MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA
Chigawo Choyamba: Zimene Akhristu Amakhulupirira
Kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kwakuthandizani kudziwa choonadi. Zimene mwaphunzira zakuthandizani kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso zakupatsani chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha m’tsogolo limodzi ndi madalitso a m’dziko lapansi la paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. Panopo, mumakhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu ndipo mwapeza madalitso ambiri chifukwa chosonkhana ndi abale mumpingo. Ndiponso mwadziwa mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ake masiku ano.—Zek. 8:23.
Pamene mukukonzekera kubatizidwa, mudzapindula kwambiri pokambirana ndi akulu zimene Akhristu amakhulupirira. (Aheb. 6:1-3) Yehova apitirize kukudalitsani pamene mukuyesetsa kuphunzira Mawu ake kuti mumudziwe bwino ndiponso kuti mudzalandire mphotho imene walonjeza.—Yoh. 17:3.
1. N’chifukwa chiyani mukufuna kubatizidwa?
2. Kodi Yehova ndi ndani?
• “Yehova ndiye Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi. Palibenso wina.”—Deut. 4:39.
• “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”—Sal. 83:18.
3. N’chifukwa chiyani muyenera kumagwiritsa ntchito dzina la Mulungu?
• “Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’”—Mat. 6:9.
• “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Aroma 10:13.
4. Kodi Baibulo limagwiritsanso ntchito mayina ena ati ponena za Yehova?
• “Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.”—Yes. 40:28.
• “Atate wathu wakumwamba.”—Mat. 6:9.
• “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yoh. 4:8.
5. Kodi Yehova Mulungu mungamupatse chiyani?
• “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.”—Maliko 12:30.
• “Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”—Luka 4:8.
6. N’chifukwa chiyani mumafuna kukhala okhulupirika kwa Yehova?
• “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miy. 27:11.
7. Kodi mumapemphera kwa ndani, ndipo kudzera m’dzina la ndani?
• “Ndithudi ndikukuuzani, ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yoh. 16:23.
8. Kodi zinthu zina zimene tingatchule popemphera ndi ziti?
• “Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira. Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.’”—Mat. 6:9-13.
• “Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”—1 Yoh. 5:14.
9. Kodi n’chiyani chingachititse kuti Yehova asamvetsere mapemphero a munthu?
• “Adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha. . . . chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.”—Mika 3:4.
• “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”—1 Pet. 3:12.
10. Kodi Yesu Khristu ndi ndani?
• “Poyankha, Simoni Petulo ananena kuti: ‘Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.’”—Mat. 16:16.
11. N’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi?
• “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.”—Mat. 20:28.
• “Iye [Yesu] anawauza kuti: ‘Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.’”—Luka 4:43.
12. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira nsembe ya Yesu?
• “Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.”—2 Akor. 5:15.
13. Kodi Yesu ali ndi ulamuliro wotani?
• “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”—Mat. 28:18.
• “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.”—Afil. 2:9.
14. Kodi mumakhulupirira kuti Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene anaikidwa ndi Yesu?
• “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?”—Mat. 24:45.
15. Kodi mzimu woyera ndi munthu?
• “Poyankha mngeloyo anauza Mariya kuti: ‘Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.’”—Luka 1:35.
• “Choncho ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.
16. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mzimu wake woyera?
• “Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova, ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.”—Sal. 33:6.
• “Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Mac. 1:8.
• “Ulosi wa m’Malemba suchokera m’maganizo a munthu. Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”—2 Pet. 1:20, 21.
17. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?
• “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Dan. 2:44.
18. Kodi mudzapindula bwanji ndi Ufumu wa Mulungu?
• “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chiv. 21:4.
19. Kodi mukudziwa bwanji kuti madalitso a Ufumu wa Mulungu abwera posachedwapa?
• “Atakhala pansi m’phiri la Maolivi, ophunzira anafika kwa iye mwamseri ndi kunena kuti: ‘Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?’ Poyankha Yesu ananena kuti: ‘. . . Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.’”—Mat. 24:3, 4, 7, 14.
• “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.”—2 Tim. 3:1-5.
20. Kodi mungasonyeze bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwa inuyo?
• “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake.”—Mat. 6:33.
• “Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo ndipo anditsatire mosalekeza.’”—Mat. 16:24.
21. Kodi Satana komanso ziwanda ndi ndani?
• “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi . . . Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake.”—Yoh. 8:44.
• “Chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”—Chiv. 12:9.
22. Kodi Satana amamunamizira chiyani Yehova komanso anthu amene amalambira Yehovayo?
• “Pamenepo mkaziyo anayankha njokayo kuti: ‘Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, “Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.”’ Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: ‘Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.’”—Gen. 3:2-5.
• “Satana anamuyankha Yehova kuti: ‘Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.’”—Yobu 2:4.
23. Kodi mungasonyeze bwanji kuti zimene Satana amanenazi ndi zabodza?
• “Um’tumikire [Mulungu] ndi mtima wathunthu.”—1 Mbiri 28:9.
• “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.
24. N’chifukwa chiyani anthu amafa?
• ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’—Aroma 5:12.
25. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?
• “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.”—Mlal. 9:5.
26. Kodi pali chiyembekezo chotani chokhudza anthu amene anamwalira?
• “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Mac. 24:15.
27. Kodi ndi angati amene amapita kumwamba kukalamulira ndi Yesu?
• “Ndinaona Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.”—Chiv. 14:1.