Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yp2 tsamba 134
  • Chitsanzo Chabwino Anyamata a Chiheberi Atatu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsanzo Chabwino Anyamata a Chiheberi Atatu
  • Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Nkhani Yofanana
  • Ayesedwa—Koma Akhulupirikabe kwa Yehova!
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Yehova Amafupa Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Buku la Danieli ndi Inu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
Onani Zambiri
Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
yp2 tsamba 134

Chitsanzo Chabwino Anyamata a Chiheberi Atatu

Hananiya, Misael, ndi Azariya anakana kugwadira fano lalikulu limene linaimikidwa ku Dura, pafupi ndi mzinda wa Babulo. Anthu onse amene analipo, anagwadira fanolo koma anyamatawa sanagonje ngakhale kuti mfumu inkawawopseza komanso anthu ena ankawakakamiza kuti agwadire fanolo. Ndipo anauza Nebukadinezara mwaulemu koma molimba mtima kuti iwo sangasiye kutumikira Yehova.—Danieli 1:6; 3:17, 18.

Anyamata amenewa anatengedwera ku ukapolo ku Babulo ali aang’ono. Iwo anali okhulupirika kuyambira ali ana ndipo anakana kudya chakudya chomwe mwina chinali choletsedwa m’Chilamulo cha Mulungu. Ndipo zimenezi zinawathandiza kuti atakula apirire mayesero ena. (Danieli 1:6-20) Iwo anadziwa kuti kumvera Yehova n’kopindulitsa kwambiri. Kodi inunso mwatsimikiza kutsatira malangizo a Mulungu ngakhale anzanu atakukakamizani kuti muchite zoipa? Mukaphunzira kumvera Yehova pazinthu zazing’ono, mudzathanso kukhala okhulupirika pazinthu zazikulu.—Miyambo 3:5, 6; Luka 16:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena