Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lv tsamba 215-tsamba 218 ndime 1
  • Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni
  • Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mulungu Amaonera Magazi
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Tsatirani Malangizo a Mulungu Wamoyo
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
lv tsamba 215-tsamba 218 ndime 1

ZAKUMAPETO

Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni

Tizigawo ta magazi. Tizigawo timeneti timatengedwa m’zigawo zikuluzikulu 4 za magazi. Zigawo zikuluzikulu zimenezi ndi maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana, ndi madzi a m’magazi. Mwachitsanzo, maselo ofiira amakhala ndi pulotini inayake yotchedwa himogulobini. Ndipo pulotini ya mtundu umenewu yotengedwa m’magazi a anthu kapena a nyama amaigwiritsa ntchito popanga mankhwala amene amaperekedwa kwa anthu amene akudwala matenda osowa magazi kapena amene ataya magazi ambiri.

M’madzi a m’magazi, omwe pafupifupi onse ndi madzi wamba, muli zinthu zambirimbiri zothandiza m’thupi monga mchere, shuga ndi zina zotero. Madzi a m’magaziwo amakhalanso ndi mapulotini ena osiyanasiyana, tinthu tina tothandiza magazi kuundana ndiponso maselo olimbana ndi matenda. Ngati munthu wadwala matenda enaake, madokotala angapereke jakisoni wa madzi otengedwa m’madzi a m’magazi a anthu amene magazi awo amatha kulimbana ndi matendawo. Ndipo m’maselo oyera amatha kuchotsamo tinthu tina timene amapangira mankhwala othandizira anthu odwala matenda a khansa kapena matenda ena oyambitsidwa ndi mavailasi.

Kodi Mkhristu ayenera kulandira mankhwala opangidwa kuchokera ku tizigawo ta magazi? M’Baibulo mulibe malamulo onena kuti alandire kapena ayi. Choncho aliyense ayenera kusankha yekha zochita mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Akhristu ena amakana tizigawo tonse ta magazi, chifukwa amaona kuti lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli limanena kuti magazi akachoka m’thupi la cholengedwa chilichonse ‘azithiridwa pansi.’ (Deuteronomo 12:​22-24) Ena amakana kuikidwa magazi kapena zigawo zikuluzikulu za magazi koma amatha kulandira mankhwala ochokera ku tizigawo ta magazi. Iwo amaona kuti tizigawo ta magazi tikachotsedwa m’magazimo sitimaimiranso moyo wa cholengedwa chimene mwachotsedwa magaziwo.

Posankha zochita pa nkhani ya tizigawo ta magazi, ganizirani mafunso awa: Kodi ndikudziwa kuti kukana tizigawo tonse ta magazi kukutanthauza kuti sindingalandire mankhwala ena amene ali ndi tinthu tina ta m’magazi tolimbana ndi matenda kapena amene amathandiza magazi kuundana kuti asiye kutuluka? Kodi ndingathe kufotokozera dokotala chifukwa chimene ndikukanira kapena kuvomerera tizigawo tina ta magazi?

Njira zopangira opaleshoni. Zina mwa njira zimenezi ndi kusungunula magazi ndiponso kupulumutsa magazi. Potsatira njira yosungunula magazi, magazi a wodwala amawapatutsa kuchoka m’thupi ndipo amamuika wodwalayo madzi owonjezera magazi. Kenako magazi opatutsidwa aja, amawaikanso m’thupi la wodwalayo. Potsatira njira yopulumutsa magazi, magazi amene amatayika popanga opaleshoni amapopedwa n’kubwezeretsedwa m’thupi la wodwalayo. Magaziwa amapopedwa pabala kapena pamalo ena amene ang’ambidwa, kenako amasefedwa n’kuwabwezeretsa m’thupi la wodwalayo. Madokotala amatsatira njirazi mosiyanasiyana, choncho Mkhristu aliyense ayenera kufunsa zimene madokotala akufuna kuchita.

Mukafuna kusankha chochita pa njira zopangira opaleshoni zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Ngati ena mwa magazi anga angatulutsidwe m’thupi langa ndipo mwina n’kusiya kuyenda kwakanthawi, kodi chikumbumtima changa chidzandilola kuona kuti magazi amenewa adakali mbali ya thupi langa, moti si ofunika kuti “[athiridwe] pansi”? (Deuteronomo 12:​23, 24) Kodi chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo chingandivutitse ngati pondipanga opaleshoni apatutsa magazi anga, n’kuwasakaniza ndi mankhwala ena, kenako n’kuwabwezeranso m’thupi mwanga? Kodi ndikudziwa kuti kukana njira zonse zachipatala zogwiritsa ntchito magazi anga omwe kukutanthauza kuti sindingalole kuyezedwa magazi, kuthandizidwa pogwiritsa ntchito makina osefa magazi kapena makina ogwira ntchito ya mtima ndi mapapo?’

Tchati patsamba 216

Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha zimene akufuna kuti madokotala achite ndi magazi ake pamene akumuchita opaleshoni. N’chimodzimodzinso ndi magazi ake amene atengedwa kuti ayezedwe kapenanso njira zina zochiritsira zimene zayamba posachedwapa zomwe amachotsa magazi ochepa m’thupi, n’kuwasakaniza ndi mankhwala ena kenako n’kuwabwezeretsanso.

MAFUNSO AMENE MUNGAFUNSE DOKOTALA

Ngati zikuoneka kuti madokotala akufuna kukupangani opaleshoni kapena kukupatsani mankhwala ophatikizapo zinthu zotengedwa m’magazi, onetsetsani kuti mwatenga khadi lopatsa munthu mphamvu yosasinthika yokusankhirani thandizo la mankhwala (DPA) ndipo mwachita zonse zofunikira kuti musaikidwe magazi. Kuwonjezera pamenepa, mungamufunse dokotala mafunso otsatirawa

  • Kodi onse amene akufuna kuchita nawo opaleshoniyi akudziwa kuti, monga wa Mboni za Yehova, ndalamula kuti zivute zitani ndisaikidwe magazi (magazi athunthu, maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana, kapena madzi a m’magazi)?

  • Ngati anena kuti mukufunikira mankhwala okhala ndi tizigawo ta magazi, kodi m’mankhwalamo muli zotani? Kodi mankhwala amenewa ndilandira ochuluka bwanji, nanga ndiziwagwiritsa ntchito bwanji?

  • Ngati chikumbumtima changa chikundilola kulandira kachigawo ka magazi, kodi pangakhale mavuto otani? Kodi ndi mankhwala ena ati amene ndingagwiritse ntchito m’malo mwa kachigawo ka magazika?

Musanasankhe chochita pa zimene takambiranazi, muuzeni Yehova nkhawa zanu m’pemphero. Iye analonjeza kuti azipereka nzeru kwa onse amene amapitiriza ‘kupempha ndi chikhulupiriro.’​—Yakobo 1:​5, 6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena