MUTU 67
Mpanda wa Yerusalemu Unamangidwanso
Zimene tafotokoza m’mutu wapitawu zisanachitike, panachitikanso zinthu zina. Nehemiya anali Mwisiraeli ndipo ankagwira ntchito kwa Mfumu Aritasasita ku Susani. Ndiyeno mchimwene wake anafika kuchokera ku Yuda n’kumuuza kuti: ‘Anthu amene anabwerera ku Yerusalemu ali pa mavuto. Mpanda wa mzinda umene Ababulo anauwononga sunakonzedwe.’ Nehemiya anakhumudwa kwambiri. Iye anaganiza zopita ku Yerusalemu kuti akathandize anthuwo ndiye anapemphera kuti mfumu imulole kupita.
Kenako mfumu inazindikira kuti Nehemiya sakusangalala. Ndiyeno inamufunsa kuti: ‘Ukuoneka wachisoni. Watani?’ Nehemiya anayankha kuti: ‘Ndilekerenji kuoneka wachisoni pamene mzinda wathu wa Yerusalemu suli bwino.’ Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ndiye ukufuna ndikuchitire chiyani?’ Nthawi yomweyo Nehemiya anapemphera chamumtima. Kenako anati: ‘Mungandilole kuti ndipite ku Yerusalemu kukamanga mpanda?’ Mfumuyo inamulola ndipo inaonetsetsa kuti akhale wotetezeka pa ulendo wake wonsewo. Inalamulanso kuti iye akhale bwanamkubwa wa Yuda ndipo anamupatsa matabwa oti akakonzere zitseko zapageti.
Nehemiya atafika ku Yerusalemu anayendera mpanda wonse. Kenako anasonkhanitsa ansembe ndi atsogoleri n’kuwauza kuti: ‘Akuluakulu, zinthu sizili bwino. Tiyenera kumanganso mpandawu.’ Anthuwo anavomera ndipo ntchito inayambika.
Koma adani a Aisiraeli ankawaseka n’kumati: ‘Nkhandwetu ikhoza kugwetsa kampanda kanuko.’ Koma Aisiraeliwo sanasamale zimenezi ndipo anapitiriza kugwira ntchitoyo. Ankamanga bwinobwino mpandawo ndipo unkaoneka wolimba.
Adaniwo anaganiza zoukira Yerusalemu kuchokera m’mbali zosiyanasiyana. Ayuda atamva zimenezo anachita mantha. Koma Nehemiya anawauza kuti: ‘Musaope. Yehova atithandiza.’ Ndiyeno anaika alonda oti aziteteza anthu amene ankagwira ntchitowo, moti adaniwo sanawaukire.
Patangotha masiku 52 ntchito yonse yomanga mpanda komanso kukonza mageti inatha. Ndiyeno Nehemiya anaitanitsa Alevi onse ku Yerusalemu kuti adzautsegulire. Anakonza zoti pakhale magulu awiri oimba. Maguluwa anadutsa pamalo okwera a mpandawo pamasitepe a Geti la Kukasupe ndipo kenaka analowera mbali zosiyana kuzungulira mzindawo. Ankaimba nyimbo zotamanda Yehova pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze. Ezara ndi gulu lina anapita mbali ina ya mzindawo ndipo Nehemiya ndi gulu lina anapita mbali ina. Magulu awiriwa anakumana pamalo amene panali kachisi. Kenako anthu onse, amuna, akazi ndi ana omwe, anapereka nsembe kwa Yehova ndipo anachita chikondwerero. Panali phokoso lachisangalalo.
“Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.”—Yesaya 54:17