Nyimbo 43
Khalani Maso, Limbani, Khalani Amphamvu
Losindikizidwa
1. Khala maso, upirire,
Limba mpaka mapeto.
Limbikatu mwachamuna,
Udzapambana ndithu.
Pomvera lamulo la Khristu,
Ukhale kumbali ya Yesu.
(KOLASI)
Khala maso, khala wolimba!
Limba mpaka mapeto!
2. Khala maso, usagone,
Wokonzeka kumvera.
Uzimvera malamulo
Ochokera kwa Yesu.
Mvera malangizo ’akulu,
Omwe atetezera nkhosa.
(KOLASI)
Khala maso, khala wolimba!
Limba mpaka mapeto!
3. Khala maso, tetezera
Uthenga wabwinowu.
Ngakhale azikutsutsa,
Uzilalikirabe.
Lengeza mokondwa padziko,
Likubwera tsiku la M’lungu!
(KOLASI)
Khala maso, khala wolimba!
Limba mpaka mapeto!
(Onaninso Mat. 24:13; Aheb. 13:7, 17; 1 Pet. 5:8.)