MUTU 14
Kuyesetsa Kuti Anthu Mumpingo Apitirize Kukhala Amtendere Komanso Oyera
CHAKA chilichonse anthu ambirimbiri amakhamukira kunyumba ya Yehova komwe ndi kulambira koyera ndipo zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. (Mika 4:1, 2) Timasangalala kwambiri kulandira anthu amenewa mu “mpingo wa Mulungu.” (Mac. 20:28) Anthuwa amayamikira mwayi umene ali nawo wotumikira nafe limodzi Yehova ndiponso mwayi wosangalala m’Paradaiso wauzimu wamtendere. Mzimu woyera wa Mulungu ndiponso malangizo anzeru a m’Mawu ake zimatithandiza kuti tipitirize kukhala mwamtendere komanso kuti mpingo ukhalebe woyera.—Sal. 119:105; Zek. 4:6.
2 Tikamatsatira malangizo a m’Baibulo timavala “umunthu watsopano.” (Akol. 3:10) Timanyalanyaza zolakwa zing’onozing’ono zimene ena angatichitire. Kuona zinthu mmene Yehova amazionera kumatithandiza kuti tisatengere zochita za anthu a m’dzikoli zomwe zimagawanitsa anthu ndipo timagwira ntchito mogwirizana ndi abale athu apadziko lonse lapansi.—Mac. 10:34, 35.
3 Komabe nthawi zina mu mpingo mumayambika mavuto ena omwe angasokoneze mtendere kapenanso kuchititsa kuti usakhale woyera. Kodi chimayambitsa mavuto amenewa n’chiyani? Nthawi zambiri mavutowo amayamba chifukwa chakuti ena sakutsatira malangizo a m’Baibulo. Tiyenera kupitirizabe kumvetsetsana chifukwa tonsefe ndife opanda ungwiro ndipo palibe amene samalakwitsa zinthu zina. (1 Yoh. 1:10) Wina angachite zinthu zina zimene zingapangitse kuti mu mpingo musakhale makhalidwe abwino ndiponso kuti usakhale woyera. Tingakhumudwe kapena kukhumudwitsa munthu wina chifukwa chochita zinthu kapena kulankhula mosaganiza bwino. (Aroma 3:23) Zimenezi zikachitika, kodi tingatani kuti zinthu ziyambirenso kuyenda bwino?
4 Mwachikondi, Yehova anaganizira zinthu zimenezi ndipo Mawu ake amatiuza zoyenera kuchita. Akulu, omwe ndi abusa auzimu, amaperekanso thandizo lauzimu kwa aliyense payekha. Tikamatsatira malangizo awo ochokera m’Malemba, tingayambirenso kukhala mwamtendere ndi ena ndiponso tingakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Tikapatsidwa malangizo kapena kudzudzulidwa chifukwa choti talakwitsa zinthu zinazake, tiyenera kuona kuti ndi umboni wakuti Atate wathu wakumwamba amatikonda.—Miy. 3:11, 12; Aheb. 12:6.
KUTHETSA KUSAMVANA PA NKHANI ZING’ONOZING’ONO
5 Nthawi zina anthu mu mpingo akhoza kusemphana maganizo pa nkhani zing’onozing’ono. Zikatero, nkhani zimenezi ziyenera kuthetsedwa mwamsanga komanso mwachikondi. (Aef. 4:26; Afil. 2:2-4; Akol. 3:12-14) Nthawi zambiri tikasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzathu, tingathetse nkhaniyo potsatira malangizo a mtumwi Petulo akuti: “Khalani okondana kwambiri, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) Baibulo limanena kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2) Ngati titamatsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizichitira anthu zimene tingakonde kuti nawonso atichitire, tikhoza kumakhululuka ndiponso kuiwala zolakwa zing’onozing’ono zimene anthu ena angatichitire.—Mat. 6:14, 15; 7:12.
6 Mukaona kuti wina wakhumudwa ndi zimene munalankhula kapena kuchita, muyenera kuyesetsa mwamsanga kuchita zimene zingathandize kuti mugwirizanenso. Muzikumbukira kuti kusemphana maganizo ndi anthu ena mu mpingo kungasokonezenso ubwenzi wanu ndi Yehova. N’chifukwa chake Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Choncho ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.” (Mat. 5:23, 24) Zingachitike kuti mwakhumudwitsana chifukwa chosamvetsetsana chabe pa nkhani zina. Zikatero, simuyenera kusiya kulankhulana. Anthu mu mpingo akamalankhulana momasuka, zimathandiza kuti pasamakhale mavuto obwera chifukwa chosamvetsetsana ndiponso zimathandiza kuthetsa mavuto omwe amayamba chifukwa cha kupanda ungwiro.
KUPEREKA MALANGIZO OYENERA A M’MALEMBA
7 Nthawi zina oyang’anira angaone kuti m’pofunika kupereka malangizo kuti athandize munthu amene sakuganiza bwino. Kuchita zimenezi n’kovuta nthawi zina. Mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Galatiya kuti: “Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu, yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.”—Agal. 6:1.
8 Akamaweta nkhosa mwachikondi, akulu angateteze mpingo ku zinthu zambiri zimene zingauwononge mwauzimu ndiponso angateteze kuti musakhale mavuto aakulu. Akulu amayesetsa kuti utumiki umene amachita mu mpingo ufanane ndi zimene Yehova analonjeza anthu kudzera mwa Yesaya kuti: “Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.”—Yes. 32:2.
KUIKA CHIZINDIKIRO ANTHU OCHITA ZOSALONGOSOKA
9 Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu anzake kuti asamale ndi anthu ena omwe akhoza kusokoneza mpingo. Iye anawauza kuti: “Tikukulangizani abale . . . kuti mupewe m’bale aliyense woyenda mosalongosoka komanso mosagwirizana ndi mwambo umene tinakupatsani.” Anamveketsa mfundoyi ponena kuti: “Ngati wina sakumvera mawu athu a m’kalatayi, muikeni chizindikiro ndipo lekani kuchitira naye zinthu limodzi, kuti achite manyazi. Komabe musamuone monga mdani, koma pitirizani kumulangiza monga m’bale.”—2 Ates. 3:6, 14, 15.
10 Nthawi zina munthu yemwe sanachite tchimo lalikulu loti n’kuchotsedwa nalo mu mpingo, akhoza kumachita zinthu mochita kuonetseratu kuti salemekeza malamulo a Mulungu omwe Akhristu ayenera kutsatira. Zochita za munthuyo zingaphatikizepo kukhala waulesi kwambiri, kumangolankhula zoipa zokhazokha zokhudza mpingo komanso anthu ena, kapena kukhala wauve kwambiri. Mwinanso ‘angamalowerere nkhani zimene sizikumukhudza.’ (2 Ates. 3:11) Angakhalenso munthu wokonda kudyera anzake masuku pamutu kapena wokonda zosangalatsa zochita kuonekeratu kuti n’zosayenera. Khalidwe loipa la anthu amenewa, likhoza kuipitsa mbiri ya mpingo komanso kufalikira kwa Akhristu ena.
11 Choyamba, akulu angayesetse kumuthandiza munthuyo pom’patsa malangizo a m’Baibulo. Koma ngati munthuyo akupitirizabe kunyalanyaza mfundo za m’Baibulo atachenjezedwa mobwerezabwereza, akulu angaone kuti m’pofunika kukamba nkhani yochenjeza mpingo. Akulu angaone ngati khalidwelo lafika poipa moti n’kusokoneza ena komanso ngati pakufunikadi kukamba nkhani. Wokamba nkhaniyo ayenera kupereka malangizo okhudza khalidwe losalongosokalo koma sayenera kutchula dzina la munthu amene akuchita khalidwelo. Zimenezi zidzathandiza anthu ena kuti apewe kugwirizana ndi munthu amene amachita khalidwe lomwe likufotokozedwa mu nkhaniyo, ngakhale kuti angapitirize kuchitira naye limodzi zinthu zauzimu komanso “kumulangiza monga m’bale.”
12 Akhristu akamachita zinthu mokhulupirika zingathandize kuti munthu wochita zosalongosokayo achite manyazi n’kusintha. Zikaoneka kuti munthuyo wasintha, si bwino kumamuonabe ngati wosokoneza.
KUSAMALIRA ZOLAKWA ZINA ZIKULUZIKULU
13 Kunyalanyaza zolakwa za ena komanso kukhululuka sikumasonyeza kuti ndife olekerera zinthu kapena kuti tikugwirizana ndi khalidwe loipalo. Sikuti zolakwa zonse zimachitika chifukwa chopanda ungwiro. Komanso sizingakhale zothandiza kunyalanyaza zolakwa zikuluzikulu. (Lev. 19:17; Sal. 141:5) Pangano la Chilamulo linkasonyeza kuti machimo ena anali aakulu kuposa ena ndipo ndi mmenenso zilili mu mpingo wachikhristu.—1 Yoh. 5:16, 17.
14 Yesu anafotokoza njira yothetsera mavuto obwera chifukwa choti Akhristu awiri asemphana maganizo pa nkhani zikuluzikulu. Taonani zinthu zitatu zimene ananena. Anati: “Ngati m’bale wako wachimwa, [1] upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, [2] upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. Akapanda kuwamvera amenewanso, [3] uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvera mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.”—Mat. 18:15-17.
15 Malinga ndi fanizo limene Yesu ananena pambuyo pa mfundo zimenezi, lomwe lili pa Mateyu 18:23-35, zikusonyeza kuti ena mwa machimo amene akufotokozedwa pa Mateyu 18:15-17 ndi okhudza ndalama kapena katundu. Mwina munthu wina angalephere kubweza ngongole kapena angachitire nzake zachinyengo. Kapenanso ingakhale miseche imene ikhoza kuipitsa kwambiri mbiri ya munthu wina.
16 Ngati muli ndi umboni woti munthu winawake wakuchimwirani mwanjira imeneyi, musafulumire kukanena kwa akulu n’cholinga choti akuthetsereni nkhaniyo. Mogwirizana ndi malangizo a Yesu, muyenera choyamba kukambirana ndi munthu amene wakulakwiraniyo. Yesetsani kuthetsa nkhaniyo muli awiri popanda kulowetsapo munthu wina. Kumbukirani kuti Yesu sananene kuti ‘upite kamodzi kokha kukam’fotokozera cholakwacho.’ Choncho ngati munthuyo sanavomereze kulakwa kwake ndiponso kupempha kuti mumukhululukire, zingakhale bwino ngati mutapitanso kukakambirana naye nthawi ina. Ngati mungathetse nkhani mwa njira imeneyi, munthu amene anakulakwiraniyo angayamikire kuti simunauze ena za tchimo lakelo kapena kumuipitsira mbiri mu mpingo. Mukatero ‘ndiye kuti mwabweza m’bale wanuyo.’
17 Ngati munthu amene wakulakwiraniyo wavomereza kulakwa kwake n’kupepesa ndiponso wakonza zimene analakwitsazo, palibe chifukwa choikokera nkhaniyo. Ngakhale kuti nkhaniyo inali yaikulu, anthu awiri olakwiranawo akhoza kuithetsa okha.
18 Ngati mwalephera kubweza mbale wanu mutamufotokozera cholakwacho ‘panokha inuyo ndi iyeyo,’ mungachite zimene Yesu ananena, zoti ‘mupiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri’ n’kukakambirana nayenso. Amene mwawatengawo ayeneranso kukhala ndi cholinga chofuna kubweza mbale wanuyo. Zingakhale bwino ngati mutatenga anthu amene analipo pamene munthuyo ankapalamula mlanduwo. Koma ngati palibe anthu ena amene anaona zinthuzo zikuchitika, mungasankhe abale ena kuti akakhale mboni pamene mukukambirana nkhaniyo. Abalewo akhale oti akudziwa bwino mmene nkhani za mtundu umenewo zimayendera kuti athe kudziwa ngati zinthu zinalakwikadi kapena ayi. Akulu amene mungawasankhe kuti akhale mboni saimira mpingo, chifukwa sanachite kusankhidwa ndi bungwe la akulu.
19 Ngati nkhaniyo sinathe mutakambirana naye kangapo, pa awiri komanso ndi mboni zina, ndipo mukuona kuti simungangoisiya, mukhoza kuuza akulu mu mpingo. Kumbukirani kuti cholinga chawo ndi kutetezera kuti mpingo ukhalebe woyera komanso kuti anthu apitirize kukhala mwamtendere. Mukauza akulu nkhaniyo, asiyireni kuti aisamalire ndipo simuyenera kukayikira zoti Yehova akuthandizani kuithetsa. Musalole kuti khalidwe la munthu wina likukhumudwitseni kapena kukulepheretsani kutumikira Yehova mosangalala.—Sal. 119:165.
20 Akulu akafufuza nkhaniyo n’kupeza umboni wakuti munthuyo anakulakwiranidi koma sakufuna kulapa ndi kusintha, angafunikire kumuchotsa mu mpingo. Akamachita zimenezi amateteza gulu la nkhosa komanso mpingo umakhala woyera.—Mat. 18:17.
KUWERUZA MILANDU IKULUIKULU
21 Machimo ngati chigololo, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, kuchitira mwano Mulungu, mpatuko, kupembedza mafano ndi machimo ena akuluakulu ngati amenewa, amafuna zambiri kuposa kungokhululukidwa ndi munthu amene walakwiridwa. (1 Akor. 6:9, 10; Agal. 5:19-21) Machimo akuluakulu ngati amenewa ayenera kufotokozedwa kwa akulu kuti awasamalire chifukwa akhoza kusokoneza mpingo komanso kuchititsa kuti usakhale woyera. (1 Akor. 5:6; Yak. 5:14, 15) Anthu ena amapita kwa akulu kukaulula za tchimo limene achita kapena kukawadziwitsa za tchimo limene ena achita. (Lev. 5:1; Yak. 5:16) Kaya akulu adziwa bwanji za tchimo lalikulu limene wa Mboni wobatizidwa wachita, ayenerabe kusankha akulu awiri kuti akafufuze nkhaniyo. Ngati apeza kuti zimene amvazo ndi zoona ndipo pali umboni wosonyeza kuti Mkhristuyo anachitadi tchimo lalikulu, bungwe la akulu lidzasankha komiti yoweruza yokhala ndi akulu atatu kapena kuposa.
22 Akulu amayesetsa kuyang’anira bwino nkhosa ndi kuziteteza ku chinthu chilichonse chimene chingawononge nkhosazo mwauzimu. Amayesetsanso kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwanzeru kuti alangize anthu amene achita tchimo ndiponso kuwathandiza kuti achire mwauzimu. (Yuda 21-23) Zimenezi zikugwirizana ndi malangizo amene mtumwi Paulo anapereka kwa Timoteyo akuti: “Pamaso pa Mulungu ndi pa Khristu Yesu, amene anaikidwiratu kudzaweruza amoyo ndi akufa, . . . ndikukulamula mwamphamvu kuti, . . . dzudzula, tsutsa, dandaulira. Chita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri.” (2 Tim. 4:1, 2) Kuchita zimenezi kumafuna nthawi, komabe imeneyi ndi mbali ya ntchito zikuluzikulu zimene akulu amachita. Mpingo umayamikira khama lawo ndipo umaona kuti ayenera kupatsidwa “ulemu waukulu.”—1 Tim. 5:17.
23 Nthawi zonse munthu akapezeka kuti wachitadi tchimo, chinthu choyamba chimene akulu amachita ndi kuyesetsa kuthandiza wolakwayo kuti achire mwauzimu. Ngati munthuyo wathandizidwa ndipo walapa mochokera pansi pamtima, chidzudzulo chimene amam’patsa mwamseri kapena pamaso pa anthu amene akudziwa za nkhaniyo, chimam’thandiza komanso chimathandiza anthu enawo kuti aphunzirepo kanthu. (2 Sam. 12:13; 1 Tim. 5:20) Nthawi zonse munthu akadzudzulidwa ndi komiti yoweruza, amaletsedwa kuchita zinthu zina. Zimenezi zimathandiza wolakwayo kuti ‘awongole njira’ zake. (Aheb. 12:13) M’kupita kwa nthawi amapatsidwa mwayi woti ayambirenso kuchita zinthu zimene analetsedwa zija ngati akusonyeza kuti akuchira mwauzimu.
KULENGEZA ZOTI MUNTHU WADZUDZULIDWA
24 Ngati komiti yoweruza yatsimikizira kuti munthuyo ndi wolapa koma zikuoneka kuti nkhaniyo idziwika kwa anthu ena mu mpingo kapena m’dera limene amakhala, kapenanso ngati akulu akuona kuti mpingo ukufunika kusamala naye munthuyo ngakhale kuti walapa, angapereke chilengezo chachidule pa nthawi ya Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu. Ayenera kulengeza kuti: “[Dzina la munthuyo] wadzudzulidwa.”
NGATI AGAMULA ZOTI MUNTHUYO ACHOTSEDWE
25 Nthawi zina munthu wochimwayo angakhale kuti sakufuna kusintha ngakhale kuti akulu ayesetsa kumuthandiza. Zikhoza kutheka kuti sanaonetse mokwanira “ntchito zosonyeza kulapa” pa nthawi imene akulu amaweruza nkhaniyo. (Mac. 26:20) Kodi zikatere angatani? Munthu wosalapayo ayenera kuchotsedwa mu mpingo kuti asamachite zinthu ndi anthu oyera a Yehova. Kuchotsa munthuyo kumathandiza kuti asasokoneze mpingo komanso kumateteza mpingowo kuti upitirizebe kukhala woyera ndiponso ndi mbiri yabwino. (Deut. 21:20, 21; 22:23, 24) Atamva za khalidwe loipa la munthu wina wa mu mpingo wa ku Korinto, mtumwi Paulo analangiza akulu mu mpingowo kuti ‘apereke munthuyo kwa Satana . . . , n’cholinga choti mzimu [wa mpingo] upulumutsidwe.’ (1 Akor. 5:5, 11-13) Paulo anafotokozanso za anthu ena a munthawi yake amene anachotsedwa mu mpingo chifukwa chochita zinthu zosemphana ndi choonadi.—1 Tim. 1:20.
26 Ngati komiti yoweruza yagamula kuti munthu wosalapayo achotsedwe, ayenera kumudziwitsa zimene agamulazo ndiponso kumufotokozera zifukwa za m’Malemba zimene wachotsedwera. Ayeneranso kumufotokozera kuti ngati akuona kuti nkhaniyo sinaweruzidwe bwino ndipo akufuna kuchita apilo, ayenera kulemba kalata ndipo afotokoze momveka bwino chifukwa chimene akuchitira apilo. Munthuyo adzapatsidwa masiku 7 oti achite apilo kuchokera pa tsiku limene komitiyo inagamula nkhaniyo. Bungwe la akulu likalandira kalata ya apilo ya munthuyo, lidzadziwitsa woyang’anira dera yemwe adzasankhe akulu oyenerera oti akhale m’komiti ya apilo imene idzamvetserenso nkhaniyo. Abale a m’komitiyi adzayesetsa kumvetseranso nkhaniyo pasanathe mlungu umodzi kuchokera pamene alandira kalatayo. Ngati munthu wachita apilo, akulu ayenera kudikira kaye asanalengeze zimene anagamula. Pa nthawi imene akudikira zimene komiti ya apilo ingagamule, munthuyo ayenera kuletsedwa kuchita zinthu zina, monga kuyankha komanso kupemphera pa misonkhano ndiponso ayenera kuimitsidwa ngati anali ndi utumiki winawake wapadera.
27 Mwayi wochita apilo ndiponso womvetseranso nkhani yake umaperekedwa kwa wolakwayo pongofuna kumukomera mtima. Choncho, ngati wolakwayo sakufuna kuonana ndi abale a m’komiti ya apilo, akulu adzalengeza zoti munthuyo wachotsedwa pambuyo poti ayesetsa kuti akumane naye.
28 Ngati wolakwayo sakufuna kuchita apilo, abale a m’komiti yoweruza adzamufotokozera kufunika kolapa komanso zimene angachite kuti adzabwezeretsedwe m’tsogolo. Zimenezi zingamuthandize kwambiri ndipo akuluwo ayenera kumufotokozera mokoma mtima pokhulupirira kuti munthuyo akhoza kusintha khalidwe lake n’kubwerera m’gulu la Yehova.—2 Akor. 2:6, 7.
KULENGEZA AMENE WACHOTSEDWA
29 Komiti yoweruza ikagamula kuti munthu wosalapayo achotsedwe mu mpingo, pamaperekedwa chilengezo chachidule chonena kuti: “[Dzina la munthuyo] salinso wa Mboni za Yehova.” Kulengezaku kumathandiza kuti anthu mu mpingo asiye kucheza ndi munthuyo.—1 Akor. 5:11.
ANTHU ODZILEKANITSA NDI MPINGO
30 Mawu akuti “kudzilekanitsa” amanena za wa Mboni wobatizidwa amene wasankha kuti sakufuna kudziwikanso monga wa Mboni za Yehova ndipo wachita kunena yekha. Kapena zochita zake zingasonyeze kuti sakufunanso kukhala mu mpingo wachikhristu. Angasonyeze zimenezi ngati walowa bungwe lomwe zolinga zake ndi zosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, moti ndi loyenera kuweruzidwa ndi Yehova Mulungu.—Yes. 2:4; Chiv. 19:17-21.
31 Mtumwi Yohane analemba za anthu ena a mu nthawi yake amene anasiya Chikhristu kuti: “Anachoka pakati pathu, koma sanali m’gulu lathu, chifukwa akanakhala a m’gulu lathu, akanakhalabe ndi ife. Sikuti onse ali m’gulu lathu ayi, ndipo iwo achoka m’gulu lathu, kuti zimenezi zidziwike.”—1 Yoh. 2:19.
32 Yehova amaona kuti munthu amene wadzilekanitsa ndi wosiyana kwambiri ndi munthu amene wasiya kusonkhana ndiponso kulalikira. Munthu amasiya kusonkhana ndi kulalikira chifukwa cholephera kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. Nthawi zinanso munthu angasiye kutumikira Yehova mwakhama chifukwa chokumana ndi mavuto enaake kapena kuzunzidwa. Akulu komanso anthu ena mu mpingo ayenera kupitiriza kuthandiza Mkhristu amene wasiya kusonkhana ndi kulalikira kuti akhalenso wolimba mwauzimu.—Aroma 15:1; 1 Ates. 5:14; Aheb. 12:12.
33 Koma ngati Mkhristu wadzilekanitsa, pamaperekedwa chilengezo chachidule ku mpingo chonena kuti: “[Dzina la munthuyo] salinso wa Mboni za Yehova.” Munthu wodzilekanitsa amaonedwa mofanana ndi munthu wochotsedwa.
KUBWEZERETSA MUNTHU
34 Munthu wochotsedwa kapena wodzilekanitsa akhoza kubwezeretsedwa mu mpingo ngati atasonyeza umboni woti walapa ndi kuonetsa kwa kanthawi ndithu kuti wasiya khalidwe lake loipa. Akamachita zimenezi amasonyeza kuti akufuna kukhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Akulu ayenera kudikira kuti padutse nthawi yokwanira, mwina miyezi, chaka kapenanso kuposerapo kuti atsimikizire ngati munthuyo walapadi. Bungwe la akulu likalandira kalata ya munthu yopempha kuti abwezeretsedwe, komiti yobwezeretsa idzakambirana naye. Komitiyo iyenera kutsimikizira kuti pali umboni woti munthuyo akuonetsa “ntchito zosonyeza kulapa” ndipo angaone ngati akufunika kumubwezeretsa pa nthawiyo kapena ayi.—Mac. 26:20.
35 Ngati munthu amene akupempha kubwezeretsedwayo anachotsedwera ku mpingo wina, komiti yobwezeretsa ya mpingo womwe akusonkhana, idzakumana ndi munthuyo ndi kumvetsera pempho lake. Ngati komitiyo yaona kuti munthuyo akhoza kubwezeretsedwa, idzafotokozera bungwe la akulu a mpingo womwe unasamalira nkhani yake maganizo awo oti munthuyo akhoza kubwezeretsedwa. Makomiti awiriwo adzagwirira ntchito limodzi pofufuza mfundo zonse zofunika. Komabe, komiti yobwezeretsa ya ku mpingo kumene munthuyo anachotsedwera ndi imene imasankha kuti munthuyo abwezeretsedwedi.
KULENGEZA ZOTI MUNTHU WABWEZERETSEDWA
36 Komiti yobwezeretsa ikatsimikiza kuti munthu wochotsedwayo kapena wodzilekanitsa walapadi ndipo akufunika kubwezeretsedwa, chilengezo choti wabwezeretsedwa chimaperekedwa ku mpingo umene anachotsedwera. Ngati munthuyo anasamukira mpingo wina, chilengezocho chimaperekedwanso ku mpingo wake watsopanowo. Polengeza ayenera kungonena kuti: “[Dzina la munthuyo] wabwezeretsedwa kukhalanso wa Mboni za Yehova.”
MILANDU YA ANA ANG’ONOANG’ONO OBATIZIDWA
37 Ana aang’ono obatizidwa akachita tchimo lalikulu, nkhaniyo iyenera kufotokozedwa kwa akulu. Zingakhale bwino kuti pamene akulu akusamalira milandu ya ana aang’ono obatizidwa, makolo awo obatizidwa azikhalapo. Makolowo ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi komiti yoweruzayo, osati kuikira kumbuyo mwana wawoyo n’cholinga chakuti asalandire chilango. Mofanana ndi milandu ya anthu akuluakulu, komiti yoweruza imayesetsa kupereka malangizo oyenerera n’cholinga choti athandize mwanayo kusintha khalidwe lake. Koma ngati mwanayo sakusonyeza kulapa, amachotsedwa mu mpingo.
OFALITSA OSABATIZIDWA AKACHITA TCHIMO
38 Koma kodi akulu angatani ngati wofalitsa wosabatizidwa wachita tchimo lalikulu? Popeza si Mboni yobatizidwa, sangachotsedwe mu mpingo. N’kutheka kuti sanamvetse mfundo za m’Baibulo ndipo malangizo achikondi akhoza kumuthandiza “kuwongola njira” zake.—Aheb. 12:13.
39 Ngati wofalitsa wosabatizidwa amene wachita tchimo lalikulu sakulapa pambuyo poti akulu awiri ayesetsa kumuthandiza, zingakhale bwino kudziwitsa mpingo. Pamaperekedwa chilengezo chachidule chonena kuti: “[Dzina la munthuyo] salinso wofalitsa wosabatizidwa.” Zikatero mpingo wonse uyenera kumuona ngati munthu wamba yemwe sanaphunzire choonadi. Ngakhale kuti munthuyo sanachotsedwe, Akhristu ayenera kusamala pochita naye zinthu. (1 Akor. 15:33) Munthu wotereyu sayeneranso kumapereka lipoti la utumiki wakumunda.
40 Pakadutsa nthawi, munthu amene anasiyitsidwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa akhoza kufuna kuti akhalenso wofalitsa. Zikatero akulu awiri angaonane naye kuti atsimikizire ngati wasinthadi khalidwe lake. Ngati akuyenereranso kukhala wofalitsa wosabatizidwa, chilengezo chachidule chimaperekedwa chonena kuti: “[Dzina la munthuyo] waikidwanso kukhala wofalitsa wosabatizidwa.”
YEHOVA AMADALITSA ANTHU OYERA AMENE AMAMULAMBIRA MWAMTENDERE
41 Anthu onse amene amagwirizana ndi mpingo wa Mulungu masiku ano amasangalala ndi madalitso auzimu amene Yehova amapereka kwa anthu ake. Tili ndi chakudya chauzimu chamwanaalirenji ndiponso tili ndi madzi ochuluka a choonadi. Kuwonjezera pamenepa, Yehova amatiteteza kudzera m’gulu lake limene likutsogoleredwa ndi Khristu. (Sal. 23; Yes. 32:1, 2) Ngakhale kuti tikukhala m’masiku ovuta otsiriza ano, timaona kuti ndife otetezeka chifukwa choti tili m’Paradaiso wauzimu.
Tikamapitiriza kukhala mwamtendere komanso kuyesetsa kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera, timaonetsa kuwala kwa choonadi cha Ufumu
42 Tikamapitiriza kukhala mwamtendere komanso kuyesetsa kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera, timaonetsa kuwala kwa choonadi cha Ufumu. (Mat. 5:16; Yak. 3:18) Tikamachita zimenezi, Mulungu adzatidalitsa ndipo tidzaona anthu ambiri akuphunzira za Yehova ndiponso kutumikira nafe limodzi pochita chifuniro chake.