESIYA

Ulosi

Pamene ukupezeka

Kukwaniritsidwa kwake

Adzabadwira ku Betelehemu

Mika 5:2

Luka 2:4-11; Yohane 7:42

Adzaitanidwa kuti atuluke ku Iguputo kumene anathawira

Hoseya 11:1

Mateyu 2:14, 15

Adzalowa mu Yerusalemu atakwera bulu

Zekariya 9:9

Mateyu 21:1-9; Yohane 12:12-15

Adzagulitsidwa ndi ndalama 30 zasiliva

Zekariya 11:12

Mateyu 26:15; 27:3-10

M’busa adzaphedwa, nkhosa zidzabalalika

Zekariya 13:7

Mateyu 26:31, 56

Adzalasidwa ali pamtengo

Zekariya 12:10

Mateyu 27:49; Yohane 19:34, 37

Adzakhala m’manda masiku atatu, kenako adzaukitsidwa

Yona 1:17; 2:10

Mateyu 12:39, 40; 16:21; 1 Akorinto 15:3-8

a Mu November 2002, nkhondo ya ku Iraq isanachitike, pulofesa wina dzina lake Dan Cruickshank anapita kudera kumene kunali mzinda wa Nineve. Iye ananena pa wailesi ya kanema ya BBC kuti: “Chakumalire kwa mzinda wa Mosul ku Iraq, kuli mabwinja a Nineve ndi a mzinda wa Nimrud. Mabwinja a mizinda iwiriyi anafufuzidwa mwakhama ndi akatswiri ofukula zinthu zakale a ku Britain kuyambira cha m’ma 1840. . . . Zimene akatswiriwa apeza zokhudza mizinda iwiriyi, yomwe anthu ena amaona kuti sinali mizinda yeniyeni, zikugwirizana kwambiri ndi zimene zinafotokozedwa

KODI MWALIMBIKITSIDWA BWANJI NDI MFUNDO ZOTSATIRAZI?

  • Yehova ndi wamphamvuyonse.—Yoweli 1:15.

  • Mulungu alibe tsankho.—Zekariya 8:23.

  • Tanthauzo lofunika kwambiri la dzina la Mulungu.—Mika 5:4.

KODI KUGANIZIRA MOZAMA MFUNDO ZOTSATIRAZI KUNGALIMBITSE BWANJI UBWENZI WANU NDI MULUNGU?

  • Mulungu ali ndi mphamvu zokwaniritsa zimene walonjeza.​—Yoweli 2:11.

  • Mulungu amakukondani kwambiri.​—Hoseya 11:4; 14:4; Zefaniya 3:17.

  • Mulungu ndi wachifundo komanso wokhululuka.​—Hoseya 2:23; Mika 7:18.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena