Nyimbo 90
Ulemerero Umene Umabwera Chifukwa cha Imvi
Losindikizidwa
1. Pakati pathu pali
Achikulire.
Akukondabe M’lungu
Sanamusiye.
Ena imfa ya mnzawo
Ikuwawawa.
Tate atonthozeni,
N’kuwalimbitsa.
(KOLASI)
Mumakumbukira
Zochita zawo.
Tate auzeni:
“Mwachita bwino.”
2. Imvi za olungama
Ndi zokongola.
Zimasangalatsadi
Tate Yehova.
Ife tikumbukire
Pa nthawi ina
Pa unyamata wawo
Ankayesetsa.
(KOLASI)
Mumakumbukira
Zochita zawo.
Tate auzeni:
“Mwachita bwino.”
(Onaninso Sal. 71:9, 18; Miy. 20:29; Mat. 25:21, 23; Luka 22:28; 1 Tim. 5:1.)