Mutu 11
“Abusa Amene Mtima Wanga Wakonda”
1, 2. (a) Kodi chingachitike n’chiyani ngati nkhosa sizikutetezedwa? (b) Kodi kalekale m’busa wa nkhosa ankagwira ntchito zotani?
HIROYASU wa ku Japan ali mwana amayi ake anagula nkhosa yamphongo ndi yaikazi. Iye ankaweta nkhosazo ndipo nkhosa yaikaziyo inkabereka ana awiri chaka chilichonse, moti nkhosazo zinayamba kuchuluka. Pamene Hiroyasu ankafika zaka 12, nkhosazo zinali zitakwana 12 kapena 13. Hiroyasu anati: “Tsiku lina m’mawa ndisanadzuke ndinamva nkhosazo zikulira. Koma ine sindinapite kukaziona nthawi yomweyo. Ndiyeno nditapita ndinaona mimbulu yambirimbiri ikuchokera kumene kunali ana a nkhosa aja, ndipo inali itawakhadzulakhadzula. Kenako ndinayamba kufufuzafufuza nkhosa yaikazi ija, ndipo ndinaipeza ili magazi okhaokha, koma ikupumabe. Nkhosa yamphongo yokha ija ndi imene inapulumuka, ndipo zina zonse zinafa. Ndinamva chisoni kwambiri ndi zimene zinachitikazi. Sindinachite bwino posapita kukaona nkhosazo nditangomva kuti zikulira, chifukwa zinalibe woziteteza ku mimbuluyo.”
2 Kalekale pafupifupi aliyense ankadziwa bwino ntchito imene m’busa ankagwira. Iye ankapita ndi nkhosa zake kumalo amene kunali msipu wabwino komanso ankaonetsetsa kuti zikudya mokwanira. Iye ankazitetezanso ku zilombo zolusa komanso ankafunafuna nkhosa zosochera. (1 Sam. 17:34-36) M’busayo ankapatsa nkhosazo mpata woti zigone pansi n’kupumula popanda wozisokoneza. Ankathandizanso nkhosazo zikamabereka ndipo kenako ankasamalira anawo. Anthu ambiri amene analemba nawo Baibulo, kuphatikizapo Yeremiya, anagwiritsa ntchito fanizo la m’busa pofotokoza za munthu amene wapatsidwa udindo wosamalira anthu, monga wolamulira kapena wotsogolera anthu pa zinthu zauzimu.
3. Kodi Yeremiya ankanena za ndani pamene anagwiritsa ntchito mawu akuti “abusa” komanso ‘kuweta’?
3 Ena mumpingo wachikhristu angamaone akulu ngati abusa pa nthawi yokhayo imene akuluwo akuchezera abale kuti awathandize ndi kuwalimbikitsa. Koma tikaona mmene Yeremiya anagwiritsira ntchito mawu akuti “abusa” ndiponso akuti ‘kuweta,’ tingaone kuti iye anagwiritsa ntchito mawuwa pofotokoza zinthu zonse zimene oyang’anira a ku Yuda ankachitira anthu awo. Kawirikawiri Mulungu ankadzudzula akalonga, aneneri ndi ansembe a ku Yuda kuti anali abusa oipa chifukwa sankathandiza anthu wamba. (Yer. 2:8) Iwo ankazunza “nkhosa” zawo komanso ankazisocheretsa ndi kuzinyalanyaza, ndipo ankangochita zinthu zokomera iwowo. Choncho anthu a Mulungu anali omvetsa chisoni kwambiri chifukwa sankasamalidwa mwauzimu. Yehova ananena kuti abusa onyengawo adzakumana ndi “tsoka,” ndipo anatsimikizira anthu ake kuti adzawapatsa abusa achikondi amene azidzathandizadi nkhosa zawo ndi kuziteteza.—Werengani Yeremiya 3:15; 23:1-4.
4. Kodi ndani akusamalira nkhosa za Mulungu masiku ano, ndipo amasonyeza mtima wotani pochita zimenezi?
4 Lonjezo la Mulungu limeneli linakwaniritsidwa kwambiri kudzera mwa Yesu, yemwe ndi M’busa Wamkulu wa nkhosa za Yehova, ndipo anadzakhala Mutu wa mpingo wachikhristu. Yesu ananena kuti iye ndi “m’busa wabwino,” amene amamveradi chifundo anthu amene akuwatsogolera. (Yoh. 10:11-15) Masiku ano Yehova akugwiritsa ntchito abusa aang’ono, kuti azisamalira nkhosa zake padziko lapansi. Ena mwa abusa amenewa ndi abale odzozedwa amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndipo ena ndi akulu a m’gulu la “khamu lalikulu,” amene amagwira ntchito yawo mokhulupirika. (Chiv. 7:9) Abusa amenewa amayesetsa kusonyeza mtima wololera kuvutikira ena potengera chitsanzo cha Yesu. Iwo amatsanzira Khristu poyesetsa kudyetsa ndi kusamalira mpingo. Ndipotu m’busa aliyense amene amanyalanyaza kapena kupondereza abale komanso kuwachitira nkhanza kapena chipongwe, adzakumana ndi tsoka. (Mat. 20:25-27; 1 Pet. 5:2, 3) Kodi Yehova amafuna kuti abusa achikhristu azichita chiyani masiku ano? Kodi tikawerenga zimene Yeremiya analemba tikuphunzira kuti akulu ayenera kukhala ndi makhalidwe komanso zolinga zotani akamagwira ntchito yawo? Tsopano tiyeni tikambirane udindo umene akulu ali nawo wothandiza ndi kuteteza abale, kuphunzitsa mumpingo komanso mu utumiki, ndiponso kuweruza.
KUTETEZA NKHOSA
5-7. (a) Kodi Yehova amafuna kuti nkhosa zake zizisamalidwa motani, ndipo n’chifukwa chiyani amatero? (b) Kodi akulu angasonyeze bwanji chikondi chenicheni kwa abale awo, kuphatikizapo osochera?
5 Mtumwi Petulo ananena kuti Yehova ndi ‘m’busa wathu ndi woyang’anira miyoyo yathu.’ (1 Pet. 2:25) Kodi Mulungu amasonyeza mtima wotani kwa “nkhosa” zake? Tingapeze yankho tikaona zimene zinkachitika m’nthawi ya Yeremiya. Yehova atadzudzula abusa oipa amene ankamwaza ndi kunyalanyaza nkhosa, iye ananena kuti ‘adzasonkhanitsa’ nkhosa zake n’kuzibweretsanso kumalo odyera nkhosazo. Ndipo analonjeza kuti anthu akewo adzawaikira abusa abwino amene ‘adzawawetadi’ ndi kuonetsetsa kuti akutetezedwa kwa adani ankhanza. (Yer. 23:3, 4) Zoonadi, nkhosa za Yehova zinali zamtengo wapatali kwa iye. Masiku anonso Yehova amaona kuti nkhosa zake n’zamtengo wapatali. Iye anazigula ndi magazi amtengo wapatali kuti zidzapeze moyo wosatha.—1 Pet. 1:18, 19.
6 Mofanana ndi abusa a nkhosa zenizeni, oyang’anira achikhristu sayenera kunyalanyaza udindo wawo wosamalira mpingo. Ngati ndinu mkulu, kodi mumakhala tcheru kuti muone zizindikiro zilizonse zosonyeza kuti abale anu akuvutika, ndipo kodi mumakhala wofunitsitsa kuwathandiza mwamsanga? Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Uyenera kudziwa bwino maonekedwe a ziweto zako. Ika mtima wako pa magulu a ziweto zako.” (Miy. 27:23) Lemba limeneli likusonyeza kuti abusa a nkhosa zenizeni amakhala akhama, ndipo izi n’zimenenso abusa auzimu mumpingo ayenera kuchita posamalira nkhosa za Mulungu. Ngati ndinu mkulu, kodi mukuyesetsa mwakhama kupewa mtima wofuna kulamulira ena? Mfundo yakuti Petulo ananena za ‘kuchita ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu,’ ikusonyeza kuti n’zotheka ndithu kuti mkulu achite zimenezi. Ndiyeno kodi mungathandize bwanji kuti zimene zalembedwa pa Yeremiya 33:12 zitheke? (Werengani.) Makolo amene akulera okha ana, akazi amasiye, mabanja amene ali ndi ana opeza, komanso anthu achikulire ndi achinyamata, angafunike kuwasamalira ndi kuwathandiza mwapadera.
7 Mofanana ndi m’busa wa nkhosa zenizeni, nthawi zina abusa mumpingo angafunike kufunafuna ndi kuthandiza anthu amene pa zifukwa zina, anachoka pagulu la nkhosa n’kusochera. Kuti mkulu achite zimenezi, angafunike kulolera kuvutikira ena komanso kudzichepetsa. Iye ayenera kukhala woleza mtima komanso kuthera nthawi yokwanira akusamalira nkhosa zimene zili m’manja mwake. Akulu mumpingo angachite bwino kudzifunsa moona mtima kuti: ‘Kodi nthawi zambiri ndimayesetsa kulimbikitsa ena m’malo mowadzudzula kapena kuwaimba mlandu? Ngati ndikufunika kusintha pa mbali imeneyi, kodi ndine wofunitsitsa kutero?’ Nthawi zina pangafunike kuthandiza munthu mobwerezabwereza asanafike poona zinthu mmene Mulungu akuzionera. Ngati m’bale kapena mlongo akuzengereza kutsatira malangizo a m’Malemba (osati chabe maganizo a akuluwo), muzikumbukira chitsanzo cha Yehova, yemwe ndi M’busa komanso Woyang’anira Wamkulu. Moleza mtima, iye sanasiye kulankhula ndi anthu ake olowerera komanso sanasiye kuyesetsa kuwathandiza. (Yer. 25:3-6) Anthu ambiri a Mulungu masiku ano sachita zinthu zoipa, koma pakafunika kupereka uphungu, mkulu ayenera kupereka uphunguwo ngati mmene Yehova anachitira.
8. Kodi abusa auzimu angatsanzire bwanji Yeremiya?
8 Yeremiya anapempherera Ayuda anzake pa nthawi imene mwayi woti iwo angabwerere kwa Yehova unali udakalipo. Iye anauza Mulungu kuti: “Kumbukirani nthawi zonse zija pamene ndinaima pamaso panu kuwalankhulira zabwino kuti muwachotsere mkwiyo wanu.” (Yer. 18:20) Mungaone kuti mawu amenewa akusonyeza kuti Yeremiya ankawafunira zabwino abale ake, osati zoipa. Masiku anonso, oyang’anira achikhristu ayenera kutengera mtima wa Yeremiya, mpaka patapezeka umboni wokwanira wosonyeza kuti munthuyo sakufuna kulapa ndipo watsimikiza ndi mtima wonse kupitiriza kuchita zinthu zoipa. Ndipotu akulu angachite bwino kuyamikira ena chifukwa cha zabwino zimene akuchita komanso kuwapempherera ali nawo limodzi kapena ali kwaokha.—Mat. 25:21.
Pa nkhani ya abusa auzimu, kodi Mulungu analonjeza chiyani kudzera mwa Yeremiya? Kodi oyang’anira achikhristu angateteze bwanji nkhosa?
“ADZAKUTHANDIZANI KUDZIWA ZINTHU ZAMBIRI”
9, 10. Kodi n’chifukwa chiyani kuti munthu akhale m’busa (kapena kuti mkulu) wabwino, amafunika kuti akhale mphunzitsi?
9 Mogwirizana ndi zimene lemba la Yeremiya 3:15 likunena, abusa achikhristu ayenera kuthandiza ena kuti ‘adziwe zinthu zambiri ndiponso kumvetsa bwino zinthu.’ Zimenezi zikutanthauza kuti ayenera kukhala aphunzitsi. (1 Tim. 3:2; 5:17) Yehova analonjeza anthu ake kuti adzawapatsa abusa abwino omwe adzachite zimenezi. Ndipo analimbikitsa Ayudawo kuti azimvera mneneri wake Yeremiya amene ankawaphunzitsa zinthu zimene zikanawathandiza kusintha. (Werengani Yeremiya 6:8.) Nkhosa zimafunika kudya mokwanira kuti zikhale zathanzi. Mofanana ndi zimenezi, kuti anthu a Mulungu akhale athanzi mwauzimu, amafunika kuwadyetsa mwauzimu ndi kuwapatsa malangizo a m’Malemba.
10 Akulu amaphunzitsa m’njira ziwiri. Njira yoyamba, iwo amathandiza abale ndi alongo amene ali kale mumpingo wachikhristu. Ndipo njira yachiwiri, iwo amathandiza anthu amene si Akhristu oona. Pa nkhani yothandiza anthu amene si Akhristu oona, kumbukirani kuti: Chimodzi mwa zifukwa zikuluzikulu zimene mpingo wachikhristu unakhazikitsidwira n’choti Akhristu azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Choncho, akulu ayenera kukhala akhama pa ntchito yolalikira. (Yer. 1:7-10) Akamachita zimenezi, iwo amakwaniritsa udindo wawo pamaso pa Mulungu ndiponso amapereka chitsanzo chabwino kwa abale awo. Ngati ndinu mkulu mungavomereze kuti kulalikira nthawi zonse limodzi ndi abale komanso alongo osiyanasiyana, kumakupatsani mpata wowathandiza kuti akhale aluso pa ntchito yolalikira ndipo inunso mumawonjezera luso lanu. Komanso mukamatsogolera mwakhama pa ntchito yolalikira, mumalimbikitsa ena ndipo zimenezi zimathandiza kuti mpingo wonse uzipita patsogolo.
11, 12. Kodi mkulu amene akufuna kukhala m’busa wabwino ayenera kuganizira mozama za chiyani?
11 Zimene akulu amaphunzitsa mumpingo ziyenera kuchokera m’Baibulo. Zikatero ndiye kuti akuperekadi chakudya chabwino chauzimu. Choncho mungathe kuona kuti ngati abusa a mumpingo akufuna kuti akhale aphunzitsi ogwira mtima, ayenera kumaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama. Poganizira mfundo imeneyi, taonani chifukwa chimene Yeremiya anafotokoza kuti n’chimene chinkalepheretsa atsogoleri a m’nthawi yake kukhala abusa abwino. Iye anati: “Abusa achita zinthu mopanda nzeru, ndipo sanayese n’komwe kufunafuna Yehova. N’chifukwa chake sanachite zinthu mozindikira, ndipo ziweto zawo zonse zabalalika.” (Yer. 10:21) Anthu amene anayenera kukhala aphunzitsi sankatsatira mfundo za m’Malemba ndiponso sankafunafuna Mulungu. Choncho sankatha kuchita zinthu mwanzeru. Ndipo Yeremiya anadzudzulanso mwamphamvu kwambiri anthu amene ankadzitcha aneneri.—Werengani Yeremiya 14:14, 15.
12 Mosiyana ndi abusa onyenga amenewo, oyang’anira achikhristu amaphunzira za Yesu ndiponso amamutsanzira. Chifukwa chochita zimenezi, amakhala abusa anzeru a nkhosa za Mulungu. Koma popeza iwo amakhala ndi zochita zambiri ndipo nthawi imawachepera, angamavutike kupeza nthawi yophunzira Mawu a Mulungu. Ngati ndinu mkulu, kodi mumakhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene mumaphunzitsa nthawi zonse ziyenera kukhala zochokera m’Mawu a Mulungu ndiponso m’malangizo ochokera ku gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru? Mukamachita zimenezi, ndiye kuti muzitha kuphunzitsa zinthu zoona, zothandiza, komanso zosonyeza kuti mukudziwa zinthu ndiponso mukuzimvetsa bwino. Ngati mukuona kuti panopa simukuphunziranso Baibulo mwakhama ngati mmene munkachitira m’mbuyomu, kodi muchita chiyani kuti mupitirizebe kukhala osiyana ndi abusa onyenga a m’nthawi ya Yeremiya?
13. Kodi n’chiyani chinathandiza Yeremiya kuti akhale mphunzitsi wabwino, ndipo abusa achikhristu masiku ano angaphunzire chiyani kwa iye?
13 Chinthu china chimene chinachititsa kuti Yeremiya aziphunzitsa mogwira mtima kwambiri n’choti ankagwiritsa ntchito mafanizo. Ndipotu Yehova ndi amene ankamuuza mafanizo oti agwiritse ntchito. Mwachitsanzo, nthawi ina iye anaponya mtsuko pansi n’kuuphwanya kenako n’kunena kuti Yerusalemu ndi anthu okhala mumzindawo adzaphwanyidwa ngati mtsukowo. Anthu amene anamuona akuchita zimenezi sakanaiwala fanizo limeneli. (Yer. 19:1, 10, 11) Chitsanzo china n’choti Yeremiya anapanga goli lathabwa n’kuliika m’khosi mwake posonyeza kuti anthu a mtundu wake adzavutika kwambiri polamulidwa ndi Ababulo. (Yer. chaputala 27 ndi 28) Mulungu sanalamule akulu a mumpingo mwanu kuti azichita zinthu ngati zimenezi pofuna kutsindika mfundo. Koma kodi simuyamikira iwo akamagwiritsa ntchito mafanizo oyenera ndiponso zochitika zenizeni pophunzitsa? Zoonadi, mafanizo ndi zitsanzo zabwino zimakhala zamphamvu komanso zolimbikitsa.
14. (a) Kodi Yeremiya ankaganizira za chiyani pamene ananena za ‘mafuta a basamu mu Giliyadi’? (b) Kodi akulu achikhristu angathandize bwanji abale awo kuti akhale athanzi mwauzimu?
14 Tiyenera kuyamikira kwambiri abusa achikhristu chifukwa cha ntchito yophunzitsa imene akugwira. M’nthawi ya Yeremiya, iye ankaona kuti anthu a mtundu wake ankafunika kuwachiritsa mwauzimu. Iye anafunsa kuti: “Kodi mu Giliyadi mulibe mafuta a basamu? Kapena kodi mulibe wochiritsa mmenemo?” (Yer. 8:22) Dera la Giliyadi, lomwe linali mbali ya Isiraeli, kum’mawa kwa Yorodano, kunkapezeka mafuta a basamu enieni, ochokera ku mitengo ya basamu. Anthu ankagwiritsa ntchito mafuta onunkhirawa ngati mankhwala, ndipo kawirikawiri ankawapaka pachilonda kuti achepetse ululu kapena kuti chipole. Koma kunalibe mankhwala owachiritsa mwauzimu. Chifukwa chiyani? Yeremiya ananena kuti: “Aneneri akulosera monama, ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo. Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.” (Yer. 5:31) Nanga bwanji masiku ano? Inu mungavomereze kuti “mu Giliyadi,” kapena kuti mumpingo mwanu, muli “mafuta a basamu.” Mafuta a basamu omwe amachepetsa ululu tingawayerekezere ndi zimene abusa achikhristu amachita pogwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba akamalimbikitsa ndi kutsogolera abale, ndiponso akamawapempherera ali pomwepo kapena ali kwaokha.—Yak. 5:14, 15.
Kodi ndi njira ziti zimene akulu amumpingo mwanu amagwiritsa ntchito pophunzitsa, zimene mumaziyamikira kwambiri? N’chifukwa chiyani kuphunzitsa kwawo kumakhala kogwira mtima?
“YEHOVA WANENA KUTI”
15, 16. N’chifukwa chiyani nkhosa zenizeni komanso zauzimu zimafunika kuzisamalira?
15 Taganizirani mmene m’busa wa nkhosa amasangalalira nkhosa zake zikabereka ana athanzi. Iye amasangalala poona kuti ntchito imene wakhala akugwira mwakhama komanso kwa nthawi yaitali posamalira nkhosazo yamupindulira. Komabe, m’busayo amadziwa kuti ana a nkhosawo ndi ofunika kuwasamalira kuti akule bwino. Mwachitsanzo, m’busayo ayenera kuonetsetsa kuti ana a nkhosawo akudya mokwanira. Komanso mitundu ina ya nkhosa imabereka ana okhala ndi michira italiitali imene imakhwekhwereka m’ndowe kapena m’matope. Popeza m’busa amafuna kuti nkhosa zake zikhale zaukhondo komanso zathanzi, amatha kudulako michirayo, ndipo amachita zimenezi mosamala kuti ana a nkhosawo asamve kupweteka kwambiri. Abusa auzimu nawonso amasamalira mwachikondi nkhosa zawo, kapena kuti anthu amumpingo mwawo. (Yoh. 21:16, 17) Akulu amasangalalanso kwambiri akaona anthu achidwi akusintha moyo wawo kuti akhale Akhristu oona. Ndipo oyang’anira achikhristuwa amafuna kuti nkhosa zonse, zazikulu ndi zazing’ono zomwe, zikhale zathanzi ndiponso kuti zizidya mokwanira. Choncho iwo satopa kuzisamalira ndi kuzithandiza ngati pakufunika kutero. Ntchito imeneyi ikuphatikizapo kukumbutsa abale awo ‘zimene Yehova wanena,’ kapena kuti zimene Malemba akutiphunzitsa.—Yer. 2:2, 5; 7:5-7; 10:2; Tito 1:9.
16 Yeremiya ankafunika kulimba mtima kuti alengeze uthenga wochokera kwa Mulungu. N’chimodzimodzinso oyang’anira mumpingo, makamaka pa nthawi imene akufunika kulankhula mopanda mantha kuti ateteze abale awo. Mwachitsanzo, m’busa wauzimu angaone kuti akufunika kuchitapo kanthu kuti ateteze munthu amene ali ngati mwana wa nkhosa wongobadwa kumene, kapenanso ngati nkhosa yaikulu, kuti asadetsedwe ndi zoipa za m’dziko la Satanali. N’kutheka kuti munthu amene akufunika kuthandizidwayo sakufuna n’komwe kupatsidwa malangizo. Koma kodi m’busa wanzeru angangoima n’kumayang’anira nkhosa yake ina ikulowera kuphompho? Ayi sangatero. Ndipotu sangaone vuto limeneli mopepuka, n’kumaganiza kuti zonse zili bwino pamene kwenikweni n’zoonekeratu kuti sizili bwino, chifukwa zingachititse kuti mtumiki mnzakeyo asakhalenso pa mtendere ndi Yehova.—Yer. 8:11.
17. Kodi m’busa angafunike kusamalira nkhosa zina mwapadera pa nthawi iti ndipo angachite bwanji zimenezi?
17 Ngati nkhosa itatengeka n’kuchoka pagulu la nkhosa zina, m’busa watcheru angaibweze mwamsanga kuti isachoke pamalo otetezeka. (Werengani Yeremiya 50:6, 7.) Mofanana ndi zimenezi, nthawi zina woyang’anira angafunike kulankhula mwamphamvu koma mwachikondi ndi anthu amene akuchita zinthu zimene zingawagwetse m’mavuto. Mwachitsanzo, mkulu angaone kuti mwamuna ndi mkazi amene ali pachibwenzi akumacheza okhaokha popanda munthu wowaperekeza, pamalo amene angathe kuchita tchimo mosavuta. Mkulu wokoma mtima komanso wozindikira angathandize anthu amenewa kuti apewe kuchita zimenezo, chifukwa zingawagwetse m’mavuto. Mosamala mkuluyo angapewe kuwaimba mlandu, koma angawauze zinthu zina zimene zingachitike ngati atapitiriza kumakhala awiriwiri, zomwe zingachititse kuti Yehova adane nawo. Mofanana ndi Yeremiya, akulu okhulupirika amadana ndi zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Choncho iwo amatsanzira Yehova, amene moleza mtima, anachonderera anthu ake kudzera mwa mneneri wake kuti: “Chonde, musachite zinthu zonyansa zoterezi zimene ndimadana nazo.” (Yer. 5:7; 25:4, 5; 35:15; 44:4) Kodi inuyo mumayamikira kuchokera pansi pa mtima chikondi chimene abusa amasonyeza nkhosa za Mulungu?
18. Kodi abusa auzimu akamagwira ntchito yawo mwakhama pamakhala zotsatira zotani zolimbikitsa?
18 N’zoona kuti si anthu onse amene Yeremiya ankawapatsa malangizo amene anamumvera. Koma ena anamumvera. Mwachitsanzo, pamene Baruki, mnzake wa Yeremiya komanso mlembi wake, ankafunika uphungu wamphamvu, Yeremiya anam’patsa uphunguwo mosazengereza. (Yer. 45:5) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Baruki anapitiriza kukondedwa ndi Mulungu ndipo anapulumuka pamene mzinda wa Yerusalemu unkawonongedwa. Mofanana ndi zimenezi, akulu masiku ano akaona kuti ntchito yawo yothandiza Akhristu anzawo ikubala zipatso zabwino, amalimbikitsidwa ‘kupitiriza kukhala odzipereka podandaulira ndi kuphunzitsa’ abale awo, chifukwa amadziwa kuti ntchito imeneyi ndi yopulumutsa miyoyo.—1 Tim. 4:13, 16.
KUPEREKA CHILANGO “PAMLINGO WOYENERA”
19, 20. Kodi akulu ali ndi udindo wotani akamathandiza anthu ochimwa?
19 Ntchito ina ya oyang’anira masiku ano ndi yokhala oweruza auzimu. Nthawi zina akulu angafunike kukambirana ndi anthu amene akuchita tchimo mwadala, n’cholinga chowathandiza kuti alape. Mokoma mtima koma mosapita m’mbali, Yehova analimbikitsa anthu amene ankachita zoipa kuti asiye kuchita zoipazo. (Yer. 4:14) Koma ngati mumpingo muli munthu amene sakufuna kusiya tchimo limene akuchita, oyang’anira ayenera kuchitapo kanthu kuti ateteze nkhosa ku makhalidwe oipa a munthuyo, amene angathe kuwononga mpingo. Potsatira malangizo a m’Malemba, iwo angafunike kuchotsa wochimwayo mumpingo. Pa nkhani zoterezi, Yehova amafuna kuti akulu azichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. Mfumu Yosiya n’chitsanzo chabwino cha munthu amene ankachita zimenezi. Iye ankatsanzira Mulungu, yemwe amakonda chilungamo, ndipo “anali kunenera mlandu anthu osautsika ndi osauka.” Poganizira zimene Yosiya anachitazi, Yehova anafunsa kuti: “Kodi sanachite zimenezi chifukwa chakuti anali kundidziwa?” Popeza Yosiya ankachita zinthu mwachilungamo, ‘zinthu zinamuyendera bwino.’ Kodi si zoona kuti inuyo mumaona kuti ndinu otetezeka, akulu a mumpingo mwanu akamayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yosiya?—Yer. 22:11, 15, 16.
20 Musakayikire kuti anthu ochimwa, Yehova amawalanga “pamlingo woyenera.” (Yer. 46:28) Choncho, mogwirizana ndi mmene zinthu zilili komanso mtima umene munthuyo wasonyeza, akulu angafunike kupereka uphungu, kulimbikitsa, kapena kudzudzula Akhristu anzawo. Ndipo nthawi zina angafunike kuchotsa mumpingo wochimwa amene sanalape. Zikatero akulu akamapemphera pagulu, sapempherera munthu wochotsedwa amene akupitirizabe kuchita tchimo, chifukwa kuchita zimenezi kulibe tanthauzo lililonse.a (Yer. 7:9, 16) Komabe potsanzira Mulungu, iwo amauza munthu wochotsedwayo zoyenera kuchita kuti Mulungu ayambirenso kumukonda. (Werengani Yeremiya 33:6-8.) Ngakhale kuti zimakhala zowawa munthu akachotsedwa mumpingo, dziwani kuti mfundo za Mulungu n’zolungama komanso zopindulitsa tonsefe.—Maliro 1:18.
21. Kodi moyo wa nkhosa za Mulungu uyenera kukhala wotani, ndipo ifeyo tingachite chiyani kuti zimenezi zitheke?
21 Abusa mumpingo akazindikira mfundo zouziridwa ndi Mulungu n’kumazigwiritsa ntchito, nkhosa zimadyetsedwa bwino, zimakhala zathanzi, komanso zimakhala zotetezeka. (Sal. 23:1-6) Choncho zimene Yeremiya akutiuza zokhudza maganizo ndi zolinga za anthu, kaya zoipa kapena zabwino, zingathandize kwambiri oyang’anira achikhristu pamene akugwira ntchito yofunika kwambiri yosamalira nkhosa za Mulungu. Chotero aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndipitiriza kugwirizana ndi akulu mumpingo posonyeza kuti ndikuyamikira njira imene Yehova akugwiritsa ntchito pophunzitsa, kulangiza ndi kuteteza anthu ake?’ Ndi bwino kuchita zimenezi chifukwa abusa amenewa ‘akuwetadi’ nkhosa za Mulungu ndi kuzithandiza “kudziwa zinthu zambiri ndiponso kumvetsa bwino zinthu.”—Yer. 3:15; 23:4.
Kodi ndi pa nthawi iti pamene oyang’anira amafunika kuchita zinthu molimba mtima? Kodi Yehova amafuna kuti akulu achikhristu azichita zinthu motani akamaweruza milandu?