Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • od mutu 17 tsamba 169-178
  • Pitirizanibe Kukhala M’gulu la Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizanibe Kukhala M’gulu la Yehova
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIFUKWA CHIYANI MAYESERO AKUCHULUKA MASIKU ANO?
  • TIYESETSE KUPIRIRA
  • KUPIRIRA MAYESERO OSIYANASIYANA
  • TIYESETSE KUKHALABE OKHULUPIRIKA
  • “Mulole Kuti Kupirira Kumalize Kugwira Ntchito Yake”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Chipiriro—Nchofunika kwa Akristu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
  • Chipiriro Chimene Chimapeza Chilakiko
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
od mutu 17 tsamba 169-178

MUTU 17

Pitirizanibe Kukhala M’gulu la Yehova

YAKOBO analemba kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8) Sikuti Yehova sangamvetsere mapemphero athu chifukwa chakuti ndi wapamwamba kwambiri komanso poti amakhala kutali. Iye amamva mapemphero athu ngakhale kuti ndife anthu opanda ungwiro. (Mac. 17:27) Koma kodi tingamuyandikire bwanji Mulungu? Tingamuyandikire ngati timayesetsa kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino polankhulana naye m’pemphero lochokera pansi pa mtima. (Sal. 39:12) Tingalimbitsenso ubwenzi wathu ndi Mulungu pophunzira Mawu ake, Baibulo, nthawi zonse. Kuphunzira Baibulo kumatithandiza kumudziwa bwino Yehova, zolinga zake komanso chifuniro chake. (2 Tim. 3:16, 17) Choncho timaphunzira kumukonda ndipo timaopa kuchita zinthu zomukhumudwitsa.​—Sal. 25:14.

2 Kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, kumatheka kudzera mwa Mwana wake Yesu. (Yoh. 17:3; Aroma 5:10) Palibe munthu amene akanatha kutithandiza kumvetsa bwino maganizo a Yehova kuposa mmene Yesu anachitira. Yesu ankawadziwa bwino kwambiri Atate wake, n’chifukwa chake ananena kuti: “Palibe amene akum’dziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso Atatewo palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.” (Luka 10:22) Choncho tikamaphunzira zokhudza mmene Yesu ankaganizira komanso mmene ankamvera, kuchokera m’Mauthenga Abwino, timakhala tikuphunzira mmene Yehova amaganizira ndi mmene amamvera. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Mulungu.

3 Tingapitirizebe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngati tipitiriza kukhala m’mbali yapadziko lapansi ya gulu lake, lotsogoleredwa ndi Mwana wake, lomwe limatiphunzitsa kuchita chifuniro cha Mulungu. Mogwirizana ndi ulosi wa pa Mateyu 24:45-47, Mbuye, yemwe ndi Yesu Khristu, anasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azipereka “chakudya pa nthawi yoyenera” kwa anthu a m’banja lake. Masiku ano, kapolo wokhulupirika amatipatsa chakudya chauzimu chochuluka. Pogwiritsa ntchito kapoloyu, Yehova amatilangiza kuti tiziwerenga Mawu ake tsiku ndi tsiku, tizisonkhana nthawi zonse komanso tizigwira nawo mwakhama ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mat. 24:14; 28:19, 20; Yos. 1:8; Sal. 1:1-3) Sitiyenera kuona mopepuka ntchito imene kapolo wokhulupirikayu ali nayo. M’malomwake tiyenera kuyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe kuti tikhalebe m’mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova, n’kumatsatira malangizo omwe gululi limatipatsa. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu. Kungatithandizenso kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso tikhale otetezeka ngakhale tikumane ndi mayesero.

N’CHIFUKWA CHIYANI MAYESERO AKUCHULUKA MASIKU ANO?

4 N’kutheka kuti mwakhala mukutumikira Yehova kwa zaka zambiri. Ngati ndi choncho, ndiye kuti mukudziwa bwino tanthauzo la kupirira zinthu zimene zimayesa chikhulupiriro chathu. Komanso ngati mwangoyamba kumene kuphunzira za Yehova ndipo mukusonkhana ndi anthu ake, muyenera kuti mukudziwa zoti Satana Mdyerekezi amatsutsa aliyense amene amagonjera ulamuliro wa Yehova. (2 Tim. 3:12) Choncho kaya mwapirira mayesero aang’ono kapena aakulu, simuyenera kuchita mantha kapena kufooka. Yehova akulonjeza kuti adzakulimbikitsani ndipo m’tsogolo adzakupatsani mphotho ya moyo wosatha, chifukwa cha kupirira kwanu.​—Aheb. 13:5, 6; Chiv. 2:10.

5 M’masiku omaliza a dziko la Satanali, tonsefe tingakumane ndi mavuto osiyanasiyana. Kungoyambira pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, Satana sanaloledwenso kupita kumwamba kumene kuli Yehova. Iye anaponyedwa padziko lapansi limodzi ndi angelo ake oipa. Choncho kuwonjezereka kwa mavuto padzikoli komanso kuzunzidwa kwambiri kwa atumiki a Yehova kukutsimikizira kuti Satana ndi wokwiya kwambiri, ndiponso ndi umboni woti tikukhala m’masiku otsiriza a ulamuliro wake woipawu.​—Chiv. 12:1-12.

6 Satana ndi wokwiya chifukwa anagonjetsedwa komanso chifukwa akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa. Choncho iye ndi ziwanda zake, akuyesetsa mmene angathere kuti asokoneze ntchito yolalikira komanso amafunitsitsa kuwononga mgwirizano wa atumiki a Yehova. Zimenezi zachititsa kuti tikhale pa nkhondo yauzimu, yomwe imafotokozedwa m’Baibulo kuti: “Sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma, maulamuliro, olamulira dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” Choncho kuti tipambane n’kukhalabe ku mbali ya Yehova, tiyenera kuvalabe zida zonse zauzimu ndipo sitiyenera kusiya kumenya nkhondoyi. Tiyenera kukhala ‘osasunthika polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.’ (Aef. 6:10-17) Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tiyenera kupirira.

TIYESETSE KUPIRIRA

7 Kupirira kumatanthauza kulimbana ndi mavuto kapena mayesero. Kumatanthauzanso kukhalabe wolimba pochita zabwino ngakhale tikumane ndi mavuto, kutsutsidwa, kuzunzidwa kapena zinthu zina zimene zingatilepheretse kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu. Kupirira kwachikhristu ndi khalidwe limene tiyenera kuliphunzira ngakhale kuti zimatenga nthawi ndithu. Tikamapita patsogolo mwauzimu, m’pamenenso timakhala opirira kwambiri. Tikamapirira mayesero ang’onoang’ono omwe tingakumane nawo pamene tayamba kutumikira Mulungu, timakhala olimba ndipo tingathe kudzapirira mayesero aakulu m’tsogolo. (Luka 16:10) Sitiyenera kudikira mpaka titakumana ndi mayesero aakulu kuti tidzasonyeze kuti ndife olimba m’chikhulupiriro, m’malomwake tiyenera kukonzekereratu tisanakumane ndi mayeserowo. Pamene mtumwi Petulo ankafotokoza mfundo yakuti tiyenera kuphunzira kupirira komanso makhalidwe ena achikhristu, analemba kuti: “Yesetsani mwakhama kuwonjezera pa chikhulupiriro chanu makhalidwe abwino, pa makhalidwe anu abwino muwonjezerepo kudziwa zinthu, pa kudziwa zinthu kudziletsa, pa kudziletsa kupirira, pa kupirira kudzipereka kwa Mulungu, pa kudzipereka kwa Mulungu kukonda abale, pa kukonda abale, chikondi.”​—2 Pet. 1:5-7; 1 Tim. 6:11.

Timakhala anthu opirira kwambiri tikamagonjetsa mayesero amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku

8 Yakobo anafotokoza m’kalata yake kufunika kophunzira kupirira, kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana, monga mukudziwira kuti chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira. Koma mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.” (Yak. 1:2-4) Yakobo ananena kuti Akhristu ayenera kumasangalala akakumana ndi mayesero chifukwa mayeserowo amawaphunzitsa kupirira. Kodi ndi mmene inuyo mumaonera? Kenako Yakobo anasonyeza kuti kupirira kumagwira ntchito yake, yotithandiza kukhala ndi makhalidwe achikhristu ndiponso kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Timakhala anthu opirira kwambiri tikamagonjetsa mayesero amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Ndiyeno kupirirako kumatithandiza kukhala ndi makhalidwe enanso abwino amene timafunikira kukhala nawo.

9 Tikamapirira timasangalatsa Yehova ndipo n’chifukwa chake adzatipatse mphotho ya moyo wosatha. Yakobo anapitiriza kunena kuti: “Wodala ndi munthu wopirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto ya moyo, umene Yehova analonjeza onse omukonda.” (Yak. 1:12) Choncho tikamapirira tidzapeza moyo. Ndipotu popanda kupirira, sitingathe kutumikira Mulungu, m’malomwake tingayambe kukopeka ndi zinthu za m’dzikoli. Komanso popanda kupirira, sitingakhale ndi mzimu wa Yehova, choncho sitingakhale ndi makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa.

10 Monga Akhristu, kuti tipitirize kupirira m’masiku ovuta ano, tiyenera kumaona moyenera mavuto amene timakumana nawo. Kumbukirani kuti Yakobo analemba kuti: “Sangalalani.” Komatu kuchita zimenezi si kophweka makamaka ngati mavutowo akuchititsa kuti munthu azimva ululu kapena kuvutika maganizo. Koma kumbukirani kuti chofunika ndi moyo wam’tsogolo. Zimene zinachitikira atumwi zingatithandize kuona mmene tingakhalire osangalala tikakumana ndi mavuto. Nkhaniyi imapezeka m’buku la Machitidwe ndipo imati: “Anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno [anawakwapula] ndi kuwalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu, kenako anawamasula. Choncho atumwiwo anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” (Mac. 5:40, 41) Atumwiwo anadziwa kuti kuvutika kwawoko unali umboni woti anamvera lamulo la Yesu ndiponso anasangalatsa Yehova. Kenako patadutsa zaka, pa nthawi imene Petulo ankalemba kalata yake yoyamba, anafotokoza kufunika kovutika chifukwa cha chilungamo.​—1 Pet. 4:12-16.

11 Nkhani ina ndi yokhudza zimene zinachitikira Paulo ndi Sila. Pamene ankachita utumiki wawo waumishonale ku Filipi, anagwidwa ndi kuimbidwa mlandu woti akusokoneza anthu mumzindawo ndiponso akuphunzitsa miyambo yosavomerezeka. Choncho, anawamenya kwambiri ndi kuwatsekera m’ndende. Baibulo limatiuza kuti ali m’ndendemo komanso akumva ululu wa mabala amene anali nawo, “chapakati pa usiku, Paulo ndi Sila anali kupemphera ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo, ndipo akaidi ena anali kuwamva.” (Mac. 16:16-25) Paulo ndi mnzakeyo anaona kuti kuzunzidwa chifukwa cha Khristu kunali koyenera ndiponso kuti unali umboni wakuti ndi okhulupirika pamaso pa Mulungu ndi anthu. Komanso anaona kuti unali mwayi wawo wolalikira uthenga wabwino kwa anthu amene ankafuna kumvetsera. Anthu ena anamvetseradi, moti usiku womwewo, munthu amene ankayang’anira ndendeyo limodzi ndi banja lake anakhala ophunzira. (Mac. 16:26-34) Paulo ndi Sila anakhulupirira Yehova, anadalira mphamvu zake ndipo ankadziwa kuti iye ndi wofunitsitsa kuwalimbikitsa ndi kuwasamalira pa mavuto awo. Mulungu anawasamaliradi ndipo sanawagwiritse fuwa lamoto.

12 Masiku anonso Yehova watipatsa zonse zofunikira kuti zitithandize tikakumana ndi mayesero. Iye amafuna kuti tipirire choncho watipatsa Mawu ake n’cholinga choti tidziwe zolondola zokhudza cholinga chake. Zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. Ndiponso tili ndi mwayi wosonkhana ndi Akhristu anzathu, wotumikira Yehova komanso wokhala naye pa ubwenzi kudzera m’pemphero. Iye amamvetsera mapemphero athu omutamanda komanso omupempha kuti atithandize kukhalabe okhulupirika. (Afil. 4:13) Ndiponso sitiyenera kuiwala mphamvu zimene timapeza tikamaganizira zinthu zimene tikuyembekezera m’tsogolo.​—Mat. 24:13; Aheb. 6:18; Chiv. 21:1-4.

KUPIRIRA MAYESERO OSIYANASIYANA

13 Mayesero amene tikukumana nawo akufanana ndi omwe ophunzira a Yesu oyambirira ankakumana nawo. Masiku ano, a Mboni za Yehova amazunzidwa komanso kutsutsidwa ndi anthu amene anauzidwa zolakwika zokhudza Mboni za Yehova. Ngati mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, atsogoleri azipembedzo ndi omwe amayambitsa kuti Akhristu azizunzidwa. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti zinthu zimene atsogoleri amenewa amachita n’zoipa komanso kuti zimene amaphunzitsa n’zabodza. (Mac. 17:5-9, 13) Nthawi zina a Mboni za Yehova amayesa kupempha maboma kuti awapatse ufulu wawo mogwirizana ndi malamulo. (Mac. 22:25; 25:11) Koma olamulira ena amaperekabe malamulo oletsa ntchito yathu n’cholinga choti athetse utumiki wathu wachikhristu. (Sal. 2:1-3) Zikatero, molimba mtima timatsatira chitsanzo cha atumwi amene anati: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Mac. 5:29.

14 Pamene mzimu wokonda kwambiri dziko lako ukuwonjezeka padziko lonse, atumiki a Mulungu amene amalalikira uthenga wabwino akukumana ndi mavuto ofuna kuwalepheretsa utumiki wawo umene Mulungu anawapatsa. Atumiki onse a Mulungu amamvera chenjezo lopezeka pa Chivumbulutso 14:9-12, lokhudza kulambira “chilombo ndi chifaniziro chake.” Timadziwa kufunika kwa mawu a Yohane akuti: “Kwa oyerawo, amene akusunga malamulo a Mulungu ndi kutsatira chikhulupiriro cha Yesu, apa ndiye pofunika kupirira.”

15 Mayesero obwera chifukwa cha nkhondo, kuukira boma, kuzunzidwa kwa Akhristu, ndi kuletsedwa kwa ntchito yathu, angapangitse kuti zikhale zovuta kuti tipitirize kulambira Mulungu poyera. Nthawi zina sizingatheke kusonkhana pamodzi ngati mpingo. Sizingathekenso kulankhulana ndi ofesi ya nthambi, kuchezeredwa ndi woyang’anira dera ndiponso mwina sizingatheke kulandira mabuku. Zinthu ngati zimenezi zitachitika, kodi mungatani?

16 Yankho ndi loti muyenera kuyesetsa kuchita chilichonse chimene mungathe malinga ndi mmene zinthu zilili. Mutha kumaphunzira panokha. Mukhozanso kumakumana m’timagulu ting’onoting’ono m’nyumba za abale n’kupanga misonkhano. Pa misonkhanoyo mungagwiritse ntchito Baibulo ndi mabuku a m’mbuyomu amene anaphunziridwa kale. Koma simuyenera kuda nkhawa kwambiri chifukwa abale a m’Bungwe Lolamulira amayesetsa mwamsanga kupeza njira yolankhulirana ndi abale audindo.

17 Komanso ngakhale mutakhala kuti muli kwanokha kopanda m’bale kapena mlongo aliyense, muzikumbukira kuti muli ndi Yehova ndi Mwana wake, Yesu Khristu. Muyenera kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba. Yehova adzapitiriza kumva mapemphero anu ndipo adzakulimbikitsani ndi mzimu wake choncho muzimudalira kuti azikutsogolerani. Muzikumbukiranso kuti ndinu mtumiki wa Yehova ndiponso wophunzira wa Yesu Khristu choncho muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu polalikira. Mukamachita zimenezi, Yehova adzakudalitsani ndipo anthu ena angayambe kulambira nanu limodzi Yehova.​—Mac. 4:13-31; 5:27-42; Afil. 1:27-30; 4:6, 7; 2 Tim. 4:16-18.

18 Ngakhale mutaopsezedwa kuti muphedwa ngati mmene zinalili ndi atumwi ndi atumiki ena, dalirani “Mulungu amene amaukitsa akufa.” (2 Akor. 1:8-10) Kukhulupirira lonjezo lakuti akufa adzaukitsidwa, kungakuthandizeni kupirira ngakhale muzunzidwe modetsa nkhawa. (Luka 21:19) Khristu Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndipo anadziwa kuti kukhulupirika kwake pamene ankayesedwa kungalimbikitse enanso kuti apirire. Kupirira kwanunso kukhoza kulimbikitsa abale anu.​—Yoh. 16:33; Aheb. 12:2, 3; 1 Pet. 2:21.

19 Kuwonjezera pa kuzunzidwa ndi kutsutsidwa, palinso zovuta zina zimene mufunika kuzipirira. Mwachitsanzo, ena amafooka chifukwa cha kupanda chidwi kwa anthu a m’gawo lawo. Ena akuvutika ndi matenda aakulu, matenda a maganizo, pamene ena akulephera kuchita zinthu zina chifukwa cha kufooka kwa thupi. Mtumwi Paulonso ankafunika kupirira vuto linalake limene linkamusowetsa mtendere mpaka nthawi zina linkasokoneza utumiki wake. (2 Akor. 12:7) Nayenso Epafurodito yemwe anali Mkhristu wa mu mpingo wa ku Filipi, ‘anavutika maganizo chifukwa [anzake] anamva kuti anali kudwala.’ (Afil. 2:25-27) Kupanda ungwiro kwathu komanso kwa anthu ena, kungachititse mavuto ena ovuta kuwapirira. Pangakhale kusagwirizana pakati pa Akhristu ena mu mpingo kapenanso pakati pa anthu a banja limodzi. Koma mukhoza kupirira ndi kupambana polimbana ndi mavuto ngati amenewa ngati mungagwiritse ntchito malangizo a m’Mawu a Yehova.​—Ezek. 2:3-5; 1 Akor. 9:27; 13:8; Akol. 3:12-14; 1 Pet. 4:8.

TIYESETSE KUKHALABE OKHULUPIRIKA

20 Tiyenera kuyesetsa kutsanzira Yesu Khristu, yemwe Yehova wamusankha kukhala Mutu wa mpingo. (Akol. 2:18, 19) Tiyenera kugwira ntchito mogwirizana ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi anthu amene apatsidwa udindo woyang’anira. (Aheb. 13:7, 17) Tikamatsatira malangizo a gulu la Mulungu ndi kumvera amene amatitsogolera, tidzakhala m’gulu la anthu ochita chifuniro cha Yehova. Tiyeneranso kugwiritsa bwino ntchito mwayi womwe tili nawo wopemphera kwa Mulungu. Kumbukirani kuti ngakhale makoma a ndende sangatilepheretse kulankhulana ndi Atate wathu wakumwamba komanso sangathe kusokoneza mgwirizano umene tili nawo ndi Akhristu anzathu.

21 Tiyeni tiyesetse kugwira ntchito yathu yolalikira ndi mtima wonse ndiponso mopirira. Tizilimbikira kugwira ntchito imene Yesu Khristu anasiyira otsatira ake pamene anawauza kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Mofanana ndi Yesu, tiyeni tipirire ndipo tiziyembekezera Ufumu ndi moyo wosatha zomwe zikubwera posachedwapa. (Aheb. 12:2) Monga ophunzira a Khristu obatizidwa, tili ndi mwayi wokwaniritsa nawo ulosi wa Yesu wonena za “mapeto a nthawi ino.” Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:3, 14) Tikamagwira nawo mwakhama ntchito yolalikirayi, tidzakhala ndi mwayi wolandira moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama la Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena