Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yc phunziro 8 tsamba 18-19
  • Yosiya Anali ndi Anzake Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yosiya Anali ndi Anzake Abwino
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Yofanana
  • Yosiya Anachita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Yosiya Ankakonda Chilamulo cha Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Mfumu Yabwino Yomaliza
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Phunzitsani Ana Anu
yc phunziro 8 tsamba 18-19
Mfumu Yosiya akumvetsera mnzake Yeremiiya

PHUNZIRO 8

Yosiya Anali ndi Anzake Abwino

Kodi ukuganiza kuti kuchita zinthu zabwino n’kovuta?— Anthu ambiri amaganiza choncho. Baibulo limatiuza kuti zinali zovuta kwambiri kwa mnyamata wina, dzina lake Yosiya, kuti achite zinthu zabwino. Koma anali ndi anzake abwino amene anamuthandiza. Tiye tikambirane za Yosiya ndi anzakewo.

Abambo ake a Yosiya anali Amoni ndipo anali mfumu ya Yuda. Amoni anali munthu woipa kwambiri ndipo ankalambira mafano. Atamwalira, Yosiya anakhala mfumu ya Yuda. Koma pa nthawiyi n’kuti Yosiya ali ndi zaka 8 zokha. Kodi ukuganiza kuti nayenso anali woipa ngati bambo ake?— Ayi, sanali woipa.

Mneneri Zefaniya kuuza anthu a ku Yuda uthenga wochokera kwa Yehova

Zefaniya anauza anthu kuti asamalambire mafano

Kuyambira ali mwana, Yosiya ankafuna kumvera Yehova. Choncho ankacheza ndi anthu okhawo amene ankakonda Yehova. Anthu amenewa anathandiza Yosiya kuti azichita zinthu zabwino. Kodi anzake ena a Yosiya anali ndani?

Mnzake wina anali Zefaniya. Zefaniya anali mneneri amene anachenjeza anthu a ku Yuda kuti adzakumana ndi zinthu zoopsa ngati angamalambire mafano. Yosiya anamvera Zefaniya ndipo ankalambira Yehova, osati mafano.

Mnzake wina wa Yosiya anali Yeremiya. Anali wofanana naye msinkhu ndipo ankakhala moyandikana komanso anakulira limodzi. Ankagwirizana kwambiri moti Yosiya atamwalira, Yeremiya analemba nyimbo yosonyeza kuti ankamusowa kwambiri Yosiya. Yeremiya ndi Yosiya ankathandizana kuti onse azilambira Yehova komanso kuti azichita zinthu zabwino.

Yosiya ndi Yeremiya ankathandizana kuti onse azichita zinthu zabwino

Kodi waphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yosiya?— Kuyambira ali wamng’ono, Yosiya ankafuna kuchita zabwino. Ankadziwa kuti ayenera kumacheza ndi anthu amene amakonda Yehova. Nawenso uzionetsetsa kuti ukucheza ndi anthu amene amakonda Yehova ndiponso amene angakuthandize kuti uzichita zinthu zabwino.

WERENGANI MAVESI AWA

  • 2 Mbiri 33:21-25; 34:1, 2; 35:25

MAFUNSO:

  • Kodi bambo a Yosiya anali ndani? Kodi nawonso ankachita zinthu zabwino?

  • Kodi Yosiya ankafuna kuchita zinthu zotani kuyambira ali mwana?

  • Tchula mayina awiri a anzake a Yosiya?

  • Kodi ungatsatire bwanji chitsanzo cha Yosiya?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena