Nyimbo 141
Kufufuza Anthu Okonda Mtendere
Yesu anatilamula kuti
tiuze anthu uthenga.
Amve mawu a Yehova.
Ankakonda nkhosa za Mulungu.
Ankazifufuza
mwakhama tsiku lonse.
Nyumba ndi nyumba, mumsewu
Timalalika kwa anthu,
Kuti posachedwa mavuto atha.
(KOLASI)
Tifufuze
okonda mtendere m’dzikoli.
Tiwapeze
Ofuna kupulumutsidwa.
Tifufuze
Paliponse.
Tifufuzabe anthu mwa khama.
Alipo ambiri
omwe tingathe kuwathandiza.
Poti timawakonda kwambiri,
Tibwererekonso
Tikawalimbikitse.
M’matauni, ndi m’midzinso,
Tikapeza omvetsera,
Timasangalala powaphunzitsa.
(KOLASI)
Tifufuze
okonda mtendere m’dzikoli.
Tiwapeze
Ofuna kupulumutsidwa.
Tifufuze
Paliponse.
(Onaninso Yes. 52:7; Mat. 28:19, 20; Luka 8:1; Aroma 10:10.)