Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 50 tsamba 120-tsamba 121 ndime 5
  • Yehova Anathandiza Mfumu Yehosafati

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Anathandiza Mfumu Yehosafati
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yehosafati Adalira Yehova
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Khalani Achangu pa Nyumba ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Apereka Chiweruzo m’Chigwa Chotsirizira Mlandu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Zimene Zili Mʼbuku la 2 Mbiri
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 50 tsamba 120-tsamba 121 ndime 5
Mfumu Yehosafati ndi gulu la oimba akutsogolera gulu la nkhondo kutuluka mu Yerusalemu

MUTU 50

Yehova Anathandiza Mfumu Yehosafati

Yehosafati anali mfumu ya Yuda ndipo anagumula malo operekera nsembe a Baala komanso anawononga mafano onse m’dzikolo. Iye ankafuna kuti anthu adziwe malamulo a Yehova. Choncho anatumiza akalonga ndi Alevi kuti akaphunzitse anthu malamulo a Yehova mu Yuda monse.

Anthu a m’mayiko oyandikana ndi Ayuda ankaopa kuwaukira chifukwa ankadziwa kuti Yehova ali nawo. Anthuwo mpaka ankapereka mphatso kwa Mfumu Yehosafati. Koma Amowabu, Aamoni ndi anthu ochokera ku Seiri anabwera kuti adzamenyane ndi Ayuda. Apa Yehosafati anadziwiratu kuti akufunika kuthandizidwa ndi Yehova. Zitatero anaitanitsa amuna, akazi ndi ana kuti abwere ku Yerusalemu. Anthuwo atafika, iye anapemphera kuti: ‘Yehova, popanda inu sitingapambane nkhondoyi. Chonde tithandizeni chifukwa sitikudziwa chochita.’

Yehova anayankha pempherolo kuti: ‘Musaope chifukwa ndikuthandizani. Aliyense angoima pamalo ake nʼkuona mmene ndingakupulumutsireni.’ Kodi Yehova anawathandiza bwanji?

Tsiku lotsatira, Yehosafati anasankha anthu oimba n’kuwauza kuti aziyenda patsogolo pa asilikali. Anthuwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu mpaka ku Tekowa komwe kunachitikira nkhondoyo.

Iwo ankaimbira Yehova mokweza ndipo iye anamenyera nkhondo anthu ake. Anachititsa kuti Amowabu ndi Aamoni ayambe kuphana okhaokha ndipo palibe amene anapulumuka. Yehova anateteza anthu a ku Yuda, asilikali komanso ansembe. Anthu a m’mayiko oyandikana ndi Ayuda anamva zimene Yehova anachitazi ndipo anadziwa kuti iye akuthandizabe anthu ake. Kodi Yehova amapulumutsa bwanji anthu ake? Amawapulumutsa m’njira zosiyanasiyana ndipo safunika kuthandizidwa ndi anthu kuti achite zimenezi.

“Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo. Aliyense angoima pamalo ake nʼkuona mmene Yehova angakupulumutsireni.”​—2 Mbiri 20:17

Mafunso: Kodi Yehosafati anali mfumu yotani? Kodi Yehova anatani pothandiza Ayuda?

2 Mbiri 17:1-19; 20:1-30

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena