MUTU 39
Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli
Yehova anapatsa Aisiraeli oweruza kuti aziwatsogolera. Koma iwo ankafuna atakhala ndi mfumu. Ndiyeno anauza Samueli kuti: ‘Anthu a mitundu yonse ali ndi mafumu. Ifenso tikufuna tikhale ndi mfumu.’ Zimenezi sizinamusangalatse Samueli, choncho anapemphera kwa Yehova za nkhaniyi. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Anthuwa sanakane iweyo koma akukana ine. Uwauze kuti n’zotheka kuti akhale ndi mfumu koma adziwe kuti mfumuyo izidzafuna zambiri kuchokera kwa iwo.’ Koma anthuwo anati: ‘Zilibe kanthu, ife tikufuna mfumu basi.’
Yehova anamuuza Samueli kuti Sauli ndi amene akhale mfumu yoyamba. Choncho Samueli anadzoza Sauli pomuthira mafuta pamutu pamene Sauliyo anapita ku Rama kukamuona.
Kenako, Samueli anaitana Aisiraeli onse kuti awaonetse mfumu yawo. Koma Sauli sankapezeka. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Chifukwa iye anali atabisala pakati pa katundu. Ndiyeno atamupeza, anamuimiritsa pakati pa anthu. Sauli anali wooneka bwino kwambiri komanso wamtali kuposa aliyense. Samueli anati: ‘Kodi mwaona munthu amene Yehova wamusankha?’ Anthuwo anafuula kuti: ‘Mfumu ikhale ndi moyo wautali!’
Poyamba Sauli ankamvera Samueli komanso Yehova koma kenako anasiya. Mwachitsanzo, mfumu sinkayenera kupereka nsembe. Nthawi ina, Samueli anauza Mfumu Sauli kuti amudikire, koma iye ankaona kuti akuchedwa. Choncho Sauli anaganiza zoti apereke yekha nsembezo. Ndiye kodi Samueli anatani? Iye anamuuza kuti: ‘Apatu simunachite bwino, simunamvere Yehova.’ Koma Sauli sanaphunzirepo kanthu.
Nthawi ina, Sauli atapita kukamenyana ndi Aamaleki, Samueli anamuuza kuti akawononge chilichonse m’dzikolo. Koma Sauli sanaphe mfumu yakumeneko dzina lake Agagi. Yehova anauuza Samueli kuti: ‘Sauli wasiya kunditsatira ndipo sakundimvera.’ Samueli atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri ndipo anapita kukauza Sauli kuti: ‘Chifukwa simukumvera Yehova, iye asankha mfumu ina.’ Pamene Samueli ankatembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mkanjo wake ndipo unang’ambika. Zitatero, Samueli anamuuza kuti: ‘Yehova wang’amba ufumu n’kuuchotsa kwa iwe.’ Yehova anakonza zoti adzapereke ufumuwo kwa munthu amene amamukonda komanso kumumvera.
“Kumvera kumaposa nsembe.”—1 Samueli 15:22